Sonyezani Mtima Wodikira!
Sonyezani Mtima Wodikira!
“Ndidzadikira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.”—MIKA 7:7.
1, 2. (a) Kodi kukhala ndi mtima wolakwika kunawawononga motani Aisrayeli m’chipululu? (b)Kodi chingachitike n’chiyani kwa Mkristu yemwe sakukulitsa mtima woyenera?
ZINTHU zambiri m’moyo zingaonedwe kukhala zotsimikizirika kapena zokayikitsa malinga ndi mtima umene tili nawo. Aisrayeli ali m’chipululu, anapatsidwa mana mozizwitsa. Anafunikira kuyang’ana dziko lopanda zomera limenelo ndi kuyamikira kwambiri Yehova kuti anawapatsa chakudya chimenechi. Kuchita zimenezi kukanasonyeza kuti anali ndi mtima wabwino. M’malo mwake, anakumbukira mitundu yosiyanasiyana ya zakudya za ku Aigupto ndi kuyamba kunyinyirika kuti mana sanali opatsa madyo. Mtimatu woipa zedi!—Numeri 11:4-6.
2 Mtima umene Mkristu lerolino ali nawo mofananamo ungapange zinthu kuoneka ngati zolimbikitsa kapena zogwetsa ulesi. Popanda kukhala ndi mtima woyenera, Mkristu angataye chimwemwe chake mosavuta, ndipo zimenezo zingakhale zoopsa kwambiri chifukwatu, monga momwe Nehemiya ananenera: “Chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu [yathu].” (Nehemiya 8:10) Kukhala ndi mtima wabwino ndiponso wachimwemwe kumatithandiza kukhala amphamvu ndipo kumalimbikitsa mtendere ndi mgwirizano mu mpingo.—Aroma 15:13; Afilipi 1:25.
3. Kodi mtima woyenera unamuthandiza motani Yeremiya m’nthaŵi zovuta?
3 Mosasamala kanthu kuti anali kukhala m’nthaŵi zovuta, Yeremiya anasonyeza mtima wabwino. Ngakhale pambuyo poonerera zinthu zochititsa mantha pa kugwa kwa Yerusalemu mu 607 B.C.E., iye anali kuonanso zinthu zabwino. Yehova sakanaiŵala Israyeli, ndipo mtunduwo unali kudzapulumuka. Yeremiya analemba m’buku la Maliro kuti: “Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka. Chioneka chatsopano m’maŵa ndi m’maŵa. Mukhulupirika ndithu.” (Maliro 3:22, 23) Atumiki a Mulungu m’mbiri yonse, ayesetsa kuti akhalebe ndi malingaliro abwino ngakhalenso achimwemwe m’mikhalidwe yovuta kwambiri.—2 Akorinto 7:4; 1 Atesalonika 1:6; Yakobo 1:2.
4. Kodi Yesu anali ndi mtima wotani, ndipo unam’thandiza motani?
4 Patatha zaka 600 Yeremiya atamwalira, kukhala ndi mtima wabwino kunam’thandiza Yesu kupirira. Timaŵerenga kuti: “Chifukwa cha chimwemwe Ahebri 12:2) Mosasamala kanthu za mtundu wa chitsutso kapena chizunzo zomwe Yesu anali kuyang’anizana nazo—ngakhale ululu wosaneneka wa pamtengo wozunzirapo—anaika malingaliro ake pa “chimwemwe choikidwacho pamaso pake.” Chimwemwe chimenecho chinali mwayi wa kudziŵikitsa ulamuliro wa Yehova ndi kuyeretsa dzina lake limodzi ndi chiyembekezo cha kudzetsera mtundu wa anthu okhulupirika madalitso ochuluka m’tsogolo.
choikidwacho pamaso pa [Yesu], anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Phunzirani Kudikira
5. Kodi ndi pachochitika chenicheni chotani pamene kukhala ndi mtima wa kudikira kudzatithandiza kusungabe kaonedwe koyenera ka zinthu?
