Kodi Ukhondo Umatanthauza Chiyani Makamaka?
Kodi Ukhondo Umatanthauza Chiyani Makamaka?
AMISHONALE a zaka za m’ma 1700 ndi m’ma 1800 ankalalikira chimene tingati “chiphunzitso cha ukhondo” chifukwa cha uve wodetsa nkhaŵa umene unali ku Ulaya ndi ku United States nthaŵi imeneyo. Chiphunzitso chimenechi chinkanena kuti uve uli ngati uchimo, pamene ukhondo umachititsa munthu kuyandikira kwa Mulungu. Mwina zimenezi n’zimene zinachititsa kuti mwambi woti “Ukhondo umayendera limodzi ndi umulungu” ukhale wotchuka kwambiri.
Mpingo wa Salvation Army umene William ndi Catherine Booth anauyambitsa, unalimbikitsa mfundo imeneyo. Malinga ndi buku lakuti Health and Medicine in the Evangelical Tradition, mawu awo ozoloŵereka oyambirira anali akuti: “Sopo, Msuzi, ndi Chipulumutso.” Ndiyeno, Louis Pasteur ndi ena atatsimikizira kuti matenda amayamba ndi tizilombo ta mabakiteriya, ukhondo unapita patsogolo ndipo panali maziko a sayansi okonza mfundo zopititsira patsogolo ukhondo wa anthu onse.
Nthaŵi yomweyo anayamba kutsatira njira zopititsira patsogolo ukhondo monga kuleka zoti wopereka umboni ku khoti azipsopsona Baibulo ndiponso kuletsa zomwera kapu imodzi pa sukulu kapena pa siteshoni za sitima. Anasinthanso zomwera kapu imodzi pa mwambo wa mgonero wa Ambuye ku tchalitchi ndipo aliyense anafunika kukhala ndi kapu yake. Inde, anthu oyamba kulimbikitsa ukhondo ameneŵa anaoneka kuti zinawayendera
bwino posintha maganizo a anthu pankhani ya ukhondo. Anthu anasinthadi maganizo moti wolemba wina anati zotsatira zake zinali zakuti anthu “anakonda kwambiri ukhondo.”Komabe mwachionekere, ‘kukonda kwambiri ukhondo’ kumeneko sikunapite patali. Posapita nthaŵi, a zamalonda anatengerapo mwayi pa zinthu zimene zinkagwiritsidwa ntchito tsiku ndi tsiku monga sopo n’kuzisintha kukhala zinthu zodzikongoletsera. Kutsatsa malonda kokopa kunachititsa anthu kukhulupirira kuti zinthu zina zogwiritsa ntchito pa ukhondo wa munthu payekha zingam’chititse munthuyo kukhala wotsogola, ena n’kumamusirira. Mawailesi a kanema amalimbikitsa maganizo ongoyerekezera ameneŵa. Anthu otchuka ndi ooneka ngati otsogola amene amawaonetsa pa nkhani zamalonda ndi m’zisudzo nthaŵi zambiri saoneka akuyeretsa panyumba, kusesa pabwalo, kutola zinyalala, kapena kuchotsa ndoŵe za amphaka kapena agalu awo.
Ndiye palinso ena amene amanena kuti kukagwira ntchito kwina kumathandiza kulipirira chilichonse, pamene ntchito ya panyumba kapena ntchito zina zoyeretsa sizipezetsa ndalama. Ndipo popeza kuti palibe phindu la ndalama, angadzivutitsirenji kusamalira malo okhala? Chimodzi mwa zotsatira za maganizo ameneŵa n’chakuti anthu ena masiku ano amaganiza kuti ukhondo umatanthauza kudzisamalira munthuwe basi.
Mmene Mulungu Amaonera Ukhondo
Palibe amene angakayike kuti ntchito yoyambirira yophunzitsa ukhondo imeneyo inathandizadi kutukula miyoyo ya anthu. Ndipotu m’pake kutero, chifukwa ukhondo ndilo khalidwe la Mulungu woyera ndi waukhondo, Yehova, ndipo ndi iye amene analiyambitsa. Amatiphunzitsa kuti tipindule mwa kukhala oyera ndi aukhondo m’njira zathu zonse.—Yesaya 48:17; 1 Petro 1:15.
