Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pindulani ndi Zomwe Munazoloŵera Kuchita

Pindulani ndi Zomwe Munazoloŵera Kuchita

Pindulani ndi Zomwe Munazoloŵera Kuchita

MWAMUNA wina anakhala zaka 12 m’dera lina lakufupi ndi mzinda wa Athens. Tsiku ndi tsiku ankadutsa msewu umodzimodzi pochoka kuntchito kupita kunyumba. Kenako anasamukira ku dera lomwe linali mbali ina ya mzindawo. Tsiku lina ataweruka kuntchito, anauyamba ulendo wa kunyumba. Atafika komwe ankakhala kale kuja, m’pamene anazindikira kuti wasokera. Chizoloŵezi ndi chomwe chinam’pititsa kunyumba yake yakale ija!

M’posadabwitsa kuti zinthu zomwe tinazoloŵera kuchita nthaŵi zina zimatchedwa kuti khalidwe, mphamvu yomwe imakhudza kwambiri miyoyo yathu. Choncho, zizoloŵezi tingaziyerekezere ndi moto. Moto ungakhale muuni wabwino kwambiri m’malo a mdima, ungafunditse matupi athu ndiponso ungatenthetse chakudya. Komatu, moto ungakhalenso mdani woipa kwambiri wowononga miyoyo ndiponso katundu. Ndi mmenenso zilili ndi zizoloŵezi. Zikakulitsidwa moyenera, zimapindulitsa kwambiri. Koma zingakhalenso zowononga.

Kwa mwamuna yemwe tam’tchula poyamba uja, zinthu zomwe anazoloŵera kuchita zinangom’tayitsa nthaŵi chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto pamsewu. Ngati ndi zinthu zofunika kwambiri, zizoloŵezi zingatithandize kupambana kapena zingatigwetse m’tsoka. Talingalirani zitsanzo zochepa chabe zopezeka m’Baibulo za zochitika zenizeni zomwe zikusonyeza mmene zizoloŵezi zingatithandizire kapena mmene zingatilepheretsere kutumikira Mulungu ndiponso kukhala naye paunansi.

Zitsanzo za m’Baibulo za Zizoloŵezi Zabwino ndi Zoipa

Nowa, Yobu, ndi Danieli, onseŵa anakhala paunansi wabwino kwambiri ndi Mulungu. Baibulo limawayamikira ‘chifukwa cha chilungamo chawo.’ (Ezekieli 14:14) Ndithudi, moyo wa anthu atatu onseŵa unasonyeza kuti anali ndi zizoloŵezi zabwino.

Nowa anauzidwa kuti akhome chingalawa, chombo chachitali kuposa bwalo la maseŵero a mpira wamiyendo ndiponso msinkhu wake wautali kuposa nyumba ya nsanjika zinayi. Wokhoma zombo aliyense wa m’nthaŵi zakale akanachita mantha kwambiri ndi chintchito chachikulu chimenecho. Koma Nowa ndi anthu asanu ndi aŵiri a m’banja mwake anakhoma chingalawacho popanda kugwiritsa ntchito zida zamakono. Kuwonjezera pamenepo, Nowa anapitirizabe kulalikira kwa anthu a m’nthaŵi yake. Sitingakayikire kuti iye ankasamaliranso zosoŵa zauzimu ndi zakuthupi za banja lake. (2 Petro 2:5) Kuti athe kuchita zonsezi, Nowa ayenera kuti anali ndi zizoloŵezi zabwino pantchito. Komanso, Nowa analembedwa m’mbiri ya Baibulo monga munthu amene ‘anayendabe ndi Mulungu woona. . . . Nowa anachita monga mwa zonse anam’lamulira Mulungu.’ (Genesis 6:9, 22; 7:5) Popeza m’Baibulo iye anatchedwa “wangwiro,” Nowa ayenera kuti anapitirizabe kuyenda ndi Mulungu chitapita Chigumula ndipo ngakhalenso anthu atapandukira Yehova pa Babele. Inde, Nowa anayendabe ndi Mulungu mpaka pa imfa yake ali ndi zaka 950.​—Genesis 9:29.

