Limbikitsani Chikhulupiriro Chanu mwa Yehova
Limbikitsani Chikhulupiriro Chanu mwa Yehova
Kukonza chiwembu chofuna kupha munthu kuli m’kati. Akuluakulu a boma onse a m’dzikolo akumana pamodzi ndipo agwirizana kuti akhazikitse lamulo latsopano. Akufuna kuti ukhale mlandu womwe chilango chake ndi kuphedwa ngati wina aliyense alambira amene Boma silinam’vomereze.
KODI nkhaniyi mwaidziŵa? Zochitika m’mbiri zili ndi zitsanzo zochuluka za anthu amene anachitira nkhanza anzawo pogwiritsa ntchito lamulo. Zomwe zili pamwambapazi zinachitika mu Ufumu wa Aperisi m’nthaŵi ya mneneri Danieli. Lamulo limene Mfumu Dariyo anakhazikitsa linali lakuti: “Aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m’dzenje la mikango.”—Danieli 6:7-9.
Kodi Danieli akanatani atamuopseza kuti adzamupha? Kodi akanapitiriza kukhulupirira Mulungu wake, Yehova, kapena akanabwerera m’mbuyo ndi kuchita zomwe mfumu inalamula? Nkhaniyo imatiuza kuti: “Podziŵa Danieli kuti adatsimikiza cholembedwacho, analoŵa m’nyumba mwake, m’chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.” (Danieli 6:10) Mbali yotsala ya nkhaniyi mukuidziŵa bwino. Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango chifukwa cha chikhulupiriro chake, koma Yehova “anatseka pakamwa mikango” ndipo anapulumutsa mtumiki wake wokhulupirikayo.—Ahebri 11:33; Danieli 6:16-22.
Nthaŵi Yodzipenda
Atumiki a Yehova lerolino akukhala m’dziko lankhanza ndipo amakumana ndi ziopsezo zambiri za moyo wawo weniweniwo ndiponso wauzimu. Mwachitsanzo, chifukwa cha chidani choopsa pakati pa mitundu m’mayiko ena, Mboni zambiri zaphedwa. Kwinakwake, atumiki a Yehova avutika kwambiri chifukwa chosoŵa chakudya, mavuto azachuma, masoka achilengedwe, matenda aakulu, ndiponso mikhalidwe ina yoika moyo pachiswe. Kuwonjezera apo, anapiriranso chizunzo, mavuto akuntchito, ndiponso ziyeso zosiyanasiyana za kuchita choipa. Zonsezi ziyenera kuti zinaopseza moyo wawo wauzimu. Ndithudi, Mdani wamkulu, Satana, ali wotsimikiza kwambiri kuwononga atumiki a Yehova pogwiritsa ntchito njira iliyonse imene ingapambane.—1 Petro 5:8.
Kodi ifeyo tingatani ngati zimenezi zitatichitikira? Ngakhale kuti n’kwachibadwa kuchita mantha ngati moyo wathu uli pangozi, tingakumbukire mawu olimbikitsa a mtumwi Paulo akuti: “Iye [Yehova] anati, sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu. Kotero kuti tinena molimbika mtima, mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?” (Ahebri 13:5, 6) Tikutsimikiza kuti Yehova amamvanso chimodzimodzi ndi atumiki ake lerolino. Komabe, kudziŵa lonjezo la Yehova n’kosiyana kwambiri ndi kukhala wotsimikiza kuti adzatichitira zomwe analonjezazo. Choncho, n’kofunika kwambiri kupenda maziko a chikhulupiriro chathu mwa Yehova ndiponso kuchita chilichonse chomwe tingathe kulimbikitsa ndi kusungabe chikhulupirirocho. Tikatero, “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima [yathu] ndi maganizo [athu] mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:7) Ndipo ziyeso zikabwera, tidzatha kuganiza bwino ndi kuthana nazo mwanzeru.
