Mulungu Amayankha Mapemphero
Mulungu Amayankha Mapemphero
Korneliyo anali mwamuna yemwe anafuna chiyanjo cha Mulungu mwa kupemphera mobwerezabwereza kuchokera pansi pa mtima. Komanso iye anagwiritsa ntchito bwino udindo wake monga mtsogoleri wa gulu lankhondo. Malinga n’kunena kwa Baibulo “anapatsa anthu [osoŵa] zachifundo zambiri.”—Machitidwe 10:1, 2.
PANTHAŴIYO, mpingo wachikristu unapangidwa ndi Ayuda okhulupirira, otembenuka, ndi Asamariya. Korneliyo anali wakunja wosadulidwa ndipo sanali mumpingo wachikristu. Kodi zimenezo zikutanthauza kuti mapemphero ake anaperekedwa mwachabe? Ayi. Yehova Mulungu anaona Korneliyo ndi ntchito zake zochitidwa mwapemphero.—Machitidwe 10:4.
Motsogozedwa ndi angelo, Korneliyo anadzagwirizana ndi mpingo wachikristu. (Machitidwe 10:30-33) Chotsatira chake chinali chakuti, iyeyo ndi a m’banja lake analandira madalitso okhala akunja osadulidwa oyamba kulandiridwa mu mpingo wachikristu. Yehova Mulungu anaona kuti kunali koyenera kuti nkhani ya Korneliyo iphatikizidwe m’nkhani za m’Baibulo. Mosakayikira, iye anasintha m’zambiri kuti moyo wake ugwirizane kotheratu ndi miyezo ya Mulungu. (Yesaya 2:2-4; Yohane 17:16) Zomwe zinachitikira Korneliyo ziyenera kukhala zolimbikitsa kwambiri kwa anthu amitundu yonse omwe akufuna kuyanjidwa ndi Mulungu lerolino. Lingalirani zitsanzo zinanso.
Zitsanzo Zamakono
Msungwana wina ku India ankafuna kwambiri chitonthozo. Anakwatiwa ali ndi zaka 21, ndipo anali ndi ana aŵiri. Koma mwana wake wachiŵiri atangobadwa, mwamuna wake anamwalira. Mwadzidzidzi, ali ndi zaka 24, anakhala mkazi wamasiye wa ana aŵiri, wamkazi wa miyezi iŵiri ndi wamwamuna wa miyezi 22. Ndithudi anafunikira chitonthozo! Kodi akanachipeza kuti? Usiku wina, akuvutika kwambiri m’maganizo anapemphera kuti, Atate Wakumwamba, chonde nditonthozeni mwa Mawu anu.”
M’maŵa wake, analandira mlendo. Anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Tsiku limenelo, utumiki wake wa kunyumba ndi nyumba unali wovuta chifukwa chakuti anali ochepa omwe anam’landira m’nyumba zawo. Atatopa ndiponso atalefulidwa, anangotsala pang’ono kuti abwerere kunyumba, komano mosadziŵika bwino anasonkhezereka kupita pa nyumba imodzi yokha. Kumeneko n’komwe anakakumana ndi mkazi wamasiye wachinyamatayo. Anamuitanira m’nyumba ndi
kulandira chofalitsa chomwe chinafotokoza Baibulo. Mkaziyu anatonthozedwa kwambiri kupyolera m’kuŵerenga chofalitsa chimenecho ndi m’kukambirana kwake ndi Mboniyo. Iye anaphunzira za lonjezo la Mulungu lodzaukitsa akufa ndi la Ufumu wa Mulungu, womwe posachedwapa udzapanga dziko lapansi kukhala paradaiso. Chofunika kwambiri n’chakuti, anadziŵa ndi kukonda Mulungu woona mmodzi yekhayo, Yehova, yemwe anayankha pemphero lake.Nora, yemwe akukhala mu mzinda wa George, ku South Africa, anapatula mwezi umodzi kuti agwire ntchito yolalikira yanthaŵi zonse. Asanayambe, anapemphera moona mtima kwa Yehova kuti amuthandize kupeza munthu yemwe analidi wofunitsitsa kuphunzira Baibulo. Dera lomwe anam’tumiza kukagwira ntchito linaphatikizapo kumudzi kwa munthu yemwe anachitira Nora mwano kwambiri pamene anam’fikira ulendo wapitawo. Molimba mtima, Nora anafikanso pakhomopo. Anadabwa kuona kuti munthu wina watsopano wotchedwa Noleen ndiye analoŵa m’nyumbayo. Komanso Noleen ndi amayi ake anakhala akupemphera kwa Mulungu kuti awathandize kumvetsetsa Baibulo. “Nditawapempha kuphunzira nane Baibulo,” akulongosola motero Nora, “anali osangalala zedi.” Noleen ndi amayi akewo anapita patsogolo mwamsanga. M’kupita kwa nthaŵi, onse anayamba kugwira ntchito yochiritsa mwauzimu limodzi ndi Nora.
