Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Wamng’ono” Wasanduka “Chikwi”

“Wamng’ono” Wasanduka “Chikwi”

“Wamng’ono” Wasanduka “Chikwi”

“Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.”​—YESAYA 60:22.

1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani mdima waphimba dziko lapansi lerolino? (b) Kodi kuunika kwa Yehova kwapitirizabe motani kuŵalira anthu ake?

“MDIMA udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira [“adzakuwalira,” NW], ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe.” (Yesaya 60:2) Mawu ameneŵa akulongosola bwino zedi mmene zinthu zakhalira padziko lapansi chiyambire 1919. Matchalitchi Achikristu akana chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu Kristu, “kuunika kwa dziko lapansi,” monga Mfumu. (Yohane 8:12; Mateyu 24:3) Chifukwa cha “udani waukulu” wa Satana, mfumu ya “olamulira a dziko lapansi a mdima uno,” zaka za m’zana la 20 zinali zankhanza yosaneneka, nthaŵi yoipitsitsa m’mbiri ya munthu. (Chivumbulutso 12:12; Aefeso 6:12, NW) Anthu ambiri akukhala mumdima wauzimu.

2 Ngakhale kuti zili choncho, kuunika kukuŵala lerolino. Yehova ‘akuŵalira’ atumiki ake, otsalira odzozedwa, omwenso ndi oimira “mkazi” wake wa kumwamba pano padziko lapansi. (Yesaya 60:1, NW) Makamaka kuchokera pa kumasulidwa kwawo muukapolo wa Babulo m’chaka cha 1919, iwowa asonyeza ulemerero wa Mulungu ndipo ‘aŵalitsa kuunika kwawo pamaso pa anthu.’ (Mateyu 5:16) Kuchoka m’chaka cha 1919 kudzafika m’chaka cha 1931, kuunika kwa Ufumu kunaŵala mowonjezereka pamene otsalira odzozedwa ameneŵa anachotseratu nsinga zotsalira za nzeru zachibabulo. Chiŵerengero chawo chinawonjezeka kwambiri pamene Yehova anali kukwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israyeli; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pawo adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.” (Mika 2:12) Ulemerero wa Yehova pa anthu ake unapitirizabe kuonekera pamene m’chaka cha 1931, analandira dzina lakuti Mboni za Yehova.​—Yesaya 43:10, 12.

3. Kodi zinadzadziŵika motani kuti kuunika kwa Yehova kudzaŵalira anthu enanso kuwonjezera pa odzozedwa?

3 Kodi Yehova anali kudzaŵalira pa otsalira a “kagulu ka nkhosa” okhawo? (Luka 12:32) Iyayi. Kope la Nsanja ya Olonda ya September 1, 1931, inatchula za gulu linanso. Pofotokoza bwino lemba la Ezekieli 9:1-11, kopelo linasonyeza kuti mwamuna wokhala ndi cholembera cha mlembi wotchulidwa m’mavesi amenewo akuimira otsalira odzozedwa. Kodi amene akuikidwa chizindikiro pamphumi ndi “mwamuna” ameneyo ndani? “Nkhosa zina,” awo omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. (Yohane 10:16; Salmo 37:29) Mu 1935, gulu la “nkhosa zina” limeneli linazindikiridwa kukhala “khamu lalikulu . . . ochokera mwa mtundu uliwonse” lomwe mtumwi Yohane analiona m’masomphenya. (Chivumbulutso 7:9-14) Kuchokera m’chakacho cha 1935 kufika tsopano lino, ntchito yaikulu yomwe yakhalapo ndiyo ya kusonkhanitsa khamu lalikulu.