Zizoloŵezi zabwino za Yobu zinam’thandiza kukhala munthu “wangwiro ndi woongoka.” (Yobu 1:1, 8; 2:3) Mwachizoloŵezi, kapena kuti nthaŵi zonse, iye ankakhala monga wansembe wabanja lake poperekera nsembe ana ake akapanga madyerero awo, kuti mwinamwake ‘achimwa, ndi kuchitira Mulungu mwano mumtima mwawo. Anatero Yobu masiku onse.’ (Yobu 1:5) Mosakayikira, zizoloŵezi zokhudza kulambira Yehova zinali zofala kwambiri m’banja la Yobu.

Danieli anatumikira Yehova “kosalekeza” kwa moyo wake wonse wautaliwo. (Danieli 6:16, 20) Kodi ndi zizoloŵezi zabwino zauzimu zotani zomwe Danieli anali nazo? Chimodzi ndi choti, ankapemphera kwa Yehova nthaŵi zonse. Ngakhale kuti panali lamulo lachifumu lotsutsana ndi zochita zake, Danieli ‘ankagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.’ (Danieli 6:10) Sakanatha kusiya chizoloŵezi chake chopemphera kwa Mulungu, ngakhale panthaŵi yomwe kuchita zimenezo kunaika moyo wake pachiswe. Mosakayikira, chizoloŵezi chimenechi chinalimbikitsa Danieli pa moyo wake wokhala wokhulupirika kwambiri kwa Mulungu. Mwachionekere, Danieli analinso ndi chizoloŵezi chabwino choŵerenga ndi kusinkhasinkha mozama pa malonjezo osangalatsa kwambiri a Mulungu. (Yeremiya 25:11, 12; Danieli 9:2) Ndithudi, zizoloŵezi zabwino zimenezi zinam’thandiza kulimbikira mpaka mapeto, kuthamanga mokhulupirika liŵiro lokapeza nalo moyo mpaka pothera penipeni.

Mosiyana ndi zimenezi, Dina anaona zoopsa chifukwa cha chizoloŵezi choipa. Iye, ‘ankapita kukaona akazi a kumeneko,’ omwe sankalambira Yehova. (Genesis 34:1) Chizoloŵezi chomwe chinkaoneka ngati chosaopsa chimenechi chinam’gwetsa m’mavuto. Choyamba, anagwiriridwa ndi Sekemu, mnyamata yemwe anthu ankati ndi “wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wake.” Kenako, kubwezera kwa alongo ake aŵiri kunawachititsa kupha amuna onse a m’mudzi wonse. Chotsatirapo chomvetsa chisoni kwambiri!​—Genesis 34:19, 25-29.

Kodi ndi motani mmene tingakhalire otsimikiza kuti zizoloŵezi zathu sizitigwetsa m’vuto ndiponso kuti zidzatipindulitsa?

Kugwiritsa Ntchito Zizoloŵezi

“Zizoloŵezi ndi chikonzero cha Mulungu,” analemba motero wafilosofi wina. Koma siziyenera kukhala chikonzero. Baibulo limasonyeza bwinobwino kuti tingasankhe kusintha zizoloŵezi zathu zoipa ndi kukulitsa zizoloŵezi zabwino.

Pokhala ndi zizoloŵezi zabwino, moyo wachikristu umakhala waphindu ndi wosavuta kuusungabe. Alex, yemwe ndi Mkristu wa ku Greece, anati: “Chizoloŵezi chotsatira mosamala kwambiri ndandanda ya ntchito zosiyanasiyana chimandithandiza kupatula nthaŵi ya mtengo wapatali.” Theophilus, yemwe ndi mkulu wachikristu, ananena kuti chizoloŵezi cholinganiza zinthu ndicho chimam’thandiza kukhala munthu waphindu. Iye anati: “Sindikayikira m’pang’ono pomwe kuti ndikanakhala kuti ndilibe chizoloŵezi cholinganiza zinthu, sindikanatha kugwira molongosoka ntchito zanga zachikristu.”