Maziko a Kukhulupirira Yehova
Ndithudi tili ndi zifukwa zambiri zokhulupirira Mlengi wathu, Yehova. Choyamba n’chakuti, Yehova ndi Mulungu wachikondi amene amasamaladi atumiki ake. M’Baibulo muli zitsanzo zosaŵerengeka zosonyeza kuti Yehova amasamalira atumiki ake mwachikondi. Pofotokoza mmene Yehova ankachitira ndi anthu ake osankhidwa, Aisrayeli, Mose analemba kuti: “Anam’peza m’dziko la mabwinja, ndi m’chipululu cholira chopanda kanthu; anam’zinga, anam’langiza, anam’sunga ngati kamwana ka m’diso.” (Deuteronomo 32:10) M’nthaŵi zamakono zino, Yehova akupitiriza kusamalira bwino atumiki ake monga gulu komanso munthu payekha. Mwachitsanzo, pamene Mboni zinali pavuto ladzaoneni losoŵa chakudya panthaŵi ya nkhondo ku Bosnia, Yehova anaonetsetsa kuti iwo akulandira zinthu zofunika kwambiri kudzera mwa abale awo a ku Croatia ndi Austria, amene analolera kuika miyoyo yawo pangozi mwa kuyenda m’dera loopsa kwambiri kuti akapereke katundu wothandizira abale awo ovutikawo. *
Popeza kuti Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse, iye amatetezadi atumiki ake pamavuto alionse. (Yesaya 33:22; Chivumbulutso 4:8) Ndipo ngakhale Yehova atalola atumiki ake ena kukhalabe okhulupirika mpaka imfa, iye amawathandizabe kukhala okhulupirika, olimba, achimwemwe, ndiponso abata mpaka mapeto. Choncho titha kukhala ndi chidaliro chofanana ndi wamasalmo yemwe anati: “Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso. Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m’kati mwa nyanja.”—Salmo 46:1, 2.
Baibulo limavumbulanso kuti Yehova ndi Mulungu wa choonadi. Izi zikutanthauza kuti nthaŵi zonse amakwaniritsa malonjezo ake. Ndipo Baibulo limam’tchula kuti ‘Mulungu wosanama.’ (Tito 1:2) Popeza kuti Yehova wanena mobwerezabwereza za kufunitsitsa kwake kuteteza ndiponso kupulumutsa atumiki ake, titha kutsimikiza ndi mtima wonse kuti ndi wokhoza komanso wokonzeka kukwaniritsa malonjezo ake.—Yobu 42:2.
Njira Zolimbikitsira Chikhulupiriro Chathu
Ngakhale kuti tili ndi zifukwa zokwanira zokhulupirira
Yehova, tisaone nkhaniyi mopepuka. Izi zili choncho chifukwa chakuti anthu padziko lapansi amakhulupirira Mulungu pang’ono chabe, ndipo zimenezi zingafooketse chikhulupiriro chathu mwa Yehova. Choncho, mpofunika khama kuti tilimbikitse ndi kusungabe chikhulupiriro chathu. Yehova akudziŵa bwino zimenezi ndipo wapereka njira zotithandiza kuchita zimenezi.Yoyamba, wapereka mawu ake olembedwa, Baibulo, lomwe limasimba ntchito zazikulu zomwe wachitira atumiki ake. Tangoganizani, kodi mungamukhulupirire motani munthu amene m’mangomudziŵa dzina lokha basi? Mwinamwake mungamukhulupirire pang’ono chabe ngati mungatero n’komwe. Kuti mum’khulupirire kwambiri mufunikira kumudziŵa njira zake ndiponso ntchito zake, si choncho kodi? Tikamaŵerenga ndi kusinkhasinkha pa nkhani za m’Baibulo ngati zimenezi, kumudziŵa kwathu Yehova ndi njira zake kumawonjezeka, ndiponso timayamikira komanso kuzindikira kwambiri za kudalirika kwake. Mwakutero timalimbikitsa chikhulupiriro chathu mwa iye. Wamasalmo anatisiyira chitsanzo chabwino kwambiri pamene anapemphera kwa Mulungu mochokera pansi pa mtima kuti: “Ndidzakumbukira zimene adazichita Ambuye; inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zoyambira kale. Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.”—Salmo 77:11, 12.
