Kuthirira Mbewu za Choonadi ku Chile
Olengeza Ufumu Akusimba
Kuthirira Mbewu za Choonadi ku Chile
KU CHIPULULU cha kumpoto kwa Chile, zaka zingadutse mvula osabwera. Koma ikabwera, nthaka yake youma gwa imasintha kukhala munda wokongola wa maluŵa osiyanasiyana. Maonekedwe okongola ameneŵa amakopa alendo ochokera m’dziko lonselo.
Komabe, chinthu chachilendo chikuchitika kwa anthu a ku Chile. Madzi a choonadi cha m’Baibulo akuyenderera ku mbali zonse za dzikolo, ndipo anthu ambiri oona mtima “akukula” kukhala ophunzira a Yesu Kristu. Njira imodzi imene ikugwiritsidwa ntchito kufalitsa madzi a choonadi ameneŵa ndi ya pa telefoni. Zochitika zotsatirazi zikusonyeza zinthu zabwino zimene zakhalapo chifukwa chotsatira njira imeneyi yochitira umboni.
• Mlaliki wa nthaŵi zonse wotchedwa Karina anapemphedwa kusonyeza chitsanzo cha umboni wa patelefoni pamsonkhano wadera. Komabe, Karina anali asanachitepo umboni wamtundu umenewu. Pofuna kum’limbikitsa kuti adzakhale ndi mbali pamsonkhano umenewo, mkulu wina pamodzi ndi mkazi wake anapenda mfundo zina limodzi ndi Karina za mmene angachitire umboni wa patelefoni. Anam’limbikitsanso kupempha Yehova kuti am’tsogolere pankhani imeneyo. Anaterodi, ndipo pomaliza anaganiza zoyesa kuimba telefoni.
Karina anasankha nambala ya telefoni ya mudzi wapafupi. Woyankha mafoni anayankha, ndipo Karina anafotokoza cholinga chimene anaimbira. Woyankhayo anakondwera nazo zimenezo, ndipo anagwirizana kudzalankhulananso patatha masiku atatu. Ulendo wobwereza wa patelefoni unachititsa kuti ayambe kuphunzira Baibulo, pogwiritsa ntchito bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Kuyambira nthaŵi imeneyo, akhala ndi maphunziro osangalatsa, ndipo Karina watumiza mabuku oyankha mafunso a mkaziyo.
• Bernarda anapezerapo mwayi kuchitira umboni kwa mwamuna wina amene mosadziŵa anaimba nambala yake ya foni. M’malo moipidwa, Bernarda anamuuza kuti ndi wa Mboni za Yehova ndipo anati atha kum’thandiza. Kenaka anayamba kukambirana, ndipo mwamunayo anamvetsera pamene ankafotokoza mmene Ufumu wa Mulungu udzathetsera kupanda chilungamo. Mwamunayo anam’patsa Bernarda nambala yake ya foni, ndipo anachita maulendo obwereza patelefoniyo. Panthaŵi ina pamene anali kukambirana, anamuŵerengera penapake m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Mwamunayo anafunsa mmene akanapezera buku lakelake, ndipo Bernarda anam’tumizira bukulo pamodzi ndi Baibulo. Makonzedwe anapangidwa kuti mwamunayo achezeredwe ndi mbale wakomweko, amene tsopano akupitiriza “kuthirira mbewu” yosangalala imeneyi.
Inde, mu nthaka yauzimu youma gwa ya dziko lino, mbewu zobisika zikudikira kumera pamene madzi a moyo a choonadi azifika. Anthu ambirimbiri aludzu akupitiriza ‘kuphuka’ ndi “kukula” kukhala atumiki okhulupirika a Yehova Mulungu.—Yesaya 44:3, 4.