Ndimayamikira Chifukwa Chokumbukira Zinthu Zamtengo Wapatali!
Mbiri ya Moyo Wanga
Ndimayamikira Chifukwa Chokumbukira Zinthu Zamtengo Wapatali!
YOSIMBIDWA NDI DRUSILLA CAINE
Munali m’chaka cha 1933, ndipo n’kuti nditangokwatiwa kumene ndi Zanoah Caine, yemwe mofanana ndi ine, anali kopotala—mlaliki wanthaŵi zonse. Chimwemwe chitadzala tsaya, ndinakonza zokagwirizana ndi mwamuna wangayo pantchito yake. Koma kuti ndichite zimenezo, ndinafunika kukhala ndi njinga. Njinga inali chinthu chokwera mtengo kwambiri chomwe sindikanatha kugula chifukwa choti zinthu panthaŵiyo sizinali bwino chifukwa cha vuto lalikulu la zachuma. Kodi ndikanatani?
ALAMU anga atatu atamva za vuto langa anafufuza m’malo otaya zinyalala m’deralo, zipangizo zakale za njinga kuti andikonzere njinga. Anazipeza, n’kuzilumikiza, nikhala njinga! Nditangodziŵa kukwera njinga, ine ndi Zanoah tinauyamba ulendo, tinatchova njinga mokondwa kudutsa m’madera a Angelezi a Worcester ndi Hereford kwinaku tikumalalikira kwa onse amene timakumana nawo.
Sindinkadziŵa kuti zimenezi, zomwe ndinkachita chifukwa cha chikhulupiriro zidzandipatsa moyo wodzala ndi chikumbumtima cha zinthu zabwino. Komabe, maziko a moyo wanga wauzimu anayalidwa ndi makolo anga omwe ndinkawakonda.
Zaka Zovuta za Nkhondo Yaikulu
Ndinabadwa mu December, m’chaka cha 1909. Nditangobadwa, amayi anga analandira buku lakuti The Divine Plan of the Ages, ndipo mu 1914 makolo anga anapita nane kokaonera “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe,” ku dera la Oldham, ku Lancashire. (Zonse ziŵirizi zinali zokonzedwa ndi anthu omwe tsopano akudziŵika ndi dzina loti Mboni za Yehova.) Ngakhale kuti ndinali mwana, ndikukumbukira bwinobwino kuti pamene timabwerera kunyumba, ndinkadumphadumpha ndi chimwemwe chifukwa cha zomwe ndinaona! Kenako, Frank Heeley anayambitsa gulu la phunziro la Baibulo
ku Rochdale, komwe tinkakhala. Kukhala nawo paphunziroli kunatithandiza monga banja kumvetsa bwino Malemba.Kukhala kwathu mwabata kunasokonekera m’chaka chomwecho chifukwa cha kubuka kwa nkhondo yaikulu, yomwe masiku ano timaitcha kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Atate anga anawasankha kuti akhale m’gulu la asilikali koma iwo anakana. Kukhoti anawatcha kuti ndi “munthu wa khalidwe labwino kwambiri,” ndipo makalata angapo anatumizidwa kuchokera kwa “anthu olemekezeka onena kuti iwo ankakhulupirira kuti zinali zoona kuti sakufuna kunyamula zida zankhondo,” inatero nyuzipepala ina yakwathuko.
M’malo mowapatsa ufulu wonse wosachita nawo zankhondo, atate anga anawalemba monga msilikali “wosamenya nkhondo yeniyeniyo basi.” Patangopita nthaŵi pang’ono anthu anayamba kutinyoza tonsefe, atate, amayi ndi ine. M’kupita kwanthaŵi, udindo wawo unapendedwanso, ndipo anapatsidwa ntchito ya zaulimi, koma alimi ena anapezerapo mwayi pa zimenezi ndi kumawapatsa malipiro ochepa mwinanso osawalipira n’komwe. Pofuna kuthandiza banja, amayi ankagwira ntchito yotopetsa kwambiri pamalo ena ochapira zovala a munthu wamba, n’kumalandira malipiro ochepa. Koma tsopano ndikuona mmene ndinalimbikitsidwira chifukwa chothera chitsikana changa ndikulimbana ndi mavuto oterowo. Kuchita zimenezo kunandithandiza kukhala woyamikira zinthu zofunika kwambiri zauzimu.
