Kuvomera Yehova Akamatipempha Kumadzetsa Mphoto Zambiri
Mbiri ya Moyo Wanga
Kuvomera Yehova Akamatipempha Kumadzetsa Mphoto Zambiri
YOSIMBIDWA NDI MARIA DO CÉU ZANARDI
“Yehova amadziŵa zimene akuchita. Ngati wakupempha kuchita chinachake, vomera modzichepetsa.” Mawu ameneŵa amene bambo analankhula zaka pafupifupi 45 zapitazo, anandithandiza kuvomera pempho loyamba limene ndinalandira kuchokera ku gulu la Yehova, loti ndikatumikire monga mtumiki wa nthaŵi zonse. Ndikuyamikira kwambiri mpaka lero zimene bambo anandilangiza chifukwa kuvomera mapempho oterowo kwandidzetsera mphoto zambiri.
M’CHAKA cha 1928, bambo analembetsa kuti azilandira magazini ya Nsanja ya Olonda ndipo anali ndi chidwi ndi Baibulo. Popeza anali kukhala m’kati mwenimweni mwa dziko la Portugal, sanathe kusonkhana ndi mpingo wa Mulungu kupatulapo kuŵerenga zofalitsa zimene anali kulandira pa positi ndi Baibulo limene linali la agogo anga. Mu 1949, banja lathu linasamukira ku Brazil, kwawo kwa mayi, ndipo tinali kukhala kunja kwa mzinda wa Rio de Janeiro. Nthaŵi imeneyi n’kuti ndili ndi zaka 13.
Anthu amene tinali kukhala nawo pafupi anatipempha kuti tipite ku tchalitchi kwawo ndipo tinapita kangapo konse. Bambo ankakonda kuwafunsa anthuwo za moto wa helo, mzimu, ndi tsogolo la dziko lapansi. Iwo ankalephera kuyankha. Motero, bambo ankakonda kunena kuti: “Tingodikira ophunzira Baibulo enieni.”
Tsiku lina munthu wakhungu anafika panyumba pathu akugaŵa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Bambo anamufunsa mafunso omwe aja, ndipo anayankha mogwira mtima kuchokera m’Baibulo. Mlungu wotsatira, wina wa Mboni za Yehova anafika panyumba pathu. Atayankha mafunso ambiri, anapempha mwaulemu kuti akufuna kupita ku “munda.” Bambo sanamvetse chimene Mateyu 13:38 pamene pamati: “Munda ndiwo dziko lapansi.” Bambo anafunsa kuti: “Kodi ndingapite nawo?” “Inde,” anawayankha motero. Tinasangalala kwambiri kuchipezanso choonadi cha Baibulo. Bambo anabatizidwa pa msonkhano wachigawo wotsatira ndipo patangopita nthaŵi yochepa, inenso ndinabatizidwa mu November 1955.
anali kutanthauza, motero anawaŵerengeraKuvomera Pempho Loyamba
Patapita chaka ndi theka, ndinalandira envulopu yaikulu yakhakhi kuchokera ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Rio de Janeiro. Mkatimo munali fomu yondipempha kuti ndifunsire ntchito yolalikira ya nthaŵi zonse. Panthaŵiyo mayi sanali kupeza bwino kwenikweni, motero ndinapempha bambo kuti andithandize maganizo. Iwo anayankha mtima uli m’malo kuti: “Yehova amadziŵa zimene akuchita. Ngati wakupempha, vomera modzichepetsa.” Atandilimbikitsa ndi mawu ameneŵa, ndinalemba zofunika pa fomuyo ndipo ndinayamba utumiki wa nthaŵi zonse pa July 1, 1957. Choyamba ananditumiza ku tawuni ya Três Rios yomwe ili m’chigawo cha Rio de Janeiro.
Poyamba, anthu a ku Três Rios sankafuna kumvetsera uthenga wathu chifukwa sitinali kugwiritsa ntchito Baibulo la Chikatolika. Zinthu zinayamba kuyenda bwino pamene tinayamba kuphunzira ndi Geraldo Ramalho yemwe anali Mkatolika weniweni. Iye anatithandiza kupeza Baibulo lomwe linali ndi siginecha ya wansembe wa m’deralo. Kuyambira pamenepo, anthu akayamba kutsutsa ndinkawaonetsa siginecha ya wansembeyo ndipo ndikatero mafunso ankathera pomwepo. Kenako, Geraldo anabatizidwa.