4. Kodi ndani omwe ali “mafumu” ndi “amitundu” otchulidwa pa Yesaya 60:3?

4 Ntchito yosonkhanitsa imeneyi inatchulidwa muulosi wa Yesaya pamene umati: “Amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka [“kuŵala,” NW] kwako.” (Yesaya 60:3) Kodi “mafumu” omwe akuwatchula panoŵa ndani? Otsalira a 144,000, omwe limodzi ndi Yesu Kristu, ali oloŵa m’nyumba a Ufumu wakumwamba, ndipo atsogolera pa ntchito yochitira umboni. (Aroma 8:17; Chivumbulutso 12:17; 14:1) Lerolino, otsalira odzozedwa oŵerengekaŵa, n’ngochepa zedi powayerekezera ndi “amitundu,” awo okhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi omwe akubwera kwa Yehova kuti aphunzitsidwe naye ndikuti aitanirenso ena kudzachita chimodzimodzi.​—Yesaya 2:3.

Atumiki a Yehova Achangu

5. (a) Kodi n’zochitika ziti zomwe zikusonyeza kuti changu cha anthu a Yehova sichinazirale? (b) Kodi ndi mayiko ati omwe anali ndi kuwonjezeka kwakukulu m’chaka cha 1999? (Onani tchati chomwe chili patsamba 17-20.)

5 Mboni za Yehova zamakono zinasonyezadi changu chosasimbika m’kati mwa zaka za zana la 20 limenelo! Ndipotu mosasamala kanthu za zitsenderezo zowonjezereka, changu chawocho sichinazirale pamene chaka cha 2000 chinali chikuyandikira. Anali kuonabe lamulo la Yesu kukhala lofunika kwambiri lakuti: “Phunzitsani anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19, 20) M’chaka chotsiriza chautumiki cha m’zaka za zana la 20, ofalitsa okangalika a uthenga wabwino anafika pa chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha 5,912,492. Anathera maola ochititsa chidwi onse pamodzi ngati 1,144,566,849 akulankhula ndi anthu ponena za Mulungu ndi zifuno zake. Anapanga maulendo obwereza okwana 420,047,796 kwa okondwerera ndipo anapangitsa maphunziro a Baibulo apanyumba okwana 4,433,884 kwaulere. N’ziŵerengero zosangalatsatu kwabasi za utumiki wachangu!

6. Kodi ndi makonzedwe atsopano ati omwe anapangidwa kaamba ka apainiya, ndipo panali zotsatirapo zotani?

6 M’mwezi wa January chaka chatha, Bungwe Lolamulira linalengeza za kusintha kwa maola ofunika kwa apainiya. Ambiri anagwiritsa ntchito mwayi umenewu mwa kuyamba upainiya wokhazikika kapena wothandiza. Mwachitsanzo, m’miyezi inayi yoyambirira m’chaka cha 1999, ofesi yanthambi ya ku Netherlands inalandira makalata a anthu ofuna kulembetsa upainiya wokhazikika oŵirikiza kanayi powayerekezera ndi makalata omwe inalandira panyengo imodzimodziyo chaka chimodzi m’mbuyo mwake. Nthambi ya ku Ghana ikuti: “Kuchokera pomwe maola atsopano ofunika kwa apainiya anayamba kugwira ntchito, chiŵerengero cha apainiya athu okhazikika chakwera moŵirikiza.” M’chaka chautumiki cha 1999, chiŵerengero cha apainiya padziko lonse lapansi chinafika 738,343, njira yabwino zedi yosonyezera ‘changu pa ntchito zokoma.’​—Tito 2:14.

7. Kodi Yehova wadalitsa motani ntchito zochitidwa mwachangu ndi atumiki ake?

7 Kodi Yehova wadalitsa ntchito zochitidwa mwachangu zimenezi? Inde. Kupyolera mwa Yesaya iye akuti: “Tukula maso ako uunguzeunguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako amuna adzachokera kutali, ndi ana ako akazi adzaleredwa pambali.” (Yesaya 60:4) “Ana aamuna” ndi “ana aakazi” odzozedwa omwe asonkhanitsidwa pamodzi akupitirizabe kutumikira Mulungu mwachangu. Ndipo tsopano, nkhosa zina za Yesu akuzisonkhanitsira kumbali ya “ana aamuna” ndi “ana aakazi” odzozedwa m’mayiko ndi m’zilumba za m’nyanja zokwana 234.

