Chikhulupiriro cha Nowa Chimatsutsa Dziko Lapansi
Chikhulupiriro cha Nowa Chimatsutsa Dziko Lapansi
KODI munamvapo za Nowa munthu woopa Mulungu amene anakhoma chingalawa kuti apulumuke chigumula cha dziko lonse? Anthu miyandamiyanda amaidziŵa bwino nkhaniyi ngakhale kuti n’njakalekale. Komabe, chimene anthu ambiri sadziŵa n’chakuti moyo wa Nowa uli ndi phindu kwa ife tonse lerolino.
Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala n’chidwi ndi nkhani yakalekale imeneyi? Kodi pali kufanana kulikonse pakati pa zochitika m’nthaŵi ya Nowa ndi m’nthaŵi yathu ino? Ngati kulipo, kodi tingapindule motani ndi chitsanzo chake?
Zochitika M’nthaŵi ya Nowa
Baibulo limasonyeza kuti Nowa anabadwa mu 2970 B.C.E.—zaka 126 Adamu atamwalira. Pomwe imafika nthaŵi yomwe Nowa anakhala ndi moyo, n’kuti padziko lapansi pali chiwawa chadzaoneni. Mbadwa zambiri za Adamu zinasankha kutsatira kupulupudza kwa kholo lawolo. Chotero ‘Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.’—Genesis 6:5, 11, 12.
Yehova anakwiya chifukwa cha zinthu zinanso osati kupanduka kwa anthu kokha. Nkhani ya mu Genesis imafotokoza kuti: “Ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha. . . . Pa dziko lapansi panali anthu akuluakulu [Anefili] masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu ataloŵa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.” (Genesis 6:2-4) Kuyerekezera mavesi ameneŵa ndi mawu omwe mtumwi Petro analemba, kumasonyeza kuti “ana aamuna a Mulungu” ameneŵa anali angelo osamvera. Anefili anali ana amene akazi anabala atagonana moswa malamulo ndi angelo omwe anavala matupi aumunthu.—1 Petro 3:19, 20.
Mawu akuti “Anefili” kutanthauza “Akugwa,” amanena za anthu ogwetsa anzawo. Iwo anali zimphona zomenya anthu. Palinso kugwirizana pakati pa tchimo la atate awo achiwerewerewo ndi khalidwe lonyansa la mu Sodomu ndi Gomora. (Yuda 6, 7) Onse pamodzi analimbikitsa kuipa padziko lapansi.
“Wangwiro M’mibadwo Yake”
Mulungu anatsimikiza kuwononga anthu chifukwa chakuti kuipa kunali kutafala kwambiri. Koma nkhani youziridwa imanena kuti: “Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova. . . . Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.” (Genesis 6:8, 9) Kodi zinatheka bwanji kuyenda ndi Mulungu m’dziko losapembedza longoyenera kuwonongedwalo?
Mosakayikira Nowa anaphunzira zambiri kuchokera kwa Lameke bambo ake. Lameke anali munthu wachikhulupiriro ndiponso anabadwa ndi kukula Adamu ali moyo. Lameke popatsa dzina mwana wake Nowa (mwina kutanthauza kuti “Mpumulo,” kapena “chitonthozo”), analosera kuti: “Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pa ntchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova.” Mulungu anakwaniritsa ulosi umenewo pamene anachotsa temberero lake pa nthaka.—Genesis 5:29; 8:21.
Kukhala ndi makolo oopa Mulungu sizitanthauza kuti ana adzakhalanso oopa Mulungu. Aliyense ayenera kumanga ubale wakewake ndi Yehova. Nowa ‘anayenda ndi Mulungu’ mwa kutsatira njira yomwe Mulungu anaivomereza. Zomwe Nowa anaphunzira zokhudza Mulungu zinamulimbikitsa kumutumikira Iye. Chikhulupiriro cha Nowa sichinazirale Mulungu atamuuza cholinga chake ‘chowononga anthu onse ndi chigumula.’—Genesis 6:13, 17.
Nowa anakhulupirira kuti chigumulacho chomwe chinali chisanachitikepo chidzachitikadi ndipo anamvera lamulo la Yehova lakuti: “Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale; upangemo zipinda m’chingalawamo, ndipo upake ndi utoto m’kati ndi kunja.” (Genesis 6:14) Kupanga chingalawa ndendende monga momwe Mulungu ananenera sinali ntchito yamaseŵera. Komabe, ‘Nowa anachita monga mwa zonse Mulungu anam’lamulira iye, momwemo anachita.’ (Genesis 6:22) Ana aamuna a Nowa omwe ndi Semu, Hamu, ndi Yafeti pamodzi ndi akazi awo, anathandizana kugwira ntchitoyo. Yehova anadalitsa chikhulupiriro choterechi. Chimenechi n’chitsanzotu chabwino kwambiri kwa mabanja lerolino!
