Yehova Amatidziŵitsa Kuŵerenga Masiku Athu
Yehova Amatidziŵitsa Kuŵerenga Masiku Athu
“Mutidziŵitse kuŵerenga masiku athu motero, kuti tikhale nawo mtima wanzeru.”—SALMO 90:12.
1. N’chifukwa chiyani n’koyenera kupempha Yehova kuti atidziŵitse “kuŵerenga masiku athu”?
YEHOVA MULUNGU ndiye Mlengi wathu ndipo ndi amene anatipatsa moyo. (Salmo 36:9; Chivumbulutso 4:11) Motero, ndiye yekha amene angatiuze mmene tingagwiritsire ntchito mwanzeru zaka zimene tili ndi moyo. N’chifukwa chake wamasalmo anapempha Mulungu kuti: “Mutidziŵitse kuŵerenga masiku athu motero, kuti tikhale nawo mtima wanzeru.” (Salmo 90:12) Salmo 90 limene mukupezeka pempho limeneli n’lofunikadi kulipenda mosamalitsa. Komabe choyamba, tiyeni tione mwachidule zimene zili m’nyimbo youziridwa ndi Mulungu imeneyi.
2. (a) Kodi ndani amene analemba Salmo 90, ndipo ayenera kuti analilemba liti? (b) Kodi Salmo limeneli liyenera kukhudza motani mmene timaonera moyo?
2 Mawu omwe ali pamwamba pa Salmo 90 akunena kuti Salmo limeneli ndilo “pemphero la Mose, munthu wa Mulungu.” Popeza salmoli likutsindika kufupika kwa moyo wa munthu, liyenera kuti analilemba Aisrayeli atawapulumutsa kuukapolo wa ku Igupto. Ndipo ayenera kuti anatero ali paulendo wawo wa zaka 40 m’chipululu, pamene imfa inapulula mtundu wosakhulupirirawo. (Numeri 32:9-13) Mulimonse mmene zinalili, Salmo 90 limasonyeza kuti moyo wa munthu wopanda ungwiro ndi waufupi. Ndiyetu tiyenera kugwiritsa ntchito mwanzeru masiku athu a mtengo wapataliwa.
3. Kodi mu Salmo 90 muli zotani?
3 Pa Salmo 90, vesi 1 mpaka 6 akufotokoza kuti Yehova ndiye malo athu okhalamo amuyaya. Mavesi 7 mpaka 12 akusonyeza zimene timafunikira kuti tigwiritse ntchito zaka zochepa zimene timakhala ndi moyo mwa njira imene iye amavomereza. Ndipo monga mmene akufotokozera pa vesi 13 mpaka 17, timafunitsitsa kuti Yehova atikonde ndi kutidalitsa. Inde, Salmo limeneli silikugwira ntchito mwachindunji pa zimene munthu aliyense payekha amakumana nazo monga mtumiki wa Yehova. Komabe, patokha tifunika kulipenda bwinobwino ndi kutsanzira kudzipereka kwa Mulungu kumene akufotokoza m’Salmo limeneli mwapemphero. Motero tiyeni tilione mosamalitsa Salmo 90 limeneli pogwiritsa ntchito zimene anthu odzipatulira kwa Mulungu aona.
Yehova Ndiye “Mokhalamo” Mwathu
4-6. Kodi Yehova wakhala bwanji “mokhalamo” mwathu?
4 Wamasalmoyo akuyamba ndi mawu akuti: “Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo m’mibadwo mibadwo. Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu [monga ndi zoŵaŵa pobereka, NW], inde, kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha, inu ndinu Mulungu.”—Salmo 90:1, 2.
5 Yehova yemwe ndi “Mulungu wosatha,” ndiye “mokhalamo” mwathu—malo othaŵirako auzimu. (Aroma 16:26) Ndife otetezeka chifukwa iye ali wokonzeka kutithandiza nthaŵi ina iliyonse monga “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Popeza timatula nkhaŵa zathu kwa Atate wathu wakumwamba kudzera mwa Mwana wake wokondedwa, ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, umasunga mitima yathu ndi maganizo athu’.—Afilipi 4:6, 7; Mateyu 6:9; Yohane 14:6, 14.
6 Timasungika mwauzimu chifukwa chakuti Yehova mophiphiritsa, ali “mokhalamo” mwathu. Amapereka “zipinda”—mipingo ya anthu ake—monga malo auzimu othaŵirako kumene abusa achikondi amathandiza kwambiri kuti titetezeke. (Yesaya 26:20; 32:1, 2; Machitidwe 20:28, 29) Ndiponso, ena a ife tikuchokera m’mabanja amene akhala akutumikira Mulungu kwa nthaŵi yaitali ndipo taona tokha kuti iye ndiye “mokhalamo m’mibadwo mibadwo.”
