Kusindikiza Mabuku Ofotokoza Baibulo Mkati mwa Chiletso
Kusindikiza Mabuku Ofotokoza Baibulo Mkati mwa Chiletso
MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI MALCOLM G. VALE
“Sindikiza buku la Children.” Ndinalandira chilangizochi kuchokera kwa woyang’anira nthambi wa Mboni za Yehova mu Australia mkati mwa Nkhondo Yadziko II, bukulo litangotulutsidwa kumene pamsonkhano wa pa August 10, 1941, ku St. Louis, Missouri, U.S.A. Kodi nchifukwa ninji chilangizochi chinali chodabwitsa?
EYA, ntchito yathu yolalikira inali italetsedwa mu January 1941, chotero kusindikizabe mabuku ngakhale oŵerengeka kukanakhala thayo lovuta. Ndiponso, bukulo Children linali lamasamba 384 la zithunzithunzi za maonekedwe a mtundu wachibadwa. Makina athu osindikizira anafunikira kukhala atsopano, mapepala ake anali ovuta kupeza, ndipo antchito ake analibe luso losindikiza mabuku achikuto cholimba.
Ndisanafotokoze mmene tinakhozera kusindikiza mabuku mkati mwa chiletso, imani ndikuuzeni mmene ndinakhalira wotumikira mogwirizana ndi ofesi ya nthambi ya Australia monga woyang’anira ntchito yosindikiza.
Chiyambi Changa
Atate wanga anali ndi bizinesi yosindikiza mabuku yopita patsogolo m’mzinda wa Ballarat, Victoria, kumene ndinabadwira mu 1914. Chotero ndinaphunzira ntchito yosindikiza mabuku pogwira ntchito m’nyumba yosindikizira ya Atate. Ndinaloŵanso m’zochitika za Tchalitchi cha Mangalande, ndikumaimba m’kwaya ya tchalitchi ndi kuliza mabelu atchalitchi. Ndinalidi ndi mwaŵi wa kuyembekezera kuphunzitsa Sande sukulu, komatu ndinali ndi mantha ndi zimenezi.
Chifukwa chake chinali chakuti ndinali ndi zikayikiro zazikulu ponena za ziphunzitso zina za tchalitchi. Zimenezi zinaphatikizapo
Utatu, moto wa helo, ndi kusafa kwa moyo wa munthu, ndipo palibe munthu amene anandiyankha mokhutiritsa. Zinandidabwitsanso kuti kaŵirikaŵiri mbusa wathu wachipembedzo analankhula mokalipa ponena za kagulu kena kachipembedzo kamene kankadzitcha kuti Mboni za Yehova. Ndinadabwa chifukwa chake kagulu kakang’ono motero kanadetsa nkhaŵa mzinda wa anthu 40,000.Tsiku lina la Sande, ndinaima kunja kwa tchalitchi mapemphero a mmaŵa atatha pamene kagulu kena ka asungwana ochokera pa Tchalitchi cha Methodist chimene chinali pafupi anadutsa. Ndiyamba kuyanjana ndi mmodzi wa iwo. Dzina lake linali Lucy, ndipo potsirizira anandiitana kwawo kuti ndikadziŵane ndi makolo ake. Tayerekezerani kudabwa kwanga pamene ndinadziŵa kuti amake, a Vera Clogan, anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Tinkakambitsirana nkhani za Baibulo zambiri, ndipo zimene ankanena zinalidi zanzeru.
Posakhalitsa, Lucy ndi ine tinakwatirana, ndipo podzafika 1939 tinali kukhala ku Melbourne, malikulu a Victoria. Ngakhale kuti Lucy anali atakhala mmodzi wa Mboni za Yehova, ndinali ndasanapangebe chosankha. Komabe, pamene Nkhondo Yadziko II inaulika mu September wa chaka chimenecho, ndinayamba kuganiza mwamphamvu ponena za zimene ndinaphunzira m’Malemba. Kuletsedwa kwa ntchito ya Mboni za Yehova mu January 1941 kunandithandizadi kupanga chosankha. Ndinapatulira moyo wanga kwa Yehova Mulungu ndipo ndinabatizidwa mofulumira pambuyo pake.