Kachiyambi Kakang’ono
Posapita nthaŵi yaitali, Daniel Hughes, wophunzira Baibulo wakhama kwambiri, anakhala bwenzi lathu lapamtima. Anali wofukula malasha ku Ruabon, mudzi womwe uli pamtunda wa makilomita 20 kuchokera ku Oswestry, komwe tinali titasamukira. Amalume a Dan, malinga ndi momwe ndinkawatchulira, ankachezera banja lathu, ndipo nthaŵi iliyonse akabwera kudzationa, nkhani zawo zinali za m’Malemba. Sankakamba nkhani wamba. Gulu lophunzira Baibulo linakhazikitsidwa ku Oswestry m’chaka cha 1920, ndipo mu 1921, Amalume a Dan anandipatsa buku lakuti Zeze wa Mulungu. Ndinalikonda kwambiri chifukwa chakuti linkapangitsa ziphunzitso za Baibulo kukhala zondiphwekera kwambiri kuzimva.
Ndiponso panali Pryce Hughes, * yemwe pambuyo pake anadzakhala mtumiki woyang’anira ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku London. Ankakhala ndi banja lake ku Bronygarth, chakufupi ndi kwathu, kumalire ndi Wales, ndipo mlongo wake, Cissie, anakhala mnzawo wapamtima wa amayi.
Ndikukumbukira chisangalalo cha mu 1922 pamene pempho ‘lolengeza Mfumu ndi ufumu wake’ linaperekedwa. M’zaka zotsatira, ngakhale kuti ndinali ndidakali pasukulu, ndinagwira nawo mwakhama ntchito yogaŵira mathirakiti apadera mu 1924, makamaka lakuti Ecclesiastics Indicted. Ndikamalingalira zaka khumi zimenezo, ndimaona kuti unali mwayi waukulu kwambiri kucheza ndi abale ndi alongo ambiri okhulupirika. Ena mwa iwo ndi monga Maud Clark * ndi Mary Grant, * yemwe ankatumikira naye limodzi, Edgar Clay, * Robert Hadlington, Katy Roberts, Edwin Skinner, * pamodzi ndi Percy Chapman ndi Jack Nathan, * omwe onse aŵiri anapita ku Canada kukathandiza ntchito kumeneko.
Nkhani ya Baibulo yakuti “Mamiliyoni Okhala ndi Moyo Lero Sadzafa Konse” inali ulaliki wapanthaŵi yake m’gawo lathu lomwe linali lalikulu kwambiri. Pa May 14, 1922, Stanley Rogers, wachibale wa Pryce Hughes anabwera kuchokera ku Liverpool kudzakamba nkhaniyi ku Chirk, mudzi wa kumpoto kwa mzinda wathu, ndipo madzulo ake anaikamba pa nyumba yoonetsera kanema ku Oswestry. Mpaka pano ndikanasunga kamodzi mwa timapepala toitanira anthu tomwe tinasindikizidwira mwambo umenewo. Kwazaka zonsezo, kagulu kathuko kanapitiriza kulimbikitsidwa chifukwa cha kuchezera kwa oyang’anira oyendayenda atatu omwe tinkawatcha kuti aulendo wachipembedzo omwe mayina awo anali Herbert Senior, Albert Lloyd, ndi John Blaney.
