Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muli Nawo M’gulu la Anthu Amene Mulungu Amawakonda?

Kodi Muli Nawo M’gulu la Anthu Amene Mulungu Amawakonda?

Kodi Muli Nawo M’gulu la Anthu Amene Mulungu Amawakonda?

“Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga.”​—YOHANE 14:21.

1, 2. (a) Kodi Yehova anasonyeza motani chikondi chake kwa anthu? (b) Kodi Yesu anayambitsa chiyani usiku wa pa Nisani 14, 33 C.E.?

YEHOVA amakonda anthu omwe iye anawalenga. Ndipotu, anawakonda anthu kwambiri “kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Pamene nthaŵi ya Chikumbutso cha imfa ya Kristu ikuyandikira, Akristu oona ayenera kuganizira kwambiri kuti Yehova “anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.”​—1 Yohane 4:10.

2 Usiku wa pa Nisani 14, 33 C.E., Yesu pamodzi ndi atumwi ake 12 anasonkhana m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu kuti achite Paskha, kukumbukira kulanditsidwa kwa Aisrayeli kuchokera ku Igupto. (Mateyu 26:17-20) Atatha kukondwerera mwambo wachiyuda umenewu, Yesu anachotsa Yudase Isikariote ndipo kenako anayambitsa mwambo wa chakudya chamadzulo chomwe chinali kudzakhala Chikumbutso chachikristu cha Imfa ya Kristu. * Mwakugwiritsa ntchito mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo wofiira monga zizindikiro zoimira thupi ndi mwazi wake, Yesu pamodzi ndi atumwi ake 11 omwe anatsala, anadyera pamodzi chakudya chimenecho. Mateyu, Marko, ndi Luka omwe analemba Mauthenga Abwino omwe amagwirizana, ndiponso mtumwi Paulo yemwe anatcha mwambowo kuti “mgonero wa Ambuye,” anatchula mwatsatanetsatane mmene Yesu anachitira chikumbutsocho.​—1 Akorinto 11:20; Mateyu 26:26-28; Marko 14:22-25; Luka 22:19, 20.

3. Kodi nkhani ya mtumwi Yohane yosimba za nthaŵi yomaliza yomwe Yesu anali ndi ophunzira ake m’chipinda chapamwamba n’njosiyana m’njira zofunika ziti ndi nkhani za olemba ena?

3 N’zochititsa chidwi kuti mtumwi Yohane sanatchule za kuyendetsa mkate ndi vinyo, mwina chifukwa chakuti panthaŵi yomwe ankalemba nkhani zake za m’Mauthenga Abwino (cha m’ma 98 C.E.), n’kuti Akristu oyambirira atazoloŵera kale kachitidwe ka chikumbutsocho. (1 Akorinto 11:23-26) Komabe mouziridwa, Yohane yekha ndiye anatchula zinthu zina zofunika kwambiri zomwe Yesu ananena ndiponso kuchita asanayambitse Chikumbutso cha imfa Yake ndiponso pambuyo pake. Nkhani zatsatanetsatane zosangalatsa zimenezi zinalembedwa m’machaputala osachepera asanu a Uthenga Wabwino wa Yohane. Machaputala ameneŵa amanena mosapita m’mbali anthu amene Mulungu amawakonda. Tiyeni tipende machaputala 13 mpaka 17 a Yohane.

Phunzirani ku Chitsanzo cha Yesu Chosonyeza Chikondi

4. Kodi Yohane anatsindika motani mfundo yaikulu ya kukumana kwa Yesu ndi ophunzira ake panthaŵi yomwe anayambitsa Chikumbutso? (b) Kodi chifukwa chimodzi chachikulu chomwe Yehova amakondera Yesu n’chotani?