Masinthidwe Aakulu m’Miyoyo Yathu
Panthaŵiyo, tinali kuchita lendi m’nyumba yabwino kwambiri m’Melbourne. Komabe, posapita nthaŵi, tinapemphedwa kusamukira m’nyumba ina limodzi ndi Mboni zina zingapo. Tinagulitsa zinthu za m’nyumba kusiyapo mbedi ndi zinthu zina ndi kusamukira m’nyumba imene inatchedwa kuti yaupainiya. Ndinapitirizabe kugwira ntchito monga wosindikiza mabuku ndipo motero ndinali wokhoza kupeza ndalama zolipirira zofunika za nyumbayo. Amuna anzanga okhala nawo anachita zofananazo. Chifukwa cha zimenezo, akazi athu ankakhala ndi phande muntchito yolalikira yanthaŵi yonse, ndipo amunafe tinkagwirizana nawo m’ntchito yolalikira ndi pamisonkhano Yachikristu madzulo ndi pakutha kwa mlungu.
Mwamsanga pambuyo pake, ine ndi mkazi wanga tinalandira kalata yochokera kuofesi ya nthambi ya Watch Tower Society yotipempha kumka ku Sydney. Tinagulitsa mbedi wathu ndi zinthu zina ndi kulipirira ndalama zake ngongole zingapo zimene tinali nazo, komano kuti tipeze ndalama zokwerera sitima kumka ku Sydney, tinachita kugulitsa mphete yachitomero ya Lucy!
Chifukwa cha malamulo a m’nthaŵi ya nkhondo ndi chiletso chongoikidwa kumene, panalibe Mabaibulo kapena mabuku ofotokoza Baibulo amene akanaitanitsidwa kuchokera kunja. Ndicho chifukwa chake ofesi ya nthambi ya Australia inasankha kuyambitsa ntchito yosindikiza mabuku yachinsinsi kuchititsa chakudya chauzimu kuperekedwabe, ndipo ndinapemphedwa kuyang’anira ntchitoyo. Ndinali ndi mwaŵi wogwira ntchito limodzi ndi mwamuna wina wa ku Scotland, George Gibb, amene anatumikira m’nyumba yosindikizira ya nthambi ya Australia kwa zaka 60. * Imeneyo ndiyo nthaŵi imene ndinalandira chilangizo chakuti: “Sindikiza buku la Children.”
Kupezanso Makina Osindikizira
Zokumana nazo zambiri zinali zopsetsa mtima, ndipo nthaŵi zina zowopsa m’zaka za zochitika zambiri za nkhondo zimenezo. Mwachitsanzo, kuti tiyambe ntchito yathu yosindikiza, tinafunikira makina. Amene tinagwiritsira ntchito kalelo kusindikizira mabuku ena nkhondo isanayambe anali atalandidwa ndi akuluakulu aboma, ndipo tsopano makina osindikizira aang’ono a Sosaite anali atatsekeredwa m’chipinda chake ndi kulondedwa. Kodi tikanatulutsa motani makinawo kumka nawo kumalo oyenera kukachita ntchito yosindikiza mobisa?
Alonda onyamula zida, osinthana zipani, analondera zinthu za Sosaite kwa maola 24 tsiku lililonse. Komabe, chipupa chimodzi chakumbuyo chinayang’anizana ndi positsira katundu wa m’sitima. Chotero usiku, pogwiritsira ntchito njira yokumbutsa lemba la Ezekieli 12:5-7, ogwira ntchito ena anyonga a pa Beteli analoŵa pachipupacho mwa kuchotsa njerwa. Ataloŵa mkati, anabwezeretsa njerwazo pamalo pake kuti pasadziŵike. Mwakuboola usiku kumeneku kwa nyengo yoposa masabata aŵiri, iwowa anapasula makina aang’ono, a Linotype, ndi makina ena angapo. Ndiyeno anatulutsira kunja mbalizo mwakachetechete, alondawo ali pantchito pamalopo!