Ndinasangalala kwambiri pamene msonkhano wadera unachitikira m’kati mwenimweni mwa tawuni ya Três Rios mu 1959. Mkulu wa apolisi amene anali kuphunzira Baibulo panthaŵiyo, anakonza zikwangwani za nsalu zopachika m’misewu zolengeza msonkhanowo m’tawuni yonseyo. Nditatumikira ku Três Rios kwa zaka zitatu, anandipempha kuti ndipite ku dera lina. Kumeneku kunali ku Itu, komwe kunali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 110 kumadzulo kwa mzinda wa São Paulo.
Mabuku Ofiira, a Bluu, ndi a Chikasu
Ine ndi mpainiya amene ndinali kugwira naye ntchito titafufuza nyumba yoti tizikhala, tinapeza malo abwino m’kati mwa tawuni kunyumba kwa mkazi wina wamasiye wokoma mtima dzina lake Maria. Anali kutisamala ngati ana ake. Komabe posakhalitsa, bishopu wa Aroma Katolika wa ku Itu anapita kwa mkazi wamasiyeyo ndi kumuuza kuti atithamangitse panyumba pakepo. Mkaziyu anakana ndipo anati: “Mwamuna wanga atamwalira simunandilimbikitse m’pang’ono pomwe. Mboni za Yehovazi zandithandiza ngakhale kuti sindili m’chipembedzo chawo.”
Zitangochitika zimenezi, mayi wina anatiuza kuti ansembe a Chikatolika a ku Itu analetsa anthu awo kulandira “buku lofiira lonena za Mdyerekezi.” Anali kunena buku lakuti “Mulungu Akhale Woona,” lofotokoza za Baibulo limene tinali kugaŵira anthu mlungu umenewo. Popeza ansembe “analetsa” buku lofiira, tinakonza zogaŵira buku la bluu (lakuti “New Heavens and a
New Earth”). Kenako, ansembe aja atamva kuti tasintha, tinayamba kugaŵira buku la chikasu (lakuti What Has Religion Done for Mankind?). Tinapitirizabe kusinthasintha motero. Mwayi wake ndiwoti tinali ndi mabuku ambiri a zikuto za mitundu yosiyanasiyana.Nditatha pafupifupi chaka ku Itu, ndinalandira telegalamu yondipempha kuti ndikatumikire kwa nthaŵi yochepa ku Beteli, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Rio de Janeiro, pokonzekera msonkhano waukulu. Ndinavomera ndi chimwemwe chodzala tsaya.
Utumiki Wina ndi Mavuto Amene Ndinakumana Nawo
Ku Beteli sikunkasoŵa ntchito yoti munthu ugwire, ndipo ndinkasangalala kuthandiza mmene ndingathere. Kunalitu kopindulitsa kuchita nawo lemba la tsiku ndi tsiku m’maŵa uliwonse ndi Phunziro la banja la Nsanja ya Olonda Lolemba lililonse madzulo. Mapemphero ochokera pansi pa mtima a Otto Estelmann ndi abale ena okhwima mwauzimu a m’banja la Beteli anali kundikhudza mtima kwambiri.
Msonkhano waukuluwo utatha, ndinalongedza katundu wanga kuti ndibwerere ku Itu, koma mosayembekezeka, mtumiki wa nthambi, Grant Miller, anandipatsa kalata yondipempha kuti ndikhaliretu pa Beteli pomwepo. M’chipinda chathu ndinali ndi mlongo Hosa Yazedjian, amene panopa akutumikirabe pa Beteli ya ku Brazil. Nthaŵi imeneyo panali anthu ochepa chabe pa Beteli. Tinalipo anthu 28 basi ndipo tonse tinali kudziŵana bwino kwambiri.
M’chaka cha 1964, João Zanardi, mtumiki wachinyamata wa nthaŵi zonse, anafika pa Beteli kudzaphunzira zina ndi zina. Ataphunzira anamutumiza kukatumikira monga mtumiki wa dera kapena woyang’anira woyendayenda m’gawo la pafupi ndi Beteli. Nthaŵi zina tinali kukumana akabwera ku Beteli kudzapereka malipoti ake. Mtumiki wa nthambi anamulola João kuti azikhala nawo pa phunziro la banja Lolemba madzulo, motero tinkatha kucheza limodzi. Ndinakwatirana ndi João mu August 1965. Ndinavomera mosangalala pempho loti ndikatumikire ndi mwamuna wanga ku ntchito yoyendera dera.