4 Chikondi ndicho mbali yaikulu m’machaputala ameneŵa omwe ali ndi uphungu wotsazikirana womwe Yesu anauza otsatira ake. Ndipotu, mawu osiyanasiyana ofanana ndi akuti “chikondi” amapezeka nthaŵi 31 m’machaputala ameneŵa. Chikondi chachikulu chomwe Yesu ali nacho kwa Atate wake, Yehova, ndiponso kwa ophunzira ake chimaonekera bwino kwambiri m’machaputala ameneŵa kuposa kwina kulikonse. Chikondi chomwe Yesu ali nacho kwa Yehova chimaonekera m’nkhani zonse za m’Mauthenga Abwino zosimba za moyo wake, koma ndi Yohane yekha yemwe analemba kuti Yesu ananena mosapita m’mbali kuti: “Ndikonda Atate.” (Yohane 14:31) Yesu ananenanso kuti Yehova amamukonda ndipo anafotokoza chifukwa chake. Anati: “Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m’chikondi changa. Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m’chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m’chikondi chake.” (Yohane 15:9, 10) Inde, Yehova amakonda Mwana wake chifukwa cha kumvera kwake. Limenelitu ndi phunziro labwino kwambiri kwa onse otsatira Yesu Kristu.

5. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti ankakonda ophunzira ake?

5 Chikondi chachikulu chomwe Yesu ali nacho kwa otsatira ake chinaonekeratu koyambirira kwenikweni kwa nkhani ya Yohane yosimba za kukumana komaliza kwa Yesu ndi atumwi ake. Yohane anasimba kuti: “Koma pasanafike phwando la Paskha, Yesu, podziŵa kuti nthaŵi yake idadza yakuchoka kutuluka m’dziko lino lapansi, kumka kwa Atate, mmene anakonda ake a Iye yekha a m’dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.” (Yohane 13:1) Usiku wosaiŵalika umenewo iye anawapatsa phunziro losaiŵalika la kutumikira ena mwachikondi. Iye anasambitsa mapazi awo. Zimenezi n’zimene aliyense wa iwo akanayenera kufunitsitsa kuchitira Yesu ndi abale awo, koma iwo sanatero. Yesu anachita ntchito yonyozeka imeneyi ndipo kenako anauza ophunzira ake kuti: “Ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.” (Yohane 13:14, 15) Akristu oona ayenera kukhala ofunitsitsa ndiponso okondwa kutumikira abale awo.​—Mateyu 20:26, 27; Yohane 13:17.

Tsatirani Lamulo Latsopano

6, 7. (a) Kodi Yohane anatchula mfundo zatsatanetsatane zofunika zotani zokhudza kuyambitsa Chikumbutso? (b) Kodi ndi lamulo latsopano lotani lomwe Yesu anapatsa ophunzira ake, ndipo kodi pa lamulo limenelo chachilendo chinali chiyani?

6 Nkhani ya Yohane yokha yosimba zomwe zinachitika m’chipinda chapamwamba usiku wa pa Nisani 14 ndiyo imatchula mwachindunji kuchoka kwa Yudase Isikariote. (Yohane 13:21-30) Kugwirizanitsa nkhani za m’Mauthenga Abwino kumasonyeza kuti Yesu anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake wom’perekayo atachoka. Kenako analankhula zambiri ndi atumwi ake okhulupirikawo, kuwapatsa uphungu ndi malangizo otsazikirana nawo. Pamene ife tikukonzekera kudzafika pa Chikumbutso, tifunika kukhala ndi chidwi chachikulu ndi zomwe Yesu ananena pamwambowo, makamaka chifukwa chakuti tikufunitsitsa kukhala m’gulu la anthu amene Mulungu amawakonda.

7 Langizo loyamba lomwe Yesu anauza ophunzira ake atayambitsa Chikumbutso cha imfa yake linali latsopano. Iye anati: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35) Kodi chachilendo chinali chiyani palamulo limeneli? Patangopita nthaŵi pang’ono usiku umenewo, Yesu anafotokoza momveka bwino lamulolo. Anati: “Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.” (Yohane 15:12, 13) Chilamulo cha Mose chinkalamula Aisrayeli ‘kukonda mnansi monga adzikonda okha.’ (Levitiko 19:18) Koma lamulo la Yesu linaposa pamenepo. Akristu anayenera kukondana monga momwe Kristu anawakondera, kukhala ofunitsitsa kufera abale awo.

