Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Nthaŵi za Kukonzanso” Zayandikira!

“Nthaŵi za Kukonzanso” Zayandikira!

“Nthaŵi za Kukonzanso” Zayandikira!

Yesu atatsala pang’ono kupita kumwamba, ena mwa ophunzira ake okhulupirika anam’funsa kuti: “Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” Yankho la Yesu linasonyeza kuti Ufumu udzabwera patapita nthaŵi. Panthaŵiyo, otsatira ake akakhala ndi ntchito yaikulu yoti agwire. Anali kudzakhala mboni za Yesu “m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.”​—Machitidwe 1:6-8.

NTCHITO imeneyo sinali yoti n’kuigwira masiku, milungu, kapena miyezi yochepa chabe. Mosasamala kanthu za zimenezo, ophunzirawo anayamba kulalikira nthaŵi yomweyo. Komabe si kuti anachotsa malingaliro awo pankhani ya kukonzanso. Mtumwi Petro analankhula za nkhaniyo kwa gulu limene linasonkhana m’Yerusalemu akumati: ‘Lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye; ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Kristu Yesu; amene thambo la kumwamba liyenera kum’landira kufikira nthaŵi za kukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m’kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.’​—Machitidwe 3:19-21.

“Nthaŵi za kukonzanso” zimenezi zinali zoti zidzayamba mu “nyengo zakutsitsimutsa” zochokera kwa Yehova. Kukonzanso koloseredwako kunali koti kudzachitika kaŵiri. Koyamba, ndiko kukonzanso kotsitsimula kwauzimu, kumene kukuchitika pakalipano. Kwachiŵiri, kunali kukhazikitsidwa kwa paradaiso weniweni padziko lapansi.

Nthaŵi za Kukonzanso Ziyamba

Monga momwe mtumwi Petro anauzira gulu la ku Yerusalemu, thambo la kumwamba ‘linam’landira Yesu.’ Izi zinali choncho mpaka chaka cha 1914, pamene Yesu anatenga mphamvu ya Ufumu ndi kuyamba kulamulira monga Mfumu yoikidwa ndi Mulungu. Panthaŵi imeneyo, Petro analosera kuti, Yehova, ‘adzatuma’ Mwana wake mu lingaliro lakuti Iye anali kudzalola kuti Yesu agwire ntchito yake monga munthu wofunika kwambiri pa zifuno za Mulungu. Baibulo limalongosola nkhaniyi mophiphiritsa likumati: “Ndipo [gulu la Mulungu la kumwamba] [li]nabala mwana wamwamuna, [Ufumu wa Mulungu m’manja mwa Yesu Kristu] amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo.”​—Chivumbulutso 12:5.

Koma mitundu ya anthu inalibe malingaliro ogonjera ulamuliro wa Kristu. Ndithudi, anazunza anthu ake okhulupirika apadziko lapansi, amene lerolino amadziŵika kuti Mboni za Yehova. Monga atumwi anzawo oyambirira, Mboni mosazengereza zinali kuchita “umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 12:17) M’mayiko osiyanasiyana munayamba zitsutso zoletsa ntchito imene Akristu oona ameneŵa ankachita. M’chaka cha 1918, mamembala a likulu la Watch Tower Society ku Brooklyn, New York, anatengeredwa ku khoti pankhani zabodza ndipo mokondera anauzidwa kukhala m’ndende nthaŵi yaitali. Panthaŵi imeneyi zinaoneka kuti ntchito yochitira umboni “kufikira malekezero ake a dziko” mu nthaŵi zamakono ilephereka.​—Chivumbulutso 11:7-10.

Komabe, m’chaka cha 1919, mamembala amene anamangidwa aja anamasulidwa ndipo kenako anauzidwa kuti pankhani zonse zabodzazo analibe mlandu. Nthaŵi yomweyo anayambanso ntchito ya kukonzanso mwauzimu. Kuyambira nthaŵi imeneyo, anthu a Yehova akhala akusangalala ndi kupita patsogolo mwauzimu kuposa nthaŵi zam’mbuyomo.

Anachita ndawala kuphunzitsa anthu amitundu yonse kusunga zinthu zimene Kristu analamula otsatira ake kuti achite. (Mateyu 28:20) Sikutsitsimula kwake kuona ena amene anali ndi mikhalidwe ya ngati yanyama akusintha malingaliro awo! Anavula umunthu wakale, umene umabala mikhalidwe ngati “kupsa mtima,” “mwano” “zonyansa zotuluka mkamwa,” ndi kuvala umunthu watsopano, ‘umene ulikukonzeka watsopano, kuti ukhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha [Mulungu] amene anaulenga uwo.’ Mu lingaliro lauzimu, mawu a mneneri Yesaya akukwaniritsidwa ngakhale pakalipano: “Mmbulu [munthu amene poyamba anali wa mikhalidwe ya ngati ya mmbulu] udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa [munthu wosonyeza mikhalidwe yofatsa], ndipo nyalungwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi.”​—Akolose 3:8-10; Yesaya 11:6, 9.

Kukonzanso Kowonjezeka Kwayandikira!

Kuwonjezera pa kukonzanso kumene kukuchitika lerolino m’paradaiso wauzimu, nthaŵi ikudza posachedwapa imene pulaneti lathuli lidzakhala paradaiso weniweni. Mbali yochepa padziko lapansi inali paradaiso pamene Yehova anaika makolo athu akalewo, Adamu ndi Hava, m’munda wa Edene. (Genesis 1:29-31) N’chifukwa chake tinganene za kukonzedwanso kwa Paradaiso. Komabe, zisanachitike zimenezi, dziko lapansi liyenera kukhala lopanda zipembedzo zonyenga zosalemekeza Mulungu. Magulu a ndale a dziko lino ndiwo adzachite mbali imeneyi. (Chivumbulutso 17:15-18) Kenako, magulu andale ndi amalonda, ndi otsatira awo omwe, adzawonongedwa. Pomalizira pake, wotsutsa Mulungu womaliza​—Satana Mdyerekezi ndi ziwanda zake​—adzatsekeredwa kwa zaka 1,000​—umene uli utali wanthaŵi ya ntchito ya kukonzanso. M’nthaŵi imeneyo, “chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa.” (Yesaya 35:1) Dziko lonse lidzakhala lopanda chisokonezo. (Yesaya 14:7) Ngakhale mamiliyoni a anthu amene anamwalira adzabwezeretsedwa ku moyo padziko lapansi. Anthu onse adzasangalala ndi mapindu okonzanso a nsembe ya dipo. (Chivumbulutso 20:12-15; 22:1, 2) Padziko lapansi sipadzakhalanso anthu akhungu, osamva, kapena olumala. “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ulamuliro wa Kristu wa Zaka 1,000 ukadzangotha, Mdyerekezi ndi ziwanda zake adzamasulidwa kwanthaŵi yochepa ndipo adzaona mmene chifuno cha Mulungu pa dziko lapansi chakwaniritsidwira panthaŵi imeneyo. Kenako, adzawonongedwa kosatha.​—Chivumbulutso 20:1-3.

Dziko lapansi likadzafika kumapeto kwa zaka 1,000 za kukonzanso, “zonse zakupuma” zidzalemekeza Yehova, ndipo zidzatero kwamuyaya. (Salmo 150:6) Kodi mudzakhala pakati pawo? Mukhoza kudzakhala.