Nthaŵi imeneyo ntchito yoyendayenda mkati mwa dziko la Brazil inali yovuta. Sindidzaiŵala maulendo amene tinkachezera gulu la ofalitsa ku tawuni ya Aranha m’chigawo cha Minas Gerais. Tinkakwera sitima ndipo kenako mtunda wonse wotsala tinkayenda pansi. Tinkatero titanyamula masutikesi, taipi, kanema, zikwama zoyenda nazo mu utumiki ndi mabuku. Tinali kusangalala kwambiri nthaŵi zonse kum’peza mbale wina wachikulire dzina lake Lourival Chantal akutidikira pa siteshoni kuti atithandize kunyamula zikwama zathu.
Ku Aranha tinali kuchitira misonkhano m’nyumba ya lendi. Tinkagona m’chipinda chimene chinali kumbuyo kwa nyumbayo. Kumbali ina ya chipindacho kunali chipika chomwe timawazako nkhuni zophikira ndi kutenthetsa madzi amene abale anali kutibweretsera mu ndowa. Pafupi ndi nyumbayo panali nsungwi. M’kati mwa nsungwizo munali kadzenje kamene tinali kukagwiritsa ntchito monga chimbudzi chathu. Usiku timasiya moto ukuyaka kuti tizilombo timene timafalitsa matenda otupitsa chiwindi ndi akapamba tisaloŵe. Mmaŵa tikamadzuka mphuno zathu zimakhala zitada bii ndi utsi. Zinalitu zochititsa chidwi kwambiri!
Luka 14:28 ndi kuŵerengera mtengo wake tisanavomere kupita ku Portugal chifukwa ntchito yathu yachikristu kumeneko anailetsa, ndipo boma la Portugal linali litatsekera m’ndende abale ambiri.
Tikutumikira m’ntchito yoyendayenda m’chigawo cha Paraná, tinalandiranso envulopu ina yaikulu yakhakhi kuchokera ku ofesi ya nthambi. Linali pempho lina lochokera ku gulu la Yehova. Panthaŵiyi anatipempha kukatumikira ku Portugal. Kalatayo inatilangiza kuganizira mfundo yachikhalidwe imene ili paKodi tingapite kudziko limene akanatha kukatizunza monga mmene anali kuwazunzira abale athuwo? João anati: “Ngati abale athu ku Portugal akukhalabe kumeneko ndi kutumikira Yehova mokhulupirika, ife tingalekerenji?” Nditakumbukira mawu olimbikitsa amene bambo anandiuza ndinavomereza kuti: “Ngati Yehova watipempha, tivomere ndi kum’dalira.” Posakhalitsa tinapita ku Beteli ku São Paulo kuti akatilangize zina ndi zina ndi kukonza makalata athu a paulendo.
João Maria ndi Maria João
Sitima ya panyanja imene tinakwera yotchedwa Eugênio C, inanyamuka padoko la Santos m’chigawo cha São Paulo, pa September 6, 1969. Tinafika ku Portugal titayenda panyanja kwa masiku asanu ndi anayi. Poyamba, tinagwira ntchito kwa miyezi ingapo ndi abale ozoloŵera, m’misewu yaing’ono ya m’matawuni a Alfama ndi Mouraria omwe ali m’chigawo chakale cha mzinda wa Lisbon. Anatiphunzitsa kukhala osamala kuti apolisi asatigwire.
Tinali kuchitira misonkhano m’nyumba za Mboni. Tikazindikira kuti anthu a m’nyumba zoyandikana nawo anayamba kukaika, tinali kusintha mwamsanga kumakachitira misonkhanoyo kudera lina kuti asaukire nyumbayo kapena kutengera abalewo kundende. Misonkhano yadera ndi yapadera tinkaiti mapikiniki. Tinkachitira m’paki ya Monsanto kunja kwa mzinda wa Lisbon, ndi ku dera lina la nkhalango lotchedwa Costa da Caparica limene linali m’mphepete mwa nyanja. Tinkavala zovala wamba pamisonkhanoyo, ndipo gulu la akalinde akuthwa maso limalondera m’malo amene kukanatha kuchokera anthu. Ngati panali kubwera wina wake wokayikitsa, tinkayamba kuseŵera, kudya, kapena kuimba nyimbo wamba.
Pofuna kuti asathe kutidziŵa, sitinkagwiritsa ntchito maina athu enieni. Abale ankatiitana kuti João Maria ndi Maria João. Sitinkagwiritsa ntchito maina athu polemberana makalata kapena m’kaundula. M’malo mwake, aliyense anapatsidwa nambala. Ndinayesetsa kupeŵa kuloŵeza pamtima
maadiresi a abale kuti ngati atanditengera kundende, ndisathe kupereka abalewo.Ngakhale kuti panali chiletso choterechi, João ndi ine tinagwiritsa ntchito mpata uliwonse kulalikira chifukwa tinkadziŵa kuti ufulu wathu ukanatha nthaŵi iliyonse. Tinaphunzira kudalira Atate wathu wa kumwamba, Yehova. Monga Mtetezi wathu, anagwiritsa ntchito angelo ake mwa njira yoti tinkaona ngati ‘tikuona wosaonekayo.’—Ahebri 11:27.
