Zinthu Zosaiwalika
Zinthu Zosaiwalika
CHAKA ndi chaka, Mboni za Yehova m’mayiko osiyanasiyana zimachita misonkhano ikuluikulu yachikristu. Kumeneko zimasangalala ndi malangizo ndi macheza olimbikitsa mwauzimu. Koma mbali zina za misonkhano yawo zimachititsa chidwi kwambiri alendo.
Mwachitsanzo, mu July 1999, Mboni zikwizikwi za ku Mozambique zinasonkhana kwa masiku atatu pa Msonkhano Wachigawo wopindulitsa wakuti “Mawu a Ulosi a Mulungu.” Kwa ambiri, kanali koyamba kupezeka pamsonkhano wotero ndipo anachita chidwi ndi zimene anamva ndi kuona.
Munthu wina pa Nyumba ya Misonkhano ku Maputo anati: “Sindinaonepo malo okongola ngati awa m’moyo wanga! M’zipinda zosambiramo munali sopo, magalasi odziyang’anira, ndiponso munali fungo labwino. Panalibe zosokoneza ngakhale phokoso la ana omenyana. Kunalibe kukankhanakankhana. Ndinaona achinyamata okondwa akukambirana zolimbikitsa. Ndinachitanso chidwi kuona aliyense atavala bwino. Ulendo wina ndidzabwera ndi ana anga ndi kum’limbikitsa mwamuna wanga kuti adzabwere kumsonkhanowu.”
Inde, anthu amaona kuona mtima, kukhulupirika ndi ukhondo wa Mboni za Yehova. N’chifukwa chiyani Mboni zili zosiyana ndi ena? Zimayesetsa kugwiritsa ntchito zomwe zimaphunzira m’Baibulo. Bwanji inuyo chaka chino osapita kukakhala nawo pa msonkhano waukulu kapena ku misonkhano ya mlungu ndi mlungu ku Nyumba yawo ya Ufumu ya kwanuko mukadzionere nokha?
[Chithunzi patsamba 32]
ZAMBIA
[Chithunzi patsamba 32]
KENYA
[Chithunzi patsamba 32]
MOZAMBIQUE