5 Ngati tingakulitse mtima monga wa Yesu, sitidzataya chimwemwe cha Yehova ngakhale ngati nthaŵi zonse zinthu sizichitika monga momwe timafunira komanso panthaŵi yomwe timayembekezera. Mneneri Mika anati: “Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa.” (Mika 7:7; Maliro 3:21) Nafenso tingasonyeze kuti tikudikira. Motani? M’njira zambiri. Choyamba, tingalingalire kuti mbale waudindo walakwa pochita zinthu ndi kuti pakufunika kumuwongolera mwamsanga. Kukhala ndi mtima wodikira kudzatichititsa kulingalira kuti, ‘Kodi analakwadi, kapena ndine amene sindikulondola? Ngati analakwa, kodi zingakhale kuti Yehova akulola zimenezo kuchitika chifukwa chakuti akudziŵa kuti munthuyo adzasintha ndi kuti kuchita zinthu mwaphuma poyesa kumuwongolera kungakhale kosafunika?’
6. Kodi mtima wodikira ungathandize motani munthu amene akulimbana ndi mavuto aumwini?
6 Mtima wodikira ungafunike ngati tasautsidwa maganizo ndi vuto laumwini kapena tikulimbana ndi chofooka chathu. Tinene kuti tapempha thandizo la Yehova, koma vutolo likungopitirizabe. Tingatani pamenepo? Tiyenera kupitirizabe kuchita chilichonse chomwe tingathe ndi mphamvu zathu kuti tithetse vutolo, ndiyeno tikatero tikhale nacho chikhulupiriro m’mawu a Yesu akuti: “Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.” (Luka 11:9) Pitirizanibe kupemphera, ndipo yembekezerani Yehova. Pa nthaŵi yoyenera ndiponso m’njira yakeyake, Yehova adzayankha mapemphero anu.—1 Atesalonika 5:17.
7. Kodi mtima wodikira udzathandiza motani kaonedwe kathu ka kumveketsa pang’onopang’ono kamvedwe kathu ka Baibulo?
7 Pamene maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa, kamvedwe kathu ka Malemba kamawongoleredwa. Komabe, nthaŵi zina tingaganize kuti kumveketsa kwina kwachedwa kwambiri. Koma ngati kumveketsako sikukuchitika panthaŵi yomwe timayembekezera, kodi ndife ofunitsitsa kudikira? Kumbukirani, Yehova anaona kuti kunali koyenera kuvumbula “chinsinsi cha Kristu” pang’ono chabe panthaŵi imodzi ndipo anachita zimenezi kwa nyengo yoposa zaka ngati 4,000. (Aefeso 3:3-6) Choncho, kodi ife tili ndi chifukwa chilichonse chotayira mtima? Kodi tikukayikira kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” waikidwa kuti apatse anthu a Yehova ‘zakudya panthaŵi yake’? (Mateyu 24:45) N’kutayiranji chimwemwe chathu chaumulungu kokha chifukwa chakuti zinthu zina sitikuzimvetsa mokwanira? Kumbukirani, Yehova ndiye amene amalinganiza nthaŵi ndi njira yomwe adzavumbulira ‘zinsinsi’ zake.—Amosi 3:7.
8. Kodi kuleza mtima kwa Yehova kwaoneka motani kukhala kopindulitsa kwa anthu ambiri?
8 Ena angagwe mphwayi chifukwa cholingalira kuti pambuyo pa zaka zambirimbiri za kutumikira mokhulupirika, sadzakhoza kuona “tsiku la Yehova lalikulu loopsa.” (Yoweli 2:30, 31) Komabe, angalimbikitsidwe ngati atayang’ana mbali yabwino. Petro anachenjeza kuti: “Yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso.” (2 Petro 3:15) Kuleza mtima kwa Yehova kwapereka mpata wakuti miyandamiyanda ya anthu owongoka mtima owonjezereka aphunzire choonadi. Si zosangalatsa kodi zimenezo? Komanso, pamene Yehova akuleza mtima kwa nthaŵi yaitali, m’pamenenso tili ndi nthaŵi yochuluka ya ‘kugwira ntchito ya chipulumutso [chathu] ndi mantha, ndi kunthunthumira.’—Afilipi 2:12; 2 Petro 3:11, 12.
