Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wosangalala ndi Wothokoza Ngakhale pa Vuto Losautsa Mtima

Wosangalala ndi Wothokoza Ngakhale pa Vuto Losautsa Mtima

Mbiri ya Moyo Wanga

Wosangalala ndi Wothokoza Ngakhale pa Vuto Losautsa Mtima

YOSIMBIDWA NDI NANCY E. PORTER

Panali pa June 5, 1947, madzulo, ku zilumba zofunda za Bahamas kumwera chakumadzulo kwa United States. Mosayembekezeka, mwamuna wina woona za anthu oloŵa ndi otuluka m’dzikolo, anafika komwe ine ndi mwamuna wanga George tinali kukhala. Anabweretsa kalata yakuti sitikuloledwa kupitiriza kukhala pa zilumbazo ndi kuti “tichoke nthaŵi yomweyo!”

INE ndi George tinali amishonale oyamba a Mboni za Yehova mu mzinda waukulu kwambiri ku Bahamas wa Nassau. Tinabwera kuno titamaliza maphunziro m’kalasi lachisanu ndi chitatu ku sukulu yophunzitsa umishonale ya Gileadi ku New York. Kodi tinalakwa chiyani kuti atithamangitse choncho titangokhalako miyezi itatu yokha? Nanga zinatheka bwanji kuti ndikhalabe konkuno kwa zaka zoposa 50?

Kukonzekera Utumiki

Ndimatsanzira kwambiri moyo wa Bambo anga a Harry Kilner. Kuti akhale a Mboni za Yehova, anadzipereka kwambiri. Choncho, anali chitsanzo chapamwamba kwa ine. Ngakhale kuti analibe moyo wamphamvu, ankapita kukalalikira pafupifupi kumapeto a mlungu uliwonse. Analidi kufunafuna Ufumu choyamba. (Mateyu 6:33) Pamene tinali ku Lethbridge, Alberta, m’dziko la Canada, m’ma 1930, sitinali opeza bwino kwenikweni, koma kanyumba kawo kokonzeramo nsapato kanali chimake cha zochitika zauzimu. Ndikukumbukira kuti kale ndili mwana, atumiki a nthaŵi zonse a Mboni za Yehova otchedwa apainiya, ankadzacheza kunyumba kwathu ndipo amatiuza zomwe anali kukumana nazo.

Mu 1943, ndinayamba utumiki wa upainiya ku Alberta kufupi ndi Fort Macleod ndi Claresholm. Panthaŵiyo, chifukwa cha nkhani zabodza zomwe otitsutsa anafalitsa, ntchito yathu yolalikira inali yoletsedwa ku Canada panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri yadziko lonse. Gawo lathu lolalikira linali lalitali makilomita 50. Koma pokhala achinyamata ndiponso amphamvu, sitinadandaule ndi kupalasa njinga kapena kuyenda pansi kupita ku midzi ing’onoing’ono ndi mafamu m’gawo lathulo. Panthaŵi imeneyi ndinali ndi mwayi wocheza ndi omwe anaphunzira ku sukulu ya Gileadi, ndipo zomwe ankasimba zinandisonkhezera kulakalaka umishonale.

Mu 1945 ndinakwatiwa ndi George Porter wa ku Saskatchewan, ku Canada. Makolo ake anali Mboni zamphamvu kuyambira mu 1916, ndipo nayenso anasankha utumiki wanthaŵi zonse kukhala ntchito yake. Gawo lathu loyamba linali chigwa chokongola cha Lynn, ku mzinda wa North Vancouver m’dziko la Canada. Posapita nthaŵi, tinaitanidwa ku Gileadi.

Kwanthaŵi yaitali, ndalankhulapo ndi anthu ophunzira ku masukulu osiyanasiyana a zaubusa, ndipo ndaona mmene maphunziro awo amenewo amawonongera kukhulupirira Mulungu ndi Mawu Ake Baibulo. Koma zimene ife tinaphunzira ku Gileadi, zinatithandiza kukhala oganiza bwino. Chachikulu n’chakuti, zinatilimbikitsa kukhulupirira Yehova Mulungu ndi Mawu ake. Anzathu omwe tinali nawo ku maphunzirowo anatumizidwa ku China, Singapore, India, m’mayiko a mu Africa, ku South America, ndi kwina kotero. Ndikukumbukirabe mmene tinasangalalira titamva kuti atitumiza ku zilumba zofunda za Bahamas.

