Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tidzaonana mu Ufumu wa Mulungu”

“Tidzaonana mu Ufumu wa Mulungu”

“Tidzaonana mu Ufumu wa Mulungu”

“Mnzanga Wokondedwa Rupert, ndiphedwa lero. Usandilire. Landira moni wanga ndipo ndikuperekanso moni kwa anthu onse kumudziko. Tidzaonana mu Ufumu wa Mulungu.”

FRANC DROZG analemba mawu ameneŵa asilikali a Nazi atangotsala pang’ono kumuwombera pa June 8, 1942. Kodi anamupha chifukwa chiyani?

Malinga ndi nkhani imene ili m’nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi ya Museum of National Liberation ku Maribor, Slovenia, wosula zitsulo ameneyu yemwe anali ndi zaka 38 anakana kuloŵa m’gulu la asilikali a ku Germany amene anawatumiza ku Slovenia, dziko limene Germany inalanda. Iye anali Bibelforscher kapena kuti Wophunzira Baibulo, dzina lomwe Mboni za Yehova zinkadziŵikira nalo m’deralo panthaŵiyo. Potsatira zimene zili pa Yesaya 2:4, iye sanathandize a Nazi pa nkhondo yawo, ndipo anawauza kuti iye anali nzika ya Ufumu wa Mulungu.​—Mateyu 6:33.

Franc anali kulengeza mokangalika uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’tauni ya kwawo ya Ptuj. (Mateyu 24:14) Ngakhale anakumana ndi mavuto ambiri, analalikira uthenga wabwino mosabwerera m’mbuyo mpaka pamene anam’manga mu May 1942.

A Nazi anazunza kwambiri Mboni za Yehova zambiri za ku Slovenia. Franc anali mmodzi mwa anthu oyamba kuphedwa kumeneko chifukwa cha chikhulupiriro chake chachipembedzo. Mofanana ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba, analimbikitsidwa ndi mawu akuti: “Tiyenera kuloŵa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.” (Machitidwe 14:22) Kukhulupirira kwake kuti boma lakumwamba limenelo ndi lenilenidi kunaonekera m’mawu ake omaliza akuti: “Tidzaonana mu Ufumu wa Mulungu.”

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Franc Drozg: Chithunzi cha Photo Archive-Museum of National Liberation Maribor, Slovenia; kalata: Yoyambirira anaisunga m’nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi ya Museum of National Liberation Maribor, Slovenia