‘Mankhwala Opaka M’maso Mwanu’
‘Mankhwala Opaka M’maso Mwanu’
MAWU ameneŵa ananena ndi Yesu Kristu ku mpingo wa m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino. Mpingo umenewu unali ku Laodikaya, ku Asia Minor.
Yesu anati: ‘Gulani mankhwala opaka m’maso mwanu, kuti mukaone.’ Sanali kunena za matenda a maso enieni, koma khungu lauzimu lomwe linkafunika mankhwala. Akristu a ku Laodikaya anali atakopeka kwambiri ndi mzimu wofuna kulemera womwe unali mumzinda womwe ankakhala. Motero iwo anayamba kunyalanyaza zinthu zauzimu zomwe zinali zofunika kwambiri.
Yesu pofotokoza kuti zimenezi n’zimene zawalepheretsa kuona bwino, anati: ‘Unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziŵa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa.’ Akristu a mumpingowo ankafunikira ‘mankhwala a m’maso’ngakhale kuti iwo sanali kudziŵa zimenezi. Mankhwala ameneŵa akanawapeza kokha mwa kugonjera ku ziphunzitso ndi malangizo a Yesu Kristu. Yesuyo anati: ‘Gulani kwa Ine.’—Chivumbulutso 3:17, 18.
Monga momwe zinalili ku Laodikaya, Akristu enieni lerolinonso ayenera kusamala kuti asakopeke, mwina mosazindikira n’komwe, ndi mzimu wokonda chuma ndi zosangalatsa womwe uli kumalo amene akukhala. Kufunika kosungabe maso auzimu ali openya bwino kwasonyezedwa m’langizo lakuti: ‘Gulani kwa [Yesu] mankhwala opaka m’maso mwanu, kuti mukaone.’
Mfundo yofunika kuidziŵa n’njakuti, munthu ayenera kuchita kugula ‘mankhwala a m’maso’ ameneŵa. Ali ndi mtengo wake. Tiyenera kuwonongerapo nthaŵi kuti tiphunzire ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu. Wamasalmo akutitsimikizira kuti Mawu ameneŵa: “Ali oyera, akupenyetsa maso [auzimu].”—Salmo 19:8.