Mungachite Moyenera Ngakhale Sanakulereni Bwino
Mungachite Moyenera Ngakhale Sanakulereni Bwino
NICHOLAS anali wosamvera kuyambira ali mwana. * M’kupita kwa nthaŵi, chifukwa cha nkhaŵa mumtima mwake, anayamba kuledzera ndi kumwa mankhwala osokoneza bongo. Nicholas anati: “Bambo anga anali chidakwa, choncho ine ndi mlongo wanga tinavutika kwambiri chifukwa cha uchidakwawo.”
Makolo a Malinda ankadziŵika ndi kulemekezedwa ndi aliyense m’mudzi mwawo monga anthu opemphera. Koma iwo analinso patsogolo m’kagulu ka mpatuko. “Zina mwa zochita zawo m’kaguluko, zinali zoipa kwa ine ndipo pokhala mwana, zinanditayitsa mtima. Kukhala wosoŵa mtengo wogwira ndi kudzimva monga wopanda pake komwe kunakhazikika mwa ine ndiwo moyo wanga kuyambira kalekale.” Anadandaula motero Malinda yemwe tsopano ali ndi zaka zopitirira 30.
Ndani angatsutse kuti ubwana wa anthu ambiri unawonongedwa ndi chiwawa, nkhanza, kunyalanyazidwa ndi makolo, ndi zoipa zina ? Mabala a mumtima a pa ubwana wosakondweretsa, angakhale aakulu. Koma kodi mavuto amenewo ayenera kuwonongeratu mwayi wa munthu wolandira choonadi cha Mawu a Mulungu ndi kukhala wachimwemwe? Ngakhale kuti anawalera motero, kodi Nicholas ndi Malinda angathe kukhala anthu okhulupirika? Taonani kaye chitsanzo cha Yosiya Mfumu ya Yuda.
Chitsanzo cha M’Malemba
Yosiya anakhala mfumu ya Yuda kwa zaka 31 m’zaka za m’ma 600 B.C.E. (659-629 B.C.E.) Panthaŵi imene Yosiya analongedwa ufumu chifukwa cha kuphedwa kwa bambo ake, zinthu zinali zitafika poipa kwambiri mu Yuda. Yuda ndi Yerusalemu anali atadzaza ndi olambira Baala ndi olumbira m’dzina la Malikamu, mulungu wamkulu wa Aamoni. Akalonga a Yuda anali “mikango yobangula,” ndi oweruza ake “mimbulu ya madzulo,” anatero Zefaniya, mneneri wa Mulungu panthaŵiyo. Choncho, chiwawa ndi chinyengo zinali ponseponse m’dzikomo. Anthu ambiri m’mitima mwawo ankati: “Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.”—Zefaniya 1:3–2:3; 3:1-5.
Kodi Yosiya anali mfumu yotani? Wodziŵa mbiri ya Baibulo Ezara, analemba kuti: “[Yosiya] nachita zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m’njira ya Davide kholo lake, osapambuka pa dzanja lamanja kapena kulamanzere.” (2 Mbiri 34:1, 2) N’zoonekeratu kuti Yosiya anatha kuchita zoyenera pamaso pa Mulungu. Koma kodi mbiri ya banja lawo inali yotani?
Kodi Analeredwa Bwino Kapena Ayi?
Pamene Yosiya amabadwa mu 667 B.C.E., n’kuti bambo ake a Amoni ali ndi zaka 16 zokha, ndipo agogo ake aamuna a Manase ndiwo anali mfumu ya Yuda. Manase anali mmodzi mwa mafumu oipa kwambiri omwe analamulirapo Yuda. Pomanga maguwa ansembe a Baala, ‘anachita choipa pamaso pa Yehova.’ Anapsereza ana ake pamoto, anachita za matsenga, kuombeza maula, kupititsa patsogolo zamizimu, ndi kupha anthu ambiri osalakwa. Kuwonjezera apo, Manase anaika m’nyumba ya Yehova fano la mlongoti wopatulika lomwe iye anasema. Iye ananyenga Yuda ndi Yerusalemu ‘kuchita choipa koposa amitundu, amene Yehova anawawononga pamaso pa ana a Israyeli.’—2 Mbiri 33:1-9.