Zomwe Zinachitika Kuti Tikhalebe

Poyerekeza maulendo omwe anzathu a ku sukuluwo anayenda, ulendo wathu wopita ku Bahamas unali waufupi. Mwamsanga, tinali kusangalala ndi nyengo yofunda, thambo lobiriŵira, madzi obiriŵira, nyumba za mitundu yowala, ndi njinga zankhaninkhani. Tikungofika kumene pa boti, tinapeza Mboni zisanu zomwe zinkatidikira. Posapita nthaŵi tinaphunzira kuti chikhalidwe cha kuno n’chosiyana kwambiri ndi zimene tinazoloŵera. Mwachitsanzo, mwamuna wanga anapemphedwa kuleka kumanditchula kuti wokondedwa tikakhala pagulu, chifukwa chakuti kaŵirikaŵiri mawuwa, amawagwiritsa ntchito ponena mkazi wachibwenzi.

Poona kuti tinkachita zinthu momasuka ndi anthu, akuluakulu achipembedzo anachita mantha ndipo posachedwa anatinamizira kuti ndife okonda Chikomyunizimu. Choncho tinalamulidwa kutuluka m’dzikolo. Koma nthaŵi yomweyo, Mboni, zomwe panthaŵiyo zinali zosakwana 20 pa zilumbazo, zinalemba pempho lakuti atilole kukhalabe ndipo anthu mazanamazana anasainira nawo pempholo. Choncho, lamulo lakuti tichoke linathetsedwa.

Kupita ku Gawo Latsopano

Choonadi cha Baibulo chinakula mofulumira m’mitima yokonda Mulungu, ndiye amishonale ambiri a ku Gileadi anatumizidwa ku Bahamas. Mu 1950 ofesi ya nthambi inakhazikitsidwa. Patapita zaka khumi, Milton Henschel, wa ku likulu ku Brooklyn, New York, anatiyendera ku Bahamas. Iye anafunsa ngati pali mmishonale amene angafune kukayamba ntchito yolalikira pa chilumba china cha Bahamas. Ine ndi George tinadzipereka. Choncho tinakakhala pachilumba cha Long Island kwa zaka 11.

Chilumba chimenechi chomwe n’chimodzi mwa zilumba zambiri zopanga dziko la Bahamas, n’chachikulu makilomita 140 m’litali ndi makilomita 6 m’lifupi. Panthaŵiyo, kunalibe matauni enieni kumeneko. Likulu lake, Clarence Town, linali ndi nyumba pafupifupi 50. Moyo wake unali wachimidzi weniweni, kopanda magetsi kapena madzi a m’mipopi. Choncho kunali koyenera kusintha moyo wathu. Pa chilumbachi, anthu amakonda kukambirana za umoyo wawo. Tinaphunzira kupewa kumafunsa anthu kuti “Mulibwanji lero?” chifukwa yankho lake limakhala lalitali lofotokoza matenda onse omwe munthuyo anadwalapo ndi mmene anachirira.

Kaŵirikaŵiri tinkalalikira ku khichini ndi khichini chifukwa anthu amakonda kukhala m’makhichini awo a kunja kwa nyumba ofoleledwa ndi udzu momwe mumakhala moto wa nkhuni. Anthu ake omwe anali alimi ndi asodzi anali osauka koma okoma mtima kwambiri. Ambiri a iwo anali opembedza komanso okonda zikhulupiriro kwabasi. Zochitika zodabwitsa ankaziona ngati zizindikiro zolosera chinachake.

Akuluakulu achipembedzo analibe manyazi kumaloŵa m’nyumba za anthu mwa kufuna kwawo n’kumawang’ambira mabuku ofotokoza Baibulo omwe timawapatsa. Amaopseza anthu amantha, koma ena samawaopa. Mwachitsanzo, mayi wina wa zaka 70 sanaope. Iye anafuna kulimvetsetsa Baibulo, ndipo mapeto ake, iye ndi anzake ena anakhala Mboni. Pamene tinali kupeza anthu ambiri ofuna choonadi pachilumbachi, George anali kuyenda pagalimoto mtunda wa makilomita 300 Lamlungu pothandiza anthuwa kufika kumisonkhano yathu.

