Okhulupirika Ndi Opanda Mantha Poponderezedwa ndi Anazi
Okhulupirika Ndi Opanda Mantha Poponderezedwa ndi Anazi
Pa June 17, 1946, Mfumukazi Wilhelmina ya ku Netherlands inatumiza uthenga wopepesa za imfa ku banja la Mboni za Yehova ku Amsterdam. Cholinga cha uthenga wopepesawo chinali kusonyeza chidwi cha mfumukaziyo pa mwana wamwamuna wa m’banjalo, Jacob van Bennekom, amene anaphedwa ndi Anazi m’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse. Zaka zingapo zapitazo, konsolo ya mzinda wa Doetinchem, mzinda wa dera la kumadzulo kwa Netherlands, inatcha msewu wina dzina la Bernard Polman, yemwenso ndi mmodzi wa Mboni za Yehova amene anaphedwa m’kati mwa nkhondoyo.
KODI n’chifukwa chiyani Anazi anaukira Jacob, Bernard, ndi enanso a Mboni za Yehova mu Netherlands m’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse? Ndipo n’chiyani chimene chinachititsa Mboni zimenezi kupitiriza kukhala zokhulupirika m’kati mwa zaka za chizunzo chankhanza ndipo pomalizira pake n’kulandira ulemu ndi kukopa chidwi cha anthu a m’dzikomo ndiponso mfumukazi? Kuti tipeze chifukwa chake, tiyeni tione zochitika zina zomwe zinayambitsa udani waukulu kwambiriwu wofanana ndi udani wa Davide ndi Goliati wa pakati pa kagulu kochepa ka Mboni za Yehova ndi chigulu cha mgwirizano wa andale ndi asilikali cha Anazi.
Zoletsedwa—Koma Zokangalika Kwambiri Kusiyana ndi Kale Lonse
Pa May 10, 1940, gulu lankhondo la Nazi mwadzidzidzi linalanda dziko la Netherlands. Popeza kuti mabuku amene ankagaŵidwa ndi Mboni za Yehova ankavumbula kuipa kwa Chinazi ndi kulimbikitsa Ufumu wa Mulungu, mwamsanga Anazi anayesa kuletsa ntchito za Mboni. M’milungu itatu yokha Anazi atalanda Netherlands, iwo mwamtseri anakhazikitsa lamulo loletsa Mboni za Yehova. Pa March 10, 1941, nyuzipepala ina inalengeza za chiletsochi, ndi kudzudzula Mboni chifukwa cholimbana ndi “ntchito zonse
zaboma ndiponso zatchalitchi.” Chotsatira chake chinali chakuti kusakasaka Mboni kunalimbikitsidwa.Chosangalatsa kwambiri chinali chakuti, ngakhale kuti gulu lankhanza kwambiri la Gestapo, kapena la apolisi akabisalira, amayang’anira matchalitchi onse, Gestapo imazunza gulu limodzi lokha la Akristu. “Chizunzo mpaka imfa,” anatero Mdatchi wina wolemba mbiri yakale Dr. Louis de Jong, “chinali pa gulu limodzi lokha la chipembedzo—Mboni za Yehova.”—Het Koninkrik der Nederlanden in de Tweede Wereldoorlog (Ufumu wa Netherlands M’kati mwa Nkhondo Yachiŵiri ya Padziko Lonse).
Bungwe la Gestapo linathandizidwa ndi apolisi achidatchi kuti lipeze ndi kumanga Mboni. Kuwonjezera pa ameneŵa, woyang’anira woyendayenda wina amene anachita mantha kwambiri nakhala wampatuko anaululira Anazi chidziŵitso chokhudza anzake akale amene amafanana nawo chikhulupiriro. Pofika ku mapeto a April 1941, Mboni zokwanira 113 zinali zitamangidwa. Kodi kuukiridwa kwa mtundu umenewu kunathetsa ntchito yolalikira?
Yankho lake limapezeka mu Meldungen aus den Niederlanden (Malipoti Ochokera ku Netherlands), chikalata chimene a Sicherheitspolizei (Apolisi Achitetezo) a ku Germany analemba mu April 1941. Ponena za Mboni za Yehova lipotilo linati: “Kagulu koletsedwa kameneka kakugwira ntchito zolimba m’dziko lonse lino, kuchita misonkhano mopanda lamulo ndi kukhoma mathirakiti okhala ndi mawu ngati ‘Kuzunza Mboni za Mulungu n’kulakwa’ ndi ‘Yehova adzalanga ozunza ndi chiwonongeko chosatha.’” Milungu iŵiri pambuyo pake chikalata chomwecho chinati “mosasamala kanthu za kulimbikitsidwa kwa njira zokhwima zimene Apolisi Achitetezo akutsata polimbana ndi ntchito za Ophunzira Baibulo, ntchito zawo zikupitirizabe kuwonjezeka.” Inde, mosasamala kanthu za chiopsezo cha kumangidwa, Mbonizo zinapitiriza kugwira ntchito yawo, kugaŵira zofalitsa zofotokoza Baibulo zoposa 350,000 mu 1941 mokha!