8. (a) Kodi chikondi chodzimana chimaphatikizapo chiyani? (b) Kodi Mboni za Yehova zimasonyeza motani chikondi chodzimana lerolino?

8 Nyengo ya Chikumbutso ndi nthaŵi yabwino kwambiri yodzipenda aliyense payekha, ndiponso monga mpingo, kuti tione ngati tili nacho chikondi chonga cha Kristu chomwe ndi chizindikiro cha Chikristu choona. Chikondi chodzimana chimenechi chingafune kuti Mkristu alolere kutaya moyo wake m’malo mopereka abale ake, ndipo nthaŵi zina, zachitikadi motero. Komabe nthaŵi zambiri, chikondi chimenechi chimaphatikizapo kulolera kudzimana zinthu zomwe timazifuna kuti tithandize ndiponso kutumikira abale athu ndi anthu ena. Mtumwi Paulo anali chitsanzo chabwino kwambiri pankhani imeneyi. (2 Akorinto 12:15; Afilipi 2:17) Mboni za Yehova n’zodziŵika padziko lonse chifukwa cha mzimu wawo wodzimana kuti zithandize abale awo ndiponso anansi awo. Zimadzipereka kuuza anthu ena choonadi cha m’Baibulo. *​—Agalatiya 6:10.

Ubale Wofunika Kuusamalira

9. Kodi timasangalala kuchitanji kuti tisungebe ubale wathu wamtengo wapatali ndi Mulungu komanso ndi Mwana wake?

9 Palibe chinthu chamtengo wapatali kwa ife kuposa kukondedwa ndi Yehova ndiponso Mwana wake Kristu Yesu. Komabe, kuti tikondedwe tifunika kuchitapo kanthu. Usiku womaliza uja womwe Yesu anali ndi ophunzira ake, anati: “Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzam’konda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.” (Yohane 14:21) Popeza kuti timaona ubale wathu ndi Mulungu ndiponso ndi Mwana wake kukhala wamtengo wapatali, timasangalala kumvera malamulo awo. Ena mwa malamulo amenewo ndi lamulo latsopano losonyeza chikondi chodzimana ndiponso lamulo lomwe Kristu anapereka ataukitsidwa la ‘kulalikira kwa anthu ndiponso kuchitira umboni,’ kuyesetsa kupanga anthu amene amalandira uthenga wabwino kukhala ophunzira.​—Machitidwe 10:42; Mateyu 28:19, 20.

10. Kodi ndi ubale wamtengo wapatali wotani umene odzozedwa ndiponso a “nkhosa zina” angakhale nawo?

10 Kenako usiku womwewo, Yesu poyankha funso la mtumwi wake wokhulupirika Yudase (Tadeyo) anati: “Ngati wina akonda Ine, adzasunga mawu anga; ndipo Atate wanga adzam’konda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.” (Yohane 14:22, 23) Ngakhale pamene akadali pompano padziko lapansi, Akristu odzozedwa oitanidwa kukalamulira ndi Kristu kumwamba, amakhala paubale wapafupi kwambiri ndi Yehova ndiponso Mwana wake. (Yohane 15:15; 16:27; 17:22; Ahebri 3:1; 1 Yohane 3:2, 24) Komanso anzawo a “nkhosa zina” omwe akuyembekeza kudzakhala padziko lapansi kosatha, nawonso amakhala ndi ubale wamtengo wapatali ndi ‘mbusa wawo m’modzi,’ Yesu Kristu, ndiponso ndi Mulungu wawo, Yehova, malinga ngati akhala omvera.​—Yohane 10:16; Salmo 15:1-5; 25:14.

“Simuli a Dziko Lapansi”

11. Kodi ndi chenjezo lofunika kuganizapo lotani lomwe Yesu anapereka kwa ophunzira ake?

11 Panthaŵi yomalizayi yomwe Yesu anakumana ndi ophunzira ake okhulupirika iye asanaphedwe, anapereka chenjezo lofunika kuganizapo lakuti: Ngati munthu akukondedwa ndi Mulungu ndiye kuti dziko lidzamuda. Iye anati: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziŵa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu. Kumbukirani mawu amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mawu anga, adzasunga anunso.”​—Yohane 15:18-20.

12. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti dziko lidzawada? (b) Kodi tonsefe tiyenera kuganizira chiyani pamene Chikumbutso chikuyandikira?

12 Yesu anapereka chenjezo limeneli kuti atumwi ake 11 ameneŵa ndiponso Akristu onse oona omwe adzakhaleko m’tsogolo asadzakhumudwe ndi kusiya chifukwa choti dziko likuwada. Iye anapitiriza kuti: “Izi ndalankhula ndi inu kuti mungakhumudwitsidwe. Adzakutulutsani m’masunagoge; koma ikudza nthaŵi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu. Ndipo izi adzachita, chifukwa sanadziŵa Atate, kapena Ine.” (Yohane 16:1-3) Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo limanena kuti, mtundu wa mneni amene anamasulidwa pano kuti ‘khumudwitsidwa’ amatanthauza “kuchititsa munthu kuyamba kusakhulupirira ndi kunyalanyaza munthu yemwe ayenera kumukhulupirira ndiponso kum’mvera; kumuchititsa kusiya kukhulupirira.” Pamene nthaŵi ya Chikumbutso ikuyandikira, tonsefe tiyenera kuganizira moyo wa anthu okhulupirika akale ndiponso a masiku ano, ndi kutsanzira chitsanzo chawo chokhalabe okhulupirika panthaŵi ya chiyeso. Musalole chitsutso kapena chizunzo kukuchititsani kusiya Yehova ndi Yesu, koma khalani wotsimikiza mtima kuwakhulupirira ndi kuwamvera.

13. Kodi Yesu anawapemphera chiyani otsatira ake m’pemphero kwa Atate wake?

13 Yesu m’pemphero lake lomaliza kwa Atate wake asanatuluke m’chipinda chapamwamba mu Yerusalemu anati: “Ine ndawapatsa iwo mawu anu; ndipo dziko lapansi linadana nawo, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi. Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:14-16) Tikutsimikiza kuti Yehova amasunga anthu amene amamukonda, amawapatsa mphamvu pamene akupitirizabe kukhala olekana ndi dziko.​—Yesaya 40:29-31.

Khalanibe M’chikondi cha Atate ndi M’chikondi cha Mwana

14, 15. (a) Kodi Yesu anadzifanizira ndi chiyani, ndipo mosiyana ndi ‘mpesa wopanda pake’ uti? (b) Kodi “nthambi” za “mpesa weniweni” ndani?

14 Panthaŵi yomwe Yesu anali kulankhula ndi ophunzira ake okhulupirika usiku wa pa Nisani 14, iye anadzifanizira ndi “mpesa weniweni” mosiyana ndi Israyeli wosakhulupirika yemwe anali ‘mpesa wopanda pake.’ Yesu anati: “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam’munda.” (Yohane 15:1) Zaka mazana ambiri mmbuyomo, mneneri Yeremiya analemba mawu omwe Yehova ananena kwa anthu ake osakhulupirikawo kuti: “Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, . . . kodi bwanji wandisandukira Ine mbewu yopanda pace, ya mpesa wachilendo?” (Yeremiya 2:21) Ndipo mneneri Hoseya analemba kuti: “Israyeli ndi mpesa wotambalala, [“wopanda pake,” NW] wodzibalira wokha zipatso. . . . Mtima wawo wagaŵikana.”​—Hoseya 10:1, 2.

15 M’malo mobala zipatso za kulambira koona, Israyeli anatsatira mpatuko ndipo anadzibalira yekha zipatso. Kutatsala masiku atatu kuti Yesu akumane ndi ophunzira ake okhulupirika, iye anauza atsogoleri achiyuda achinyengowo kuti: “Ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.” (Mateyu 21:43) Anthu atsopano amenewo ndiwo “Israyeli wa Mulungu,” wopangidwa ndi Akristu odzozedwa okwanira 144,000 ndipo ali ngati nthambi za “mpesa weniweni,” Kristu Yesu.​—Agalatiya 6:16; Yohane 15:5; Chivumbulutso 14:1, 3.