“Ntchito Iliyonse Yabwino”

8. Kodi Mboni za Yehova n’zachangu pa ‘ntchito zabwino’ ziti?

8 Akristu ali ndi udindo wolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kuthandiza omwe achita chidwi kukhala ophunzira. Ndipotu iwo ali ‘okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ (2 Timoteo 3:17) Chotero, iwo mwachikondi amasamalira mabanja awo, kuchereza alendo, ndi kuyendera odwala. (1 Timoteo 5:8; Ahebri 13:16) Ndipo antchito odzifunira nawo ali kalikiliki pa ntchito monga yomanga Nyumba za Ufumu, ntchito yomwe imachitiranso umboni. Ku Togo, Nyumba ya Ufumu imodzi itamangidwa, akuluakulu a tchalitchi cha chikoka kwambiri chakomweko anali ofunitsitsa kudziŵa chifukwa chake Mboni za Yehova zinali zokhoza kumanga zokha nyumba zawozawo pamene tchalitchicho chimachita kulemba ntchito anthu ena kuti aŵamangire! Nthambi ya ku Togo inapereka lipoti lakuti kumanga Nyumba za Ufumu zokongola kulinso ndi zotsatira zabwino kwambiri ku malo oyandikana nazo mwakuti anthu ena ayesetsa kuchita lendi kapena kumanga nyumba m’malo oyandikana ndi kumene Nyumba za Ufumu zimenezi zidzamangidwa.

9. Kodi Mboni za Yehova zachitanji pamene kwagwa masoka?

9 Nthaŵi zina, ntchito yabwino yamtundu winanso imafunika. M’mayiko ambiri munagwa masoka m’chaka chautumiki chathachi, ndipo kaŵirikaŵiri anthu oyambirira kufika pamalowo kudzapereka thandizo anali a Mboni za Yehova. Mwachitsanzo, mbali yaikulu ya chilumba cha Honduras inawonongedwa ndi mphepo ya mkuntho yotchedwa Mitch. Mwamsanga nthambi yakumeneko inakhazikitsa makomiti oona ngozi zamwadzidzidzi kuti ilinganize zokapereka thandizo. Mboni za m’Honduras komanso za m’mayiko ena ambiri zinapereka zovala, chakudya, mankhwala ndi zinthu zina zofunika kwambiri. Makomiti Omanga a Zigawo anagwira ntchito mwaluso zedi pomanganso nyumba. Posapita nthaŵi, abale athu omwe ankavutika chifukwa cha tsokalo anathandizidwa kuti athe kubwerera ku ntchito zawo zamasiku onse. Ku Ecuador, Mboni za Yehova zinathandiza abale awo pamene madzi amphamvu anasefukira ndi kuwononga nyumba zawo. Ataonerera momwe Mbonizo zinathandizira pa vutolo, munthu wina wamkulu m’boma anati: “Kukanakhala kuti ndinalemba ntchito gulu ili, ndikanachita zodabwitsa kwabasi! Anthu onga ngati inuyo ayenera kukhala m’mbali zonse zadziko lapansi.” Ntchito zabwino zoterozo zimadzetsa chitamando pa Yehova Mulungu ndipo zili umboni wa ‘chipembedzo [chathu chomwe] chimapindula m’zonse.’​—1 Timoteo 4:8.

Iwo “Auluka Ngati Mtambo”

10. Ngakhale kuti chiŵerengero cha odzozedwa chikucheperacheperabe, kodi n’chifukwa chiyani dzina la Yehova likulengezedwa kwambiri lerolino kuposa kale?

10 Tsono Yehova akufunsa kuti: “Ndani awa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda ku mazenera awo? Zoonadi, zisumbu zidzandilandira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisi kutenga ana ako aamuna kutali . . . Alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu awo adzakutumikira.” (Yesaya 60:8-10) Woyambirira kuchitapo kanthu pa ‘kuŵala’ kwa Yehova anali “ana [ake] aamuna,” Akristu odzozedwa. Ndipo kenako anali “alendo,” anthu a khamu lalikulu, omwe mokhulupirika akutumikira abale awo odzozedwa, ndi kutsatira utsogoleri wawo polalikira uthenga wabwino. Chotero, ngakhale kuli kwakuti chiŵerengero cha odzozedwa chikumka n’chicheperachepera, dzina la Yehova likulengezedwa padziko lonse lapansi kuposa kale lonse.

