Okonzeka Mokwanira Kukhala Aphunzitsi a Mawu a Mulungu
Okonzeka Mokwanira Kukhala Aphunzitsi a Mawu a Mulungu
“Mulungu . . . anatikwaniritsa ife tikhale atumiki.”—2 AKORINTO 3:5, 6.
1, 2. Kodi matchalitchi ena nthaŵi zina ayesayesa kuchita chiyani pankhani yolalikira, koma n’chifukwa chiyani zimenezo zimalephereka nthaŵi zambiri?
KODI mungamve bwanji mutapatsidwa ntchito yoti mugwire yomwe simudziŵa kugwira kwake? Taganizani izi: Zinthu zofunikira pantchitoyo akupatsani ndipo zipangizo zogwirira ntchitoyo zilipo zonse. Koma simukudziŵa n’ pang’ono pomwe kuti amatani kugwira kwake. Ndiponso, ntchito imene mwapatsidwayi ikufunika mwamsanga. Anthu akudalira inuyo. Zingakhaletu zokhumudwitsa kwambiri.
2 Nkhani imeneyi si yongoyerekezera chabe. Taganizani chitsanzo chotsatirachi. Nthaŵi zina, matchalitchi ena achikristu amayesa kukonza zoti azichita utumiki wa kukhomo ndi khomo. Izi zimalephereka nthaŵi zambiri ndipo zimazimiririka m’milungu yochepa kapena miyezi yoŵerengeka. Chifukwa chiyani? Matchalitchi Achikristu sanathandize otsatira awo kukhala oyenerera kugwira ntchitoyi. Ngakhale atsogoleri a matchalitchiwo ndi osayenerera kugwira ntchito yolalikira imeneyo, ngakhale kuti amaphunzira zaka zambirimbiri ku masukulu akudziko ndi m’maseminale. N’chifukwa chiyani tikunena zimenezi?
3. Kodi ndi mawu ati amene awagwiritsa ntchito katatu pa 2 Akorinto 3:5, 6, ndipo amatanthauza chiyani?
3 Mawu a Mulungu amafotokoza zimene zimayeneretsa mlaliki woona wa uthenga wabwino wachikristu. Mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu; amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki.” (2 Akorinto 3:5, 6) Onani mawu amene awagwiritsa ntchito katatu palembali akuti ‘kukwanira.’ Kodi amatanthauzanji? Buku lotanthauzira mawu a m’Baibulo lakuti Vine’s Expository Dictionary of Biblical Words limati: “Likamanena za zinthu [liwu loyambirira la Chigiriki limeneli] limasonyeza ‘kukwanira’ . . . ; likamanena za anthu, limatanthauza ‘kudziŵa,’ ‘kuyenerera.’” Motero munthu amene ali wokwanira ndiye kuti ‘akudziŵa’ ndipo akuyenerera kugwira ntchito imene wapatsidwa. Inde, atumiki oona a uthenga wabwino ndi oyeneretsedwa kugwira ntchito imeneyi. Ndi odziŵa, okhoza, kapena oyenerera kulalikira.
4. (a) Kodi chitsanzo cha Paulo chikusonyeza bwanji kuti amene angayenerere utumiki wachikristu si anthu osankhika ochepa chabe? (b) Kodi ndi njira zitatu ziti zimene Yehova amagwiritsa ntchito kutiyeneretsa kukhala atumiki?
4 Koma kodi kuyenerera kumeneko kumachokera kuti? M’maluso amene munthu ali nawo? M’nzeru zapamwamba? Mwa maphunziro apadera m’masukulu otchuka? Mtumwi Paulo mwachionekere anali nazo zonse zimenezi. (Machitidwe 22:3; Afilipi 3:4, 5) Komatu, iye anavomereza modzichepetsa kuti ziyeneretso zake monga mtumiki sizinachokere ku maphunziro apamwamba a kusukulu, koma kwa Yehova Mulungu. Kodi ziyeneretso zimenezo ndi za anthu osankhika ochepa okha? Paulo analembera mpingo wa ku Korinto za ‘kukwanira kwathu.’ Mosakayika, zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amaonetsetsa kuti atumiki ake onse okhulupirika ndi odziŵa, okhoza kugwira ntchito imene wawapatsa kuti achite. Kodi Yehova amawayeneretsa motani Akristu oona lerolino? Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene amagwiritsa ntchito: (1) Mawu ake, (2) mzimu wake woyera, ndi (3) gulu lake la padziko lapansi.
Mawu a Yehova Amatiyeneretsa
5, 6. Kodi Malemba Opatulika amathandiza motani Akristu oona?