Kodi n’chiyani chimene chinatheketsa kagulu kakang’ono koma komakulakula ka Mboni mazana ochepa kameneka kulimba mtima kuyang’anizana ndi adani awo owopsa kwambiriwo? Monga mneneri wokhulupirika Yesaya wakale, Mbonizo zinaopa Mulungu, osati munthu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti zinakhulupirira kwambiri mawu olimbikitsa a Yehova kwa Yesaya akuti: “Ine, inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa?”—Yesaya 51:12.
Kupanda Mantha Kutamandidwa
Podzafika kumapeto kwa 1941, chiŵerengero cha Mboni zimene zinamangidwa chinakwera kufika pa 241. Komabe, ndi ochepa amene anaopa munthu. Willy Lages, membala wankhanza kwambiri wa gulu la apolisi akabisalira la ku Germany, anati “90 peresenti ya Mboni za Yehova anakana kuulula chilichonse, pamene chiŵerengero chochepa kwambiri cha magulu ena a zipembedzo
n’chimene chinatha kungokhala chete, osanena kanthu kalikonse.” Zimene anafotokoza mtsogoleri wachipembedzo wachidatchi Johannes J. Buskes, amene anaikidwa m’ndende pamodzi ndi Mboni zina zikutsimikizira mawu a Lages. Mu 1951, Buskes analemba kuti:“Panthaŵiyo, ndinayamba kuwachitira ulemu kwambiri chifukwa cha kukhulupirira kwawo Mulungu ndi kulimba kwa chikhulupiriro chawo. Sindidzaiŵala ngakhale pang’ono mnyamata wina—ayenera kuti anali ndi zaka zakubadwa zosaposera pa 19—amene anagaŵa timabuku toneneratu za kugwa kwa Hitler ndi Ulamuliro wa Nazi. . . . Akanatulutsidwa m’ndendemo m’kati mwa miyezi isanu ndi umodzi ngati akanalonjeza kuti sadzapitiriza ntchito imeneyo. Iye anakana kwam’tuwagalu kusiya kuchita zimenezi, ndipo analamulidwa kukagwira ntchito yachibalo kwa moyo wake wonse ku Germany. Tinadziŵa bwino lomwe chimene zimenezo zimatanthauza. M’maŵa wotsatira pamene anatengedwa ndipo titatsanzikana naye, ndinamuuza kuti tizimuganizira ndi kumam’pempherera. Yankho lake linali kungoti: ‘Musadere nkhaŵa za ine. Ufumu wa Mulungu udzabwera ndithu.’ Chinthu ngati chimenecho simungachiiwale, ngakhale mutakhala wotsutsa motani ziphunzitso za Mboni za Yehova zimenezi.”
Mosasamala kanthu za chitsutso chankhanza, chiŵerengero cha Mboni chinapitirizabe kuwonjezeka. Ngakhale kuti anali 300 okha nkhondo yadziko yachiŵiri itatsala pang’ono kuyamba, mu 1943 chiŵerengero chinali chitakwera mpaka 1,379. N’zomvetsa chisoni kuti podzafika kumapeto kwa chaka chimenecho, 54 mwa Mboni zoposa 350 zimene zinamangidwa zinali zitafa m’misasa yachibalo yosiyanasiyana. Ndipo mu 1944, panali Mboni za Yehova zokwana 141 za mu Netherlands zimene zinali zikadali m’misasa yachibalo yosiyanasiyana.
Chaka Chomaliza cha Chizunzo cha Anazi
Pambuyo pa tsiku lotchedwa D day, June 6, 1944, kuzunzidwa kwa Mboni kunaloŵa chaka chomaliza. Anazi ndi anzawo anali kugonja pazankhondo. Munthu angaganize kuti panthaŵi imeneyi Anazi akanasiya kusakasaka ndi kugwira Akristu osalakwa. Koma ngakhale zinali choncho, m’chaka chimenecho, Mboni zina zokwanira 48 zinamangidwa, ndiponso zina 68 mwa Mboni zimene zinali kundende zinafa. Mmodzi wa ameneŵa anali Jacob van Bennekom, wotchulidwa poyambapo.
