Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupeza Chitetezo M’dziko Loopsali

Kupeza Chitetezo M’dziko Loopsali

Kupeza Chitetezo M’dziko Loopsali

KUYENDA m’dera lomwe atcheramo mabomba kungaphetse munthu. Ndiyeno, kodi sikungakhale kothandiza mutakhala ndi mapu osonyeza malo oterowo? Komanso, bwanji ngati mutaphunzira kuzindikira mabomba osiyanasiyana. Mwachionekere, chidziŵitso choterocho chingakuchepetsereni ngozi yophulitsidwa ndi mabomba kapena kuphedwa.

Baibulo lingafanizidwe ndi mapu amenewo pamodzi ndi maphunziro ozindikira mabomba. M’Baibulo muli nzeru yosalephera pankhani yopeŵa ngozi ndiponso kuthetsa mavuto omwe amadza m’moyo.

Taonani lonjezo lotsimikizira lopezeka pa Miyambo 2:10, 11 lakuti: “Pakuti nzeru idzaloŵa mumtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakuchinjiriza.” Nzeru ndiponso kuzindikira zomwe zatchulidwa apa n’zochokera kwa Mulungu osati kwa munthu ayi. “Koma womvera [nzeru ya Mulungu] adzakhala osatekeseka, nadzakhala phee osaopa zoipa.” (Miyambo 1:33) Tiyeni tione mmene Baibulo lingalimbikitsire chitetezo chathu ndiponso mmene lingatithandizire kupeŵa mavuto ambiri.

Kupeŵa Ngozi Zakupha

Ziŵerengero zofalitsidwa posachedwapa ndi bungwe la zaumoyo padziko lonse la World Health Organization (WHO) zikuonetsa kuti anthu pafupifupi 1,171,000 amafa pangozi zapamsewu chaka n’chaka. Enanso pafupifupi 40 miliyoni amavulala, ndipo ena oposa mamiliyoni asanu ndi atatu amapuwala.

Ngakhale kuti n’kosatheka kukhala otetezeka kotheratu poyendetsa galimoto, kumvera malamulo apamsewu kumawonjezera kwambiri chitetezo cha aliyense payekha. Ponenapo za akuluakulu a boma amene amaika ndiponso kulimbikitsa malamuloŵa, Baibulo limati: “Anthu onse amvere maulamuliro aakulu.” (Aroma 13:1) Anthu oyenda m’magalimoto amene amatsatiradi uphungu umenewu amachepetsa ngozi pamodzi ndi zotsatira zake zoopsazo.

Chinanso chomwe chimakakamiza anthu kuyendetsa galimoto mosamala, ndicho kulemekeza moyo. Ponena za Yehova Mulungu, Baibulo limati: “Chitsime cha moyo chili ndi Inu.” (Salmo 36:9) Chotero moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Choncho, tilibe ufulu wochotsa mphatsoyi kwa munthu aliyense kapena kusonyeza kusalemekeza moyo, ngakhale wathu womwe.​—Genesis 9:5, 6.

Kaŵirikaŵiri, kulemekeza moyo kumaphatikizapo kuonetsetsa kuti galimoto ndi nyumba yathu n’zotetezedwa mmene kungathekere. Mu Israyeli wakale, chitetezo ankachiganizira kwambiri m’mbali iliyonse yokhudza moyo. Mwachitsanzo, akamanga nyumba, Chilamulo cha Mulungu chinkafuna kuti denga lake​—malo omwe banja linkakonda kuchitirapo zinthu​—likhale ndi kampanda. “Muzimanga kampanda pa tsindwi lake, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.” (Deuteronomo 22:8) Ngati wina wagwa chifukwa choti lamulo lotetezali silinatsatidwe, Mulungu ankaona kuti mwini nyumbayo ndiye wachititsa zimenezo. Mosakayikira, kutsatira mfundo yachikondi ya m’lamulo limeneli kungachepetse ngozi kuntchito ngakhale kokasangalala.

Kulimbana ndi Zizoloŵezi Zakupha

Malinga ndi zomwe linanena bungwe la WHO, tsopano anthu opitirira biliyoni imodzi padziko lonse amasuta fodya, ndipo anthu pafupifupi mamiliyoni anayi amafa pachaka chifukwa cha fodya. Chiŵerengerochi chikuyembekezeka kukwera kufika pa anthu pafupifupi mamiliyoni khumi m’zaka 20 ndi 30 zikubwerazi. Kuwonjezera apo, anthu miyandamiyanda amene amasuta fodya komanso kugwiritsa ntchito mankhwala “osangulutsa” osokoneza bongo, adzawononga thanzi lawo ndi umoyo wawo chifukwa cha zizoloŵezi zawozo.

Ngakhale kuti Mawu a Mulungu samatchula mwachindunji kugwiritsa ntchito fodya kapena mankhwala osokoneza bongo, mfundo zake zingatiteteze ku zochita zoterezi. Mwachitsanzo, 2 Akorinto 7:1 amalangiza kuti: “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.” N’zodziŵikiratu kuti fodya ndiponso mankhwala osokoneza bongo amaipitsa kapena kudetsa thupi ndi makemikolo ambiri ovulaza. Komatu Mulungu amafuna kuti matupi athu akhale ‘opatulika,’ kutanthauza osadetsedwa ndiponso oyera. (Aroma 12:1) Kodi simukuvomereza kuti kutsatira mfundo zimenezi kudzachepetsa ngozi yaikulu ku moyo wa munthu?

