Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumatani Pakachitika Chinyengo?

Kodi Mumatani Pakachitika Chinyengo?

Kodi Mumatani Pakachitika Chinyengo?

YUDASI ISIKARIOTE m’munda wa Getsemane, anadza kwa Yesu “nampsompsonetsa.” Umenewu unali mwambo wosonyeza chikondi. Koma kumpsompsona kwa Yudasi kunali konyenga, kofuna kuti amudziŵikitse Yesu kwa anthu amene anafika usikuwo kuti adzamugwire. (Mateyu 26:48, 49) Yudasi anali wachinyengo​—munthu amene amadzionetsera ngati wabwino pomwe sali wotero. Munthu wachinyengo amabisa zolinga zake zoipa mwa kusonyeza kuona mtima kongovala ngati chinyawu. Liwu la Chigiriki limene analitembenuza kuti “wonyenga” limatanthauza kuti “munthu amene amayankha” ndipo limatanthauzanso munthu amene amachita zisudzo. M’kupita kwa nthaŵi, anthu anayamba kuligwiritsa ntchito liwuli kutanthauza munthu amene amachita zinthu n’cholinga choti anyenge ena.

Kodi mumatani pakachitika chinyengo? Mwachitsanzo, kodi mumakwiya mukaona opanga ndudu za fodya akulimbikitsa anthu kuti azisuta ngakhale a zamankhwala apeza kuti kusuta fodya kumawononga moyo? Kodi mumaipidwa ndi chinyengo cha osamalira anthu amene amazunza anthu amene apatsidwa kuti awasamalire? Kodi zimakupwetekani kwambiri mukaona kuti mnzanu amene munali kumudalira ndi wosakhulupirika? Kodi chinyengo cha chipembedzo chimakukhudzani motani?

“Tsoka inu . . . Onyenga!”

Taganizani mmene anthu a chipembedzo ankachitira panthaŵi imene Yesu anali padziko lapansi. Alembi ndi Afarisi anali kudzionetsera ngati aphunzitsi okhulupirika a Chilamulo cha Mulungu. Koma kunena zoona, anali kuphunzitsa ziphunzitso za anthu zimene zinachititsa anthu kusasamala za Mulungu. Alembi ndi Afarisi anali kuumirira kwambiri mbali iliyonse ya chilamulo, koma ankanyalanyaza mfundo zachikhalidwe zofunika kwambiri zimene zinasonyeza chikondi ndi chifundo. Pagulu ankadzionetsera ngati anthu odzipereka kwa Mulungu, koma kumbali anali anthu oipa zedi. Zimene ankachita zinali zosiyana kwambiri ndi zimene anali kunena. Amachita zinthu ndi cholinga choti “aonekere kwa anthu.” Anali kufanana ndi “manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m’katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.” Yesu povumbula chinyengo chawo molimba mtima anawauza mobwerezabwereza kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga!”​—Mateyu 23:5, 13-31.

Mukanakhala kuti munalipo nthaŵi imeneyo, mwina mukanaipidwa ndi anthu achipembedzo onyenga amenewo monga mmene akanachitira munthu wina aliyense woona mtima. (Aroma 2:21-24; 2 Petro 2:1-3) Koma kodi mukanalola chinyengo cha alembi ndi Afarisi amenewo kukuchititsani kuipidwa mpaka poti n’kukana chipembedzo china chilichonse, kuphatikizapo chimene Yesu Kristu ndi ophunzira ake anali kuphunzitsa ndi kutsatira? Kodi zimenezo sizikanakuchititsani kutaya mwayi?

Khalidwe lachinyengo la anthu a zipembedzo lingatichititse kuipidwa ndi zipembedzo. Komabe, kuchita zimenezi kungatilepheretse kuzindikira kuona mtima kwa olambira oona. Ndipotu, zimene tingachite kuti tidziteteze ku chinyengo, zingatichititse kuti tisakhale ndi mabwenzi enieni. Motero, m’pofunika kuchita mwanzeru ndiponso mosamala tikaona kuti pachitika chinyengo.

“Yang’anirani”

Choyamba, tifunika kuphunzira kuzindikira chinyengo. Nthaŵi zina zimenezi n’zovuta. Banja lina linaphunzira zimenezi litavutika kwambiri. Mayi wa m’banjamo anakomoka. Posumira mlandu chipatala chimene kunachitikira zimenezi chifukwa choti ogwira ntchito pa chipatalacho sanatsatire malamulo a ntchito yawo, banjalo linapeza loya amene analinso wolalikira m’tchalitchi cha komweko. Ngakhale kuti chipatalacho chinapereka ndalama zokwana madola 3.4 miliyoni pothetsa nkhaniyo, tsoka la banjalo linawonjezeka. Mayiyo anamwalira ali waumphaŵi ndipo panalibe ndalama zoti alipirire mwambo wake wa maliro. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti loya wawoyo anaba ndalama zambiri zimene chipatalacho chinapereka. Posimba za loya ameneyu, magazini ina ya zamalamulo inati: “Ngati anali kulalikira khalidwe limene ankachita . . . , uthenga wake uyenera kuti unali woti: tiyeni tiwadyere anthu masuku pamutu.” Kodi tingadziteteze bwanji kwa anthu ngati ameneŵa?

