1922—Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo
“MULUNGU . . . amatithandiza kuti tipambane kudzera mwa . . . Yesu Khristu.” (1 Akor. 15:57) Mawu amenewa omwe anali lemba la chaka la 1922, anatsimikizira Ophunzira Baibulo kuti Yehova adzawapatsa mphoto chifukwa cha kukhulupirika kwawo. M’chaka chimenecho, iye anadalitsadi alaliki akhamawa. Anawadalitsa pamene anayamba kusindikiza okha mabuku awo komanso kugwiritsa ntchito wailesi pofalitsa uthenga wa Ufumu. Zimene zinachitikanso pambuyo pake m’chaka chomwecho zinasonyeza kuti Yehova ankadalitsa anthu ake. Ophunzira Baibulo anasonkhana pamodzi pamsonkhano wosaiwalika womwe unachitikira ku Cedar Point, ku Ohio, U.S.A. Zimene zinachitika pamsonkhanowu zinakhudza ntchito ya gulu la Yehova kuchokera nthawi imeneyo mpaka pano.
“ANALI MAGANIZO OSANGALATSA”
Pamene ntchito yolalikira inkakula, pankafunikanso mabuku ambiri. Abale ku Beteli ya ku Brooklyn ankasindikiza magazini koma ankadalira makampani ena kuti aziwasindikizira mabuku a zikuto zolimba. Ndiyeno kwa miyezi yambiri, kampani imene inkathandiza posindikiza mabuku inkalephera kusindikiza mabuku okwanira oti azigwiritsidwa ntchito polalikira. Choncho M’bale Rutherford anafunsa M’bale Robert Martin, yemwe anali woyang’anira fakitale yathu, ngati zinali zotheka kuti azisindikizanso okha mabuku.
M’bale Martin anafotokoza kuti, “Amenewa anali maganizo osangalatsa chifukwa zinkatanthauza kuti tinkafunika kukhala ndi fakitale yathuyathu yosindikiza mabuku.” Choncho abale anagula malo ku 18 Concord Street ku Brooklyn komanso zipangizo zina zonse zofunikira.
Komabe si onse amene anasangalala ndi zimene zinachitikazi. Pulezidenti wa kampani imene inkasindikiza mabuku athu ija, anabwera kudzayendera malo athuwa. Iye anati: “Muli ndi zipangizo zabwino kwambiri zosindikizira mabuku, koma palibe olo mmodzi yemwe akudziwa mmene mungazigwiritsire ntchito. Pakamatha miyezi 6, zonsezi zikhala zitawonongeka.”
M’bale Martin anati: “Zomwe ananenazi zinkaoneka ngati zomveka. Koma ife tinkadziwa kuti Yehova ndi amene atithandize ndipo anatithandizadi.” M’bale Martin ankanena zoona chifukwa posakhalitsa, mashini atsopanowa ankasindikiza mabuku 2,000 pa tsiku.
KULALIKIRA ANTHU AMBIRI KUDZERA PAWAILESI
Kuwonjezera pa kusindikiza okha mabuku, anthu a Yehova anayamba kugwiritsa ntchito wailesi polalikira uthenga wabwino. Lamlungu masana pa 26 February, 1922, M’bale Rutherford analankhula kwa nthawi yoyamba pawailesi. Iye anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Anthu Mamiliyoni
Ambiri Amene Ali Ndi Moyo Sadzafa,” pawailesi ya KOG ku Los Angeles, ku California, U.S.A.Anthu pafupifupi 25,000 anamvetsera nkhaniyi. Anthu ena analemba makalata poyamikira pulogalamuyi. Imodzi mwa makalatawo inachokera kwa Willard Ashford wa ku Santa Ana, ku California. Iye anayamikira M’bale Rutherford chifukwa cha nkhani “yolimbikitsa komanso yosangalatsa.” Iye anawonjezera kuti: “M’banja mwathu munali anthu atatu omwe ankadwala. Choncho sizikanatheka kumvetsera nkhani yanuyi zikanakhala kuti sinaulutsidwe pawailesi, ngakhale zikanakhala kuti mumakambira kufupi ndi kwathu kuno.”
M’milungu yotsatira, mapulogalamu ambiri anayamba kuulutsidwa pawailesiyi. Pamene chakachi chinkatha, lipoti la mu Nsanja ya Olonda linasonyeza kuti anthu pafupifupi 300,000 anali atamva uthenga wabwino kudzera pawailesi.
Ophunzira Baibulo analimbikitsidwa kwambiri ndi zimenezi. Choncho anaganiza zokhala ndi wailesi yawoyawo ku Staten Island, kufupi ndi Beteli ya ku Brooklyn. M’zaka zotsatira, iwo anayamba kugwiritsa ntchito wailesi ya WBBR, kuti athe kufalitsa uthenga wabwino kwa anthu ambiri komanso kumadera ambiri.
“ADV”
Nsanja ya Olonda ya June 15, 1922, inalengeza kuti padzakhala msonkhano waukulu womwe udzachitikire ku Cedar Point ku Ohio, kuyambira pa 5 mpaka 13 September, 1922. Ophunzira Baibulo anasangalala kwambiri pomwe anafika ku Cedar Point.
Munkhani yake yotsegulira msonkhanowu, M’bale Rutherford anauza anthu onse omwe anabwerawo kuti: “Sindikukayikira kuti Ambuye . . . adalitsa msonkhanowu ndipo uchititsa kuti uthenga wabwino ulalikidwe padzikoli kuposa kale lonse.” Okamba nkhani onse pamsonkhanowu, ankalimbikitsa abale ndi alongo kuti azigwira ntchito yolalikira.
