Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi malamulo oletsa ukwati wa pachibale amene ali m’Chilamulo cha Mose amagwira ntchito kwa Akristu lerolino pa mlingo wotani?
Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisrayeli sichinafotokoze zambiri zokhudza miyambo ya ukwati ndi kachitidwe kake. Komabe, chilamulocho chimaletsa maukwati ena. Mwachitsanzo, pa Levitiko 18:6-20, timapeza mndandanda wa kugonana koletsedwa kwa ‘anthu a pachibale choyandikana,’ NW. Malemba ameneŵa akufotokoza mwatsatanetsatane anthu apachibale amene sayenera kukhalira malo amodzi. N’zoona kuti Akristu satsatira Chilamulo cha Mose kapena kumangika ndi malamulo a m’menemo. (Aefeso 2:15; Akolose 2:14) Koma ngakhale zili choncho, sizikutanthauza kuti Akristu angangonyalanyaza nkhani imeneyi posankha munthu woti akwatirane naye. Pali zifukwa zingapo zimene sangachitire zimenezo.
Choyamba, mayiko ali ndi malamulo okhudza ukwati wa anthu apachibale choyandikana, ndipo Akristu afunika kumvera malamulo a m’dziko limene akukhala. (Mateyu 22:21; Aroma 13:1) Malamulo ameneŵa amasiyanasiyana m’mayiko ambiri. Malamulo ambiri amakono okhudza nkhani imeneyi awakhazikitsa makamaka poganizira za majini. Tikudziŵa kuti ana amene angabadwe kwa anthu a pachibale choyandikana amene akwatirana, angakhale pangozi yobadwa ndi zilema kapena matenda obadwa nawo. Pa chifukwa chimenechi, ndiponso chifukwa chakuti afunika ‘kumvera maulamuliro aakulu,’ Akristu amene akufuna kukwatirana amamvera malamulo a m’dziko limene akukhala.
Ndiyeno pali mfundo ya zimene zili zololeka ndi zosaloleka m’dera limene munthu akukhala. Pafupifupi m’chikhalidwe chilichonse muli malamulo ndi miyambo yoletsa ukwati wa anthu a pachibale choyandikana kwambiri, ndipo nthaŵi zambiri amakuona kukwatirana koteroko kuti n’kulaula, motero amaletsa ukwati wotero. Ngakhale kuti zikhalidwe zosiyanasiyana zili ndi malamulo osiyana oletsa maukwati apachibale, “m’zikhalidwe zambiri, anthuwo akakhala a pachibale choyandikana kwambiri, malamulo owaletsa kukhalira malo amodzi amakhalanso okhwima kwambiri,” limatero buku lakuti The Encyclopædia Britannica. Motero, ngakhale kuti atakhalira pamodzi sikungakhale kulaula, Akristu safunika kunyalanyaza miyambo yonse kapena zinthu zimene anthu a kumalo kumene akukhala amaziona kuti n’zosayenera, kuti asatonzetse mpingo wachikristu kapena dzina la Mulungu.—2 Akorinto 6:3.
Chikumbumtima chimene Mulungu anatipatsa sitifunikanso kuchinyalanyaza. Anthu onse amabadwa ali ndi maganizo a chimene chili choyenera ndi chosayenera, chabwino ndi choipa. (Aroma 2:15) Chikumbumtima chawo chimawauza zimene zili zoyenera ndi zimene zili zosayenera kapena zolakwika, ndipo sichingatero kokha ngati achiwononga kapena kuchipha chifukwa chochita zoipa mobwerezabwereza. Yehova anatchula mfundo imeneyi pamene anapatsa Aisrayeli lamulo lake loletsa kukwatirana kwa anthu a pachibale choyandikana kwambiri. Timaŵerenga kuti: “Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Aigupto, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m’malemba awo.” (Levitiko 18:3) Akristu amatsatira chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo ndipo salola kuti chinyengedwe ndi maganizo olakwika a chabwino ndi choipa amene anthu amitundu ali nawo.—Aefeso 4:17-19.
Kodi tapeza mfundo yotani pa zimene takambiranazi? Ngakhale kuti Akristu satsatira Chilamulo cha Mose, chikumbumtima chawo chimawauza mosapita m’mbali kuti kukwatirana kwa anthu apachibale choyandikana kwambiri—monga bambo ndi mwana wawo wamkazi, mayi ndi mwana wawo wamwamuna, mchimwene ndi mlongo wake—n’kosaloleka n’pang’ono pomwe kwa Akristu. * Chikakhala kuti chibalecho sichoyandikana kwambiri, Akristu amazindikira kuti pali malamulo a m’dziko limene akukhala onena za ukwati wovomerezeka. Ndiponso amazindikira kuti pali miyezo imene anthu a m’dera limene iwo akukhala amaona kuti ndi yoyenera ndiponso yogwirizana ndi chikhalidwe chawo. Zimenezi n’zofunika kuziganizira kwambiri kuti tigwirizane ndi langizo la m’Malemba lakuti: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse.”—Ahebri 13:4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Onani nkhani yakuti, “Kodi Akristu Afunika Kuona Motani Maukwati Osayenera?” mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya March 15, 1978, masamba 25-6. Pamenepo tinafotokoza mwatsatanetsatane nkhani imeneyi.