9. Ngati timalephera kukwanitsa zimene timafuna titachita mu utumiki wa Yehova, kodi mtima wodikira udzatithandiza motani kupirira mkhalidwewo?
9 Mtima wodikira umatithandiza kuti tisafooke pamene chitsutso, matenda, ukalamba, kapena mavuto ena alionse atijejemetsa mu utumiki wa Ufumu. Yehova amafuna kuti tim’tumikire ndi mtima wonse. (Aroma 12:1) Komabe, Mwana wa Mulungu, yemwe amachitira “nsoni wosauka ndi waumphawi,” safuna zochuluka kuposa zomwe ife tingakwanitse; Yehovanso satero. (Salmo 72:13) Chotero, tikulimbikitsidwa kuchita zomwe tingathe, kuyembekezera moleza mtima kufikira zinthu zitasintha—kaya m’dongosolo lino la zinthu kapena m’dongosolo lomwe lili mkudzalo. Kumbukirani kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”—Ahebri 6:10.
10. Ndi mkhalidwe wosakhala waumulungu uti womwe munthu wa mtima wodikira angaupeŵe? Fotokozani.
10 Mtima wodikira umatithandizanso kupeŵa kudzikuza. Ena omwe akhala ampatuko sanali ofunitsitsa kudikira. Mwinamwake analingalira kuti panali kufunikira kwa kusintha zinthu zinazake, mwina pa kamvedwe ka Baibulo kapena pa nkhani zina zokhudza gulu. Komabe, sanazindikire kuti mzimu wa Yehova umatsogolera kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kusintha zinthu mu nthaŵi Yake yoikika, osati m’nthaŵi yomwe ife tingaone ngati nthaŵi yabwino yosintha zinthu. Ndipo kusintha kulikonse kuyenera kugwirizana ndi chifuno cha Yehova, osati malingaliro athu ayi. Ampatuko amalola kudzitukumula kukuta malingaliro awo ndi kuŵakhumudwitsa. Koma ngati akanatsanzira mtima wa Kristu, akanasungabe chimwemwe chawo ndi kukhalabe m’gulu la anthu a Yehova.—Afilipi 2:5-8.
11. Kodi nthaŵi yomwe tingathere podikira tingaigwiritse ntchito motani kuti tipindule nayo, ndipo tingakhale tikutsanzira chitsanzo chayani?
11 N’zoona kuti kukhalabe ndi mtima wodikira sikutanthauza kukhala waulesi kapena kungokhala phwii osachita china chilichonse. Tili n’zochita zambiri. Mwachitsanzo, tiyenera nthaŵi zonse kupanga phunziro laumwini la Baibulo ndi kuti potero tikasonyeze chidwi chimodzimodzicho pa zinthu zauzimu chomwe aneneri okhulupirika ngakhalenso angelo anasonyeza. Pofotokoza za chidwi choterocho, Petro anati: “Kunena za chipulumutso ichi anafunafuna nasanthula aneneri . . . zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.” (1 Petro 1:10-12) Si phunziro laumwini lokha limene sitiyenera kulinyalanyaza, kupezeka pa misonkhano nthaŵi zonse komanso pemphero, siziyenera kunyalanyazidwa. (Yakobo 4:8) Awo amene amasonyeza kuzindikira zosoŵa zawo zauzimu mwa kudya chakudya chauzimu nthaŵi zonse ndi kuyanjana ndi Akristu anzawo amasonyeza kuti atengera mtima wa Kristu.—Mateyu 5:3.
Khalani ndi Kaonedwe Koyenera
12. (a) Kodi Adamu ndi Hava anafuna ufulu wotani? (b)Kodi pakhala zotsatira zotani pa kutsatira njira ya Adamu ndi Hava kwa mtundu wa anthu?