Nthaŵi Yosankha
Mu 1929, ndinasankha kuti ndibatizidwe. Ndinali ndi zaka 19, ndipo nthaŵi yomweyo, ndinakumana ndi chiyeso changa choyambirira. Ndinadziŵana ndi mnyamata wina yemwe atate ake Deuteronomo 7:3; 2 Akorinto 6:14.
anali andale. Tinakondana ndipo anandifunsira za ukwati. Buku lakuti Government linali litatulutsidwa chaka chimodzi zimenezo zisanachitike, chotero ndinam’patsa buku limodzi. Koma pasanapite nthaŵi yaitali ndinazindikira kuti iye alibe chidwi ndi boma lakumwamba, yomwe inali nkhani yaikulu m’bukulo. Ndinadziŵa kuchokera pa zomwe ndinkaphunzira kuti Aisrayeli akale analamulidwa kusapanga mgwirizano uliwonse wa ukwati ndi anthu osakhulupirira ndiponso kuti mfundo imeneyi imagwira ntchito kwa Akristu. Choncho, ndinam’kana ngakhale kuti kunali kovuta kutero.—Ndinalimbikitsidwa ndi mawu a mtumwi Paulo akuti: “Tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.” (Agalatiya 6:9) Nawonso okondedwa Amalume a Dan anandithandiza pamene analemba kuti: “Pamavuto aakulu ndiponso aang’onoang’ono, gwiritsa ntchito Aroma 8, vesi ya 28,” yomwe imati: “Ndipo tidziŵa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.” Sikuti kunali kophweka, koma ndinadziŵa kuti ndasankha chinthu cholondola. M’chaka chomwecho ndinalembetsa ukopotala.
Kuthana Ndi Vuto
Mu 1931 tinalandira dzina lathu latsopano lakuti Mboni za Yehova, ndipo m’chaka chimenecho tinakhala ndi ndawala yaikulu pogwiritsa ntchito kabuku kakuti The Kingdom, the Hope of the World. Wandale, mtsogoleri wachipembedzo, ndi wamalonda aliyense tinam’patsa kabukuka. Gawo langa linali kuchokera ku Oswestry mpaka ku Wrexham, mtunda wa makilomita 25 kuloŵera kumpoto kwa Oswestry. Chinali chintchito kuti ndikwanitse gawo lonselo.
M’chaka chotsatira, pamsonkhano wachigawo ku Birmingham, panalengezedwa kuti pakufunika antchito odzifunira okwana 24. Mwamsangamsanga, anthu 24 tinapereka maina athu kuti tikufuna utumiki watsopanowo, osadziŵa kuti unali wotani. Tinadabwa kwambiri pamene anatiika aŵiriaŵiri kuti tigaŵire kabuku komwe kaja ka The Kingdom, the Hope of the World titadzikoloŵeka zikwangwani kumbuyo ndi kumaso, zolemera kwambiri zolengeza za Ufumu.
Ndinkachita manyazi kwambiri kugwira ntchito m’mabwalo a tchalitchi, koma ndinadzilimbikitsa ndi kuti mumzindamo munalibe aliyense wondidziŵa. Koma, munthu woyamba kundilankhula anali mzanga wakale wa kusukulu yemwe anangondiyang’ana n’kulankhula modabwa kuti: “N’chifukwa chiyani wavala chonchi?” Chochitika chimenecho chinandithandiza kuthetsa kuopa anthu komwe ndinali nako!
Kuloŵerera M’kati Mwenimweni mwa Gawo
Mu 1933, ndinakwatiwa ndi Zanoah, yemwe mkazi wake anamwalira ndipo iye anali wamkulu kuposa ine ndi zaka 25. Mkazi wake woyamba anali Wophunzira Baibulo wakhama kwambiri, ndipo Zanoah anapitirizabe kutumikira mokhulupirika pambuyo pa imfa ya mkazi wake woyambayo. Patapita nthaŵi pang’ono, tinasamuka ku England kupita ku gawo lathu latsopano ku North Wales, mtunda wa pafupifupi makilomita 150 kuchokera ku England. Makatoni, masutukesi, ndi katundu wina wofunika tinazikoloweka pa mahandulo a njinga zathu, wina n’kum’mangirira pamtanda ndi wina m’mabasiketi a kutsogolo kwa njinga, koma tinakafika bwinobwino! Sitinkasiya njinga mu utumiki wathuwo, tinkakwera njinga popita kulikonse, ngakhale kutsala pang’ono kufika pamwamba pa phiri la Cader Idris, phiri la ku Wales lotalika mamita pafupifupi 900. Zinali zosangalatsa kwambiri kupeza anthu olakalaka kumva “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.”—Mateyu 24:14.