Kuwonjezera pa Baibulo, tili ndi mabuku omwe gulu la Yehova limafalitsa omwenso ali magwero a chakudya chauzimu chamwana alirenji. Mwa zina zomwe zimapezeka m’mabuku ameneŵa ndi nkhani zolimbikitsa zosimba za moyo wa atumiki amakono a Mulungu kusonyeza mmene Yehova wawathandizira ndiponso kuwapulumutsa pamene anakumana ndi mavuto othetsa nzeru. Mwachitsanzo, Martin Poetzinger yemwe m’kupita kwanthaŵi anadzakhala membala wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anadwala kwambiri pamene ankachita utumiki waupainiya m’dera lina ku Ulaya kutali ndi kwawo. Analibe ndalama ndipo panalibe dokotala aliyense amene ankafuna kudzamuona. Koma Yehova sanamutaye. Potsirizira pake, mkulu wa pachipatala cha m’deralo anauzidwa nkhaniyi. Popeza kuti mkuluyo anali kukhulupirira Baibulo kwambiri, anamusamalira Mbale Poetzinger ngati akusamala mwana wake, koma mwaulere. Kuŵerenga nkhani ngati zimenezi kungalimbikitse chikhulupiriro chathu mwa Atate wathu wakumwamba.
Thandizo linanso lapamwamba kwambiri limene Yehova watipatsa kuti tilimbikitse chikhulupiriro chathu mwa iye ndilo mwayi wamtengo wapatali wa pemphero. Mtumwi Paulo amatiuza mwachikondi kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” (Afilipi 4:6) Mawu akuti “m’zonse” angaphatikizepo maganizo athu, zomwe tikufuna, zomwe zikutichititsa mantha, ndiponso zomwe zikutidetsa nkhaŵa. Tikamapemphera kaŵirikaŵiri ndiponso mochokera pansi pa mtima m’pamene chikhulupiriro chathu mwa Yehova chidzakhale cholimba.
Pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi, nthaŵi zina ankapita kumalo ayekha kopanda phokoso kukapemphera. (Mateyu 14:23; Marko 1:35) Asanasankhe zochita pankhani yaikulu iye anachezera usiku wonse kupemphera kwa Atate wake. (Luka 6:12, 13) Mpake kuti chikhulupiriro cha Yesu mwa Yehova chinali cholimba kwabasi mwakuti anatha kupirira ziyeso zoopsa kwambiri kuposa za munthu wina aliyense. Mawu ake omaliza pa mtengo wozunzirapo anali akuti: “Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga.” Mawu achikhulupiriro amenewo anasonyeza kuti mpaka mapeto chikhulupiriro chake mwa Atate wake sichinazirale, ngakhale kuti Yehova sanaloŵerere kuti am’pulumutse.—Luka 23:46.
Deuteronomo 31:12; Ahebri 10:24, 25) Kusonkhana koteroko kunalimbikitsa chikhulupiriro chawo mwa Yehova zomwenso zinawathandiza kupirira ziyeso zovuta za chikhulupiriro. M’dziko lina mu Africa kumene ntchito yolalikira inatsekedwa, Mboni za Yehova zinalibe mwayi wotetezedwa ndi apolisi, kupeza mapasipoti, mitchato, chithandizo chamankhwala, ndiponso ntchito. Nkhondo itaulika m’dera lina, anthu 39 a mpingo wina wapafupi kuphatikizapo ana anakhala kunsi kwa mlatho kwa miyezi inayi m’chipululu kuti apulumuke nkhondoyo m’tauni yakwawo. Zinthu zitafika pothina chonchi, kukambirana kwawo nkhani za m’Baibulo tsiku ndi tsiku ndiponso misonkhano ina zinawalimbikitsa kwambiri. Chotero anatha kupirira mavutowo ali olimba mwauzimu. Zimenezi zikusonyeza bwino lomwe kufunika kosonkhana nthaŵi zonse ndi anthu a Yehova.