M’miyezi yoyambirira pamene kunalibe Mboni zina, ine ndi George tinakhalabe auzimu mwa kupanga misonkhano yonse yachikristu nthaŵi zonse. Kuwonjezera apo, tinkaphunziranso nkhani mu Nsanja ya Olonda Lolemba lililonse usiku ndi kuŵerenga Baibulo. Tinkaŵerenganso magazini onse a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! tikangowalandira.

Bambo anga anamwalira tili ku Long Island. M’chilimwe chaka chotsatira, mu 1963, tinaitana mayi kuti azidzakhala pafupi nafe. Ngakhale kuti anali okalamba, anatha kukhala pachilumba cha Long Island mpaka imfa yawo mu 1971. Lerolino, pachilumba cha Long Island pali mpingo ndi Nyumba ya Ufumu yatsopano.

Vuto Losautsa Mtima

Mu 1980, George anaona kuti thanzi lake layamba kuwonongeka. Kunali kuyamba kwa nthaŵi yoŵaŵa kwambiri pa moyo wanga. Ndinaona mwamuna wanga wokondeka, wantchito mnzanga, ndi bwenzi, akuvutika ndi matenda a Alzheimer. Khalidwe lake linasinthiratu. Kenako anadwala kwambiri kwa zaka zinayi mpaka mu 1987 pamene anamwalira. Ankadzikakamiza kupita nawo kolalikira ndi kumisonkhano ngakhale kuti zimenezo zinkandipangitsa kukhetsa misozi kaŵirikaŵiri. Chikondi cha abale athu achikristu chandilimbikitsa kwambiri iye atamwalira, koma ndimam’kumbukirabe kwambiri.

Kulankhulana kwabwino ndiponso koŵirikiza, n’chomwe chinali chapadera kwambiri mu ukwati wanga ndi George. Poti tsopano George kulibe, ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cholimbikitsa atumiki ake ‘kupemphera kosaleka,’ ‘kulimbika chilimbikire m’kupemphera,’ ndi kugwiritsa ntchito “pemphero lonse.” (1 Atesalonika 5:17, 18; Aroma 12:12, 13; Aefeso 6:18) N’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova ali n’chidwi ndi umoyo wathu. Ndimadzimvadi ngati wamasalmo yemwe anaimba kuti “Wolemekezeka Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu.” (Salmo 68:19) Kusadera nkhaŵa zam’tsogolo, kuvomereza kulephera kwanga pazinthu zina, ndi kuthokoza madalitso a tsiku ndi tsiku, monga Yesu anatilangizira, n’kofunika kwambiri pa moyo.​—Mateyu 6:34.

Mphoto Zosangalatsa mu Utumiki

Kutanganidwa mu utumiki, kwandithandiza kuti ndisamaganize kwambiri zakale. Choncho ndimapeŵa maganizo opsinja mtima. Kuphunzitsa anthu ena choonadi cha m’Baibulo kumandisangalatsa. Kumandipangitsa kukhala ndi ndondomeko yabwino ya zinthu zauzimu ndi moyo wokhazikika.​—Afilipi 3:16.

Tsiku lina, mayi wina yemwe ndinalankhula naye za uthenga wa Ufumu n’tangofika kumene zaka 47 zapitazo, anandiimbira telefoni. Anali mwana wa mmodzi mwa anthu oyamba kuphunzira nawo Baibulo ku Bahamas mu 1947. Mayi ake, bambo ake, ndi abale ake onse anakhala a Mboni za Yehova ndi zidzukulu zawo zomwe. Abale ake oposa 60 ndi Mboni za Yehova. Koma iye sanavomereze choonadi. Tsopano wakonzeka kukhala mtumiki wa Yehova Mulungu. N’zosangalatsatu kuona Mboni zochepa zomwe ine ndi George tinazipeza ku Bahamas zikuchuluka kuposa 1,400.

