N’chifukwa Chiyani Mumatumikira Mulungu?
N’chifukwa Chiyani Mumatumikira Mulungu?
Tsiku lina, mfumu yoopa Mulungu inalangiza mwana wake motere: “Um’dziŵe Mulungu wa atate wako, um’tumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu.” (1 Mbiri 28:9) N’zoonekeratu kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake azimutumikira ndi mtima wachimwemwe ndi wothokoza.
MONGA Mboni za Yehova, timavomereza mosavuta kuti pamene tinamva za malonjezo a Baibulo koyamba, mitima yathu inali yodzala ndi kuyamika. Tsiku lililonse tinaphunzira kanthu kena katsopano ponena za zolinga za Mulungu. Pamene tinali kuphunzira zambiri za Yehova, chilakolako chathu chofuna ‘kum’tumikira ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu,’ chinakhala champhamvu.
Ambiri amene amakhala Mboni za Yehova amapitiriza kutumikira Yehova mosangalala kwambiri kwa moyo wawo wonse. Komabe, Akristu ena amayamba bwino, koma m’kupita kwa nthaŵi amaiwala zifukwa zamphamvu zomwe zimatisonkhezera kutumikira Mulungu. Kodi izi zakuchitikirani? Ngati ndi choncho, musataye mtima. Chisangalalo chomwe chinatha chingapezedwenso. Motani?
Kumbukirani Madalitso Anu
Choyamba, sinkhasinkhani za madalitso a Mulungu amene mumalandira tsiku ndi tsiku. Ganizirani za mphatso zabwino za Yehova: zinthu zamitundumitundu zomwe analenga—zimene aliyense angapeze kaya akhale munthu wotani kapena ngati ali wolemera kapena wosauka—mphatso zachilengedwe za chakudya ndi madzi, thanzi lomwe muli nalo, kudziŵa kwanu choonadi cha Baibulo, ndiponso chachikulu koposa, mphatso ya Mwana wake. Imfa yake inatsegula njira yoti mutumikire Mulungu ndi chikumbumtima choyera. (Yohane 3:16; Yakobo 1:17) Pamene mukusinkhasinkha kwambiri za ubwino wa Mulungu, mudzawonjezera kumuyamikira. Chifukwa cha kuyamikira zonse zimene wakuchitirani, mtima wanu udzakusonkhezerani kumutumikira. Mosakayikira, mudzayambanso kumva monga mmene anamvera wamasalmo yemwe analemba kuti: “Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazichita n’zambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu. . . . Zindichulukira kuziŵerenga.”—Salmo 40:5.
Mawu awa analembedwa ndi Davide, yemwe analinso kukumana ndi mavuto. Ali mnyamata, anathera nthaŵi yake yaitali akuthaŵathaŵa pamene Mfumu yoipa Sauli ndi asilikali ake anali kumufunafuna kuti amuphe. (1 Samueli 23:7, 8, 19-23) Komanso Davide, anali ndi zofooka zakenso zomwe anali kulimbana nazo. Iye anavomereza izi mu Salmo la 40: “Zoipa zosaŵerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga.” (Salmo 40:12) Inde, Davide anali ndi mavuto, koma sanagonjetsedwe ndi mavutowo. Anaganizira mmene Yehova anamudalitsira ngakhale anali m’mavutowo, ndipo anaona kuti madalitso amenewo anali ochuluka kwambiri kuposa mavuto akewo.
Mukaona kuti mavuto anu kapena maganizo anu odziyesa wopanda pake akupanikizani, ndi bwino kuyamba mwakumbukira madalitso anu monga mmene anachitira Davide. Mosakayikira, kuyamikira madalitso amenewo n’kumene kunakusonkhezerani kuti mudzipatulire kwa Yehova.
Maganizo omweomwewo, angakuthandizeni kupezanso chisangalalo chomwe chinali chitatha komanso kutumikira Mulungu ndi mtima woyamikira.Misonkhano ya Mpingo Ingathandize
Kuphatikiza pa kusinkhasinkha za ubwino wa Yehova patokha, timafunikanso kuyanjana ndi Akristu anzathu. N’kolimbikitsa kusonkhana nthaŵi zonse ndi amuna, akazi, ndi achinyamata omwe amakonda Mulungu ndiponso otsimikiza kum’tumikira. Chitsanzo chawo chingatisonkhezere kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Kufika kwathu pa Nyumba ya Ufumu kungawalimbikitsenso iwowo.
N’zoona kuti pamene tafika panyumba kuchokera kuntchito yotopetsa kapena pamene tagwa mphwayi ndi mavuto ena kapena chofooka china, kumakhala kovuta kuganizira zopita kukasonkhana ku Nyumba ya Ufumu. Panthaŵi zoterozo, tiyenera kudzikakamiza, kapena kuti ‘kupumpuntha thupi’ lathu kotero kuti timvere lamulo la kusonkhana ndi Akristu anzathu.—1 Akorinto 9:26, 27; Ahebri 10:23-25.
Kodi ngati tikufunikira kuchita zimenezi, ndiye kuti sitimukondadi Yehova? Ayi ndithu. Akristu okhwima a m’nthaŵi zakale omwe anali ndi chikondi chenicheni kwa Mulungu, anafunikira khama kuti achite chifuniro chake. (Luka 13:24) Mtumwi Paulo anali mmodzi wa Akristu oterowo. Pofotokoza poyera mmene anali kumvera mumtima, iye anati: “Ndidziŵa kuti m’kati mwanga, ndiko m’thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza. Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.” (Aroma 7:18, 19) Anauzanso Akorinto kuti: “Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho. . . . Pakuti ngati ndichita ichi chivomerere, mphoto ndili nayo; koma ngati si chivomerere, anandikhulupirira m’udindo.”—1 Akorinto 9:16, 17.
Monga mmene ambiri a ife tilili, Paulonso anali ndi zizoloŵezi zauchimo zomwe zinali kudodometsa chilakolako chake chofuna kuchita zabwino. Komabe, analimbana nazo mwamphamvu zizoloŵezizo ndipo nthaŵi zambiri anali kuzigonjetsa. N’zoona kuti Paulo sanakwanitse zimenezi mwa mphamvu zake zokha. Iye analemba kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) Yehova, yemwe anapatsa Paulo mphamvu, adzakupatsani inunso mphamvu kuti muchite chabwino ngati mutamupempha kuti akuthandizeni. (Afilipi 4:6, 7) Choncho, ‘menyani zolimba nkhondo ya chikhulupiriro,’ ndipo Yehova adzakudalitsani.—Yuda 3, NW.
Simuyenera kumenya nkhondo imeneyi panokha. M’mipingo ya Mboni za Yehova, akulu achikristu okhwima amene akupirira mu “nkhondo ya chikhulupiriro” imeneyi, ndi okonzeka kukuthandizani. Ngati mutapempha thandizo kwa mkulu, adzayesetsa kulankhula nanu ‘molimbikitsa.’ (1 Atesalonika 5:14) Cholinga chake ndicho kukhala “monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo.”—Yesaya 32:2.
“Mulungu ndiye chikondi” ndipo amafuna kuti atumiki ake am’tumikire chifukwa cha kum’konda. (1 Yohane 4:8) Ngati chikondi chanu kwa Mulungu chikufunikira kuchisonkhezera, tsatirani njira zoyenera monga tafotokozera m’nkhani ino. Mukatero mudzasangalala.