M’kupita kwanthaŵi tinagula makina enanso kwina, ndipo posapita nthaŵi tinayamba mwamphamvu ntchito yosindikiza mobisa yochitidwa m’malo osiyanasiyana mu Sydney monse. Motero, tinali okhoza kusindikiza ndi kuika zikuto osati buku la Children lokha komanso mabuku aakuluwo The New World, “The Truth Shall Make You Free,” ndi The Kingdom Is At Hand, ndiponso ma Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 1942, 1943, 1944, ndi 1945. Ndiponso, mkati mwa chiletso cha zaka zimenezo zankhondo, Mboni za Yehova mu Australia monse sizinaphonye kulandira kope la Nsanja ya Olonda. Zimenezi zinatitsimikiziritsa mwachindunji kuti mkono wa Yehova sufupika.—Yesaya 59:1.
Kuchita ndi Otifikira Mwadzidzidzi
Mkati mwa nyengo ya kufufuza kwakukulu kwa munthaŵi ya nkhondo, makampani osindikiza mabuku anali kufikiridwa mwadzidzidzi ndi akuluakulu aboma amene ankaona zimene anali kusindikiza. Chifukwa chake, makina athu amodzi obisidwawo anali ndi chiwiya chochenjezera, chotabinya ndi mwendo chimene chinali pafupi ndi munthu wolandira alendo pantchito. Nthaŵi zonse pamene anaona munthu wosamdziŵa kapena amene anamlingalira kukhala wofufuza atatulukira pakhomo, ankaponda chotabinyiracho.
Pamene chiwiyacho chinatabinyidwa, kunali kochititsa nthumanzi kuona anthu akutulukira m’mazenera a mbali zonse! Anthu amene analembedwa kukhala ogwira ntchito anatsalira momwemo kuti abise mapepala osindikizidwa alionse a maganizi a Nsanja ya Olonda kapena mabuku ena a Baibulo opangidwa. Kuti achite zimenezi, ankagwiritsira ntchito mapepala a ukulu wofanana ndi mabuku ena amene anali kusindikizidwira anthu ena amalonda.
Mkati mwa kufikiridwa kwina koteroko, anthu ena aŵiri ofufuza anakhalira mabuku a nkhani zoseketsa, amene anali ampangidwe waukulu, komano pansi pake panali mapepala a magazini a Nsanja ya Olonda amene anali atasindikizidwa usiku wapitawo. M’chipinda china chosindikizira cha kumbali ina ya mzindawo, tinkasindikizamo mabuku a malonda nthaŵi ya masana ndi kusindikiza makope a Nsanja ya Olonda usiku ndi pakutha kwa milungu.
Kuthetsa Vuto Lathu la Kusoŵa Mapepala
Kupeza mapepala osindikizirapo kunali vuto lalikulu. Komabe, makampani ena osindikiza amene sanafune mtokoma wawo wonse wa mapepala chifukwa cha kutsika kwa malonda mkati mwa nkhondo anali ofunitsitsa kugulitsa mapepala awo otsala—inde, ndi mtengo wokwera nthaŵi zonse. Komabe, panthaŵi ina, tinalandira mapepalawo kuchokera kwina.
Sitima ya panyanja yonyamula katundu yobwera ku Australia inali ndi mtokoma waukulu wa mapepala ofiirira, komano sitimayo inabooka panyanja ndipo madzi oloŵa pang’onopang’ono mkati mwake ananyoŵetsa
mapepala ambiri. Mtokoma wonsewo anauika pamalonda amtengo wotsika, ndipo motidabwitsa ndife tokha amene tinali kufuna kugula mapepalawo. Zimenezi zinatikhozetsa kuwagula pamtengo wotsika kwambiri. Tinaumika mapepalawo padzuŵa, motero tikumatetezera ambiri kuti asaonongeke, ndiyeno tinawaduladula kuti akhale aukulu woyenera kugwiritsidwa ntchito pamakina athu osindikizira.Kodi tikagwiritsira ntchito motani mapepala ofiirira ameneŵa? Tinalingalira moyenera kuti oŵerenga mabuku ankhani zoseketsa angasangalale nawobe pamapela ofiirira ameneŵa. Motero, tinagwiritsira ntchito mapepala oyera omwe tinali titapatsidwa kusindikizira mabuku ankhani zoseketsa kusindikizira Nsanja ya Olonda ndi zinthu zina za Sosaite.