Chitsanzo china chomwe chikusonyeza mphamvu ya pemphero ndi cha mwamuna wina ndi mkazi wake omwe amakhala mumzinda wa Johannesburg ku South Africa. Usiku wina wa Loŵeruka m’chaka cha 1996, ukwati wa Dennis ndi Carol unangotsala pang’ono kuti usweke. Pamapeto pake anagwirizana kuti apemphere thandizo, ndipo anaterodi mobwerezabwereza usiku umenewo. M’maŵa wake, nthaŵi ya 11 koloko, Mboni za Yehova ziŵiri zinagogoda pachitseko chawo. Dennis anayankha kugogodako ndikuwauza kuti adikire kufikira ataitana mkazi wake. Kenako Dennis anachenjeza Carol kuti ngati angaitanire Mbonizo m’nyumba mwawomo, kukhala kovuta kuti azichotse. Carol anam’kumbutsa Dennis kuti anali kupempherera thandizo ndipo anati limeneli lingathe kukhala yankho la Mulungu ku mapemphero awo. Chotero Mbonizo anaziitanira m’nyumba, ndipo phunziro la Baibulo linayamba ndi buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Zomwe Dennis ndi Carol anaphunzira zinawasangalatsa kwambiri. Madzulo atsiku lomwelo, anakapezeka pa msonkhano ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yakomweko kwa nthaŵi yoyamba. Mwa kugwiritsa ntchito chidziŵitso chomwe amaphunzira kuchokera m’Baibulo, Dennis ndi Carol anapeza njira zothetsera mavuto awo a m’banja. Tsopano ndi olambira a Yehova achimwemwe ndi obatizidwa ndipo nthaŵi zonse amauza mabwenzi awo zikhulupiriro zawo zozikidwa pa Baibulozo.
Bwanji Ngati M’madzimva Monga Wosayenerera Kupemphera?
Anthu ena oona mtima angadzimve kukhala osayenerera kupemphera chifukwa cha njira yawo yoipa ya moyo. Yesu Kristu anakambapo nkhani ya munthu woteroyo, wokhometsa msonkho wonyozeka. Pakuloŵa m’bwalo la kachisi, mwamuna ameneyu anadzimva kukhala wosayenerera kupita pamalo omwe amayenera kupempherera nthaŵi zonse. “Alikuima patali . . . anadziguguda pachifuŵa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.” (Luka 18:13) Malinga n’kunena kwa Yesu, munthu uyu anamvedwa ndi Mulungu. Izi zikusonyeza kuti Yehova Mulungu alidi wachifundo ndipo n’ngwofunitsitsa kuthandiza ochimwa olapa moona mtima.
Lingalirani wachinyamata wina wa ku South Africa wotchedwa
Paul. Monga mnyamata, Paul ankapita ku misonkhano yachikristu limodzi ndi amayi ake. Koma ali kusukulu ya sekondale, anayamba kuyanjana ndi achinyamata omwe sankatsata njira za Mulungu. Atasiya sukulu, anakagwira ntchito m’gulu lankhondo m’boma lakale la tsankho ku South Africa. Kenaka, mosayembekezera, bwenzi lake lalikazi, linathetsa chibwenzi chawo. Njira ya moyo yosakhutiritsa imeneyi inam’khumudwitsa kwambiri Paul. “Usiku wina,” iye akukumbukira, “ndinapemphera kwa Yehova ndikupempha thandizo lake, ngakhale kuti ndinali ndisanafike kwa Mulungu moona mtima m’pemphero kwa zaka zambiri.”Posapita nthaŵi pambuyo pa pemphero limeneli, amayi ake a Paul anamuitana kudzakhala nawo pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu cha chaka ndi chaka. (Luka 22:19) Paul anazizwa ndi zomwe anachita amayi akezi, popeza kuti iye anali woloŵerera ndipo analibe chidwi ndi Baibulo. “Ndinaona chiitano chimenechi kukhala yankho la Yehova ku pemphero langa ndipo ndinalingalira kuti ndinayenera kuchitapo kanthu ndithu.” Kuchokera panthaŵiyo, Paul anayamba kupezeka pa misonkhano yonse yachikristu. Ataphunzira Baibulo kwa miyezi inayi, anali woyenera kubatizidwa. Komanso, analeka maphunziro ake auinjiniya ndi kusankha ntchito yanthaŵi zonse yolalikira. Lerolino, Paul ndi munthu wosangalala, salinso wodera nkhaŵa ndi moyo wake wapapitapo. Kwa zaka 11 zapitazo, wakhala akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ku South Africa.
Ndithudi, Yehova Mulungu amayankha mapemphero mwachifundo ndipo “ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.” (Ahebri 11:6) Posachedwapa tsiku lalikulu la Yehova lifika ndi kuthetsa kuipa konse. Panthaŵi ino, Yehova akuyankha mapemphero a anthu ake omwe akupempha chilimbikitso ndi chitsogozo pamene mwachangu akugwira ntchito yofunika yochitira umboni. Chotero, miyandamiyanda ya anthu ochokera m’mitundu yonse akugwirizanitsidwa ndi mpingo wachikristu ndipo akudalitsidwa ndi chidziŵitso cha m’Baibulo chomwe chimatsogolera ku moyo wosatha.—Yohane 17:3.
[Chithunzi patsamba 5]
Pemphero la Korneliyo lochokera pansi pa mtima linachititsa kuti mtumwi Petro am’chezere
[Chithunzi patsamba 6]
Pemphero lathandiza anthu ambiri m’nthaŵi ya mavuto
[Zithunzi patsamba 7]
N’kwabwino kupempherera thandizo kuti tilimvetse bwino Baibulo
Mwamuna ndi mkazi okwatirana angapempherere thandizo kuti alimbitse ukwati wawo