Jacob pamene anali ndi zaka 18 zakubadwa anali mmodzi mwa anthu 580 amene anabatizidwa monga Mboni za Yehova mu 1941. Mwamsanga pambuyo pake anasiya ntchito yabwino kwambiri chifukwa chakuti inafuna kuti aloŵerere pa nkhani zandale. Anayamba ntchito yopereka mauthenga ndi kuyamba kutumikira monga mtumiki wanthaŵi zonse. Iye anagwidwa ndi kumangidwa pamene amakasiya mabuku ofotokoza Baibulo. Pamene anali ndi zaka 21 mu August 1944,
Jacob analembera banja lake kalata kuchokera kundende ina ya mu mzinda wa Rotterdam:“Ndili bwino kwambiri ndiponso wachimwemwe kwambiri. . . . Tsopano ndakhala ndikufunsidwa mafunso maulendo anayi. Maulendo aŵiri oyambirirawo anali oŵaŵa kwambiri, ndipo ndinamenyedwa koopsa, koma mwa mphamvu ya Ambuye ndi chisomo chake, mpaka tsopano lino sindinaululepo kanthu kalikonse. . . . Ndayamba kale kukamba nkhani kuno, zonse zokwanira zisanu ndi imodzi, ndi chiŵerengero chonse cha omvetsera chokwanira 102. Ena mwa ameneŵa akusonyeza chidwi ndipo analonjeza kuti akadzangomasulidwa, adzapitiriza kutero.”
Pa September 14, 1944, Jacob anam’tengera ku msasa wachibalo mu mzinda wachidatchi wa Amersfoort. Kumenekonso iye anapitirizabe kulalikira. Motani? Mkaidi mnzake anakumbukira kuti: “Akaidi amatola zidutswa za ndudu zotayidwa ndi alonda a ndende ndi kugwiritsa ntchito mapepala a Baibulo kukulungira ndudu. Nthaŵi zina Jacob amatha kuŵerenga mawu ochepa pa pepala la Baibulo limene latsala pang’ono kuti ligwiritsidwe ntchito yokulungira ndudu. Nthaŵi yomweyo, amatha kugwiritsa ntchito mawu amenewo panthaŵi imene akutilalikira. Posapita nthaŵi tinam’patsa dzina losemera lakuti ‘Mwamuna wa Baibulo.’”
Mu October 1944, Jacob anali pakati pa gulu lalikulu la akaidi amene analamulidwa kukumba mbuna zoti muzigwera akasinja. Jacob anakana kugwira nawo ntchito imeneyo chifukwa chakuti chikumbumtima chake sichinamulole kuchirikiza ntchito za nkhondo. Iye sanavomerebe, ngakhale kuti alonda ankamuopseza kaŵirikaŵiri. Pa October 13, mkulu wina wa ndende anachotsa Jacob kumalo kwayekha ndi kum’bwezera kumalo antchito. Apanso, Jacob anamamatirabe ku mfundo zake. Pomalizira pake, Jacob analamulidwa kukumba manda ake ndipo anamuwombera ndi mfuti n’kufa.
Kusakasaka Mboni Kupitirizabe
Kulimba mtima kwa Jacob ndi ena kunakhumudwitsa Anazi ndipo kunachititsa kusakidwa kwinanso kwa Mboni. Mmodzi mwa amene amawafunafuna kwambiri anali Evert Kettelari wa zaka 18. Poyamba, Evert anathaŵa ndi kubisala, koma pambuyo pake anamangidwa ndi kumenyedwa kwambiri n’cholinga choti awauze za Mboni zina. Iye anakana ndipo m’malo mwake anatumizidwa ku Germany kuti akagwire ntchito ya chibalo.
Mwezi womwewo, October 1944, apolisi anayamba kufunafuna mlamu wa Evert, Bernard Luimes.
Pamene anam’peza, iye anali pamodzi ndi Mboni zina ziŵiri—Antonie Rehmeijer ndi Albertus Bos. Albertus anali atatha kale miyezi 14 mu msasa wachibalo. Komabe, atatulutsidwa, iye mokangalika anapitirizabe ntchito yolalikira. Poyamba amuna atatuwo anamenyedwa kwambiri ndi Anazi, ndipo kenako anawomberedwa ndi mfuti n’kufa. Nkhondoyo itatha m’pamene matupi awo anapezedwa ndi kuikidwa m’manda bwinobwino. Nkhondoyo itangotha manyuzipepala ambiri analemba za kuphedwa kumeneku. Imodzi mwa manyuzipepalawo inalemba kuti Mboni zitatuzo zinakanitsitsa kugwirira Anazi ntchito iliyonse yosemphana ndi lamulo la Mulungu ndipo inawonjezera kuti “pachifukwa chimenechi, iwo anayenera kupereka miyoyo yawo.”Komabe, pa November 10, 1944, Bernard Polman, wotchulidwa kumayambiriroyo, anamangidwa ndi kutumizidwa kukagwira ntchito yokhudzana ndi za nkhondo. Mwa anthu onse amene anakakamizidwa kukagwira ntchitowo, iye yekha ndi amene anali Mboni ndipo ndi yekhayo amene anakana kugwira nawo ntchito imeneyi. Alonda anayesayesa njira zosiyanasiyana n’cholinga choti am’gonjetse. Sanapatsidwe chakudya. Komanso anamenyedwa ndi zibonga, zokumbira, ndi mtibo wa mfuti. Kuwonjezera pamenepo, iye analamulidwa kuyenda m’madzi ozizira akuya kulekeza m’maondo, ndipo kenako anatsekeredwa m’kanyumba kachinyontho, momwe anakhala usiku wonse ndi zovala zake zonyoŵa. Komabe, Bernard sanagonje.