Ulendo wina, tikulalikira nyumba ndi nyumba ku Porto, tinakumana ndi mwamuna wina amene anatiumiriza kuti tiloŵe m’nyumba yake. Mlongo amene ndinali kulalikira naye anavomera mosakayika, ndipo sindikanachitira mwina koma kumutsata. Ndinachita mantha nditaona chithunzi cha munthu wina atavala yunifolomu ya usilikali pakhomo lalikulu la nyumbayo. Tikanachita chiyani tsopano? Anatiuza kuti tikhale pansi, ndipo kenako anandifunsa kuti: “Kodi ukanalola kuti mwana wako akakhale msilikali ngati akanamuuza kuti akaloŵe ntchitoyi?” Panafunika kuyankha mochenjera. Nditapemphera chamumtima, ndinayankha mtima uli pansi kuti: “Ndilibe ana ndipo ndikukhulupirira kuti ngati ndikanakufunsani funso longoyerekezera ngati limeneli, mukanandiyankha chimodzimodzi.” Anangokhala duu. Ndiyeno ndinapitiriza kuti : “Koma mukanandifunsa mmene munthu umamvera mchimwene wako kapena bambo ako akamwalira, ndikanayankha chifukwa mchimwene wanga ndi bambo anga anamwalira.” Misozi inayamba kutuluka m’maso mwanga pamene ndinali kulankhula, ndipo ndinaona kuti iyenso anatsala pang’ono kulira. Anafotokoza kuti si kale pamene mkazi wake anamwalira. Anamvetsera mwachidwi pamene ndinali kufotokoza chiyembekezo cha kuuka kwa akufa. Ndiyeno tinatsanzika mwaulemu ndipo tinachoka popanda vuto lililonse. Tinangosiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova.
Ngakhale kuti ntchito yathu anailetsa, tinathandiza anthu oona mtima kudziŵa choonadi. Ku Porto mwamuna wanga anayamba kuphunzira ndi munthu wamalonda dzina lake Horácio, amene anapita patsogolo mofulumira. Kenako, mwana wake, Emílio yemwe anali dokotala wabwino kwambiri, anaphunziranso za Yehova ndipo anabatizidwa. Zoonadi, palibe chingalepheretse mzimu wa Yehova.
“Simukudziŵa Zimene Yehova Adzalola”
Mu 1973, ine ndi João anatipempha kuti tikakhale nawo pa Msonkhano wa Mayiko wakuti “Kupambana kwa Mulungu” ku Brussels, Belgium. Kunali abale zikwizikwi ochokera ku Spain ndi ku Belgium pamodzinso ndi nthumwi zochokera ku Mozambique, Angola, Cape Verde, Madeira, ndi ku Azores. Mbale Knorr wochokera ku likulu ku New York anatilimbikitsa m’ndemanga zake zomaliza kuti: “Pitirizani kutumikira Yehova mokhulupirika. Simukudziŵa zimene Yehova adzalola. Sitidziŵa mwina msonkhano wa mayiko wotsatira mudzachitira ku Portugal!”
Chaka chotsatira ntchito yolalikira anaivomereza mwalamulo ku Portugal. Ndipo zimene Mbale Knorr ananena zinachitikadi ndendende pamene mu 1978, tinachita msonkhano wathu woyamba wa mayiko ku Lisbon. Unalitu mwayi waukulu kuyenda m’misewu ya Lisbon kulalikira mogwiritsa
ntchito zikwangwani, magazini, ndiponso kuwaitana anthu kuti akamve nawo nkhani ya onse. Inde, zimene tinali kulakalaka kwambiri zinachitikadi.Abale athu a Chipwitikizi tinali kuwakonda kwambiri. Ambiri mwa iwo anaikidwa m’ndende ndi kumenyedwa chifukwa monga Akristu iwo sanaloŵerere m’ndale. Tinkafuna kupitirizabe kutumikira ku Portugal. Koma sizinatero. Mu 1982, João anayamba kudwala mtima ndipo ofesi ya nthambi inatilangiza kuti tibwerere ku Brazil.