Ntchito Yofunika ya Akazi
Mkati mwa zaka za nkhondozo, akazi ambiri Achikristu mu Australia anaphunzira ntchito yokonza mabuku. Masana ena achilimwe otentha kwambiri, ena a iwo anali kugwira ntchito okha m’garaji ina yaing’ono imene tinkachitamo lendi yokhala m’kamsewu kodutsa kutseri kwa nyumba m’mzinda wa Sydney. Kuti asadziŵidwe, anatseka mazenera onse ndi chitseko. Miphika ya guluu inkatulutsa nthunzi yonunkha, ndipo kunja kunali kutentha kosaneneka. Chotero anavula zovala natsala ndi zamkati.
Mwadzidzidzi, anamva kugogoda pakhomo. Alongo Achikristuwo anafunsa mofuula kuti anali yani wogogodayo, ndipo ofesala wa ntchito wa boma anayankha. Anali kuchokera kudipatimenti imene inali ndi mphamvu m’nthaŵi ya nkhondoyo kutumiza anthu kumka kumalo alionse kumene anthu antchito anali kufunika. Alongowo anayankha mofuula kuti sangamlole kuloŵa panthaŵiyo popeza kuti anali kugwira ntchito atavala zovala zamkati zokha chifukwa cha kutentha.
Ofesalayo anakhala chete kwakanthaŵi; ndiyeno anafuula kuti akupita kukaonana ndi ena m’deralo. Anati adzafikanso maŵa kudzafufuza malowo. Nthaŵi yomweyo akazi Achikristu ameneŵa anatilizira lamya, ndipo tinatumiza lole usiku umenewo kukatenga zinthu zonse zimene ogwira ntchitowo anali kumamatiza, kuzisamutsira kwina.
Anthu ochuluka amene anagwira ntchito yathu yosindikiza mobisayo anali asanagwirepo ntchito yosindikiza, chotero zimene zinachitidwa zinanditsimikiziritsa mtima kuti mzimu wa Yehova unagaŵira chithandizo chofunika ndi chitsogozo. Unali mwaŵi waukulu kwa ine ndi mkazi wanga, Lucy, amene
anagwira ntchito yoika zikuto mabuku, kutenga mbali m’zochitika zonsezi.Kodi ntchito yathu inayang’aniridwa motani m’masiku ovuta amenewo? Wogwirira malo a woyang’anira nthambi wa Mboni za Yehova analandira lamulo lochokera kuboma lomletsa kuyendayenda, akumalamulidwa kukakhala kutauni ya pamtunda wa makilomita 100 kunja kwa Sydney. Lamulolo linamletsa kutuluka m’deralo kupyola makilomita asanu ndi atatu kuchokera pakati patauniyo. Galimoto lililonse linkapatsidwa malita anayi a petulo pamwezi. Koma abale anapanga chiwiya chaluso chotulutsa mafuta a galimoto—chitini chachitsulo cholemera pafupifupi theka la tani, choikidwa kumbuyo kwa galimoto. Makala ankayaka mkati mwake, akumatulutsa carbon monoxide monga mafuta agalimoto. Usiku ungapo mlungu uliwonse, abale ena oyang’anira limodzi nane tinayenda ulendo mwanjira imeneyi kukaonana ndi woyang’anira nthambiyo m’khwaŵa la pafupi ndi tauni kumene anabindikiritsidwako. Motero, tinkakambitsirana nkhani zambiri tisanakolezenso makala a chiwiya chotulutsa mafuta a galimoto ndi kubwerera ku Sydney mbandakucha.