M’nthaŵi imeneyo, aŵiri mwa alongo a Bernard, amene sanali Mboni za Yehova, analoledwa kudzamuona. Anamulangiza kuti asinthe maganizo ake, koma sizinam’chititse kusintha malingaliro. Pamene iwo anafunsa Bernard ngati angam’chitire chinthu chinachake, iye anawauza kuti apite kunyumba ndi kukaphunzira Baibulo. Kenako om’zunzawo analola mkazi wake amene anali ndi pakati kuti adzamuone, akumayembekezera kuti mkaziyo amufooketsa. Koma kubwera kwake ndiponso mawu ake olimbikitsa zinangothandizira kulimbitsa cholinga cha Bernard cha kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu. Pa November 17, 1944, Bernard anawomberedwa ndi mfuti ndi anthu asanu mwa anthu amene amam’zunza pamene ena onse okakamizidwa kugwira ntchitowo akuonerera. Ngakhale pambuyo poti Bernard wafa, thupi lake litadzala ndi zipolopolo, mkulu wa alondawo anakwiya kwambiri kotero kuti anatulutsa volovolo ndi kuwombera Bernard m’maso ake onse.
Ngakhale kuti nkhanza zimenezi zinamvetsa chisoni Mboni zimene zinadziŵa za kuphedwaku, izo zinakhalabe zokhulupirika ndi zopanda mantha ndipo zinapitiriza ntchito yawo yachikristu. Mpingo wina waung’ono wa Mboni za Yehova, wapafupi ndi pamene Bernard anaphedwera, mwamsanga pambuyo pa kuphedwaku unapereka lipoti lakuti: “Mwezi uno, mosasamala kanthu zanyengo yozizira ndi mavuto amene Satana akutipinga nawo, tatha kuwonjezera ntchito yathu. Chiŵerengero cha maola amene tathera m’munda chinachoka pa 429 kufika pa 765. . . . Mbale wina pamene amalalikira, anakumana ndi mwamuna wina amene anatha kum’chitira umboni wabwino. Mwamunayo anafunsa ngati chimenechi ndi chikhulupiriro chimodzimodzi ndi cha mwamuna amene anaphedwa uja. Atamva kuti ndi chimenecho, mwamunayo anafuula kuti: ‘Ndi munthu wodabwitsa, ndi chikhulupiriro chodabwitsa! Ameneyo ndi amene ndimati ngwazi m’chikhulupiriro!’”
Akukumbukiridwa Ndi Yehova
Mu May 1945, Anazi anagonjetsedwa ndipo anathamangitsidwa m’dziko la Netherlands. Mosasamala kanthu za chizunzo chosaletseka m’nthaŵi ya nkhondo, chiŵerengero cha Mboni za Yehova chinali chitawonjezereka kuchoka pa mazana ochepa ndi kufika pa oposa 2,000. Ponenapo za Mboni za m’nthaŵi ya nkhondo zimenezi, wolemba mbiri Dr. de Jong anavomereza kuti: “Ambiri mwa iwo sanalole kukana chikhulupiriro chawo ngakhale kuti ankaopsezedwa komanso ankazunzidwa.”
Chotero, pali chifukwa chabwino kuti akuluakulu ena a boma anakumbukira Mboni za Yehova chifukwa cha kulimba mtima kwawo mu ulamuliro wa Anazi. Chofunika kwambiri n’chakuti mbiri yabwino ya Mboni za m’nthaŵi ya nkhondo zimenezi idzakumbukiridwa ndi Yehova ndiponso Yesu. (Ahebri 6:10) Mu Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Yesu Kristu umene wayandikirawo, Mboni zokhulupirika ndi zolimba mtima zimenezi zomwe zinapereka miyoyo yawo kutumikira Mulungu zidzaukitsidwa kuchokera ku manda, ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso!—Yohane 5:28, 29.
[Chithunzi patsamba 24]
Jacob van Bennekom
[Chithunzi patsamba 26]
Nyuzipepala ikulengeza za lamulo la kuletsedwa kwa Mboni za Yehova
[Zithunzi patsamba 27]
Kulamanja: Bernard Luimes; m’munsi: Albertus Bos (kulamanzere) ndi Antonie Rehmeijer; m’munsi: Ofesi ya Sosaite ku Heemstede