Ifeyo, monga Akristu, tikulimbikitsidwa kuti “tipitirizebe kuyenda molongosoka ndi chizoloŵezi chomwechi.” (Afilipi 3:16, NW) “Chizoloŵezi chimaphatikizapo khalidwe lochita chinthu chimodzimodzi nthaŵi zambirimbiri.” Zizoloŵezi zabwino zoterozo zimatipindulitsa chifukwa choti sitifunikira kutenga nthaŵi yaitali tikusinkhasinkha pa chilichonse choti tichite. Zili choncho chifukwa tinakhazikitsa kale dongosolo labwino lomwe timatsatira chifukwa cha chizoloŵezi chathu. Zinthu zomwe tazizoloŵera kwambiri timangozindikira titazichita. Mofanana ndi mmene zizoloŵezi zoyendetsa bwino galimoto zingathandizire dalaivala kuganiza mwamsanga njira yopulumukira pangozi yapamsewu, momwemonso zizoloŵezi zabwino zingatithandize kusankha mofulumira zinthu zoyenera kuchita pamene tikuyenda m’njira yathu yachikristu.

Monga momwe Mngelezi wina wolemba mabuku, Jeremy Taylor, analembera: “Ntchito zimabala zizoloŵezi.” Ngati zizoloŵezi zathu zili zabwino, tingachite zinthu zabwino mosavutikira kwenikweni. Mwachitsanzo, ngati ife monga atumiki achikristu tili ndi chizoloŵezi chogwira nawo ntchito yolalikira nthaŵi zonse, n’kosavuta ndipo n’kosangalatsa kwambiri kupita mu utumiki wakumunda. Posimba za atumwi, timaŵerenga kuti ‘masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira za Kristu Yesu.’ (Machitidwe 5:42; 17:2) Mosiyana ndi zimenezi, ngati timangochita nawo ulaliki mwakamodzikamodzi, tingamade nkhaŵa, ndi kufuna nthaŵi yochuluka kuti tiyambe kumasuka mu utumiki tisanayambe kukhutira ndi ntchito yofunikayi yachikristu.

N’chimodzimodzinso ndi mbali zina za zochita zathu zachikristu. Zizoloŵezi zabwino zingatithandize kuti nthaŵi zonse ‘tiziŵerenga Mawu a Mulungu usiku ndi usana’. (Yoswa 1:8; Salmo 1:2) Mkristu wina ali ndi chizoloŵezi choŵerenga Baibulo kwa mphindi 20 mpaka 30 asanapite kokagona. Ngakhale pamene watopa kwambiri, amaona kuti ngati wapita kukagona osaŵerenga, sangathe kugona bwino. Amayenera kudzuka ndi kusamalira chosoŵa chauzimu chimenecho. Chizoloŵezi chabwino chimenechi cham’thandizanso kuŵerenga Baibulo lonse kamodzi pachaka kwa zaka zingapo.

Yesu Kristu, yemwe ndi Chitsanzo chathu, anali ndi chizoloŵezi chofika pa misonkhano pomwe anthu ankakambirana Baibulo. “Tsiku la Sabata analoŵa m’sunagoge, monga anazoloŵera, naimiriramo kuŵerenga m’kalata.” (Luka 4:16) Kwa Joe, mkulu yemwe ali ndi banja lalikulu ndipo amagwira ntchito kwa maola ambiri, chizoloŵezi chinam’thandiza kum’patsa chilakolako chofika pa misonkhano nthaŵi zonse. Iye anati: “Chizoloŵezichi chimandithandiza kupitabe patsogolo, ndi kundilimbikitsa kwambiri kuti ndithe kugwira ntchito zovuta ndiponso kupambana polimbana ndi mavuto.”​—Ahebri 10:24, 25.

Zizoloŵezi ngati zimenezi ndi zofunika kwambiri pa liŵiro lachikristu lokapeza nalo moyo. Lipoti lochokera ku dziko lina komwe anthu a Yehova akhala akuzunzidwa linati: “Anthu omwe ali ndi zizoloŵezi zabwino zauzimu ndiponso oyamikira kwambiri choonadi sakuvutika kukhala olimba mayesero akafika. Koma anthu omwe ‘m’nthaŵi yabwino’ amaphonya misonkhano, sapita kaŵirikaŵiri ku utumiki wakumunda ndiponso omwe amabwerera m’mbuyo pankhani zing’onozing’ono nthaŵi zambiri amagwa akakhala pachiyeso ‘chonga moto.’”​—2 Timoteo 4:2.