Titangokhalako nthaŵi pang’ono, anthu anatiuza kuti munthu wina wodziŵika ndi dzina loti Tom Pryce wakhala akuwalalikira, monga momwe tinkachitira ife. M’kupita kwanthaŵi tinazindikira kuti Tom ankakhala pa Long Mountain, kufupi ndi Welshpool. Ndipo zinali zodabwitsa kwambiri kudziŵana naye. M’kati mwa masiku anga oyambirira a ntchito yolalikira, ndinagaŵira Tom buku lothandiza kuphunzirira Baibulo lakuti Reconciliation. Analiphunzira payekha, n’kulembera kalata ku London yopempha mabuku ena, ndipo kuyambira nthaŵi imeneyo anauza ena za chikhulupiriro chake chatsopano mwakhama. Tinkachezerana kwanthawi yaitali, ndipo nthaŵi zambiri tonse atatu tinkaphunzirira pamodzi n’cholinga chofuna kulimbikitsana.
Ngozi Idzetsa Madalitso
Mu 1934 makopotala onse a kufupi ndi North Wales anaitanidwa kupita ku tauni ya Wrexham kukathandiza kugaŵira kabuku kakuti Righteous Ruler. Tsiku limodzi tisanayambe ndawala yapadera imeneyi, panachitika ngozi yokhudza dziko lonse. Kuphulika kwa mgodi wa malasha ku Gresford, makilomita atatu kuloŵera kumpoto kwa Wrexham, kunapha antchito a pamgodiwo okwana 266. Ana oposa 200 anakhala opanda bambo ndipo akazi 160 anakhala amasiye.
Tinafunikira kudziŵa ofedwawo, kuwachezera, ndi kuwagaŵira kabukuko. Pa mayina omwe ndinapatsidwa panali mayi Chadwick omwe mwana wawo wa zaka 19 anamwalira. Pamene ndinapita kukawachezera, n’kuti Jack, mwana wawo wamwamuna wamkulu atabwera kudzawalimbikitsa. Mnyamatayo anandizindikira koma sananene zimenezo. Pambuyo pake anaŵerenga kabukuko ndiye n’kufufuza kabuku kena kakuti The Final War komwe ndinamusiyira zaka zingapo m’mbuyo mwake.
Jack ndi mkazi wake dzina lake May anafufuza komwe ndin’kakhala ndipo anabwera kudzafuna mabuku ena. Mu 1936 anavomera kuchitira misonkhano m’nyumba mwawo ku Wrexham. Miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pa kuchezera kwa Albert Lloyd, mpingo unakhazikitsidwa ndipo Jack Chadwick anakhala woyang’anira wotsogolera. Ndipo panopo ku Wrexham kuli mipingo itatu.
Moyo M’kalavani ya chi Gypsy
Pofika panthaŵiyi, n’kuti tikugona paliponse pamene tapeza chifukwa choti tinali kuyendayenda, koma Zanoah anaona kuti kunali kofunika kuti tikhale ndi nyumba yathuyathu, nyumba yoti tingathe kumaikoka kupita nayo ku malo osiyanasiyana. Mwamuna wanga anali kalipentala waluso wa mtundu wa chi Gypsy, ndipo anakhoma kalavani ya chi Gypsy kuti tizikhalamo. Tinaitcha kuti Elizabeti, dzina la m’Baibulo lotanthauza kuti “Mulungu Wopata.”