12 Mulungu atalenga mwamuna ndi mkazi oyambawo, iye ndiye anali ndi ulamuliro wonse wa kuika miyezo pa chabwino ndi choipa. (Genesis 2:16, 17) Adamu ndi Hava anafuna kudziimira paokha popanda chitsogozo cha Mulungu, ndipo zotsatira zake zinali mtundu wa dziko lotizinga lamakonoli. Mtumwi Paulo anati: “Monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Zaka 6,000 za mbiri ya anthu kuchokera m’nthaŵi ya Adamu zasonyeza choonadi cha mawu a Yeremiya akuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Kuvomereza kuti mawu a Yeremiyawo n’ngoona si kuvomera kulephera. Koma ndi mmenedi zinthu zilili. Amafotokoza zochitika m’zaka mazana onsewo pamene “wina [w]apweteka mnzake pom’lamulira” chifukwa chakuti anthu achita ulamuliro popanda chitsogozo cha Mulungu.—Mlaliki 8:9.
13. Ndi kaonedwe koyenera kati komwe Mboni za Yehova zili nako pa zinthu zomwe anthu angathe kuchita?
13 Poona mkhalidwe wa zinthu womwe mtundu wa anthu ulimo, Mboni za Yehova zikuzindikira kuti pali malire pa zinthu zomwe munthu angathe kuchita mwachipambano m’dongosolo la zinthu lamakono lino. Kukhala ndi mtima wabwino kungatithandize kusungabe chimwemwe chathu, koma si ndiyo njira yothetsera vuto lililonse. Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1950, mtsogoleri wina wachipembedzo wa ku America analemba buku lomwe linagulidwa kwambiri lotchedwa The Power of Positive Thinking, (Mphamvu ya Kuganiza Zabwino). Bukulo linafotokoza kuti zopinga zambiri zingathe kugonjetsedwa ngati tiyesa kuzithetsa tili ndi malingaliro abwino. Ndithudi kuganiza kwabwino n’chinthu chapamwamba zedi. Koma zochitika zikusonyeza kuti chidziŵitso, luso, zinthu zakuthupi zimene tili nazo, komanso zinthu zina zambiri zimaika malire pa zomwe ife aliyense payekha angathe kuchita bwino lomwe. Ndipo padziko lonse, mavuto n’ngaakulu kwabasi kotero kuti anthu sangathe n’komwe kuwathetsa—ngakhale ataganiza bwino motani!
14. Kodi Mboni za Yehova zili ndi malingaliro oipa? Fotokozani.
14 Chifukwa cha kaonedwe kawo koyenera pa nkhani ngati zimenezo, nthaŵi zina Mboni za Yehova zimanenedwa kuti zili ndi malingaliro olakwika. Mosiyana ndi zimenezo, izo n’zofunitsitsa kuuza anthu za Mmodzi yekha yemwe angakonze mavuto a mtundu wa anthu kwa muyaya. Pochita zimenezi amatsanziranso mtima wa Kristu. (Aroma 15:2) Ndipo n’ngotanganidwa kuthandiza anthu kupeza unansi wabwino ndi Mulungu. Akudziŵa kuti pambuyo pake, zimenezi zidzakwaniritsa chinthu chabwino kwambiri.—Mateyu 28:19, 20; 1 Timoteo 4:16.
15. Kodi ntchito ya Mboni za Yehova imasintha motani anthu kukhala abwino?
15 Mboni za Yehova sizinyalanyaza mavuto a anthu amene akukhala nawo, makamaka makhalidwe odetsa osemphana ndi Malemba. Munthu wosonyeza chidwi asanakhale m’modzi wa Mboni za Yehova, amasintha, kaŵirikaŵiri amafunikira kugonjetsa zizoloŵezi zake zomwe sizikondweretsa Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11) Motero Mboni za Yehova zathandiza anthu omvera kugonjetsa uchidakwa, kumwerekera ndi mankhwala ozunguza bongo, chisembwere, ndi kukopeka kutchova juga. Anthu osintha mikhalidwe ameneŵa aphunzira kupezera mabanja awo zinthu zofunika mozindikira udindo wawo komanso m’njira zachilungamo. (1 Timoteo 5:8) Anthu ndi mabanja akathandizidwa m’njira imeneyi, mavuto amachepa pamudzi —anthu omwerekera ndi mankhwala osokoneza bongo amachepa, ziwawa za m’mabanja zimachepa, ndi zina zotero. Mwa kukhala nzika zotsata malamulo ndiponso mwa kuthandiza ena kusintha miyoyo yawo kukhala yabwino, Mboni za Yehova zachepetsa nkhaŵa yomwe mabungwe omwe amagwira ntchito yothetsa mavuto a anthu amakhala nayo.