Pewani Zizoloŵezi Zoipa, Gwiritsani Ntchito Zizoloŵezi Zabwino

Anthu akhala akunena kuti ‘munthu ayenera kukulitsa zizoloŵezi zokhazo zomwe akufuna kuti zizimulamulira.’ Zizoloŵezi zoipa zimalamuliradi mopondereza. Komabe, n’zotheka kuzisiya.

Stella, kanthaŵi kena, ankakonda kuonera wailesi yakanema mopitirira muyeso. Iye anavomereza kuti: “Chizoloŵezi choipa chilichonse chomwe ndinakhalapo nacho, chinkayamba ndi chifukwa ‘chabwino.’” Mmenemu ndi mmene zinalili ndi chizoloŵezi chake choonera wailesi yakanema mopitirira muyeso. Anadziuza kuti azionera ndi cholinga choti “apumuleko pang’ono” kapena kuti “asintheko zochita.” Koma chizoloŵezi chakecho chinafika posalamulirika, n’kumam’pangitsa kuonerera wailesi yakanema kwa maola ochuluka. Iye anati, “Chizoloŵezi choipachi chinandichedwetsa kupita patsogolo mwauzimu.” Chifukwa chochita khama, kenako anachepetsa nthaŵi yoonerera wailesi yakanema ndiponso kumasankha bwino mapulogalamu. “Nthaŵi zonse ndimayesetsa kukumbukira chifukwa chake ndinkafuna kusiya chizoloŵezichi, ndipo ndimadalira Yehova kuti ndikwanitse cholinga changa,” anatero Stella.

Mkristu wina dzina lake Charalambos anatchula chizoloŵezi choipa chomwe chinam’lepheretsa kupita patsogolo mwauzimu​—chizoloŵezi chochedwetsa zinthu. “Nditazindikira kuti chizoloŵezi chochedwetsa zinthu n’choipa, ndinayamba kusintha moyo wanga. Popanga zolinga, ndinalinganiza nthaŵi yeniyeni ndiponso mmene ndidzayambire kukwaniritsa zolingazo. Mankhwala ake anali kusasinthasintha zomwe ndaganiza kapena zomwe ndalinganiza kuchita, ndipo chakhala chizoloŵezi chabwino mpaka pano.” Inde, zizoloŵezi zabwino ndizo zaloŵa mmalo zabwino kwambiri za zizoloŵezi zoipa.

Anthu omwe timacheza nawo angatipangitsenso kukhala ndi zizoloŵezi zabwino kapena zoipa. Zizoloŵezi zabwino zimafafanizika, monganso momwe zoipa zimachitira. Monga momwe ‘mayanjano oipa amaipitsira makhalidwe okoma,’ mabwenzi abwino angapereke zitsanzo za zizoloŵezi zabwino zofunika kutsanzira. (1 Akorinto 15:33) Chofunika kwambiri ndi choti, zizoloŵezi zingalimbitse kapena kufooketsa unansi wathu ndi Mulungu. Stella anati: “Ngati zizoloŵezi zili zabwino, zimapangitsa kuti kuyesetsa kwathu kutumikira Yehova kukhale kosavuta. Ngati zili zoipa, zimapinga khama lathu.”

Khazikitsani zizoloŵezi zabwino, ndipo zitsatireni. Zidzakhala mphamvu yabwino ndi yopindulitsa pa moyo wanu.

[Chithunzi patsamba 19]

Monga moto, zizoloŵezi zingapindulitse kapena kuwononga

[Chithunzi patsamba 21]

Chinali chizoloŵezi cha Yesu kukhala m’sunagoge pa tsiku la Sabata poŵerenga Mawu a Mulungu

[Zithunzi patsamba 22]

Zizoloŵezi zabwino zauzimu zimalimbitsa unansi wathu ndi Mulungu