Yehova Mulungu ndi chitsanzo chabwino pankhani imeneyi. Ukhondo ndiponso makhalidwe ake ena osaoneka tikutha kuwaona m’zinthu zimene iye analenga. (Aroma 1:20) Tingaone kuti chilengedwe sichiyambitsa kuipitsa malo kokhalitsa. Dziko lapansi pamodzi ndi zinthu zamoyo zimene zilimo zimadziyeretsa zokha modabwitsa, ndipo dzikoli analikonza kuti zinthu zizikhalamo mwaukhondo. Ukhondo umenewu ungachokere kwa Wokonza waukhondo yekha basi. Motero, tikuona kuchokera pa zimenezi kuti olambira Mulungu afunika kukhala aukhondo m’mbali zonse za moyo wawo.
Mbali Zinayi za Ukhondo
Baibulo limatchula mbali zinayi za ukhondo zimene olambira Mulungu afunika kuyesetsa kuzitsatira. Tiyeni tizipende mbali zimenezi imodzi ndi imodzi.
Ukhondo Wauzimu. Imeneyi ndi mbali ya ukhondo yofunika kwambiri kuposa ina iliyonse chifukwa ndi imene ingachititse munthu kudzapeza moyo wosatha. Komabe, nthaŵi zambiri imeneyi ndi mbali yaukhondo imene anthu amainyalanyaza kuposa ina iliyonse. Kunena mwachidule, kukhala waukhondo mwauzimu kumatanthauza kusadumpha malire amene Mulungu waika pakati pa kulambira koona ndi konyenga, chifukwa Mulungu amaona kulambira kulikonse konyenga kukhala kodetsedwa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; Ndipo Ine ndidzalandira inu.” (2 Akorinto 6:17) Wophunzira Yakobo anafotokozanso mosapita m’mbali pa mfundo imeneyi pamene anati: “Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: . . . kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.”—Yakobo 1:27.
Mulungu anatsutsa poyera kuphatikiza kulambira konyenga ndi kulambira koona. Kulambira konyenga nthaŵi zambiri kumaphatikizapo khalidwe loipa ndi mafano ndi milungu yonyansa. (Yeremiya 32:35) N’chifukwa chake Akristu akulimbikitsidwa kupeŵa kukhudzidwa ndi kulambira kulikonse kodetsa.—1 Akorinto 10:20, 21; Chivumbulutso 18:4.
Ukhondo wa Makhalidwe. Pa mfundo iyinso, Mulungu akusiyanitsa bwinobwino makhalidwe oyera ndi oipa. Anthu ambiri m’dziko lapansi masiku ano afika pa mlingo umene wafotokozedwa pa Aefeso 4:17-19 kuti: “Odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, . . . amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo.” Kuganiza konyansa kumeneko kumaonekera m’njira zambiri, zoonekera ndiponso zobisika, n’chifukwa chake Akristu afunika kukhala osamala.
Anthu okonda Mulungu amadziŵa kuti uhule, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, kugonana ukwati usanachitike, ndiponso kuonera zolaula n’kuswa miyezo ya Yehova ya ukhondo wa makhalidwe. Komabe, makhalidwe oipa ameneŵa ali ponseponse m’nkhani za zosangalatsa ndi za mafashoni. Motero, Akristu afunika kusamala kupeŵa makhalidwe ameneŵa. Kuvala chovala chachifupi kapena chovala choonetsa m’kati ku misonkhano yachikristu kapena pamalo amene Akristu akucheza pamodzi kumachititsa kuti ena ayang’anitsitse thupi la munthuyo mosayenera ndipo zimasonyeza kuti munthuyo sanaonetse khalidwe loyera. Kuphatikiza pa kubweretsa maganizo oipa a kudziko pamalo pamene pali Akristu, kuvala kotero kungachititsenso ena kuganizira zoipa. Imeneyi ndi mbali imene Akristu afunika kuyesetsa posonyeza “nzeru yochokera kumwamba.”—Yakobo 3:17.
Ukhondo wa maganizo. M’kati mwa maganizo athu simufunika kukhala malo osungiramo malingaliro oipa. Yesu anachenjeza za kuganizira zoipa pamene anati: “Yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28; Marko 7:20-23) Mawu ameneŵa akugwiranso ntchito chimodzimodzi pankhani yoonera zithunzi ndi mafilimu oonetsa zamaliseche, kuŵerenga nkhani zonena za kugonana konyansa, ndi kumvetsera nyimbo za mawu odzutsa chilakolako choipa. Motero, Akristu ayenera kupeŵa kudzidetsa mwa kukhala ndi maganizo oipa amene angayambitse kulankhula kapena kuchita zinthu zosayenera.—Mateyu 12:34; 15:18.