11. (a) Kodi n’chiyani chomwe chikupitirizabe ndipo pakhala zotsatira zotani m’chaka cha 1999? (b) Kodi ndi mayiko ati omwe anali ndi ziŵerengero zapamwamba za obatizidwa mu 1999? (Onani tchati chomwe chili patsamba 17-20.)

11 Zotsatira zake n’zakuti, anthu miyandamiyanda akusonkhana kudzapeza chisungiko mumpingo wachikristu, “monga nkhunda ku mazenera awo.” Anthu zikwi mazana ambiri akuwonjezeka chaka ndi chaka, ndipotu njira idakali yotsegula kwa enanso ambiri. Yesaya anati: “Zipata zako zidzakhalabe zotseguka, sizidzatsekedwa usana pena usiku, kuti abwere nacho kwa iwe chuma cha amitundu.” (Yesaya 60:11) Chaka chathachi anthu okwana 323,439 anabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova, ndipotu iye sanatsekebe zipatazo. “Zofunika za amitundu onse,” a khamu lalikulu, akusonkhanira kudzaloŵa m’zipatamo. (Hagai 2:7) Palibe ndi mmodzi yemwe mwa ofuna kuchoka kumdimawo yemwe adzabwerera. (Yohane 12:46) Tikupemphatu onse otereŵa kuti apitirizebe kuyamikira kwawo kuunika!

Kulimba Mtima Poyang’anizana ndi Chitsutso

12. Kodi anthu omwe amakonda mdima ayesa motani kuzimitsa kuunikako?

12 Awo amene amakonda mdima amadana ndi kuunika kwa Yehova. (Yohane 3:19) Ena ayesa kuzimitsa kuunikako. Zimenezi si zachilendo ayi. Ngakhalenso Yesu, “kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse” anatonzedwa, kutsutsidwa, ndipo pamapeto pake n’kuphedwa ndi nzika zinzake za m’dzikolo. (Yohane 1:9) M’kati mwa zaka zonse za m’zana la 20, Mboni za Yehova nazonso zazunzidwa, kuikidwa m’ndende, kuletsedwa kupembedza, ngakhalenso kuphedwa kumene pamene mokhulupirika zinali kupitirizabe kuŵalitsa kuunika kwa Yehova. M’zaka zaposachedwapa, otsutsa ayesayesa kufalitsa bodza m’zoulutsira nkhani, bodza lokhudza awo amene akuŵalitsa kuunika kwa Mulungu. Ena amafunitsitsa kuti anthu akhulupirire kuti Mboni za Yehova n’zoopsa ndikuti siziyenera kupatsidwa ufulu wochuluka kapenanso kuti ziyenera kuletsedwa kupembedza. Kodi otsutsa ameneŵa apambana?

13. Kodi n’chiyani chomwe chakhala chotsatirapo cha kuuza oulutsa nkhani mwanzeru zoona zake zenizeni zokhudza ntchito yathu?

13 Ayi. Pamene kunali koyenera, Mboni za Yehova zapita kwa oulutsa nkhaniwo kukafotokoza zoona zake zenizeni. Zotsatira zake n’zakuti, dzina la Yehova lasindikizidwa ponseponse m’manyuzipepala ndi m’magazini ndiponso laulutsidwa m’mawailesi ndi pawailesi yakanema. Zimenezi zinapangitsa kuti ntchito yolalikira ikhale ndi zotsatira zabwino zedi. Mwachitsanzo, ku Denmark, pologalamu ina pa TV yadzikolo inakamba nkhani yakuti “Chifukwa chomwe chikhulupiriro cha anthu a m’Denmark chikuziralira.” Mboni za Yehova ndiponso anthu enanso oimira zipembedzo zina anafunsidwa. Pambuyo pake, mkazi wina yemwe anaonerera pologalamuyo anathirira ndemanga akumati: “Sikunali kovuta kuzindikira omwe anali ndi mzimu wa Mulungu.” Ndipo pambuyo pake anayamba kuphunzira Baibulo.