Ndimakumbukira bwino kwambiri malo ena omwe tinakhalapo, munali m’munda wa zipatso m’mbali mwa mtsinje. Ine ndinkangoona ngati Paradaiso! Palibe chomwe chinatilepheretsa kukhala osangalala m’zaka zomwe tinakhala m’kalavaniyo, ngakhale kuti inali yochepa. M’nyengo yozizira, nthaŵi zambiri nsalu za pabedi zinkauma ndi chisanu n’kuphathikika ku zipupa za kalavani, ndipo nthaŵi ndi nthaŵi tinkakhala ndi vuto la mame. Ndiponso tinkafunikira kumakatunga madzi, nthaŵi zina kuchoka nawo kutali, koma tinathandizana kuthetsa mavuto ameneŵa.
M’nyengo ina yozizira ndinadwala ndipo tinali ndi chakudya chochepa ndiponso opanda ndalama. Salmo 37:25: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: Ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.” Anandiyang’ana n’kunena kuti: “Ngati sipachitika kena kalikonse posachedwapa, tiyamba kupemphetsa, ndipo sindikuganiza kuti Mulungu angalole zimenezo kuti zichitike!” Kenako anapita kukalalikira kwa anzathu oyandikana nawo nyumba.
Zanoah anakhala pabedi, n’kundigwira dzanja, ndi kundiŵerengeraZanoah atabwera dzuŵa lili paliwombo, kuti adzandipangire kenakake koti ndimwe, panali kalata yake. Inali ndi £50 zochokera kwa atate ake. Zaka zingapo zimenezi zisanachitike, Zanoah anam’namizira kuti waba katundu, komano panthaŵiyi n’kuti zitadziŵika kuti sanabe. Mphatso imeneyi inali yom’pepesera. Zinafika panthaŵi yake!
Phunziro Labwino Kwambiri
Nthaŵi zina timapeza phunziro pa chinachake patadutsa zaka zambiri. Mwachitsanzo: Ndisanasiye sukulu mu 1927, ndinalalikira kwa anzanga onse a m’kalasi ndi aphunzitsi—kupatulapo mmodzi, Lavinia Fairclough. Ndinaganiza kuti ndisauze Mayi Fairclough za zomwe ndinkaganiza pa moyo wanga, chifukwa chakuti panalibe aliyense yemwe ankachita chidwi ndi zimenezo, komanso chifukwa choti sitinkagwirizana ndi Mayi Fairclough. Ndinadabwa, komanso ndinasangalala kwambiri, zaka ngati 20 pambuyo pake pamene amayi anga anandiuza kuti mphunzitsi ameneyu wabwera kudzachezera anzake onse akale pamodzi ndi ana ake a sukulu kudzawauza kuti tsopano ndi wa Mboni za Yehova!
Titakumana, ndinafotokoza chifukwa chake sindinawauze poyambirira za chikhulupiriro changa ndiponso ntchito yomwe ndinakonza kugwira kwa moyo wanga wonse. Anakhala duu, kumvetsera ndiyeno n’kunena kuti: “Nthaŵi yonseyi ndakhala ndikufunafuna choonadi. Chinali chinthu chomwe ndakhala ndikuchilakalaka m’moyo wanga!” Chochitika chimenecho chinali phunziro labwino koposa—lakuti ndisalephere kulalikira kwa aliyense yemwe ndakumana naye ndiponso ndisamaweruziretu munthu aliyense.
Nkhondo Inanso ndi Zochitika Pambuyo Pake
Zizindikiro zankhondo zinayamba kuoneka pamene timafika chakumapeto kwa m’ma 1930. Mchimwene wanga Dennis, yemwe anali wamng’ono kwa ine ndi zaka 10 anamuuza kuti amulola kusamenya nawo nkhondo ngati sasiya ntchito yomwe amagwira. Anali asanasonyezepo chidwi chachikulu m’choonadi, choncho ine ndi mwamuna wanga tinapempha apainiya a komwe iye ankakhala, Rupert Bradbury ndi mng’ono wake David kuti akacheze naye. Anaterodi, ndipo anaphunzira naye Baibulo. Dennis anabatizidwa mu 1942, kenako anayamba upainiya, ndipo anasankhidwa kukhala woyang’anira woyendayenda mu 1957.
