Anthu Amakono Ofera Chikhulupiriro Akuchitira Umboni ku Sweden
Olengeza Ufumu Akusimba
Anthu Amakono Ofera Chikhulupiriro Akuchitira Umboni ku Sweden
LIWU lachingelezi lakuti martyr linachokera ku liwu lachigiriki lakuti martyr lomwe limatanthauza “mboni.” M’Chingelezi liwu limeneli limatanthauza “munthu amene amachitira umboni mwa kufera chikhulupiriro chake.” Akristu ambiri a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anachitira umboni Yehova mwa kufera chikhulupiriro chawo.
Mofananamo, m’zaka za m’ma 1900, Mboni zikwizikwi zinaphedwa ndi anthu otsatira Hitler chifukwa chosaloŵerera m’nkhani za ndale ndiponso m’nkhani za dzikolo. Anthu amakono ofera chikhulupiriro chawo ameneŵa amaperekanso umboni wamphamvu. Tamvani zomwe zinachitika ku Sweden posachedwapa.
Pa chikondwerero chokumbukira kuti patha zaka 50 kuchokera pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inatha, boma la Sweden linakonza zoti pakhale zochitika zosiyanasiyana zophunzitsa anthu za kuphedwa kwa anthu ambiri komwe chipani cha Nazi chinachita. Mutu wa zochitika zimenezo unali wakuti, Mbiri Yosaiŵalika. Mboni za Yehova anazipempha kuti zichite nawo zimenezo ndipo zisimbe zomwe zinawachitikira.
Mboni zinavomera pempholo ndipo zinakonza chionetsero chimene chinali ndi mutu wakuti, Anthu Oiŵalika Omwe Anaphedwa ndi a Nazi. Chionetserochi anayamba kuchionetsa m’Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova ku Strängnäs. Mboni zomwe zinapulumuka zinasimba zomwe zinawachitikira kwa alendo opitirira 8,400 omwe anabwera pa tsiku loyambali. Pomwe chimatha chaka cha 1999, chionetserochi anali atachionetsa m’nyumba zosungiramo zinthu zochititsa chidwi zopitirira 100 ndi m’malaibulale a m’dziko lonse la Sweden ndipo anthu oposa 150, 000 anaonera chionetserochi. Akuluakulu a boma ambiri anali m’gula la alendo omwe anafika ndipo anathirira ndemanga zabwino pa zomwe anaonazo.
Palibe chochitika china kuposa chimenechi chokhudza ntchito za Mboni za Yehova ku Sweden chomwe anthu ambiri anachionerera ndiponso kuchifalitsa m’manyuzipepala ndi m’zofalitsira nkhani. Alendo ambiri ankafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani simunatiuze m’mbuyo monsemu zomwe zinakuchitikirani panthaŵi yomwe Anazi anapulula anthu?”
M’dera lina chionetserochi chitatha, mpingo wina wakumeneko unapereka lipoti la kukwera kwa chiŵerengero cha maphunziro a Baibulo apanyumba ndi 30 peresenti. Mboni ina inaitana mnzake wogwira naye ntchito kuti akaonerere chionetserochi. Munthuyo anavomera ndipo anabwera ndi mnzake wina. Atatha kuonerera, mnzake wa munthuyo, wamkazi, ananena kuti sakumvetsa kuti zingatheke bwanji anthu kukhala ndi chikhulupiriro cholimba choncho mpaka kulolera kuphedwa m’malo mosayina chikalata chosonyeza kusiya chikhulupiriro chawo. Zimenezi zinachititsa kuti akambirane zambiri, ndipo kenako anayamba kuphunzira naye Baibulo.
Mofanana ndi anzawo a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, anthu okhulupirika ofera chikhulupiriro chawo a m’zaka za m’ma 1900 ameneŵa, achitira umboni molimba mtima kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona amene tiyenera kumukhulupirira mosagwedera ndiponso kumumvera mokhulupirika.—Chivumbulutso 4:11.
[Mawu a Chithunzi patsamba 13]
Mkaidi wa ku msasa: Państwowe Muzeum Oświęcim-Brzezinka, mwachilolezo cha USHMM Photo Archives