7. Kodi mapiri ‘anabadwa’ ndipo dziko lapansi analilenga monga ndi “zoŵaŵa pobereka” mu lingaliro lotani?
7 Yehova wakhala alipo kuyambira mapiri “asanabadwe” kapena dziko lapansi lisanalengedwe monga ndi “zoŵaŵa pobereka.” M’kuona kwa anthu, inali ntchito yaikulu kwabasi kulenga dziko lapansili ndi zinthu zimene zilimo zimene zina mwa izo n’zosamvetsetseka mmene anazipangira. Ndipo wamasalmoyo ponena kuti mapiri ‘anabadwa’ ndipo analenga dziko monga ndi “zoŵaŵa pobereka,” akusonyeza ulemu waukulu chifukwa cha ntchito imene Yehova anali nayo polenga zinthu zimenezi. Kodi ifenso sitingasonyeze ulemu ngati umenewo ndi kuyamikira zimene Mlengi anachita?
Yehova ndi Wokonzeka Kutithandiza
8. Kodi mawu akuti Yehova ali Mulungu “kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha” akutanthauzanji?
8 Wamasalmoyu anaimba kuti: “Inde, kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha, Inu ndinu Mulungu.” “Nthaŵi yosayamba” kapena “nthaŵi yosatha” inganene za zinthu zimene zili ndi pothera koma nthaŵi yake yothera siikudziŵika. (Eksodo 31:16, 17; Ahebri 9:15) Koma pa Salmo 90:2 ndi malo ena m’Malemba Achihebri, pamene mawu akuti “nthaŵi yosayamba” kapena “nthaŵi yosatha” amapezeka, amatanthauza “kwamuyaya.” (Mlaliki 1:4) Sitingathe kumvetsa kuti n’zotheka bwanji kuti Mulungu wakhala alipo nthaŵi zonse. Komabe, Yehova alibe chiyambi ndipo sadzakhala ndi mapeto. (Habakuku 1:12) Iye alipo nthaŵi zonse ndipo ali wokonzeka kutithandiza.
9. Kodi wamasalmo akufananitsa zaka 1,000 za moyo wa munthu ndi chiyani?
9 Wamasalmo anamuuzira kunena kuti zaka 1,000 za moyo wa munthu zikufanana ndi nthaŵi yochepa chabe kwa Mlengi wamuyaya. Polankhula kwa Mulungu, iye analemba kuti: “Mubweza munthu akhale fumbi; nimuti, Bwererani inu, ana a anthu. Pakuti pamaso panu zaka zikwi zikhala ngati dzulo, litapita, ndi monga ulonda wa usiku.”—Salmo 90:3, 4.
10. Kodi Mulungu ‘amam’bweza motani munthu kuti akhale fumbi’?
10 Munthu amafa, ndipo Mulungu ‘amam’bweza kuti akhale fumbi,’ kutanthauza kuti, munthu amabwerera ku “fumbi,” monga dothi lofumbutuka. Kwenikweni, Yehova amati: ‘Bwerera ku fumbi kumene unatengedwa.’ Genesis 2:7; 3:19) Zimenezi zikukhudza aliyense kaya wamphamvu kapena wofooka, wolemera kapena wosauka. Zili choncho chifukwa chakuti palibe munthu wopanda ungwiro amene ‘angaombole mbale kapena kum’perekera dipo kwa Mulungu, kuti akhale ndi moyo osafa [“kosatha,” NW].’ (Salmo 49:6-9) Tikuthokozatu kwambiri kuti ‘Mulungu anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.’—Yohane 3:16; Aroma 6:23.
(11. N’chifukwa chiyani tinganene kuti nthaŵi imene ife tingaone kuti ndi yaitali ndi yochepa kwambiri kwa Mulungu?
11 Kwa Yehova, Metusela amene anakhala ndi moyo zaka 969 sanakwanitse tsiku. (Genesis 5:27) Kwa Mulungu, zaka 1,000 zili ngati dzulo lapitali, nthaŵi ya maola 24 okha basi. Wamasalmo ananenanso kuti Mulungu amaona zaka 1,000 ngati ulonda wausiku wa maola anayi pamsasa. (Oweruza 7:19) Inde, nthaŵi imene ife tingaione kuti ndi yaitali, ndi nthaŵi yaifupi kwambiri kwa Mulungu wamuyaya, Yehova.