Kodi kumanga chingalawa inali ntchito yaikulu motani? Yehova analamulira Nowa kuti akhome chibokosi chachikulu chamatabwa cha nsanjika zitatu ndiponso chosaloŵa madzi. M’litali mwake chinali mamita 133, m’lifupi mamita 22, ndipo msinkhu wake unali mamita 13. (Genesis 6:15, 16) Chingalawa ngati chimenechi chikanatha kunyamula katundu wochuluka ngati amene sitima zikuluzikulu zonyamula katundu za masiku ano zimanyamula.
Inalitu ntchito yofunika chamuna! Mwachionekere inali ntchito yofuna kudula mitengo yambirimbiri, kuinyamula kupita nayo ku malo opangira chingalawacho, ndiponso kuicheka kukhala matabwa kapena milimo. Panafunikanso kupanga makwerero aatali, kusongola zisonga zolumikizira matabwa, kupeza phula lomatira kuti madzi asamaloŵe, ndiponso kupeza zipangizo zosiyanasiyana ndi zina zambiri. Ntchitoyo iyenera kuti inaphatikizaponso kukambirana ndi anthu amalonda ndi kulipira katundu ndi ntchito yomwe anagwira. Panafunikanso akalipentala a luso kuti athe kulumikiza bwino matabwa ndi kupanga chingalawa cholimba. Tangoganizani,
ntchitoyo inatengatu pafupifupi zaka 50 kapena 60!Kenako Nowa anayenera kupeza chakudya chokwanira cha banja lake ndiponso cha nyama. (Genesis 6:21) Anayenera kusonkhanitsa khwimbi la nyama ndi kuziloŵetsa m’chingalawa. Nowa anachita zonse zomwe Mulungu anam’lamulira ndipo ntchito yonse inatha. (Genesis 6:22) Madalitso a Yehova anachititsa kuti ntchitoyo ithe bwinobwino.
“Mlaliki wa Chilungamo”
Kuwonjezera pa kukhoma chingalawa, Nowa anachenjeza ndi kutumikira Mulungu mokhulupirika monga “mlaliki wa chilungamo.” Koma anthu “sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.”—2 Petro 2:5; Mateyu 24:38, 39.
Kungolingalira mmene mikhalidwe yoipa yauzimu ndi yamakhalidwe inalili panthaŵiyo, titha kuona mmene anthu osamverawo ankasekera ndiponso kuchitira chipongwe banja la Nowa. Anthuwo ayenera kuti ankaganiza kuti banja la Nowa lapenga. Komabe Nowa analimbikitsa banja lake mwauzimu moti silinatengere chiwawa, chiwerewere, ndi kupanduka kwa anthu osapembedzawo. Chotero Nowa anatsutsa dziko lapansi la m’nthaŵiyo mwa zimene ankalankhula ndiponso zochita zake zomwe zinasonyeza chikhulupiriro chake.—Ahebri 11:7.
Anapulumuka Chigumula
Mulungu anauza Nowa kuti aloŵe m’chingalawa mvula itatsala pang’ono kuyamba. “Yehova anatseka chitseko” banja la Nowa ndi nyama zitaloŵa kuti aliyense mwa onyoza aja asaloŵe. Chigumula chitafika angelo osamvera aja anavula matupi awo aumunthu ndi kuthaŵa chigumulacho. Koma bwanji nanga za anthu ena? Zamoyo zonse zomwe zinali kunja kwa chingalawa ndiponso Anefili aja, zinatha psiti! Nowa yekha ndi banja lake ndiwo anapulumuka.—Genesis 7:1-23.
Nowa ndi banja lake anakhala m’chingalawa chaka chathunthu ndi masiku khumi. Iwo anali ndi ntchito yodyetsa ndi kumwetsa nyama, kuchotsa ndowe, ndiponso kusunga nthaŵi. Buku la Genesis limatchula molondola nthaŵi ya mbali iliyonse ya Chigumula ngati chikalata cholongosola kayendedwe ka sitima yapamadzi. Zimenezi zimasonyeza kuti nkhaniyi ndi yoona.—Genesis 7:11, 17, 24; 8:3-14.
Mosakayikira Nowa adakali m’chingalawacho anatsogolera banja lake pokambirana nkhani zauzimu
ndiponso kuthokoza Mulungu. Mwachionekere zomwe zinachitika Chigumula chisanafike zinasungidwa kudzera mwa Nowa ndi banja lake. Nkhani zodalirika zachikhalidwe zomwe iwo ankasimba kapena mabuku ena a mbiri yakale omwe anali nawo zinali zopindulitsa kwambiri kuziphunzira pa nthaŵi ya Chigumula.Zinalitu zosangalatsa kwambiri kwa Nowa ndi banja lake kutuluka m’chingalawa ndi kupondanso pa nthaka youma! Chinthu choyamba chomwe Nowa anachita atatuluka chinali kumanga guwa la nsembe ndi kuimira banja lake monga wansembe, kupereka nsembe kwa Amene anawapulumutsa.—Genesis 8:18-20.