Lachisanu pa 8 September, anthu pafupifupi 8,000, omwe anadzaza muholo yomwe munkachitikira msokhanowu, ankayembekezera mwachidwi kumva nkhani ya M’bale Rutherford. Iwo ankayembekezera kuti iye afotokoza tanthauzo la mawu akuti “ADV,” omwe anali patimapepala
towaitanira kumsonkhanowo. Pamene anthuwo ankakhala pansi, n’kutheka kuti ena anaona kuti kutsogolo pamwamba pa pulatifomu panali chinsalu chokulungidwa. Arthur Claus, yemwe anabwera kumsonkhanowu kuchokera kwawo ku Tulsa, ku Oklahoma, U.S.A., anapeza malo abwino n’cholinga choti azimvetsera bwinobwino, popeza kuti pa nthawiyo kunalibe zokuzira mawu.“Tinkamvetsera mwatcheru liwu lililonse”
Pofuna kuti pasakhale zosokoneza, tcheyamani analengeza kuti aliyense wobwera mochedwa sakanaloledwa kulowa muholo ya msonkhanoyo pa nthawi ya nkhani ya M’bale Rutherford. Pa nthawi ya 9:30 m’mawa, M’bale Rutherford anayamba nkhani yake potchula mawu a Yesu a pa Mateyu 4:17 akuti: “Ufumu wakumwamba wayandikira.” Pofotokoza zimene zidzachitike kuti anthu amve za Ufumuwu, iye anati: “Yesu mwiniyo ananena kuti pa nthawi ya kukhalapo kwake, adzagwira ntchito yokolola kuti asonkhanitse anthu ake okhulupirika.”
Pokumbukira zimene zinachitika pa nthawiyo, M’bale Claus, yemwe anali muholo ya msonkhanoyo ananena kuti: “Tinkamvetsera mwatcheru liwu lililonse.” Koma mwadzidzidzi M’bale Claus anadwala ndipo anafunika kutuluka muholoyo. Iye anatuluka muholoyo ngakhale kuti sankafuna chifukwa ankadziwa kuti saloledwanso kulowa.
Patangopita maminitsi ochepa, anayamba kupeza bwino. Iye anafotokoza kuti akuyenda kubwerera kuholo ya msonkhanoyo, anamva anthu akuwomba m’manja kwambiri. Zimenezi zinamusangalatsa moti anaganiza zoti amvetserebe mbali yotsala ya nkhaniyi ngakhale kuti anafunika kukwera padenga kuti zimenezi zitheke. M’bale Claus yemwe anali ndi zaka 23 pa nthawiyo, anapeza njira yokwerera padengapo. Padenga pa holoyi panali mawindo omwe anali otsegula ndipo anaona kuti “nkhani yonse inkamveka bwinobwino pamwambapo.”
Koma M’bale Claus sanali yekha pamwambapo. Anapezaponso anzake ena. M’modzi wa iwo,
dzina lake Frank Johnson, anafunsa M’bale Claus kuti, “Kodi uli ndi mpeni wakuthwa?”M’bale Claus anayankha kuti: “Eya ndili nawo.”
Frank anati: “Ndiwe yankho la pemphero lathu. Ukuona chinsalu chachikulu chakulungidwachi? Chamangidwa kumisomali ili apayi. Uzimumvetsera mwatcheru Jajiyu. * Akangonena kuti, ‘choncho lengezani, lengezani,’ udule zingwe 4 izi.”
Choncho M’bale Claus, mpeni uli m’manja, ankadikirira kuti nthawiyi ifike. Posakhalitsa nkhani ya M’bale Rutherford inafika pachimake. Mwansangala komanso mwamphamvu, M’bale Rutherford analankhula mofuula kuti: “Mukhale mboni za Ambuye zokhulupirika komanso zoona. Pitirizani kumenya nkhondo mpaka mbali iliyonse ya Babulo itawonongedwa. Lengezani uthengawu kwina kulikonse. Dziko lonse lidziwe kuti Yehova ndiye Mulungu ndipo Yesu Khristu ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. Lero ndi tsiku lalikulu kuposa masiku onse. Onani, Mfumu yayamba kale kulamulira! Ndipo inu ndi atumiki ake olengeza za Ufumuwu. Choncho, lengezani, lengezani, lengezani za Mfumu ndi Ufumu wake!”
M’bale Claus anafotokoza kuti iye limodzi ndi abale ena aja anadula zingwe zija ndipo chinsalucho chinatambasuka pang’onopang’ono. Mogwirizana ndi zilembo zakuti “ADV” zija, pachinsalucho panali mawu akuti: “Lengezani za Mfumu ndi Ufumu wake.”
NTCHITO YOFUNIKA KWAMBIRI
Msonkhano wa ku Cedar Point unathandiza abale kuti aziona ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu kukhala yofunika ndipo anthu ofunitsitsa ankasangalala kugwira nawo ntchitoyi. Kopotala wina (panopa timati mpainiya) wa ku Oklahoma, U.S.A., analemba kuti, “Tinkalalikira m’dera la migodi ya malasha komwe anthu anali osauka kwambiri.” Iye anafotokoza kuti nthawi zambiri anthu akamva uthenga wopezeka m’magazini ya Golden Age, yomwe panopa timati Galamukani!, “ankagwetsa misozi.” Iye anati, “Tinkasangalala chifukwa tinkatha kuwatonthoza.”
Ophunzira Baibulo ankadziwa kufunika kwa mawu a Yesu a pa Luka 10:2, akuti: “Zokolola n’zochulukadi, koma antchito ndi ochepa.” Pamene chakachi chinkatha, iwo anali atatsimikiza mtima kuposa kale kuti alengeze uthenga wa Ufumu kwina kulikonse.
^ Nthawi zina M’bale Rutherford ankadziwika kuti “Jaji” chifukwa anagwirapo ntchitoyi ku Missouri, U.S.A.