Apambana Mlandu M’khoti Lapamwamba la Federal Constitution
Apambana Mlandu M’khoti Lapamwamba la Federal Constitution
MBONI ZA YEHOVA ku Germany zinapambana mlandu m’khoti lapamwamba la Federal Constitution ku Karlsruhe. Motero zinatenga sitepe lofunika pankhani yakuti zidziŵike monga bungwe lovomerezeka mwalamulo.
Mboni za Yehova zakhala zikulalikira ku Germany kwa zaka zoposa 100. Maulamuliro aŵiri opondereza a zaka za m’ma 1900—ulamuliro wa Hitler ndi wa Chikomyunizimu—anazunza Mboni mwakhanza, komabe izo zinapirira. Kuyambira mu 1990, Mboni zinafuna kuti zidziŵike monga bungwe lovomerezeka mwalamulo. Makhoti ang’ono aŵiri anagamula mokomera Mboni koma khoti lina lalikulu linakana pempho lawo. Motero, anachita apilo ku khoti lapamwamba la Federal Constitution, limene linalengeza chigamulo chake pa December 19, 2000.
Onse Anagamula Mokomera Mboni za Yehova
Oŵeruza onse asanu ndi aŵiri a khotilo anagamula mokomera Mboni. Oŵeruzawo anasintha zimene khoti la Federal Administrative linagamula mu 1997 ndipo analilangiza khotilo kuti lipendenso pempho la Mboni.
Khoti la Federal Constitution linapezerapo mwayi wofotokoza ubale wofunika pakati pa Boma ndi magulu azipembedzo. Kwenikweni, chipembedzo amachivomereza “chifukwa cha zochita zake osati zikhulupiriro zake.”
Khotilo linanenanso kuti Mboni zikamakana “kuloŵerera m’zandale monga Akristu, sizitsutsana ndi mfundo za demokalase” ndipo “safuna kuti akhazikitse boma la mtundu wina mmalo mwa demokalase.” Choncho, kusachita nawo zisankho za ndale kusakhale chifukwa chokanira pempho la Mboni lakuti adziŵike mwalamulo.—Yohane 18:36; Aroma 13:1.
Khotilo linapitiriza kunena kuti wokhulupirira aliyense—kaya ndi wa Mboni kapena wachipembedzo china—nthaŵi zina angapeze kuti zimene Boma lalamula zikutsutsana ndi zikhulupiriro zake. Ngati munthuyo amvera chikumbumtima chake mwa “ kutsatira zikhulupiriro zake zachipembedzo koposa lamulo,” Boma liyenera kuzindikira kuti sakulakwa ndiponso kuti sanapitirire malire a ufulu wachipembedzo.—Machitidwe 5:29.
Zimene khotilo linagamula zinamveka ponseponse. Pafupifupi nyuzipepala iliyonse ya ku Germany inalemba za chigamulochi. Mawailesi onse aakulu akanema ndi oulutsa mawu anaulutsa malipoti a nkhaniyi kapena zimene anafunsa zokhudza nkhaniyi. Dzina la Yehova linamveka ponseponse ku Germany kuposa kale lonse.
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
AP Photo/Daniel Maurer