Njira ina yolimbikitsira chikhulupiriro chathu mwa Yehova ndiyo kusonkhana nthaŵi zonse ndi anthu amene amamukhulupirira ndi mtima wonse. Yehova analamula anthu ake kusonkhana nthaŵi zonse kuti aphunzire za iye ndiponso kulimbikitsana. (Potsiriza, kuti tilimbikitse chikhulupiriro chathu mwa Yehova tiyenera kupitirizabe kugwira ntchito yolalikira Ufumu mwachangu, kukhala okonzeka nthaŵi zonse kuuza ena uthenga wabwino. Izi zikusonyezedwa ndi zomwe zinachitikira wofalitsa wina wachitsikana ku Canada yemwe anadwala kwambiri matenda a leukemia. Ngakhale pamene anali kudwala kwambiri iye anafuna kukhala mpainiya wokhazikika kapena kuti mtumiki wanthaŵi zonse. Kwanthaŵi yochepa yomwe anapezako bwino, iye anatha mwezi umodzi akuchita utumiki wa upainiya wothandiza. Kenako matendawo anakula kwambiri ndipo anamwalira miyezi ingapo yotsatira. Komabe, anakhalabe wolimba mwauzimu mpaka mapeto, ndipo chikhulupiriro chake mwa Yehova sichinagwedezekepo n’kamodzi komwe. Amayi ake anakumbukira kuti: “Mpaka mapeto, iye anali kuganizira kwambiri za ena kuposa za iye mwini. Anali kulimbikitsa ena kuŵerenga Baibulo, akumawauza kuti, ‘Tidzakhala limodzi m’Paradaiso.’”
Kusonyeza Chikhulupiriro Chathu mwa Yehova
“Monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.” (Yakobo 2:26) Zomwe Yakobo ananena zokhudza kukhulupirira Mulungu zili chimodzimodzinso ndi kumudalira kwathu. Kaya timanena moŵirikiza chotani kuti timakhulupirira Mulungu, koma ngati sitisonyeza kumukhulupirira kumeneko m’zochita zathu ndiye kuti zimenezo zilibe ntchito. Abrahamu anakhulupirira kwambiri Yehova ndipo anasonyeza chikhulupiriro chakecho mwa kumvera malamulo ake mosanyinyirika, mpaka kufikira pokonzeka kupereka nsembe mwana wake, Isake. Chifukwa cha kukhulupirika ndi kumvera kwapadera kumeneku, Abrahamu anadziŵika kukhala bwenzi la Yehova.—Ahebri 11:8-10, 17-19; Yakobo 2:23.
Tisadikire ziyeso zazikulu kuti tisonyeze kukhulupirika kwathu kwa Yehova. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m’chaching’onong’ono alinso wosalungama m’chachikulu.” (Luka 16:10) Tiphunzire kukhulupirira Yehova m’zochita zathu za tsiku ndi tsiku, kum’mvera iye ngakhale m’zinthu zomwe zingaoneke ngati zochepa. Tikaona mapindu omwe amadza chifukwa cha kumvera kotereku, chikhulupiriro chathu mwa Atate wathu wakumwamba chidzalimba ndipo chidzatitheketsa kuthana ndi ziyeso zazikulu ndi zoopsa.
Pamene dzikoli likuyandikira mapeto ake oopsawo, anthu a Yehova mosakayikira adzakumana ndi ziyeso ndiponso ngozi zambiri. (Machitidwe 14:22; 2 Timoteo 3:12) Mwa kukulitsa chikhulupiriro cholimba mwa Yehova tsopano lino, tingayembekezere kudzapulumuka kuloŵa m’dziko latsopano lolonjezedwa—kaya mwa kupulumuka pa chisautso chachikulu kapena mwa kuukitsidwa. (2 Petro 3:13) Tisalole mpang’ono pomwe kuti kusoŵa chikhulupiriro kutiwonongere unansi wathu wamtengo wapatali ndi Yehova. Tikatero, ndiye kuti zomwe zinanenedwa kwa Danieli atalanditsidwa m’dzenje la mikango zinganenedwenso kwa ife kuti: “Pathupi pake sipadaoneke bala, popeza anakhulupirira Mulungu wake.”—Danieli 6:23.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Kuti mumve nkhani yonse onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 1994, masamba 23-7.
[Chithunzi patsamba 9]
Kuŵerenga nkhani za atumiki okhulupirika a Yehova monga Martin Poetzinger, n’kolimbikitsa chikhulupiriro kwambiri