Kuthana ndi Zizoloŵezi Zoopsa

Anthu ambiri amadya ndiponso kumwa mopambanitsa. Zotsatira za kudya mopambanitsa zingaphatikizepo matenda a shuga, kansa, ndiponso matenda a mtima. Kumwetsa moŵa kumachititsa mavuto enanso, monga uchidakwa, matenda oumitsa chiŵindi otchedwa cirrhosis, kutha kwa maukwati, ndiponso ngozi zapamsewu. Komanso, kudya pang’ono kwambiri n’kovulazanso ndipo kungayambitse matenda oopsa otchedwa anorexia nervosa.

Ngakhale kuti Baibulo si buku lamankhwala, ilo limapereka malangizo osapita m’mbali pankhani ya kufunika kodya ndi kumwa moyenera. “Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru, ulunjikitse mtima wako m’njiramo. Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka.” (Miyambo 23:19-21) Komanso, Baibulo limanena kuti kudya ndi kumwa n’kosangalatsa. “Munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”​—Mlaliki 3:13.

Baibulo limalimbikitsanso kaonedwe kabwino ka maseŵera olimbitsa thupi, likumavomereza kuti “chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono.” Komano, limawonjezera kuti: “Chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8) Mwina mungafunse kuti, ‘kodi chipembedzo chingapindule motani tsopano?’ Chingapindule m’njira zambiri. Kuwonjezera pa kukulitsa mbali yofunika zedi yauzimu m’moyo wa munthu, chipembedzo chimalimbikitsa mikhalidwe yopindulitsa monga chikondi, chimwemwe, mtendere, ndiponso kudziletsa​—zomwe zimachititsa munthu kuoneka bwino ndiponso kukhala wathanzi.​—Agalatiya 5:22, 23.

Zotsatira Zoŵaŵa za Chiwerewere

Masiku ano, anthu miyandamiyanda anyalanyaza mwambo wa makhalidwe abwino ndipo mliri wa AIDS ndiwo china mwa zotsatira zake. Malinga ndi zomwe linanena bungwe la zaumoyo la WHO, anthu opitirira 16 miliyoni afa chiyambire mliri wa matenda a AIDS ndipo padakali pano anthu pafupifupi 34 miliyoni ali ndi kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa AIDS. Odwala AIDS ambiri anatenga matendaŵa kudzera m’njira yachiwerewere, majekeseni omwe zidakwa zamankhwala osokoneza bongo zimagwiritsa ntchito, kapena kuikidwa magazi okhala ndi kachilomboka.

Zotsatira zina za kunyalanyaza makhalidwe abwino ndizo matenda monga mabomu, chinzonono, matenda a kutupa chiŵindi otchedwa hepatitis B ndi C ndiponso chindoko. Ngakhale kuti maina a matendaŵa sankatchulidwa m’nthaŵi za m’Baibulo, ziwalo zomwe matenda ena opatsirana m’njira yachiwerewere ofala panthaŵiyo ankagwira zinkadziŵika. Mwachitsanzo, Miyambo 7:23 imafotokoza zotsatira zoopsa za chiwerewere monga ‘muvi wopyoza mphafa [“chiŵindi,” NW] yake.’ Chindoko komanso matenda a kutupa chiŵindi, nthaŵi zambiri amagwira chiŵindi. Ndithudi, uphungu wa m’Baibulo wakuti Akristu ‘asale mwazi ndi dama’ ulidi wapanthaŵi yake ndiponso wachikondi!​—Machitidwe 15:28, 29.

Msampha wa Chikondi Chapandalama

Pofuna kulemera msanga, anthu ambiri amagwiritsa ntchito ndalama zawozo mosayenera. N’zomvetsa chisoni kuti kuchita zoterozo nthaŵi zambiri kumawonongetsa chumacho. Komabe, kwa mtumiki wa Mulungu, Baibulo limati: “Agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosoŵa.” (Aefeso 4:28) N’zoona kuti si nthaŵi zonse kuti munthu wolimbikira ntchito amalemera. Komabe, iye amakhala pamtendere mumtima, amadzilemekeza, ndipo ngakhale ndalama zomwe angapereke zingagwiritsidwe ntchito yaphindu.

Baibulo limachenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi chapandalama; chimene ena pochikhumba, . . . anadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.” (1 Timoteo 6:9, 10) Sitingakane kuti ambiri ‘ofuna kukhala achuma’ amalemeradi. Koma kodi amakumana ndi mavuto otani? Kodi sizoona kuti umoyo wawo, mabanja awo, uzimu wawo, ngakhalenso tulo tawo zimasokonekera?​—Mlaliki 5:12.

