“Kodi N’chiyani Chikuchitika M’France?”
“Kodi N’chiyani Chikuchitika M’France?”
“Ufulu, ufulu wokondedwa.” Ameneŵa ndi mawu a nyimbo ya fuko la France yakuti “La Marseillaise.” Mosakayika, ufulu ndi wofunika kuulemekeza. Komabe, zimene zachitika posachedwapa ku France zayambitsa nkhaŵa yakuti ufulu wofunika kwambiri ukuchepa. N’chifukwa chake, Lachisanu pa November 3, 2000, Mboni za Yehova zikwizikwi zinagaŵira mathirakiti okwana 12 miliyoni a uthenga wapadera wa mutu wakuti “Kodi N’chiyani Chikuchitika M’France? Kodi Ufulu Ukutha?”
ATSOGOLERI a ndale ndi magulu odana ndi zipembedzo zing’onozing’ono ku France akhala akuukira Mboni za Yehova kwa zaka zambiri tsopano. Zimenezi zachititsa kuti Mboni zivutike monga munthu payekha, mpingo, ndiponso dziko lonselo. Komabe, pa June 23, 2000, khoti lalikulu kwambiri m’France la Conseil d’État linapereka chigamulo chosaiŵalika chogwirizana ndi zigamulo za makhoti aang’ono okwana 31 pa milandu yoposa 1,100. Khoti lalikululo linagamula kuti kulambira kwa Mboni za Yehova n’kogwirizana kotheratu ndi malamulo a m’France ndi kuti ayenera kukhala ndi ufulu wosakhomera msonkho Nyumba zawo za Ufumu, ufulu umene zipembedzo zina zonse zinapatsidwa.
Komabe, mosalabadira m’pang’ono pomwe chigamulochi, Unduna wa Zachuma ku France ukuumirirabe kuti Mboni za Yehova zizikhoma msonkho pamene malamulo a dzikolo amanena kuti mabungwe a zipembedzo sayenera kutero. Undunawu wanena kuti zopereka zimene Mboni ndi anthu ena amapereka posonkhana m’mipingo yokwana 1,500 m’France azizikhomera msonkho wa 60 peresenti. Panopa nkhaniyi ili kukhoti.
Cholinga cha ndawala imene tatchula pamwambayo chinali kuvumbula nkhani imeneyi ndi kusonyeza ngozi imene ingakhalepo pa misonkho yosemphana ndi malamuloyi *
ndi malamulo amene akufuna kukhazikitsa amene angachepetse ufulu wachipembedzo wa anthu onse.Tsiku Lalitali
Patsiku la ndawalayi, Mboni za m’mipingo ina zinayamba kugaŵira thirakitilo 2 koloko m’maŵa. Anagaŵira kunja kwa masiteshoni a sitima ndi m’mafakitale ndipo kenako anakagaŵira kumabwalo a ndege. Pa 6 koloko anthu ku Paris amakhala ali pikitipikiti. Mboni zodzipereka pafupifupi 6,000 anazigaŵira malo abwino omwe zikanatha kukumana ndi anthu opita ku ntchito. Mtsikana wina anati: “Zimene mukuchita kuti pakhale ufulu wachipembedzo n’zabwino. Enanso nkhani imeneyi ikuwakhudza osati Mboni za Yehova zokha.” Ku Marseilles, Mboni zoposa 350 zinagaŵira thirakitili m’masiteshoni a njanji yapansi pa nthaka ndi m’misewu. M’kati mwa ola limodzi lokha, wailesi ya dzikolo inalengeza za ndawalayi ndi kuwauza omvetsera ake kuti asadabwe Mboni za Yehova zikawafikira. Ku Strasbourg, komwe kuli likulu la khoti la European Court of Human Rights, apaulendo amene anali pa siteshoni ina yaikulu anaima pamzere moleza mtima kuti alandire thirakitili. Loya wina ananena kuti ngakhale kuti iye si Mboni, anali kuitsatira nkhaniyi mwachidwi chifukwa zimene Mboni zinali kuchita n’zofunika ndiponso zachilungamo.
Pa 8 koloko, ngakhale kuti kunali mvula yambiri, Mboni zokwana 507 zinafufuza anthu mu mzinda wa kumapiri wa Grenoble kapena kusiya mathirakiti m’mabokosi a makalata. Oyendetsa galimoto ndi sitima zazing’ono ataona kuti chinachake chikuchitika, anaima ndi kupempha thirakiti. Mu mzinda wa kumadzulo wa Poitiers, apaulendo amene anafika pasitima pa 9 koloko anali atalandira kale thirakiti pokwera sitimayo. Ku Mulhouse, pafupi ndi malire ndi dziko la Germany, mathirakiti 40,000 anali atagaŵidwa kale.