16. N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova sizidziloŵetsa m’magulu akudziko osintha zinthu?
16 Choncho, kodi Mboni za Yehova zasintha mikhalidwe m’dzikoli? Eya, zaka khumi zapitazo, chiŵerengero cha Mboni zokangalika chinawonjezereka kuchoka pa chiŵerengero chomwe chinangotsala pang’ono kukwana 3,800,000 ndi kukafika pafupifupi 6,000,000. Kumeneko ndi kuwonjezereka kwa pafupifupi ndi 2,200,000. Ambiri mwa ameneŵa analeka makhalidwe osalungama atakhala Akristu. Miyoyo yambiri inasintha bwino! Komabe, chiŵerengero chimenechi n’chochepa kwambiri pochiyerekezera ndi kuwonjezereka kwa chiŵerengero cha anthu padziko lonse kochitika panthaŵi imodzimodziyo—875,000,000! Mboni za Yehova zaona kuti kuthandiza anthu omvetsera ndiko magwero a chimwemwe, ngakhale kuti zikuzindikira kuti ndi anthu ochepa chabe omwe adzatenga njira yopita nayo ku moyo. (Mateyu 7:13, 14) Pamene Mboni zikuyembekezera kusintha kwabwino kwa padziko lonse lapansi komwe Mulungu yekha ndiye angakuchititse, sizidziloŵetsa m’magulu akudziko osintha zinthu, omwe kaŵirikaŵiri amayamba ndi cholinga chabwino koma pamapeto pake amalephera ngakhalenso kuyambitsa ziwawa.—2 Petro 3:13.
17. Kodi Yesu anachitanji pothandiza anthu amene anali kukhala nawo, koma kodi sanachite chiyani?
17 Potsatira njira imeneyi, Mboni za Yehova zimasonyeza kudalira Yehova monga momwe Yesu anachitira ali padziko lino lapansi. Kalero m’zaka za zana loyamba, Yesu anachita zozizwitsa za machiritso. (Luka 6:17-19) Anaukitsa ngakhale akufa. (Luka 7:11-15; 8:49-56) Koma sanachotse vuto la matenda kapena kugonjetsa mdaniyo imfa. Iye anadziŵa kuti sinali nthaŵi yomwe Mulungu analinganiza kudzachita zimenezo. Ndi maluso apamwamba a munthu wangwiro, Yesu mwachionekere akanatha kuchita zochuluka kuti athetse mavuto aakulu a zandale ndi a anthu. Zikuoneka kuti ena mwa anthu a m’nthaŵi yake ankafuna kuti iye aloŵe ufumu ndi kuchita zimenezo, koma Yesu anakana. Timaŵerenga kuti: “Anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m’dziko lapansi. Pamenepo Yesu, pozindikira kuti ali kufuna kudza kudzam’gwira Iye, kuti am’longe ufumu, anachokanso kumka kuphiri payekha.”—Yohane 6:14, 15.
18. (a) Kodi Yesu wasonyeza motani mtima wodikira nthaŵi zonse? (b)Kodi zochita za Yesu zasintha motani chiyambire 1914?
18 Yesu anakana kuloŵerera m’ndale kapena m’ntchito yakuthupi chifukwa chakuti anadziŵa kuti nthaŵi yakuti iye alandire mphamvu za ufumu ndi kuchita ntchito za machiritso kwa wina aliyense kwina kulikonse inali isanakwane. Ngakhale pambuyo pa kukwera kumwamba m’moyo wosafa wauzimu, anali wofunitsitsabe kuyembekezera nthaŵi yoikika ya Yehova asanayambe kuchita china chilichonse. (Salmo 110:1; Machitidwe 2:34, 35) Komabe, kuchokera pamene anakhazikitsidwa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu mu 1914, akutulukirabe “wolakika kuti alakike.” (Chivumbulutso 6:2; 12:10) Ndifetu oyamikira zedi kugonjera ku ufumu wake, pamene ena amene amadzinenera kuti ndi Akristu asankha kukhalabe osadziŵa chilichonse cha ziphunzitso za m’Baibulo zokhudza Ufumuwo!