Munthu wanzeru amazindikira kuti “moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Ndalama ndiponso katundu wina n’zofunika m’madera ambiri. Kwenikweni, Baibulo limanena kuti “ndalama zitchinjiriza,” komabe limawonjezera kuti “kudziŵa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.” (Mlaliki 7:12) Mosiyana ndi ndalama, chidziŵitso cholondola ndiponso nzeru zingatithandize m’zochita zonse makamaka m’nkhani zokhudza moyo wathu.​—Miyambo 4:5-9.

Nthaŵi Pamene Nzeru Yokha Ndiyo Idzatiteteze

N’zoona kuti nzeru posachedwapa ‘idzasunga moyo wa eni ake’ m’njira yosayerekezeka​—kuwateteza pa “chisautso chachikulu” chomwe chikuyandikira mofulumira, pomwe Mulungu adzawononge oipa. (Mateyu 24:21) Malinga ndi zomwe Baibulo limanena, anthu panthaŵiyo adzataya ndalama zawo m’misewu monga chinthu chodetsedwa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti adzazindikira zinthu zitavuta kale kuti golidi ndiponso siliva sadzawagulira moyo pa “tsiku la mkwiyo wa Yehova.” (Ezekieli 7:19) Mosiyana ndi zimenezo, “khamu lalikulu” lomwe mwanzeru ‘linakundika chuma chawo m’mwamba’ mwa kuika zinthu zauzimu patsogolo m’moyo wawo, lidzapindula ndi chuma chodalirika ndi kudzapeza moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso.​—Chivumbulutso 7:9, 14; 21:3, 4; Mateyu 6:19, 20.

Kodi tingapeze bwanji tsogolo lodalirika limeneli? Yesu anayankha kuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Anthu miyandamiyanda apeza chidziŵitso chimenechi m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Anthuŵa sikuti ali ndi chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo chokha ayi, komanso amakhala amtendere ndiponso otetezedwa lerolino. Zili monga wamasalmo ananenera kuti: “Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.”​—Salmo 4:8.

Kodi mungaganize za gwero lina lililonse la chidziŵitso lomwe lingakuthandizeni mokwanira kuchepetsa ngozi ya thanzi lanu ndiponso moyo wanu monga momwe Baibulo limachitira? Palibetu buku lina lamphamvu ngati Baibulo, ndipo palibe buku lina lomwe lingakuthandizeni kupeza chitetezo m’dziko loopsali. Bwanji osaliŵerenga kwambiri mosamalitsa?

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 6]

Kupeza Moyo ndi Chitetezo Zabwinopo​—Mothandizidwa ndi Baibulo

Pofuna kuthaŵa mavuto a m’moyo, mtsikana wina wotchedwa Jane * nthaŵi zonse ankasuta chamba, fodya wamba, komanso ankamwa mankhwala osokoneza bongo a cocaine, amphetamines, LSD, ndi ena ambiri. Iye analinso chidakwa. Malinga ndi zomwe Jane ananena, mwamuna wake ankachitanso zomwezo. Tsogolo lawo linali lomvetsa chisoni. Kenako Jane anakumana ndi Mboni za Yehova. Iye anayamba kupita kumisonkhano yachikristu ndiponso kuŵerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, omwe ankapatsanso mwamuna wake. Onse anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Atayamba kuzindikira miyezo yapamwamba ya Yehova, iwo anasiya kumwa moŵa mwauchidakwa ndiponso mankhwala onse osokoneza bongo. Zotsatira zake? “Moyo wathu watsopano watibweretsera chimwemwe chachikulu,” analemba motero Jane patapita zaka zambiri ndithu. “Ndikuthokoza Yehova kwambiri chifukwa cha mphamvu yoyeretsa ya Mawu ake, mpumulo omwe tili nawo, ndiponso moyo wabwino umene tikukhala tsopano.”

Phindu lokhala wantchito wokhulupirika lasonyezedwa bwino lomwe ndi zomwe zinachitikira Kurt, yemwe ntchito yake inali yosamala makompyuta. Kompyuta ina yatsopano inkafunika, ndipo bwana wake anam’tuma Kurt kuti akagule ina pamtengo wabwino. Kurt anapeza koti akagule kompyutayo ndipo anagwirizana mtengo wake. Komano, wolemba matikiti analakwitsa moti mtengo womwe analemba unali wotsika ndi ndalama zokwana madola 40,000 a ku U.S. Atadziŵa kuti wolemba matikitiyo walakwitsa, Kurt anayimba foni ku kampaniyo ndipo mkulu wa pakampaniyo ananena kuti kwa zaka 25 zomwe wakhala akugwira ntchito sanaonepo kukhulupirika koteroko. Kurt anafotokoza kuti chikumbumtima chake chinaphunzira Baibulo. Zotsatira zake zinali zakuti mkuluyo anaitanitsa makope a maganizi a Galamukani! omwe amafotokoza za kukhulupirika pantchito okwana 300 kuti akagaŵire antchito anzake. Koma Kurt, chifukwa chokhulupirika kwakeko anam’kweza pantchito.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 30 Mayina asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 7]

“Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula.”​—YESAYA 48:17