Nthaŵi zina anthu amandifunsa ngati ndimadandaula kuti ndilibe ana. N’zoona kuti kukhala ndi ana lingakhale dalitso. Koma chikondi chomwe ana anga, adzukulu anga ndi adzukulu tudzi anga auzimu amandisonyeza nthaŵi zonse, n’choposa chimene makolo ambiri amalandira. Ndithudi, ‘ochita zabwino’ ndiwo amakhala okondwa kwambiri. (1 Timoteo 6:18) N’chifukwa chake ndimayesetsa kuchita zambiri pa utumiki mogwirizana ndi umoyo wanga.

Tsiku lina ndili pa ofesi ya dokotala wamano, mtsikana wina anandipeza nati: “Inu simundidziŵa, koma ine ndakudziŵani. Ndangoti ndikuuzeni kuti ndimakukondani.” Kenako anafotokoza mmene anaphunzirira choonadi cha m’Baibulo ndi kuthokoza amishonalefe chifukwa chobwera ku Bahamas.

Tsiku linanso pochokera ku holide, ndinapeza duŵa lokongola pakhomo la kumene ndikukhala tsopano ku nthambi ya Mboni za Yehova ku Nassau. Linali ndi mawu akuti: “Takulandirani ndi manja aŵiri.” Ndikuthokoza kwambiri. Zimandipangitsa kukonda Yehova kwambiri poona mtundu wa anthu omwe Mawu ake, gulu lake, ndi mzimu wake wapanga. Zoona, Yehova amatithandiza kudzera mwa anthu omwe timakhala nawo.

Ndikuthokoza Kwambiri

Si kuti moyo wanga wakhala wopanda mavuto nthaŵi zonse ngakhale panopo. Koma pali zambiri zomwe ndiyenera kuthokoza. Kusangalatsa kwa utumiki, chikondi ndi kukoma mtima kwa abale ndi alongo ambiri achikristu, kusamalidwa ndi gulu la Yehova, choonadi chosangalatsa cha m’Baibulo, chiyembekezo chodzakhalanso ndi okondedwa akadzaukitsidwa kwa akufa, ndi zaka 42 zomwe ndinali pabanja ndi mtumiki wokhulupirika wa Yehova. Tisanakwatirane, ndinapemphera kuti ndikhale wothandiza kwa mwamuna wanga nthaŵi zonse kuti apitirizebe utumiki wanthaŵi zonse, womwe ankaukonda kwambiri. Mokoma mtima Yehova anayankha pemphero limenelo. Choncho, ndikufuna kusonyeza kuyamika Yehova mwa kukhala wokhulupirika kwa iye nthaŵi zonse.

Alendo ambiri amabwera kudzacheza kuno ku Bahamas. Amawononga ndalama zambiri kudzasangalala ndi nyengo yofunda. Posankha kutumikira Yehova kulikonse komwe gulu lake lingafune, ndasangalala kuyendayenda m’zilumbazi, kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Koma chofunika kwambiri chomwe ndadziŵa ndi kuchiyamikira, ndicho chikondi cha anthu aubwenzi kwambiri a ku Bahamas.

Ndikuthokoza kwambiri amene anaphunzitsa makolo anga choonadi, ndi kuti makolo angawo anandipatsa chilakolako chofunafuna Ufumu wa Mulungu poyamba ndikali wamng’ono. Nawonso atumiki achinyamata a Yehova masiku ano angapeze madalitso ochuluka ataloŵa “pakhomo lalikulu” la mwayi waukulu wowonjezera utumiki. (1 Akorinto 16:9) Nanunso mungathokoze kwambiri mutagwiritsa ntchito moyo wanu kulemekeza “Mulungu wa milungu,” Yehova.​—Deuteronomo 10:17; Danieli 2:47.

[Chithunzi patsamba 24]

Kulalikira mumsewu ku Victoria, B.C., mu 1944

[Chithunzi patsamba 24]

Ine ndi George tinapita kusukulu ya Gileadi mu 1946

[Chithunzi patsamba 25]

Ine ndi George kumaso kwa nyumba ya amishonale mu mzinda wa Nassau, ku Bahamas mu 1955

[Chithunzi patsamba 26]

Nyumba ya amishonale ku Deadman’s Cay komwe tinatumikirako kuyambira mu 1961 mpaka mu 1972