Ukhondo wakuthupi. M’Baibulo, chiyero ndi ukhondo wakuthupi n’zogwirizana kwambiri. Mwachitsanzo, Paulo analemba kuti: “Okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Motero, Akristu oona afunika kuyesetsa kuti thupi lawo, nyumba yawo, ndi pamalo pamene iwo ali, zizikhala zoyera ndi zaudongo malinga ndi mmene angathere. Ngakhale kumene madzi osamba kapena ochapira ndi osoŵa, Akristu afunika kuyesetsa mmene angathere kuti akhale aukhondo ndiponso ooneka bwino.
Kuti munthu akhale waukhondo mwakuthupi, afunikanso kupeŵa kugwiritsa ntchito fodya kwa mtundu uliwonse, kuledzera, ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Zinthu zimenezi zimaipitsa ndi kuwononga thupi. Mbusa amene akufotokozedwa m’Nyimbo ya Solomo anasangalala ndi fungo labwino la zovala za mtsikana wa ku Sulami. (Nyimbo ya Solomo 4:11) N’kwabwino kwambiri kusamala thupi lathu pofuna kupeŵa kuwanunkhitsa anthu amene tili nawo pafupi. Mafuta onunkhira angakhale abwino kwambiri, koma sayenera kuloŵa m’malo mwa kusamba ndi kuchapa zovala nthaŵi zonse.
Kukhala Wosamala
Anthu angapitirire muyeso pankhani ya ukhondo wakuthupi. Kukhala opambanitsa pankhani ya ukhondo kungatichititse kusasangalala ndi
moyo. Kungatidyerenso nthaŵi yathu ya mtengo wapatali. Komanso, nyumba ya uve ndi yosasamalika ingafune ndalama zambiri kuti tiikonzetse. M’malo mokhala opambanitsa kapena auve, pali njira zabwino zochititsa kuti panyumba pathu pakhale paukhondo ndi pooneka bwino.Musachulutse zinthu m’nyumba. M’nyumba kapena m’chipinda mmene zinthu zangoti mbwee, mumavuta kuyeretsa ndipo fumbi silingaoneke bwino m’malo ochuluka zinthu ngati amenewo. M’nyumba mmene mulibe zinthu zambiri simuvuta kukonza. Baibulo limalimbikitsa moyo wosalira zambiri pamene linati: “Pokhala nazo zakudya ndi zopfunda, zimenezi zitikwanire.”—1 Timoteo 6:8.
Ikonzeni kukhala yaudongo. Anthu onse amene amakhala m’nyumbamo ali ndi udindo wokonza nyumbayo kuti izikhala yaukhondo. Nthaŵi zambiri zimayamba ndi zipinda kukhala zosasamalika kenako nyumba yonseyo imakhala yopanda udongo. Udongo umatanthauza kuti chilichonse chili m’malo mwake. Mwachitsanzo, sibwino kuika zovala zakuda pansi m’chipinda chogona. Ndiponso sibwino kuika zidole ndi zida zogwirira ntchito pena paliponse chifukwa zimenezi zitha kuchititsa ngozi. Ngozi zambiri za panyumba zimachitika chifukwa chosoŵa udongo.
Inde, ukhondo ndi wogwirizana ndi moyo wachikristu. Pofotokoza za moyo wotsatira malangizo a Mulungu, mneneri Yesaya ananena za “njira yopatulika.” Ndiyeno anawonjezera mfundo yofuna kuganizapo yakuti, “audio [“auve,” NW] sadzapita mmenemo.” (Yesaya 35:8) Inde, kukhala aukhondo pakalipano kumapereka umboni wamphamvu wa chikhulupiriro chathu m’malonjezo a Mulungu akuti posachedwapa adzakhazikitsa dziko lapansi la paradaiso laukhondo. Ndiyeno, anthu onse adzalemekeza Yehova Mulungu m’mbali zonse za dziko lokongolali mwa kutsatira kotheratu miyezo yake yangwiro yaukhondo.—Chivumbulutso 7:9.
[Chithunzi patsamba 6]
Anthu onse amene amakhala m’nyumbamo ali ndi udindo wokonza nyumbayo kuti ikhale yaukhondo
[Chithunzi patsamba 7]
Dziko lapansi limadziyeretsa lokha modabwitsa