Manase anali woipa kwambiri mwakuti Yehova anam’lola kumangidwa m’matangadza ndi kum’tengera ku Babulo, umodzi mwa mizinda ikuluikulu ya ufumu wa Asuri. Ali ku ukapolo, Manase analapa, nadzichepetsa, ndi kupempha Yehova kuti amukhululukire. Mulungu anamva 2 Mbiri 33:10-17.
pempho lake loti am’komere mtima ndipo anam’bwezeretsa mu ufumu ku Yerusalemu. Kenako Manase anayamba kukonza zinthu ndipo zotsatira zake zinali zabwino.—Kodi kuipa kwa Manase ndi kulapa kwake, kunam’khudza motani mwana wake Amoni? Iye anali woipa kwambiri. Pamene Manase analapa ndi kuyesetsa kuyeretsa mtunduwo mwa kuchotsa zodetsa zomwe anayambitsa yekha, Amoni sanam’thandize. Atakhala mfumu ali ndi zaka 22, Amoni “anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira Manase atate wake.” M’malo modzichepetsa kwa Yehova, “Amoni . . . anachulukitsa kupalamula kwake.” (2 Mbiri 33:21-23) Pamene Amoni anakhala mfumu ya Yuda, n’kuti Yosiya ali ndi zaka zisanu ndi chimodzi zokha. Ubwana wake unali woipa bwanji!
Ulamuliro woipa wa Amoni unatha zaka ziŵiri pamene atumiki ake anam’konzera chiwembu ndi kumupha. Komabe anthu anapha achiwembuwo ndi kulonga ufumu Yosiya mwana wake.—2 Mbiri 33:24, 25.
Ngakhale kuti panachitika zoipa panthaŵi ya ubwana wake, Yosiya anachita zoyenera pamaso pa Yehova. Ulamuliro wake unali wopambana ndipo Baibulo limati: “Asanabadwe iye panalibe mfumu [y]olingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu yake yonse, monga mwa chilamulo chonse cha Mose; atafa iyeyu sanaukanso wina wolingana naye.”—2 Mafumu 23:19-25.
Zimene Yosiya anachita n’chitsanzo cholimbikitsa kwa amene anakumana ndi zoipa paubwana wawo. Kodi chitsanzo chimenechi chingatiphunzitse chiyani? N’chiyani chinathandiza Yosiya kusankha njira yoyenera ndi kupitirizabe kuitsatira?
Yesetsani Kudziŵa Yehova
Chitsanzo chabwino chomwe chinalipo Yosiya ali mwana ndicho cha Manase, agogo 2 Mbiri 34:1-3.
ake aamuna olapa aja. Baibulo silinafotokoze kuti kaya aŵiriwa anali oyandikana motani, ndiponso kuti Yosiya anali ndi zaka zingati pamene Manase analapa. Popeza kuti mabanja achiyuda sankakhala motalikirana, mwina Manase anayesetsa kuteteza mdzukulu wakeyo ku mikhalidwe yoipayo mwa kum’phunzitsa kulemekeza Yehova Mulungu woona ndi mawu ake. Mbewu iliyonse ya choonadi imene Manase anafesa mu mtima mwa Yosiya, mwinanso kuphatikizapo mikhalidwe ina yabwino, mapeto ake inabala zipatso. Atakhala mfumu ya Yuda kwa zaka zisanu ndi zitatu, Yosiya, yemwe panthaŵiyo anali ndi zaka 15 anafuna kum’dziŵa Yehova ndi kuchita chifuno chake.—Pamene ena anali ana, anthu okha omwe anali kugwirizana nawo pa zauzimu angakhale wachibale, wongodziŵana naye, kapena woyandikana naye nyumba. Komabe ngati mgwirizanowo angausamalire bwino, mbewu zimene zafesedwa zingadzabale zipatso zabwino m’tsogolo. Malinda yemwe tam’tchula poyamba uja, anayandikana nyumba ndi munthu wina wachikulire yemwe nthaŵi zonse ankam’bweretsera magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kunyumba kwake. Pom’kumbukira mwachikondi, anati: “Chomwe chinandichititsa chidwi kwambiri ndi munthuyo n’chakuti sankakondwerera maholide. Zimenezi zinali zofunika kwambiri kwa ine chifukwa chakuti pa holide ya Halloween imene amakhulupirira kuti mfiti ndi ziwanda zimaoneka pa tsikulo usiku ndi pa maholide ena, pankachitika miyambo yosiyanasiyana m’kagulu ka mpatuko ka makolo anga.” Pambuyo pa zaka khumi, mnzake atamuitanira ku msonkhano wachikristu ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, Malinda anakumbukira mnansi amene uja ndipo mosazengereza anavomera. Zimenezi zinamuthandiza kufunafuna choonadi.