Nthaŵi Yovuta
Abale a ku ofesi ya nthambi ku Brazil anatithandiza kwambiri ndipo anatitumiza kuti tikatumikire ku Mpingo wa Quiririm mu mzinda wa Taubaté m’chigawo cha São Paulo. Matenda a João anakulirakulirabe, ndipo posakhalitsa sanathenso kumachoka panyumba. Anthu achidwi anali kufika kunyumba kwathu kudzaphunzira Baibulo. Tinali kuchita msonkhano wa utumiki wa kumunda tsiku lililonse pamodzinso ndi phunziro la buku kunyumba komweko. Zimenezi zinali kutithandiza kulimbabe mwauzimu.
João anapitiriza kuchita zomwe akanatha potumikira Yehova mpaka pamene anamwalira pa October 1, 1985. Ndinali wachisoni ndipo ndinavutika maganizo, komabe ndinatsimikiza mtima kupitiriza utumiki wanga. Chinthu chinanso chimene chinandibwezera m’mbuyo chinali mbala zimene zinathyola nyumba yanga ndi kuba pafupifupi chilichonse mu April 1986. Kwanthaŵi yoyamba m’moyo wanga, ndinalibe chimwemwe chifukwa chosoŵa mnzanga ndipo ndinali ndi mantha. Anthu ena aŵiri okwatirana anandipempha kuti ndikakhale nawo kwa kanthaŵi ndipo ndinathokoza kwambiri.
Kumwalira kwa João ndi kundibera katundu kunakhudza kutumikira kwanga Yehova. Ndinalibenso chidaliro mu utumiki. Nditalembera kalata ku ofesi ya nthambi kuwadziŵitsa za mavuto anga, anandiitana kuti ndikakhale ku Beteli kwa kanthaŵi kuti ndikathe kukhazikika maganizo. Inalitu nthaŵi yolimbikitsa kwambiri.
Nditayamba kukhazikika maganizo, ndinavomera kukatumikira ku tawuni ya Ipuã imene ili m’chigawo cha São Paulo. Ndinali wotanganidwa ndi kulalikira, komabe nthaŵi zina ndinali kutaya mtima. Zikachitika zimenezi, ndinali kuwaimbira telefoni abale ku mpingo wa Quiririm ndipo banja limodzi linkabwera kudzandichezera kwa masiku angapo. Kundichezera kumeneku kunkandilimbikitsa kwambiri. M’chaka choyamba chimene ndinakhala ku Ipuã, abale ndi alongo okwana 38 anayenda maulendo aatali kudzandiona.
Mu 1992, patapita zaka zisanu ndi chimodzi kuchokera pamene João anamwalira, gulu la Yehova linandipemphanso kuti ndisamuke ndikatumikire mu mzinda wa Franca m’chigawo cha São Paulo, kumene ndikutumikira monga mtumiki wa nthaŵi zonse mpaka pano. Anthu a m’gawo la kuno amamvetsera choonadi kwambiri. Mu 1994, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi mkulu woyang’anira mzindawu. Panthaŵiyi anali kuchititsa misonkhano yokopa anthu kuti amusankhe kukhala phungu wa nyumba ya malamulo ya ku Brazil. Ngakhale kuti anali wotanganidwa kwambiri, tinali kuphunzira Lolemba lililonse madzulo. Popeŵa kuti anthu asamusokoneze tikamaphunzira, iye anali kutseka telefoni yake. Ndinasangalalatu kwambiri kumuona akusiya ndale pang’onopang’ono, ndi kumanganso banja lake mothandizidwa ndi choonadi. Iye ndi mkazi wake anabatizidwa mu 1998.
Ndikamayang’ana mmbuyo, ndinganene kuti m’moyo wanga monga mtumiki wa nthaŵi zonse ndapeza nawo madalitso adzaoneni ndi mwayi waukulu wotumikira Yehova. Kuvomera zimene Yehova anandipempha kudzera m’gulu lake kwandidzetseradi mphoto zambiri. Ndipo ndili wokonzeka kuvomera ngati angandipemphenso m’tsogolomu monga mmene ndachitira m’mbuyomu.
[Zithunzi patsamba 25]
Mu 1957 pamene ndinayamba utumiki wa nthaŵi zonse, ndi lerolino
[Chithunzi patsamba 26]
Ndili pamodzi ndi banja la Beteli la ku Brazil mu 1963
[Chithunzi patsamba 27]
Pa ukwati wathu mu August 1965
[Chithunzi patsamba 27]
Msonkhano wadera ku Portugal nthaŵi imene ntchito yolalikira inali yoletsedwa
[Chithunzi patsamba 28]
Kulalikira mumsewu ku Lisbon nthaŵi ya Msonkhano wa Mayiko mu 1978 wakuti “Chikhulupiriro Chopambana”