Kodi Mulungu Amene Mumakhulupirira Ndi Weniweni?
Kodi Mulungu Amene Mumakhulupirira Ndi Weniweni?
Gulu la anthu oyendera malo atsopano lomwe bungwe la American Museum of Natural History linatumiza, linali pa ulendo wawo wokaona dziko la Arctic lomwe woyendera malo wina Robert E. Peary anali atanena kuti analiona zaka pafupifupi zisanu ndi ziŵiri mmbuyomo mu 1906.
PEARY ali pa chilumba cha Cape Colgate kumpoto chakumadzulo kwa North America, anaona zomwe zinkaoneka ngati mapiri oyera a dziko lomwe linali patali. Iye analitcha dziko lomwe ankaliona kutalilo kuti Crocker, dzina la m’modzi mwa anthu amene ankamuthandiza ndi ndalama. Gulu la anthu omwe anapita kukatsimikiza za dzikolo ayenera kuti anakondwa kwambiri ataona mwachimbuuzi kutsogolo kwawo, zitunda, mitsinje, ndiponso mapiri okutidwa ndi chipale chofeŵa. Koma pasanapite nthaŵi anazindikira kuti anali kungoona chizimezime cha nyanja ya Arctic. Chizimezime chimenechi chinanyenga Peary, moti pamene ankazindikira zimenezi n’kuti atawononga kale nthaŵi, mphamvu, ndiponso ndalama kuti akayendere malo omwe sanali enieni.
Lerolino, anthu ambiri amadzipereka kwambiri ndiponso kuwonongera nthaŵi yawo potumikira milungu imene amakhulupirira kuti ndi yeniyeni. M’nthaŵi ya atumwi a Yesu, anthu anali kulambira milungu monga Herme ndi Zeu. (Machitidwe 14:11, 12) Masiku ano, milungu imene Ashinto, Ahindu ndiponso zipembedzo zina za padziko lapansi zimalambira ilipo yambirimbiri. Inde, monga momwe Baibulo limanenera, “iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri.” (1 Akorinto 8:5, 6) Kodi milungu yonseyi ingakhale yeniyeni?
Milungu ‘Yosakhoza Kupulumutsa’
Mwachitsanzo, taganizirani za kugwiritsa ntchito mafano kapena zizindikiro polambira. Anthu amene amakhulupirira kapena kugwiritsa ntchito mafano popemphera, amaona kuti mafanowo ali ndi mphamvu zoposa za anthu zomwe zitha kuwapatsa mphoto kapena kuwapulumutsa pa ngozi. Koma kodi mafano angapulumutsedi munthu? Wamasalmo anaimba za mafano kuti: “Mafano a Salmo 135:15-17; Yesaya 45:20.
amitundu ndiwo siliva ndi golidi, ntchito ya manja a anthu. Pakamwa ali napo koma osalankhula; maso ali nawo, koma osapenya; makutu ali nawo, koma osamva; inde, pakamwa pawo palibe mpweya.” Zoonadi, mafano ndi milungu ‘yosakhoza kupulumutsa.’—N’zoona kuti anthu opanga mafano angadzitamandire kuti mafano omwe anapanga ndi manja awo ali ndi moyo ndiponso mphamvu. Ndipo anthu olambira mafanowo amawakhulupirira kwambiri. Mneneri Yesaya anati: “Iwo amanyamula [fano] pa phewa, nalisenza, nalikhazika m’malo mwake, nilikhala chilili; pamalo pakepo silidzasunthika; inde, wina adzalifuulira, koma silingathe kuyankha, kapena kum’pulumutsa m’zovuta zake.” (Yesaya 46:7, NW) Zoona n’zakuti, mafano alibe moyo ngakhale anthu atawakhulupirira motani. Mafano osema ndiponso ziboliboli zoterozo ndi milungu “yopanda pake.”—Habakuku 2:18, NW.
Kulambira mafano kapena kulambira anthu ochita zosangalatsa, anthu otchuka pa zamaseŵera, a za ndale, ndiponso atsogoleri ena achipembedzo, n’kofalanso kwambiri lerolino. Komanso, anthu ambiri amaona ndalama kukhala mulungu wawo. Mulimonsemo, mafano amawaona ngati ali ndi phindu pamene alibe phindu m’pang’ono pomwe. Iwo sapereka ndiponso sangapereke zomwe anthu omwe amawakhulupirira angafune. Mwachitsanzo, chuma chingaoneke kuti chingathetse mavuto ambiri, komabe mphamvu ya chuma n’njonyenga. (Marko 4:19) Wofufuza wina anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani chinthu chimene anthu ambiri amachilakalaka kuchipeza ndiponso kuchikhulupirira kuti chimathetsa mavuto onse chimakhala ndi zotsatirapo zosiyanasiyana zokhumudwitsa ndiponso zosautsa kwambiri wina akachipeza? Inde, kufunafuna chuma kungafune kuti munthu anyalanyaze zinthu zenizeni zaphindu monga thanzi labwino, moyo wabanja wosangalatsa, mabwenzi apamtima, kapenanso ubale wamtengo wapatali ndi Mlengi. Kuona chuma kukhala mulungu kulibe phindu chifukwa chuma ndi ‘fano lopanda pake.’—Yona 2:8, NW.
‘Panalibe Wovomereza’
N’kupusa kutchula chinachake kuti n’chenicheni pamene sichili chenicheni. Olambira mulungu wa Baala m’nthaŵi ya Eliya anazindikira mfundo imeneyi nkhwangwa ili m’mutu. Iwo ankakhulupirira kuti Baala anali ndi mphamvu zobweretsa moto kuchokera kumwamba kuti utenthe nsembe za nyama. Ndipotu, “[a]naitana dzina la Baala, kuyambira m’mawa kufikira pausana nati, Baala, timvereni ife.” Kodi Baala anali ndi makutu oti n’kumva kapena pakamwa poti n’kulankhula? Nkhaniyo imapitiriza kuti: “Koma panalibe mawu kapena wovomereza.” Inde, ‘panalibe wakuwamvera.’ (1 Mafumu 18:26, 29) Baala sanali mulungu weniweni, kapena wamoyo ayi.
Choncho, n’kofunikatu kwambiri kuti tidziŵe ndiponso kumalambira Mulungu amene ali weniweni. Koma kodi iye ndani? Ndipo kodi kumukhulupirira kungatipindulitse motani?
[Zithunzi patsamba 3]
Mnzake wa Peary dzina lake Egingwah akufufuza kuti apeze dziko
Robert E. Peary
[Mawu a Chithunzi]
Egingwah: Kuchokera m’buku lakuti The North Pole: Its Discovery in 1909 Under the Auspices of the Peary Arctic Club, 1910; Robert E. Peary: NOAA
[Zithunzi patsamba 4]
Ambiri amanyengedwa ndi zinthu zimene anthu amalambira padziko lapansi pano