5 Choyamba, kodi Mawu a Mulungu amatiyeneretsa motani kukhala atumiki? Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteo 3:16, 17) Motero Malemba Opatulika amatichititsa kukhala ‘oyenera, okonzeka’ kuchita ‘ntchito yabwino’ yophunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Nanga bwanji za anthu onse a m’Matchalitchi Achikristu? Iwo amaŵerenga Baibulo. Kodi zikutheka bwanji kuti buku lomwelo lithandize anthu ena kukhala atumiki aluso pamene ena ayi? Yankho lake lagona pa mmene timaonera Baibulolo.
6 N’zachisoni kuti anthu ambiri amene amapita kutchalitchi savomereza uthenga wa m’Baibulo ‘monga momwe uli ndithu, mawu a Mulungu.’ (1 Ates. 2:13) Pankhaniyi, Matchalitchi Achikristu apanga mbiri yochititsa manyazi. Kodi atsogoleri amatchalitchiwo akamaliza kuphunzira kwa zaka zambirimbiri m’masukulu a zaumulungu, amakhala okonzeka mokwanira kukhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu? Ayi. Ophunzira ena amayamba maphunziro awo a kuseminale akukhulupirira Baibulo koma pomaliza maphunzirowo amakhala akulikayikira. Ndiyeno, m’malo molalikira mawu a Mulungu, amene ambiri a iwo sawakhulupiriranso, utumiki wawo amaulunjikitsa pa zinthu zina. Amakhalira kumbuyo anthu ena omwe akutsutsana pa ndale, amalimbikitsa kugwirizanitsa mfundo zachikristu ndi mavuto a kakhalidwe ka anthu, kapena kutsindika mafilosofi a anthu m’maulaliki awo. (2 Timoteo 4:3) Mosiyana ndi ameneŵa, Akristu oona amatsanzira chitsanzo cha Yesu Kristu.
7, 8. Kodi panali kusiyana kotani pa mmene Yesu ankaonera Mawu a Mulungu ndi mmene atsogoleri a chipembedzo a m’nthaŵi yake ankachitira?
7 Yesu sanalole atsogoleri achipembedzo a m’nthaŵi yake kusokoneza maganizo ake. Yesu anagwiritsa bwino ntchito malemba opatulika, kaya pophunzitsa kagulu kochepa, monga atumwi ake, kapena khamu la anthu. (Mat. 13:10-17; 15:1-11) Kachitidwe kotere kanamusiyanitsa ndi atsogoleri a zipembedzo a m’nthaŵi imeneyo. Iwo anali kuletseratu anthu wamba kuphunzira zinthu zakuya za Mulungu. Ndipotu, unali mwambo masiku amenewo kukhulupirira kuti zigawo zina za Baibulo n’zozama kwambiri ndi zovuta kumva kotero kuti mphunzitsi angakambirane zigawozo ndi wophunzira yekhayo amene anali kumukonda kwambiri basi—ndipo ngakhale pamene akutero, ankakambirana monong’ona ataphimba kumutu! Atsogoleri achipembedzo amenewo anali kukhulupirira kuti akhoza kuona malodza pokambirana zigawo zina za Baibulo monganso mmene anali kukhulupirira pankhani yotchula dzina la Mulungu.
8 Kristu sankatero. Iye anali kukhulupirira kuti anthu onse anafunika kulingalira ‘mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu,’ osati anthu osankhika ochepa chabe ayi. Yesu sanafune kuulula chinsinsi chodziŵira Malemba kwa kagulu kochepa chabe ka ophunzira. Anauza ophunzira ake kuti: “Chimene ndikuuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m’khutu, muchilalikire pa machindwi a nyumba.” (Mateyu 4:4; 10:27) Yesu anafunitsitsa kuwadziŵitsa za Mulungu anthu ochuluka zedi amene iye akanatha.
9. Kodi Akristu oona amaligwiritsa ntchito bwanji Baibulo?
9 Nkhaŵa yathu yaikulu pophunzitsa iyenera kukhala Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, nthaŵi zambiri sikokwanira kungoŵerenga mavesi omwe tasankha m’Baibulo pokamba nkhani m’Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Tingafunike kufotokoza, kuperekapo fanizo, ndi kusonyeza mmene tingagwiritsire ntchito lemba limene tikukambiranalo. Cholinga chathu ndi kuchotsa uthenga wa m’Baibulo pa masambawo ndi kuusindikiza pa mitima ya omvetsera athu. (Nehemiya 8:8, 12) Baibulo liyeneranso kugwiritsidwa ntchito ngati munthu wina akufunika kum’patsa uphungu kapena kumulanga kuti asinthe. Ngakhale kuti anthu a Yehova amalankhula zinenero zosiyanasiyana ndiponso amachokera m’madera osiyanasiyana, onse amalemekeza Baibulo, lomwe ndi buku lofunika kuposa buku lina lililonse.