16. Kodi Yesu anawalimbikitsa kuchita chiyani atumwi 11 okhulupirika aja, ndipo kodi tinganene chiyani za otsalira okhulupirika m’masiku otsiriza ano?

16 Yesu anauza atumwi 11 omwe anali naye m’chipinda chapamwamba chija kuti: “Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, [“aitengulira,” NW] kuti ikabale chipatso chochuluka. Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.” (Yohane 15:2, 4) Mbiri yamakono ya Mboni za Yehova imasonyeza kuti otsalira okhulupirika a Akristu odzozedwa akhalabe ogwirizana ndi Mutu wawo, Kristu Yesu. (Aefeso 5:23) Iwo avomereza kuyeretsedwa ndi kutenguliridwa. (Malaki 3:2, 3) Kuyambira mu 1919, iwo abala zipatso za Ufumu zochuluka, kuyamba ndi Akristu odzozedwa owonjezera, kenako, kuchokera mu 1935, anzawo a “khamu lalikulu” lomwe likuwonjezekabe.​—Chivumbulutso 7:9; Yesaya 60:4, 8-11.

17, 18. (a) Kodi ndi mawu ati a Yesu amene amathandiza odzozedwa ndiponso a nkhosa zina kukhalabe m’chikondi cha Yehova? (b) Kodi kufika pa Chikumbutso kudzatithandiza motani?

17 Yesu anapitiriza kunena mawu omwe amagwira ntchito kwa Akristu odzozedwa ndi anzawo. Iye anati: “Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga. Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m’chikondi changa. Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m’chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m’chikondi chake.”​—Yohane 15:8-10.

18 Tonsefe timafuna kukhalabe m’chikondi cha Mulungu, ndipo zimenezi zimatilimbikitsa kukhala Akristu obala zipatso. Timachita zimenezi mwa kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kulalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mateyu 24:14) Komanso timayesetsa kusonyeza “chipatso cha Mzimu” m’miyoyo yathu. (Agalatiya 5:22, 23) Kufika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu kudzatilimbikitsa kuchita zimenezi motsimikiza kwambiri chifukwa tidzakumbutsidwa za chikondi chachikulu chomwe Mulungu ndi Kristu ali nacho kwa ife.​—2 Akorinto 5:14, 15.

19. Kodi m’nkhani yotsatira tikambirana thandizo lowonjezereka lotani?

19 Yesu atayambitsa Chikumbutso, analonjeza kuti Atate wake adzawatumizira otsatira ake okhulupirika ‘nkhoswe, Mzimu Woyera.’ (Yohane 14:26) M’nkhani yotsatirayi tiona mmene mzimu umenewu umathandizira odzozedwa ndiponso a nkhosa zina kukhalabe m’chikondi cha Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Potsatira kaŵerengedwe ka Baibulo, Nisani 14 ya chaka chino cha 2002 idzayamba Lachinayi, March 28, dzuŵa likuloŵa. Usiku umenewo, Mboni za Yehova padziko lonse zidzasonkhana kukumbukira imfa ya Ambuye, Yesu Kristu.

^ ndime 8 Onani machaputala 19 ndi 32 m’buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Mafunso Obwereramo

• Kodi ndi phunziro lothandiza lotani la utumiki wachikondi lomwe Yesu anapatsa ophunzira ake?

• Kodi nthaŵi ya Chikumbutso n’njoyenera kudzipenda poganizira za chiyani?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhumudwa ndi chenjezo la Yesu lakuti dziko lidzatida ndiponso kutizunza?

• Kodi “mpesa weniweni” ndani? Nanga “nthambi” zake ndani, ndipo ziyenera kuchita chiyani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Yesu anapatsa atumwi ake phunziro losaiŵalika pankhani yotumikira ena mwachikondi

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Ophunzira a Kristu amamvera lamulo lake losonyeza chikondi chodzimana