14. Kodi posachedwapa otsutsa adzakakamizika kuzindikira chiyani mwamanyazi?

14 Mboni za Yehova zikudziŵa ndithu kuti ambiri m’dzikoli adzaŵatsutsa. (Yohane 17:14) Komabe, amalimbikitsidwa ndi ulosi wa Yesaya wakuti: “Ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira ku mapazi ako, nadzakutcha iwe, mudzi wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israyeli.” (Yesaya 60:14) Posachedwapa, otsutsaŵa adzazindikira mwamanyazi kuti kwenikweni iwo anali kulimbana ndi Mulungu mwiniyo. Ndani angapambane pakulimbana kumeneko?

15. Kodi Mboni za Yehova ‘zikuyamwa mkaka wa amitundu’ m’njira ziti, ndipo kodi zimenezi zasonyezedwa motani pantchito yawo yophunzitsa ndi kulalikira?

15 Yehova akupitirizabe kulonjeza kuti: “Ine ndidzakusandutsa changwiro chosatha . . . Iwe udzayamwanso mkaka wa amitundu, nudzayamwa bere la mafumu, nudzadziŵa kuti Ine Yehova, ndine mpulumutsi wako.” (Yesaya 60:15, 16) Inde, Yehova ndi Mpulumutsi wa anthu ake. Ngati am’dalira iyeyo, adzakhaladi ‘kosatha.’ Ndipo ‘adzayamwa mkaka wa amitundu,’ kugwiritsa ntchito zina mwa zipangizo zomwe zilipo pothandiza kupititsa patsogolo kulambira koona. Mwachitsanzo, kugwiritsa ntchito makompyuta mwanzeru komanso njira zamakono zotumizira mauthenga, zimatheketsa kufalitsa Nsanja ya Olonda m’zinenero 121 ndiponso Galamukani! m’zinenero 62 panthaŵi imodzimodzi ndi Chingelezi. Pologalamu yapadera yapakompyuta inakonzedwa kuti ithandize potembenuza Baibulo la New World Translation m’zinenero zatsopano, ndipotu kutembenuza kumeneku kwadzetsa chimwemwe chosaneneka. Pamene Baibulo la Malemba Achigiriki Achikristu linatulutsidwa m’Chikroati m’chaka cha 1999, anthu zikwizikwi anakhetsa misozi yachisangalalo. Mbale wina wachikulire anati: Ndaliyembekezera Baibulo limeneli kwanthaŵi yaitali zedi. Tsopano ndiyenera kumwalira mwamtendere!” Makope a Baibulo lonse la New World Translation kapena zigawo zake zokha omwe afalitsidwa m’zinenero 34 aposa 100 miliyoni.

Miyezo Yapamwamba ya Makhalidwe

16, 17. (a) Ngakhale kuti n’kovuta, n’chifukwa chiyani kusungabe miyezo yapamwamba ya Yehova kuli kofunika? (b) Kodi n’chokumana nacho chotani chomwe chikusonyeza kuti achinyamata angapeŵe kuipitsidwa ndi dziko?

16 Yesu anati: “Yense wakuchita zoipa adana nako kuunika.” (Yohane 3:20) Kumbali ina, awo amene akukhalabe m’kuunika amakonda miyezo yapamwamba ya Yehova. Yehova, kudzera mwa Yesaya, akuti: “Anthu ako adzakhalanso onse olungama.” (Yesaya 60:21a) Chingakhaledi chothetsa nzeru kusungabe miyezo yolungama m’dziko lomwe chisembwere, kunama, umbombo, ndi kudzikuza zili zofala. Mwachitsanzo, mayiko ena akutukuka pa chuma ndipo n’chapafupi kuti munthu aike mtima wake wonse pa kupeza chumacho. Komabe, Paulo anachenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.” (1 Timoteo 6:9) Zimakhala zomvetsa chisoni kwabasi pamene winawake waloŵerera kotheratu m’zamalonda mwakuti zam’chititsa kulekeratu kuchita zinthu zofunika zedi monga kusonkhana kwachikristu, kuchita utumiki wopatulika, kutsatira mfundo za makhalidwe abwino, ngakhale kusamalira maudindo a m’banja!