Dzichepetseni kwa Mulungu
Ulamuliro wa Yosiya unali wotchuka ndi kusintha kwambiri zinthu zachipembedzo mu Yuda. Atagwira ntchito yothetsa kulambira mafano ndi kuyeretsa dziko la Yuda kwa zaka zisanu ndi chimodzi, Yosiya anayamba kukonza nyumba ya Yehova. Ntchito imeneyo ili m’kati, Mkulu wa Ansembe Hilikiya anapeza chinthu cha mtengo wapatali. Anapeza buku lenileni “la chilamulo cha Yehova.” Hilikiya anapereka buku lochititsa chidwi limeneli kwa mlembi Safani yemwe anakauza mfumu zomwe zinachitikazo. Kodi Yosiya yemwe panthaŵiyo anali ndi zaka 25 anadzitama chifukwa cha zimene anachita?—2 Mbiri 34:3-18.
“Atamva mfumu mawu a chilamulo, anang’amba zovala zake,” analemba motero Ezara. Kumeneku kunali kusonyeza chisoni kochokera mu mtima chifukwa anadziŵa kuti makolo awo sanatsate malamulo onse a Mulungu. Anasonyezadi kudzichepetsa! Nthaŵi yomweyo mfumu inatumiza nthumwi zisanu kwa mneneri wamkazi Hulida kukafunsira kwa Yehova. Chifukwa cha zimenezi, nthumwizo zinabweretsa uthenga wakuti: ‘Popeza mtunduwo sunamvere chilamulo cha Yehova, udzakumana ndi tsoka. Koma chifukwa iwe, mfumu Yosiya unadzichepetsa, udzaikidwa m’manda ako mwa mtendere ndipo sudzaona tsoka.’ (2 Mbiri 34:19-28) Yehova anasangalala ndi mtima wa Yosiya.
Kaya tinaleredwa motani, ifenso tikhoza kudzichepetsa kwa Mulungu woona Yehova, ndi kusonyeza ulemu kwa iye ndi Mawu ake Baibulo. Nicholas amene tam’tchula poyamba uja anachita zimenezi. Iye anati: “Ngakhale kuti moyo wanga unali wodzala ndi mavuto chifukwa cha mankhwala osokoneza bongo ndi kumwa moŵa mwauchidakwa, ndinkachita chidwi ndi Baibulo ndipo ndinkafuna moyo wokhala ndi cholinga. Mapeto ake ndinakumana ndi Mboni za Yehova, ndinasintha moyo wanga, ndi kulandira choonadi.” Inde, tingakhale aulemu kwa Mulungu ndi Mawu ake mosaganizira za mikhalidwe yomwe tinakula nayo.
Pindulani ndi Zomwe Yehova Wakonza
Yosiya analinso kulemekeza kwambiri aneneri a Yehova. Iye anafunsira kwa mneneri wamkazi Hulida komanso anali kumvera aneneri ena a m’nthaŵiyo. Mwachitsanzo, Yeremiya ndi Zefaniya anali kalikiliki kudzudzula kulambira mafano kochitidwa mu Yuda. Kumvetsera uthenga wawo kuyenera kuti kunam’patsa mphamvu Yeremiya 1:1, 2; 3:6-10; Zefaniya 1:1-6.