Pofika 10 koloko, mipingo yambiri inali itagaŵira mathirakiti oposa theka la mathirakiti awo. Pofika masana, anthu amene ankakana kulandira mathirakiti anali ochepa chabe ndipo panali kukambirana kochititsa chidwi ndi anthu ambiri. Ku Besançon, komwe ndi pamtunda wa makilomita oposa 80 okha kuchokera ku malire ndi Switzerland, mnyamata wina anachita chidwi ndi nkhani za Baibulo ndipo anafunsa chifukwa chake Mulungu walola kuvutika. Mboni inam’pempha kukapitiriza kukambiranako pa Nyumba ya Ufumu imene inali pafupi. Nthaŵi yomweyo anayamba kuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
Masana, Mboni zambiri zinagwiritsa ntchito nthaŵi yawo yopuma kulalikira kwa ola limodzi kapena aŵiri. Madzulo onse, anapitiriza kugaŵira mathirakiti, ndipo mipingo yambiri inamaliza pa 3 koloko kapena pa 4 koloko madzulowo. Mumzinda wa Reims anthu ena amene anali kuphunzira kapena kusonkhana ndi Mboni za Yehova m’mbuyomo ananena kuti akufuna kugwirizananso ndi mpingo. Ku Bordeaux, maphunziro a Baibulo atatu apanyumba anayambika. Mu mzinda womwewo, Mboni ina italoŵa m’sitolo kuti igule nyuzipepala, inapeza mulu wa mathirakiti pakauntala. Mwini wa sitoloyo, yemwe anali Mboni kale, analandira thirakitilo ndipo ataona kufunika kwake, anachita fotokope m’kumagaŵira anthu.
Ku Le Havre ku Normandy, mkazi wina wachipulotesitanti atamva pawailesi kuti Mboni za Yehova akuzikhometsa msonkho pa zopereka zawo
anakhudzidwa mtima kwambiri. Analandira thirakiti ndi mtima wonse ndipo anayamikira Mboni chifukwa chotsutsa kupanda chilungamo kumeneku molimba mtima. Pa nthaŵi ya 7:20 madzulo, wailesi yakanema ya chigawo cha Lyons inachitira ndemanga za kugaŵira thirakitili. Inati: “Mmaŵawu kunali kosavuta kupewa madontho a mvula kusiyana ndi kupeŵa kulandira mathirakiti a Mboni za Yehova.” Atolankhani anafunsa Mboni ziŵiri ndipo zinafotokoza chifukwa chake anachita ndawala imeneyi.Mboni zina pofuna kuti zichite nawo ndawalayi zitaŵeruka kuntchito, zinagaŵira anthu oweruka kuntchito ndi kuika mathirakiti ena m’mabokosi a makalata. M’matawuni ena monga Brest ndi Limoges—otchuka chifukwa cha dongo lapadera lopangira zoumbaumba—anthu ochokera ku mafilimu 11 koloko usiku, anali ena mwa anthu omaliza kulandira thirakiti tsiku limenelo. Mathirakiti otsala anawasonkhanitsa ndi kuwagaŵa m’maŵa tsiku lotsatira.
Zotsatira Zake
Mboni ina inalemba kuti: “Anthu amene amatida akuganiza kuti akutifooketsa. Komatu, akutilimbikitsa.” M’mipingo yambiri, Mboni 75 mwa Mboni 100 zilizonse zinagaŵira nawo thirakitili tsiku limenelo ndipo ena anagaŵira kwa maola 10, 12, kapena 14. Ku Hem, kumpoto kwa France, Mboni ina itagwira ntchito usiku, inagaŵira mathirakiti kuyambira 5 koloko m’maŵa mpaka 3 koloko madzulo. Mumzinda wapafupi wa Denain, kumene kwakhala mpingo kuyambira mu 1906, Lachisanu Mboni 75 zinagaŵira mathirakiti kwa maola 200. Ena anagaŵiranso mathirakitiŵa mofunitsitsa ngakhale kuti anali okalamba, ena sanali kupeza bwino m’thupi, ndiponso nyengo sinali bwino. Mwachitsanzo, ku Le Mans, alongo atatu a zaka za m’ma 80 anaika mathirakiti m’mabokosi a makalata kwa maola aŵiri ndipo mbale wina anagaŵira mathirakiti pa siteshoni ya njanji ali pa njinga ya olemala. Ndipo zinalitu zolimbikitsa kwambiri kuona kuti Mboni zambiri zimene zinali zofooka zinachita nawo ntchito yapaderayi!
Mosakayika konse, kugaŵira thirakitili kunapereka umboni waukulu. Anthu alionse, omwe ambiri a iwo sapezedwa m’nyumba zawo kaŵirikaŵiri, analandira thirakitili. Anthu ambiri anaona kuti ntchito imeneyi inachita zazikulu kuposa kuteteza ufulu wa Mboni. Ochuluka anaona kuti ndawalayi inateteza ufulu wa chikumbumtima ndi wa chipembedzo wa anthu onse a ku France. Umboni wa zimenezi unaoneka pamene anthu ambiri anapempha mathirakiti ena kuti akapatse mabwenzi awo, ogwira nawo ntchito, kapena achibale awo.
Inde, Mboni za Yehova ku France n’zonyadira kuti zadziŵikitsa dzina la Yehova ndi kuteteza zinthu za Ufumu. (1 Petro 3:15) Akuyembekeza ndi mtima wonse ‘kuti m’moyo mwawo akhale odekha mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekeza monse’ ndi kutinso anthu ena zikwizikwi adzawatsanzira kutamanda Atate wawo wa kumwamba, Yehova.—1 Timoteo 2:2.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Ndawala yofanana ndi imeneyi inachitika mu January 1999 imene inatsutsa kupondereza zipembedzo. Onani Nsanja ya Olonda ya August 1, 1999, tsamba 9, ndi buku lakuti 2000 Yearbook of Jehovah’s Witnesses masamba 24-6.