Kodi Ukhondo Ndi Wofunika Motani?
Kodi Ukhondo Ndi Wofunika Motani?
ANTHU amatanthauzira ukhondo mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mayi akauza mwana kuti asambe m’manja ndi kusukusula kumaso, mwanayo angaganize kuti kuika zala zake m’madzi amene akutuluka pa mpope ndi kunyoŵetsa milomo yake n’zokwanira. Koma Mayi amadziŵa bwino. Amamutenga n’kubwerera naye ku bafa ndipo amam’sambitsa m’manja ndi kumaso ndi sopo komanso madzi ambiri ngakhale kuti mwanayo angalire pokana kusukusula.
N’zoona kuti miyezo ya ukhondo si yofanana padziko lonse, ndipo anthu amakula ndi maganizo osiyana pa nkhani ya ukhondo. Kale m’mayiko ambiri, malo a pasukulu aukhondo ndiponso ooneka bwino amathandiza ophunzira kukhala aukhondo. Lerolino, mabwalo amaseŵero a sukulu zina ndi odzala ndi zinyalala ndipo amafanana ndi kudzala osati monga mabwalo ochezera kapena ochitirako masewero olimbitsa thupi. Nanga bwanji m’kalasi? Darren, yemwe amasamalira pa sukulu ina ya sekondale ku Australia anati: “Tsopano ndi m’makalasi momwe ndi mwa uve.” Ophunzira ena akauzidwa kuti “Tolani zinyalala” kapena “Yeretsani,” amaona ngati ndi chilango. Vuto n’lakuti aphunzitsi ena amagwiritsa ntchito kuyeretsa monga njira yolangira ophunzira.
Komanso, anthu achikulire sapereka zitsanzo zabwino zaukhondo nthaŵi zonse, kaya pa moyo wa tsiku ndi tsiku kapena pankhani za malonda. Mwachitsanzo, malo ambiri a anthu onse ndi oipa ndiponso osaoneka bwino. Mafakitale ena amaipitsa malo okhala. Komabe, anthu ndi amene amachititsa malo kukhala oipa osati mafakitale kapena malonda omwe sadziŵa kanthu. Ngakhale kuti vuto la padziko lonse limeneli la kuipitsa malo ndi zotsatira zake zoŵaŵa limachitika makamaka chifukwa cha dyera, mbali ina ya vutoli imachitika chifukwa cha uve wa munthu payekha. Mkulu wa bungwe la Commonwealth wakale wa ku Australia anavomereza mfundo imeneyi pamene anati: “Nkhani zonse zokhudza umoyo wa anthu zimayambira pa ukhondo wa munthu aliyense payekha.”
Komabe, ena amaganiza kuti ukhondo ndi nkhani ya munthu aliyense payekha ndipo wina aliyense zisamukhudze. Kodi zimenezi n’zoona?
Ukhondo ndi wofunika kwambiri pankhani ya chakudya—kaya tagula pamsika, tikudya mu lesitilanti, kapena tikudya kunyumba kwa mnzathu. Okonza ndi kuperekera chakudyacho afunika kukhala aukhondo kwambiri. Manja a litsiro a anthu okonza ndi kuperekera chakudyacho kapena a ife amene tikudya, angayambitse matenda ambiri. Bwanji za zipatala—malo amene
timayembekezera kuti ayenera kukhala aukhondo kuposa malo ena alionse? Magazini ina yakuti The New England Journal of Medicine inanena kuti kusasamba m’manja kwa madokotala ndi manesi kungakhale chifukwa chimene odwala ambiri kuchipatala amakhala ndi matenda opatsirana amene amafunika ndalama zokwana madola mabiliyoni khumi pachaka kuti achize matendawo. M’pake kuti timafuna kuti wina asaike pangozi thanzi lathu chifukwa cha uve wake.Imakhalanso ngozi yaikulu kwambiri munthu wina akaipitsa madzi amene timagwiritsa ntchito kaya mwadala kapena chifukwa chakuti sanakhale kaye pansi n’kuganiza. Ndiponso kodi munthu angakhale wotetezeka kuyenda opanda nsapato m’mbali mwa nyanja m’mene muli majekeseni akutha ntchito amene anthu okonda mankhwala osokoneza bongo ndi ena anataya? Mwinanso funso lofunika kwambiri kwa munthu aliyense payekha n’lakuti: Kodi ndife aukhondo kunyumba kwathu?
Suellen Hoy, m’buku lake lakuti Chasing Dirt, anafunsa kuti: “Kodi ndife aukhondo monga mmene tinalili m’mbuyomo?” Anayankha kuti: “Ayi.” Iye ananena kuti chifukwa chachikulu chimene chachititsa zimenezi ndicho kusintha kwa miyezo ya makhalidwe. Anthu akakhala kuti sakhalakhala panyumba, amangolemba ntchito munthu wina kuti aziwayeretsera. Zotsatira zake n’zakuti anthu sakuona ngati kuyeretsa malo kuti akhale aukhondo nthaŵi zonse n’kofunika kwambiri. Mwamuna wina anati: “Sinditsuka bafa koma ineyo ndimasamba. Malinga ngati ine ndizioneka bwino ngakhale nyumba yanga ikhale yosaoneka bwino.”
Komabe, ukhondo umatanthauza zambiri osati maonekedwe akunja okha ayi. Umaphatikizapo kakhalidwe kabwino. Umaphatikizaponso mmene maganizo ndi mtima wathu zilili zimene zimakhudza makhalidwe athu ndi kulambira kwathu. Tiyeni tione mmene zimenezi zilili choncho.