Kodi Kudikira N’kokhumudwitsa Kapena N’kopatsa Chimwemwe?
19. Ndi liti pamene kudikira ‘kumadwalitsa mtima,’ nanga ndi liti pamene kumakhala magwero a chimwemwe?
19 Solomo anadziŵa kuti kudikira kungakhale kokhumudwitsa. Iye analemba kuti: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” (Miyambo 13:12) Ndithudi, ngati munthu akukhala n’chiyembekezo pa zinthu zosatsimikizirika, mtima wake ungadwale chifukwa cha kukhumudwa. Komabe, kuyembekezera zochitika zosangalatsa—mwinamwake ukwati, kubadwa kwa mwana, kapena kukumananso ndi anthu omwe timawakonda—kungatipatse chimwemwe cha chiyembekezo tsiku la chochitikacho lidakali kutali. Chimwemwe chimenecho chimakula ngati tigwiritsa ntchito nthaŵi ya kudikira kwathuko mwanzeru, mwa kumakonzekera chochitika chikubweracho.
20. (a) N’zochitika zapadera zotani zomwe tikuyembekezera ndi mtima wonse kudzaziona? (b)Tingapeze motani chimwemwe pamene tikuyembekezera kukwaniritsidwa kwa zifuno za Yehova?
20 Pamene tili ndi chidaliro chonse kuti ziyembekezo zathu zidzakwaniritsidwa—ngakhale kuti sitikudziŵa nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwakeko—nthaŵi ya kuyembekezera siyenera ‘kudwalitsa mtima.’ Alambiri okhulupirika a Mulungu akudziŵa kuti Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu wayandikira. Ali otsimikizira kuti adzaona mapeto a imfa ndi matenda. Poyembekezera mwachidwi, iwo mwachimwemwe akudikira nthaŵi pamene adzalandira miyandamiyanda ya anthu oukitsidwa, kuphatikizapo okondedwa awo omwe anamwalira. (Chivumbulutso 20:1-3, 6; 21:3, 4) M’nthaŵi zamavuto osatha zino, ali ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha kuona Paradaiso akukhazikitsidwa padziko lapansi. (Yesaya 35:1, 2, 7) N’kwanzerutu tsono kugwiritsa ntchito nthaŵi ya kuyembekezera imeneyi mosamala kwambiri, kukhala “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse”! (1 Akorinto 15:58) Pitirizanibe kudya chakudya chauzimu. Mangani ubwenzi weniweni ndi Yehova. Funafunani ena omwe mitima yawo imawasonkhezera kutumikira Yehova. Limbikitsani alambiri anzanu. Gwiritsani ntchito kotheratu nthaŵi iliyonse imene Yehova adzapereka. Choncho, kudikira Yehova ‘sikudzadwalitsa mtima wanu.’ M’malo mwake, kudzakupatsani chimwemwe chochuluka!
Kodi Mungalongosole?
• Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali ndi mtima wodikira?
• Kodi Akristu angafunikire kukhala ndi mtima wodikira m’mikhalidwe yotani?
• N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova n’zokhutiritsidwa maganizo kudikira Yehova?
• Kodi mungapange motani kuyembekezera Yehova kukhala magwero a chimwemwe?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 12]
Yesu anapirira chifukwa cha chimwemwe choikidwa pamaso pake
[Chithunzi patsamba 13]
Ngakhale pambuyo pa zaka zambiri za utumiki, tingakhalebe achimwemwe
[Zithunzi patsamba 15]
Anthu miyandamiyanda asintha miyoyo yawo mwa kukhala Mboni za Yehova