12. Kodi Mulungu ‘amawakokolola’ motani anthu?
12 Mosiyana ndi kukhalapo kwa Mulungu kwamuyaya, nthaŵi imene munthu amakhala ndi moyo pakalipano ndi yaifupi kwambiri. Wamasalmo anati: “Muwatenga [“Muwakokolola,” NW] ngati ndi madzi aakulu, akhala ngati tulo; m’mamaŵa akhala ngati msipu wophuka. M’mamaŵa uphuka bwino; madzulo ausenga, nuuma.” (Salmo 90:5, 6) Mose anaona Aisrayeli zikwi zambiri akumwalira m’chipululu, Mulungu atawakokolola ngati madzi osefukira. M’Baibulo la New International Version anatembenuza mbali ya salmo imeneyi kuti: “Muwakokolola anthu m’tulo ta imfa.” Ndipotu, nthaŵi imene anthu opanda ungwiro amakhala ndi moyo ili ngati “tulo” ta nthaŵi yochepa chabe, imene ikufanana ndi tulo ta usiku umodzi.
13. Kodi ‘tili ngati msipu’ motani, ndipo zimenezi ziyenera kukhudza motani mmene timaganizira?
13 Anthufe ‘tili ngati msipu umene umaphuka bwino m’mamaŵa’ koma pofika madzulo umakhala utafota chifukwa cha kutentha kwa dzuŵa. Inde, moyo wathu ndi waufupi monga mmene ulili udzu umene umafota m’tsiku limodzi lokha. Ndiyetu tiyeni tisawononge nthaŵi yamtengo wapatali imene tili ndi moyoyi. M’malo mwake, tiyeni tifunitsitse kuti Mulungu atitsogoze mmene tingagwiritsire ntchito zaka zimene tatsala nazo m’dongosolo la zinthu lino.
Yehova Amatithandiza “Kuŵerenga Masiku Athu”
14, 15. Kodi Salmo 90:7-9 linakwaniritsidwa motani kwa Aisrayeli?
14 Wamasalmoyo polankhula kwa Mulungu anawonjezera kuti: “Pakuti tiwonongeka mu mkwiyo wanu; ndipo m’kuzaza kwanu tiopsedwa. Munaika mphulupulu zathu pamaso panu, ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu. Pakuti masiku athu onse apitirira mu ukali wanu; titsiriza moyo wathu ngati lingaliro [“kunong’ona,” NW].”—Salmo 90:7-9.
15 Aisrayeli osakhulupirika ‘anawonongeka mu mkwiyo wa Mulungu.’ ‘M’kuzaza kwake anaopsedwa.’ Ena “anamwazika m’chipululu” chifukwa Mulungu anawaweruza. (1 Akorinto 10:5) Yehova ‘anaika mphulupulu zawo pamaso pake.’ Anadziŵerengera mlandu kwa Mulungu chifukwa cha zolakwa zimene anali kuchita poyera. Komanso ‘zoipa zobisika,’ kapena kuti machimo osaonekera, anali ‘pamaso pake.’ (Miyambo 15:3) Popeza ukali wa Mulungu unawayakira, Aisrayeli osalapawo ‘anatsiriza moyo wawo ngati kunong’ona.’ Motero, nthaŵi yaifupi imene timakhala ndi moyoyi ili ngati mpweya umene umadutsa pamilomo yathu ponon’gona.
16. Ngati ena akuchita tchimo mwamseri, kodi afunika kuchita chiyani?
16 Ngati titachita tchimo mwamseri, tingathe kuwabisira anthu kwa nthaŵi yaitali ndithu. Koma zolakwa zathu zobisikazo zidzakhala ‘pamaso pa Yehova,’ ndipo zidzawononga ubale wathu ndi iye. Kuti tikonzenso ubale wathu ndi Yehova, tidzafunika kupemphera kuti atikhululukire. Tisiye zolakwa zathu ndipo tilandire moyamikira thandizo lauzimu limene akulu achikristu angapereke. (Miyambo 28:13; Yakobo 5:14, 15) Titatero zidzakhalatu bwino kwambiri kusiyana ndi kuti ‘titsirize moyo wathu ngati kunong’ona,’ ndi kuwononga chiyembekezo chathu chodzakhala ndi moyo kosatha.