Yosiya pothetsa kulambira konyenga.—“Mbuye” Yesu Kristu, wasankha gulu la om’tsatira odzozedwa, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azipereka chakudya chauzimu panthaŵi yoyenera. (Mateyu 24:45-47) Pogwiritsa ntchito mabuku ofotokoza Baibulo, ndi misonkhano ya mpingo, gulu la kapolo limatisonyeza phindu lotsatira uphungu wa m’Baibulo ndi kutipatsa maganizo a mmene tingaugwiritsire ntchito pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. N’kofunikatu kuti tigwiritse ntchito zomwe Yehova wakonza potithandiza kuthetsa makhalidwe alionse oipa omwe takhala nawo kwanthaŵi yaitali! Kuyambira ali mwana, Nicholas ankadana kwambiri ndi ulamuliro. Ngakhale pamene anali kuphunzira choonadi cha Mawu a Mulungu, vuto limeneli linam’lepheretsa kutumikira Yehova mokwanira. Kusintha khalidwe limeneli kunali kovuta kwa iye. Koma m’kupita kwa nthaŵi analithetsa. Motani? Iye akuti: “Pothandizidwa ndi akulu aŵiri omvetsa zinthu, ndinavomereza vuto langa ndi kuyamba kugwiritsa ntchito malangizo awo achikondi a m’Malemba. Ngakhale kuti nthaŵi zina ndimakwiya nazo pang’ono, tsopano ndathetsa khalidwe langa lopanduka.”
Malinda nayenso, amafunsira maganizo kwa akulu pankhani zofunika kwambiri pa moyo wake. Polimbana ndi kupanda chiyembekezo ndi maganizo odziona ngati wopanda phindu omwe anayamba akali mwana, nkhani zosiyanasiyana za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, n’zamtengo wapatali kwambiri kwa iye. Iye anati: “Nthaŵi zina pamakhala ndime ngakhale chiganizo chaching’ono kwambiri chomwe chimandifika pamtima. Zaka pafupifupi zisanu ndi zinayi zapitazo, ndinayamba kumasunga nkhani zoterezi m’kabuku kuti ndizitha kuzionanso mosavuta.” Tsopano ali ndi mabuku atatu okhala ndi nkhani 400!
Iyayi, anthu sayenera kuvutika kwa moyo wonse chifukwa cha moyo woipa m’banja lawo. Mothandizidwa ndi Yehova, angachite moyenera mwauzimu. Monga mmene zilili kuti kuleredwa bwino sikutanthauza kuti munthu adzakhala wokhulupirika, kuleredwa moipa sikulepheretsa munthu kukhala woopa Mulungu.
Atapeza buku la Chilamulo pokonzanso kachisi, Yosiya ‘anachita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda chotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wake wonse.’ (2 Mbiri 34:31) Ndipo sanafooke potsata pangano lake mpaka imfa. Malinda ndi Nicholas nawonso n’ngotsimikiza kukhalabe okhulupirika kwa Yehova Mulungu nthaŵi zonse. Nanunso tsimikizani mtima kum’yandikira Mulungu ndi kum’tumikira mokhulupirika. Khulupirirani kuti mudzakwanitsa, pakuti Yehova akulonjeza kuti: “Usawope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usawopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; ine, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.”—Yesaya 41:10, 13.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Mayina ena asinthidwa.
[Zithunzi patsamba 26]
Ngakhale sanaleredwe bwino, Yosiya anafuna kudziŵa Yehova ndi kuchita zoyenera m’moyo wake
[Chithunzi patsamba 28]
Akulu angakuthandizeni kusintha khalidwe lomwe mwakhala nalo kwa nthaŵi yaitali
[Chithunzi patsamba 28]
“Nsanja ya Olonda” ndi “Galamukani!” zingakuthandizeni kukhalabe wokhulupirika