Yesu anawalangiza anthu a m’nthaŵi yake amene anakumana ndi chinyengo chachipembedzo kuti: “Yang’anirani.” (Mateyu 16:6; Luka 12:1) Inde, tisamale. Anthu angaoneke ngati ali ndi zolinga zabwino ndi kusonyeza kuona mtima ndithu, koma tifunika kusamala ndipo sitifunika kuvomereza mwamsanga chilichonse chimene munthu anganene chabe chifukwa chakuti akuoneka ngati woona mtima. Kodi sitingayang’anitsitse ndalama yathu ya pepala kuiona ngati ilidi yeniyeni ngati titamva kuti anthu ena akugwiritsa ntchito ndalama yachinyengo?

Anthu a chinyengo amapezekanso ngakhale mumpingo wachikristu choona. Wophunzira Yuda anachenjeza za anthu achinyengo otero kuti: “Iwo ndiwo okhala mawanga [“ali ngati mwala pansi pa madzi,” NW] pa mapwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziŵeta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso.”​—Yuda 12.

‘Kuyang’anira’ kukutanthauza kupeŵa kunyengedwa ndi munthu amene amadzionetsera ngati amakonda anthu ena pomwe ndi wodzikonda ndipo ali ndi maganizo amene sali ozikidwa pa Mawu a Mulungu. Munthu woteroyo ali ngati mwala wakuthwa pansi pa nyanja ya bata yemwe angachititse anthu amene sadziŵa zambiri kusweka mwauzimu monga chimachitira chombo. (1 Timoteo 1:19) Munthu wachinyengo angaoneke ngati akufuna kutsitsimula mwauzimu koma m’malo mwake amapezeka kuti ndi ‘mtambo wopanda madzi, wosabweretsa konse mvula. Monga mtengo wopanda chipatso, munthu wachinyengo alibe zipatso zenizeni zachikristu. (Mateyu 7:15-20; Agalatiya 5:19-21) Inde, tifunika kukhala tcheru kuti tipeŵe anthu onyenga ngati amenewo. Komabe, tichite zimenezo popanda kukayikira zolinga za munthu aliyense.

“Musaweruze”

N’zosavuta kwa anthu opanda ungwiro kuona zolakwa za anthu ena koma n’kumanyalanyaza zolakwa zawo. Komabe, khalidwe limeneli limachititsa kuti tinyengedwe mosavuta. Yesu anati: “Wonyenga iwe! tayamba kuchotsa m’diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m’diso la mbale wako.” Tiyenera kutsatira langizo ili: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa . . . Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda uli m’diso la iwe mwini suuganizira?”​—Mateyu 7:1-5.

Nthaŵi zina ena akaoneka ngati achita chinyengo, tiyenera kusamala kuti tisafulumire kuwanena kuti ndi achinyengo. Mwachitsanzo, mtumwi Petro “anadzibweza, ndi kudzipatula yekha” kwa Akristu anzake omwe sanali Ayuda ku Antiokeya kuti asangalatse alendo a Chiyuda amene anachokera ku Yerusalemu. Barnaba ‘nayeso anatengedwa ndi kugwidwa m’maso pamodzi ndi Petro ndi anthu ena.’ Petro anachita zimenezi ngakhale kuti iye ndi amene anapatsidwa udindo wapadera wotsegulira anthu Akunja njira yakuti mpingo wachikristu uwalandire. (Agalatiya 2:11-14; Machitidwe 10:24-28, 34, 35) Koma kufooka kumeneku kwa Barnaba ndi Petro sikunawaike m’gulu la anthu achinyengo onga alembi ndi Afarisi kapena Yudasi Isikariote.

“Chikondano chikhale chopanda chinyengo”

Yesu analangiza kuti: “Pochitira anthu ena zabwino, musamaimbe lipenga​—monga mmene amachitira ochita zisudzo m’masunagoge ndi m’misewu amene amafuna kuti anthu awatame.” (Mateyu 6:2, Phillips) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikondano chikhale chopanda chinyengo.” (Aroma 12:9) Iye analimbikitsa Timoteo wachinyamata kuti akhale ndi “chikondi chochokera mu mtima woyera . . . ndi chikhulupiriro chosanyenga.” (1 Timoteo 1:5) Anthu adzatikhulupirira ngati chikondi chathu ndi chikhulupiriro chathu n’zenizeni​—zosasakanikirana ndi kudzikonda ndi chinyengo. Tidzawalimbikitsadi anthu amene ali pafupi nafe. (Afilipi 2:4; 1 Yohane 3:17, 18; 4:20, 21) Ndipo koposa zonse, Yehova adzatiyanja.

Koma amene akuchita chinyengo adzafa. M’kupita kwa nthaŵi, munthu amene akuchita chinyengo adzaonekera poyera. Yesu Kristu anati: “Palibe kanthu kanavundikiridwa, kamene sikadzaululidwa; kapena kanthu kobisika, kamene sikadzadziŵika.” (Mateyu 10:26; Luka 12:2) Mfumu ya nzeru Solomo inati: “Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.”​—Mlaliki 12:14.

Padakali pano, tingalolelenji chinyengo cha anthu ena kutisokoneza mpaka kufika posoŵa chikondi chenicheni cha mabwenzi oona? N’zotheka kukhala ochenjera koma popanda kukayikira mopambanitsa. Ndipotu tiyeni tiyesetse kuti chikondi chathu ndi chikhulupiriro chathu zisakhale zachinyengo.​—Yakobo 3:17; 1 Petro 1:22.

[Zithunzi pamasamba 22, 23]

Kodi mukanalola chinyengo cha alembi ndi Afarisi kukuchititsani kuti musatsatire Yesu Kristu ndi ophunzira ake?