17. Kodi anthu ambiri amakhala ndi moyo zaka zingati, ndipo zaka zathu n’zodzala ndi chiyani?
17 Wamasalmo pofotokoza za nthaŵi imene anthu opanda ungwiro amakhala ndi moyo anati: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi aŵiri, kapena tikakhala nayo mphamvu ndi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwawo kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithaŵa ife tomwe.” (Salmo 90:10) Anthu ambiri amakhala ndi moyo kwa zaka 70, ndipo Kalebe ali ndi zaka 85 ananena kuti anali ndi mphamvu zapadera. Pali ena amene anakhala ndi moyo kwa zaka zoposa 70. Ena mwa iwo ndi Aroni (zaka 123), Mose (zaka 120), ndi Yoswa (zaka 110). (Numeri 33:39; Deuteronomo 34:7; Yoswa 14:6, 10, 11; 24:29) Koma anthu osakhulupirika amene anatuluka mu Igupto, amene anawaŵerenga kuyambira a zaka 20 kupita m’tsogolo anafa asanapitirire zaka 40. (Numeri 14:29-34) Lerolino, m’mayiko ambiri anthu amangokhala ndi moyo kwa zaka zimene wamasalmoyu ananena. Zaka zathu n’zodzala ndi “chivuto ndi chopanda pake.” Zimatha mwamsanga, “ndipo tithaŵa ife tomwe.”—Yobu 14:1, 2.
18, 19. (a) Kodi “kuŵerenga masiku athu motero kuti tikhale nawo mtima wanzeru,” kumatanthauzanji? (b) Kodi kusonyeza kwathu nzeru kudzatilimbikitsa kuchita chiyani?
18 Kenako wamasalmoyo akuimba kuti: “Adziŵa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani, ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani? Mutidziŵitse kuŵerenga masiku athu motero, kuti tikhale nawo mtima wanzeru.” (Salmo 90:11, 12) Palibe amene akudziŵa bwinobwino mphamvu ya mkwiyo wa Mulungu kapena kuti ukali wake ndi waukulu motani, ndipo zimenezi ziyenera kukulitsa kuopa kwathu Yehova kom’patsa ulemu. Ziyeneradi kutilimbikitsa kum’pempha kuti ‘atidziŵitse kuŵerenga masiku athu motero, kuti tikhale nawo mtima wanzeru.’
19 Mawu a wamasalmoŵa ndi pemphero lakuti Yehova aphunzitse anthu ake mmene angasonyezere nzeru posamala zaka zawo zimene zatsala ndi kuzigwiritsa ntchito mwa njira imene Mulungu amavomereza. Zaka 70 zimene munthu amakhala ndi moyo ndi masiku pafupifupi 25,500 basi. Komabe, kaya tili ndi zaka zingati, ‘sitidziŵa chimene chidzagwa maŵa, pakuti tili utsi, wakuonekera kanthaŵi, ndipo kenako ukanganuka.’ (Yakobo 4:13-15) Popeza ‘nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika zimatigwera ife tonse,’ sitingadziŵe kuti tikhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali bwanji. Ndiyetu tiyeni pakali pano tipempherere nzeru zoti tilimbane ndi mayesero, kukhala bwino ndi ena, ndi kutumikira Yehova mmene tingathere—inde, tipemphe lero! (Mlaliki 9:11; Yakobo 1:5-8) Yehova amatitsogoza ndi Mawu ake, mzimu wake, ndi gulu lake. (Mateyu 24:45-47; 1 Akorinto 2:10; 2 Timoteo 3:16, 17) Kusonyeza nzeru kumatilimbikitsa ‘kuthanga tafuna Ufumu wa Mulungu’ ndi kugwiritsa ntchito masiku athu mwa njira imene imalemekeza Yehova ndi kusangalatsa mtima wake. (Mateyu 6:25-33; Miyambo 27:11) N’zoona kuti kum’lambira ndi mtima wonse sikudzathetsa mavuto athu onse, koma kudzabweretsadi chimwemwe chochuluka.
Madalitso a Yehova Amatipatsa Chimwemwe
20. (a) Kodi Mulungu ‘amamva chisoni’ motani? (b) Kodi Yehova adzatani nafe ngati tachita tchimo lalikulu koma talapa moona mtima?