Potsirizira, mlandu wa kuletsedwa kwa Mboni za Yehova unatengeredwa ku Bwalo Lamilandu Lapamwamba la Australia. Woweruza analengeza chiletsocho kukhala “chopanda pake, chosalongosoka, ndi chotsendereza” ndipo anachotsera Mboni za Yehova milandu yonse yowaneneza kuukira boma. Bwalo Lamilandu Lapamwamba lonselo linachilikiza chosankha chimenechi, kotero kuti tinakhoza kutulukira poyera ndi kupitiriza ntchito yathu ya Ufumuyo yololedwa mwalamulo.
Kugaŵiridwa Ntchito Inanso ndi Madalitso
Nkhondo itatha anthu ambiri amene anali atagwira nafe ntchito yosindikiza analoŵa utumiki waupainiya. Ena a iwo pambuyo pake anamka ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ku New York. Lucy ndi ine tinalinso ndi chonulirapo chimenecho m’maganizo, komano mwana wathu wamkazi anabadwa. Ndiyeno ndinalingalira zobwerera kukagwira ntchito yosindikiza. Tinapemphera kwa Yehova kuti nthaŵi zonse atithandize kuika zinthu Zaufumu pamalo oyamba, ndipo iye watero. Ndinaloŵa muntchito yotumikira mwanjira ina.
Lloyd Barry, amene tsopano akutumikira monga chiŵalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York, anandilizira lamya. Panthaŵiyo anali woyang’anira woyendayenda mu Sydney. Anafunsa ngati ndinali kudziŵa za deti la msonkhano wathu wadera wotsatira. Pamene ndinayankha kuti inde, anati: “Tikufuna kuti uyang’anire dipatimenti ya chakudya.”
Nditakayikira kwakanthaŵi, ndinati moziya: “Komatu sindinachitepo zimenezo m’moyo wanga.”
“Eya, Mbale,” iye anayankha moseka, “tsopano ndiyo nthaŵi yoti muphunzire!” Ndipo ndinaphunziradi, ndi kupitirizabe kulandira thayo la kuyang’anira dipatimenti ya chakudya, ngakhale pamisonkhano yaikulu, kwa zaka zoposa 40.
M’zaka zonsezo, kampani yathu yosindikiza mabuku inakula, ndipo zimenezi zinafuna kuti ndipange maulendo angapo kumka kutsidya kwa nyanja. Nthaŵi zonse ndinkagwirizanitsa maulendowo ndi misonkhano ya mitundu yochitidwira mu New York City ndi malo ena mu United States. Zimenezi zinandipatsa mwaŵi wothera nthaŵi yambiri ndiri ndi awo amene anali kuyang’anira madipatimenti osiyanasiyana amsonkhano, makamaka dipatimenti ya chakudya. Motero, nditabwerera ku Australia, ndinali wokhoza bwino kwambiri kutumikira zosoŵa za pamsonkhano.
Chifukwa cha kukalamba kwathu, nthaŵi zina Lucy ndi ine timadabwa ngati tikanachita zowonjezereka kukanakhala kuti tinabadwa mochedwerapo. Kumbali ina, kubadwa kwathu wina mu 1916 ndipo wina mu 1914, timakuona kukhala mwaŵi wodabwitsa kukhala titaona maulosi a Baibulo akumachitika. Ndipo timathokoza Yehova kaamba ka dalitso lomwe takhala nalo m’kuphunzira ndi anthu ambiri ndi kuwathandiza kudziŵa chowonadi ndi kuwaona tsopano akumtumikira monga atumiki obatizidwa. Pemphero lathu nlakuti tipitirizebe kumtumikira kwamuyaya, tikumamvomereza kosatha monga Mfumu Yolamulira ya chilengedwe chonse.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 14 Onani The Watchtower, ya September 15, 1978, masamba 24-7.
[Zithunzi patsamba 29]
Nyumba yosindikizira mabuku ku Beteli ya ku Strathfield, 1929-73
George Gibb woimirira pafupi ndi amodzi a makina osindikizira amene anatulutsidwa m’chipinda chosindikizira kudzera pachipupa chakumbuyo