Yamikirani Ndipo Sangalalani
Yamikirani Ndipo Sangalalani
“MTIMA wofuna kuyamikira n’chibadwa cha anthu onse,” inatero nyuzipepala ya ku Canada yakuti Calgary Herald. Nyuzipepalayo inagwira mawu a ophunzira ena a pasukulu ya pulayimale a zaka zisanu ndi zinayi amene aphunzitsi awo anawauza kuti alembe zinthu zonse zomwe iwowo amayamikira. Mnyamata wina ananena kuti amayamikira banja lawo ‘chifukwa chakuti lakhala likumusamala.’ Mtsikana wina nayenso anati amayamikira banja lawo. Ananena kuti: “Makolo anga amandisunga bwino, ndine wathanzi, amandisamalira, amandikonda, amandipatsa chakudya, ndipo popanda makolo anga sindikanakhala ndi moyo.”
Kusayamikira kumachititsa kusakhutira. Malinga ndi zomwe ananena wafilosofi yemwenso ndi wamaphunziro apamwamba a zaumulungu wotchedwa James I. Packer, “anthufe tinalengedwa kuti tikhale ndi moyo modalira Mulungu ndi anthu anzathu.” Zimenezi zimatikumbutsa uphungu wanzeru wa m’Baibulo womwe unaperekedwa zaka mazana ambiri m’mbuyomu kuti: “Khalani akuyamika.” (Akolose 3:15) Mawu othokoza ndiponso oyamikira ena kuchokera pansi pa mtima amathandiza kukulitsa ubale wothandizana.
Kuwonjezera apo, tikamayamikira ndiponso kuona anzathu kukhala ofunika timasonyezanso kuyamikira Yehova, ndipo iye amaona zimenezi. Baibulo limati: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” (2 Mbiri 16:9) Mulungu akutitsimikizira kuti amakumbukira ndiponso kuyamikira chikondi chomwe anthu amasonyeza ku dzina lake. (Ahebri 6:10) Inde, m’pake kuti tiziyamikira chifukwa chakuti khalidwe laumulungu limeneli tikamalisonyeza tsiku ndi tsiku limasangalatsa Yehova ndipo limawonjezera chimwemwe chathu. Zili monga momwe Miyambo 15:13 amanenera kuti: “Mtima wokondwa usekeretsa nkhope.”