20 Zikanakhalatu bwino kwambiri tikanati tizisangalala m’moyo wathu wonse. Pa mfundo imeneyi, Mose anapempha kuti: “Bwerani, Yehova; Salmo 90:13, 14) Mulungu salakwa. Komabe, ‘amamva chisoni’ ndipo ‘amabweza’ mkwiyo wake ndi chilango chake ngati chenjezo lake loti awalanga lachititsa anthu olakwa kusintha maganizo ndi makhalidwe awo. (Deuteronomo 13:17) Motero, ngakhale titachita tchimo lalikulu koma n’kulapa moona mtima, Yehova ‘angatikhutitse nacho chifundo chake,’ ndipo tingathe ‘kufuula mokondwera.’ (Salmo 32:1-5) Ndipo mwa kutsatira njira zolungama, Mulungu adzatichitira chifundo ndipo tidzatha “kukondwera masiku athu onse”—inde, kwa moyo wathu wonse.
kufikira liti? Ndipo alekeni [“amvereni chisoni,” NW] atumiki anu. Mutikhutitse nacho chifundo chanu m’maŵa; ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.” (21. Kodi Mose ayenera kuti anali kupempha chiyani m’mawu ake amene ali pa Salmo 90:15, 16?
21 Wamasalmo anapemphera kuchokera pansi pa mtima kuti: “Tikondweretseni monga mwa masiku mudatizunzaŵa, ndi zaka tinaona choipa. Chochita Inu chioneke kwa atumiki anu, ndi ulemerero wanu pa ana awo.” (Salmo 90:15, 16) Mose ayenera kuti anali kupempha Mulungu kuti adalitse Israyeli ndi chikondwerero kwa masiku ofanana ndi amene anazunzika ndi zaka zimene anavutika. Anapempha kuti “chochita” cha Mulungu chodalitsa Aisrayeli chionekere kwa atumiki Ake ndipo ulemerero Wake uonekere pa ana awo. Ifenso tingapemphere kuti anthu omvera adzadalitsidwe m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza.—2 Petro 3:13.
22. Malinga ndi Salmo 90:17, kodi tingapempherere chiyani?
22 Salmo 90 likumaliza ndi pempho lakuti: “Ndipo chisomo chake cha Yehova Mulungu wathu chikhale pa ife; ndipo mutikhazikitsire ife ntchito ya manja athu; inde, ntchito ya manja athu muikhazikitse.” (Salmo 90:17) Mawu ameneŵa akusonyeza kuti tingapemphe Mulungu kuti adalitse ntchito yathu pom’tumikira. Monga odzozedwa kapena anzawo a “nkhosa zina,” tikusangalala kuti tili ndi “chisomo chake cha Yehova.” (Yohane 10:16) Ndife osangalalatu kuti Mulungu ‘wakhazikitsira ife ntchito ya manja athu’ monga olengeza Ufumu ndi ntchito zina.
Tiyeni Tipitirize Kuŵerenga Masiku Athu
23, 24. Kodi tingapindule bwanji posinkhasinkha Salmo 90?
23 Kusinkhasinkha Salmo 90 kuyenera kukulitsa kudalira kwathu Yehova yemwe ndi “mokhalamo” mwathu. Mwakulingalira mawu ake ofotokoza za kufupika kwa nthaŵi imene timakhala ndi moyo, tiyenera kudziŵa bwino kwambiri kufunika koti Mulungu atitsogoze poŵerenga masiku athu. Ndipo ngati tipitirizabe kufunafuna ndi kusonyeza nzeru za Mulungu, tidzatsimikiza kuti Yehova adzatichitira chifundo ndi kutidalitsa.
24 Yehova adzapitiriza kutidziŵitsa kuŵerenga masiku athu. Ndipo ngati titsatira malangizo ake, tidzapitiriza kuŵerenga masiku athu kwamuyaya. (Yohane 17:3) Komabe, ngati tikufunadi kudzakhala ndi moyo kosatha, Yehova akhale pothaŵirapo pathu. (Yuda 20, 21) Monga mmene tionere m’nkhani yotsatira, mfundo imeneyi anaifotokoza bwino kwambiri m’mawu olimbikitsa a m’Salmo 91.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Yehova wakhala bwanji “mokhalamo” mwathu?
• N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi wokonzeka kutithandiza nthaŵi zonse?
• Kodi Yehova amatithandiza motani “kuŵerenga masiku athu”?
• Kodi n’chiyani chimatithandiza “kukondwera masiku athu onse”?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 10]
Yehova anali Mulungu kuyambira “asanabadwe mapiri”
[Chithunzi patsamba 12]
Kwa Yehova, Metusela amene anakhala ndi moyo zaka 969 sanakwanitse tsiku
[Zithunzi patsamba 14]
Yehova ‘wakhazikitsira ife ntchito ya manja athu’