Mwana wathu wamkazi, Elizabeth, anabadwa mu 1938, ndipo Zanoah anawonjezera kalavani kuti izitikwanira. Pamene mwana wathu wamkazi wachiŵiri, Eunice, anabadwa mu 1942, tinaona kuti kunali kwanzeru kuti tipeze nyumba yokhazikika. Choncho, Zanoah anasiya upainiya kwazaka zingapo, ndipo tinakaloŵa nyumba ina yaing’ono kufupi ndi ku Wrexham. Kenako, tinakakhazikika ku mzinda wa Middlewich, womwe ndi woyandikana ndi dera la Cheshire. Mwamuna wanga wokondedwa anamwalirira kumeneko mu 1956.
Ana athu aakazi aŵiri anakhala alaliki anthaŵi zonse, ndipo onse aŵiri akusangalala m’mabanja mwawo. Eunice ndi mwamuna wake, yemwe ndi mkulu, akutumikirabe monga apainiya apadera ku London. Nayenso mwamuna wa Elizabeth ndi mkulu mu mpingo, ndipo akukhala ku Preston, Lancashire. Ndimasangalala kwambiri kuti iwo, ana awo, ndiponso zidzukulutudzi zanga akukhala nane pafupi.
Ndimayamikira kuti ndimatha kuyenda kuchoka pa khomo lakumaso kwa nyumba yanga kupita ku Nyumba ya Ufumu yomwe ili tsidya lina la msewu. M’zaka zingapo zapitazi, ndakhala ndikusonkhana ndi gulu lolankhula Chigujarati, lomwe limasonkhana pa holo yomweyo. Kuphunzira chinenerochi kwakhala kovuta chifukwa choti tsopano sindimvetsa kwenikweni. Nthaŵi zina kumavuta kuti ndimve mawu ake ambiri omwe ndi ovuta, ngati momwe munthu wamng’ono angachitire. Komabe ndi zosangalatsa ngakhale kuti zikuvuta.
Ndimathabe kulalikira kukhomo ndi khomo ndiponso kuchititsa maphunziro a Baibulo m’nyumba mwanga. Anzanga akabwera kudzandiona, nthaŵi zonse ndimasangalala kukumbukira zina mwa zomwe zinandichitikira kalekale. Ndimayamikira kwambiri chifukwa cha chikumbumtima chamtengo wapatali cha madalitso omwe ndalandira pamene ndikusonkhana ndi anthu a Yehova kwazaka pafupifupi 90.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 13 Nkhani yosimba mbiri ya moyo wa Pryce Hughes, yamutu wakuti “Kuyendera Limodzi ndi Gulu Lokhulupirika,” inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya April 1, 1963.
^ ndime 14 Nkhani za mbiri ya moyo wa atumiki a Yehova okhulupirika ameneŵa zinatuluka m’makope oyambirira a Nsanja ya Olonda.
^ ndime 14 Nkhani za mbiri ya moyo wa atumiki a Yehova okhulupirika ameneŵa zinatuluka m’makope oyambirira a Nsanja ya Olonda.
^ ndime 14 Nkhani za mbiri ya moyo wa atumiki a Yehova okhulupirika ameneŵa zinatuluka m’makope oyambirira a Nsanja ya Olonda.
^ ndime 14 Nkhani za mbiri ya moyo wa atumiki a Yehova okhulupirika ameneŵa zinatuluka m’makope oyambirira a Nsanja ya Olonda.
^ ndime 14 Nkhani za mbiri ya moyo wa atumiki a Yehova okhulupirika ameneŵa zinatuluka m’makope oyambirira a Nsanja ya Olonda.
[Chithunzi patsamba 25]
Kapepala koitanira anthu kolengeza za nkhani ya Baibulo yakuti “Mamiliyoni Okhala ndi Moyo Lero Sadzafa Konse,” yomwe ndinaimva pa May 14, 1922
[Chithunzi patsamba 26]
Ndili ndi Zanoah, titangokwatirana kumene mu 1933
[Chithunzi patsamba 26]
Nditaima pafupi ndi “Elizabeti,” kalavani yathu yomwe mwamuna wanga anakhoma