“Monga Masiku a Nowa”
Yesu Kristu anati: “Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:37) Akristunso lerolino ndi alaliki achilungamo. Iwo akulimbikitsa anthu kuti alape. (2 Petro 3:5-9) Popeza Yesu anafanizira kufika kwake ndi masiku a Nowa, mwina tingadzifunse kuti, kodi Nowa ankaganizanji Chigumula chisanafike? Kodi nthaŵi ina sanaganizepo kuti ntchito yake yolalikira ilibe phindu? Kodi anali kutopa nthaŵi zina? Baibulo silinenapo kanthu pa nkhaniyi. Limangotiuza kuti Nowa anamvera Mulungu.
Kodi mukuona kufanana kwa zochitika za m’nthaŵi ya Nowa ndi m’nthaŵi yathu? Nowa anamvera Yehova ngakhale kuti anthu anali kum’tsutsa ndiponso kuvutika. N’chifukwa chake Yehova anati Nowa anali wolungama. Banja la Nowa silinadziŵe nthaŵi yeniyeni yomwe Mulungu anali kudzabweretsa Chigumula koma iwo ankadziŵa kuti chidzabwera ndithu. Kukhulupirira mawu a Mulungu kunathandiza Nowa kulimbikirabe m’zaka zonse zomwe anagwira ntchito yokhoma chingalawa ndiponso yolalikira yomwe mwina inkaoneka ngati yopanda phindu. Inde, timauzidwa kuti: “Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.”—Ahebri 11:7.
Kodi Nowa anachipeza bwanji chikhulupiriro choterocho? Mwachionekere iye anali kupeza nthaŵi yosinkhasinkha zinthu zonse zomwe ankadziŵa zokhudza Yehova ndipo analola kuti zimenezo zimutsogolere pa moyo wake. Mosakayikira Nowa anali kulankhula kwa Mulungu m’pemphero. Ndipotu anamudziŵa kwambiri Yehova mpaka “anayenda ndi Mulungu.” Nowa mokondwera anapatula nthaŵi yocheza ndi kusamalira banja lake mwachikondi monga mutu wa banja. Zimenezi zinaphatikizapo kusamalira zinthu zauzimu za mkazi wake, ana ake aamuna atatu, ndiponso apongozi ake.
Mofanana ndi Nowa, Akristunso oona lerolino amadziŵa kuti posachedwapa Yehova adzathetsa dongosolo losapembedza lomwe lilipoli. Sitikudziŵa tsikulo kapena nthaŵi koma timadziŵa kuti kutsatira chikhulupiriro ndi kumvera za “mlaliki wachilungamo” kudzatibweretsera “chipulumutso cha moyo.”—Ahebri 10:36-39.
[Bokosi patsamba 29]
Kodi Zinachitikadi?
Akatswiri a zachikhalidwe cha anthu asonkhanitsa nthano zokhudza chigumula zokwana 270. Nthanozo azipeza pafupifupi m’mitundu ndi m’mayiko onse. Katswiri wina dzina lake Claus Westermann anati: “Nkhani ya chigumula amaidziŵa padziko lonse. Nkhaniyi yangokhala mbali ya chikhalidwe chathu monga mmene ilili nkhani yonena za kulengedwa kwa zinthu. N’zodabwitsadi kwambiri kuti kulikonse padziko lapansi timapeza nkhani yosimba za chigumula chakalekale chimenechi.” Kodi n’chifukwa chiyani? Katswiri wothirira ndemanga wina dzina lake Enrico Galbiati anati: “N’chifukwa chakuti kupezeka kwa nkhani yakalekaleyi m’chikhalidwe cha anthu osiyanasiyana ndi umboni wakuti inachitikadi.” Komabe, chofunika kwambiri kwa Akristu kuposa zomwe amaphunziro apamwamba anena n’chakuti, iwo amadziŵa kuti ngakhale Yesu weniweniyo anavomereza kuti Chigumula chinachitikadi.—Luka 17:26, 27.
[Bokosi patsamba 30]
Kodi Anefili Analipodi?
Nkhani zosimba kugonana kosaloleka kwa milungu ndi anthu ndiponso za “zimphona” zomwe zinabadwa chifukwa cha kugonana kumeneku zinali zodziŵika bwino m’maphunziro apamwamba a zaumulungu a Agiriki, Aigupto, Augariti, Ahuriya ndi Amesopotamiya. Milungu ya m’nthanthi za Agiriki inali ngati anthu ndiponso yokongola kwambiri. Iyo inali kudya, kumwa, kugona, kugonana, kukangana, kumenyana, kusocheretsa ndiponso kugwirira chigololo. Inali yachinyengo ndiponso yambanda ngakhale kuti ankanena kuti inali yoyera. Zimphona monga Achilles, ankazinena kuti zinali mbadwa za milungu ndi anthu ndipo kuti zinali kuchita zinthu zoposa mphamvu yaumunthu. Komabe zimphonazo zinali kufa. Choncho, zomwe Genesis amanena zokhudza Anefili zimatitsegula maso kuti mwina nthanthi zoterezi zinayamba chifukwa cha zimenezi.