17 Kusungabe miyezo yolungama kungakhale kovuta makamaka kwa achinyamata, chifukwa chakuti abwenzi awo ambirimbiri aloŵerera m’kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo ndi chiwerewere. Ku Suriname, msungwana wina wazaka 14 zakubadwa anafikiridwa ndi mnyamata wina wooneka bwino pasukulu ina ndi kumupempha kuti agone naye. Msungwanayo anakana, ndipo anafotokoza kuti Baibulo limaletsa anthu osakwatirana kuchita zinthu zoterozo. Asungwana ena pasukulupo anam’nyoza kwambiri ndipo anayesayesa kukakamiza msungwana mnzawoyo kuti asinthe maganizo ake, akumanena motsimikiza kuti aliyense amafunitsitsa atagona ndi mnyamata yemwe iye ankamukanayo. Koma, msungwanayo anakanitsitsa kwa mtu wagalu. Patapita milungu yoŵerengeka, mnyamata uja anapezeka ali ndi kachilombo ka HIV ndipo anadwala kodetsa nkhaŵa. Msungwanayu anali wosangalala zedi kuti anamvera lamulo la Yehova lakuti ayenera ‘kusala dama.’ (Machitidwe 15:28, 29) Mboni za Yehova n’zonyadira kwambiri ndi achinyamata awo omwe sasunthika pachinthu chabwino. Chikhulupiriro chawo, limodzinso ndi chamakolo awo, ‘chimakuza’ ndi kulemekeza, dzina la Yehova Mulungu.​—Yesaya 60:21b.

Yehova Wachulukitsa

18. (a) Kodi n’chinthu chachikulu chiti chomwe Yehova wachitira anthu ake? (b) Kodi n’chiyani chomwe chikusonyeza kuti kukula kudzapitirizabe, ndipo n’ziyembekezo zaulemerero zotani zimene zidzakwaniritsidwa kwa awo okhala m’kuunika?

18 Inde, Yehova akuunikira, kudalitsa, kutsogolera, ndiponso kulimbitsa anthu ake. M’zaka za zana la 20, iwowa aona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesaya akuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” (Yesaya 60:22) Komwe kanali kagulu kochepa, kapena kuti “wamng’ono,” kalelo mu 1919, kaposa “chikwi” tsopano. Ndipotu gululi likukulirakulirabe! Chaka chathachi anthu okwana 14,088,751 anafika paphwando la Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Ambiri a iwo sanali Mboni zokangalika. Tili okondwa kuti iwoŵa anafika pachochitika chofunika chimenecho, ndipo tikuwapempha kuti apitirizebe kulondola kuunika. Yehova akuunikirabe anthu ake moŵala kwambiri. Chitseko choloŵera m’gulu lake chidakali chotseguka. Tsono itanirani onse akhaletu ofunitsitsa kukhalabe m’kuunika kwa Yehova. Zimenezo zatidzetsera madalitso ochuluka zedi tsopano lino! Ndipo n’chimwemwe chosasimbikadi chomwe kuchita zimenezi kudzatidzetsera m’tsogolo pamene chilengedwe chonse chidzatamanda Yehova ndi kukondwera m’kuŵala kwa ulemerero wake!​—Chivumbulutso 5:13, 14.

Kodi Mungafotokoze?

Kodi ndani omwe asonyeza ulemerero wa Yehova m’masiku otsiriza ano?

Kodi n’chiyani chomwe chikusonyeza kuti changu cha anthu a Yehova sichinazirale?

Kodi ndi ntchito zina zabwino ziti zomwe Mboni za Yehova zatanganidwa nazo?

Mosasamala kanthu za chitsutso choopsa, kodi tili otsimikizira kuti chiyani?

[Mafunso]

[Tchati pamasamba 17-20]

LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 1999 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Zithunzi patsamba 15]

Anthu akusonkhanabe kudzaloŵa m’gulu la Yehova

[Chithunzi patsamba 16]

Tili okondwa kwabasi kuti Yehova wasiya chitseko chili chotseguka kuti anthu okonda kuunika aloŵe