Kodi Mukugwiritsa Ntchito Nthaŵi Moyenera?
Kodi Mukugwiritsa Ntchito Nthaŵi Moyenera?
MTUMWI Paulo analangiza Akristu a ku Efeso m’zaka za zana loyamba kuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.” (Aefeso 5:15, 16) N’chifukwa chiyani langizoli linali loyenera? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyenera kudziŵa zomwe Akristu mu mzinda wakalekale umenewu anali kukumana nazo.
Mzinda wa Efeso unali wodziŵika ndi kulemera kwake, chiwerewere chosaneneka, umbanda ponseponse, ndi zausatana zosiyanasiyana. Kuwonjezera apo, Akristu anali kulimbana ndi zikhulupiriro zafilosofi zonena za nthaŵi. Agiriki a ku Efeso omwe sanali Akristu sankakhulupirira kuti nthaŵi imapita m’tsogolo osabwereranso. Filosofi yachigiriki inawaphunzitsa kuti moyo umabwerezedwabwerezedwa popanda malire. Munthu yemwe wawononga nthaŵi yake mosayenera m’moyo, angadzaipezenso m’moyo wina. Maganizo amaneŵa, akanasonkhezera Akristu a ku Efeso kukhala ndi mtima wonyalanyaza nthaŵi yochitira zinthu zomwe Yehova wakonza kuphatikizapo kuweruza. Choncho langizo la Paulo lakuti agwiritse ntchito nthaŵi moyenera linali lofunika.
Paulo sanali kunena nthaŵi wamba. Liwu lachigiriki lomwe anagwiritsa ntchito limatanthauza nthaŵi yosankhika, nthaŵi yoyenerera ntchito inayake. Paulo analangiza Akristu a m’zaka za zana loyambawo kugwiritsa ntchito mwanzeru nthaŵi yamtengo wapatali, kapena kuti nyengo yapadera, imene anali kusangalala nayoyo isanathe, komanso Mulungu asanaleke kusonyeza chifundo chake ndi kupereka chipulumutso.—Aroma 13:11-13; 1 Atesalonika 5:6-11.
Tikukhala m’nthaŵi yamtengo wapatali ngati imeneyo. M’malo mwa kusakaza nthaŵi yapaderayi yomwe sidzapezekanso pofunafuna zosangalatsa zosakhalitsa zomwe dzikoli limapereka, Akristu amachita mwanzeru ngati agwiritsa ntchito nthaŵiyi ‘kudzipereka kwa Mulungu.’ Mwakutero, amalimbitsa ubwenzi ndi Mlengi wawo, Yehova Mulungu.—2 Petro 3:11; Salmo 73:28; Afilipi 1:10.