10. Kodi uthenga wouziridwa wa m’Baibulo ungatithandize bwanji?
10 Mawu a Mulungu amakhala amphamvu tikawalemekeza motero. (Ahebri 4:12) Amathandiza anthu kusintha miyoyo yawo, monga kusiya makhalidwe osemphana ndi malemba monga dama, chigololo, kulambira mafano, kuledzera, ndi kuba. Athandiza anthu ambiri kuvula umunthu wakale ndi kuvala watsopano. (Aefeso 4:20-24) Inde, ngati tilemekeza Baibulo kuposa malingaliro kapena mwambo uliwonse wa anthu ndi kuligwiritsa ntchito mokhulupirika, lingatithandizedi kukhala odziŵa, okonzeka mokwanira kukhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu.
Mzimu wa Yehova Umatiyeneretsa
11. Kodi n’chifukwa chiyani mzimu woyera wa Yehova moyenerera anautcha “mthandizi”?
11 Chachiŵiri, tiyeni tikambirane zimene mzimu woyera wa Yehova, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito, umachita potikonzekeretsa mokwanira. Tisaiwale kuti mzimu wa Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa mphamvu zonse zimene zilipo. Yehova wapatsa ulamuliro Mwana wake wokondedwa kuti azigwiritsa ntchito mphamvu yosaneneka imeneyi pothandiza Akristu onse oona. Yesu moyenerera anatcha mzimu woyera kuti ndi “mthandizi.” (Yoh. 16:7, NW) Analimbikitsa otsatira ake kupempha mzimuwu kwa Yehova, ndipo anawatsimikizira kuti Yehova adzawapatsa mowolowa manja.—Luka 11:10-13; Yakobo 1:17.
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani n’kofunika kuti tizipempherera mzimu woyera kuti utithandize muutumiki wathu? (b) Kodi Afarisi anasonyeza motani kuti mzimu woyera sunali kugwira ntchito mwa iwo?
12 Tifunika kupempherera mzimu woyera tsiku ndi tsiku, makamaka kuti utithandize mu utumiki wathu. Kodi mphamvu yogwira ntchito imeneyo ingatithandize bwanji? Ingalimbikitse maganizo athu ndi mitima yathu, kutithandiza kusintha, kukula mwauzimu ndi kuvala umunthu watsopano m’malo mwa wakale. (Akolose 3:9, 10) Ingatithandize kukhala ndi makhalidwe amtengo wapatali onga a Kristu. Ambiri a ife tinganene pamtima mawu a pa Agalatiya 5:22, 23. Mavesi amenewo amandandalika zipatso za mzimu wa Mulungu. Choyamba ndi chikondi. Chikondi ndi chofunika kwambiri pa utumiki wathu. Chifukwa chiyani?
13 Chikondi chimalimbikitsa kwambiri. Kukonda Yehova ndi kukonda anthu anzathu kumachititsa Akristu oona kuuza anthu ena uthenga wabwino. (Marko 12:28-31) Popanda chikondi choterechi, sitingayenerere kukhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Taonani mmene Yesu ndi Afarisi anasiyanira. Mateyu 9:36 amanena za Yesu kuti: “Koma iye, poona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” Kodi Afarisi anali kuwaona motani anthu wamba? Iwo anati: ‘Khamu ili losadziŵa chilamulo, likhala lotembereredwa.” (Yohane 7:49) Afarisi amenewo sanali kukonda anthu koma kunyansidwa nawo. Mwachionekere, mzimu wa Yehova sunali kugwira ntchito mwa iwo.
14. Kodi chitsanzo cha Yesu chosonyeza chikondi muutumiki wake chiyenera kutilimbikitsa motani?
14 Yesu anawamvera chifundo anthu. Ankazindikira kuti iwo anali kumva kupweteka. Ankadziŵa kuti anali kuzunzidwa, anali okambululudwa, ndi omwazikana, monga nkhosa zopanda mbusa. Yohane 2:25 amatiuza kuti Yesu ‘ankadziŵa chimene chinali mwa munthu.’ Yesu ankadziŵa bwino kwambiri za mmene munthu alili popeza anali Mmisiri wa Yehova polenga zinthu. (Miyambo 8:30, 31) Kudziŵa kumeneku kunakulitsa chikondi chake. Chikondi choterechi chitilimbikitsetu nthaŵi zonse kugwira ntchito yolalikira! Ngati tikuona kuti tifunika kuwongolera pankhani imeneyi, tiyeni tipempherere mzimu woyera wa Yehova ndiyeno tichite zinthu mogwirizana ndi mapemphero athuwo. Yehova adzatiyankha. Adzatumiza mphamvu yosaletseka imeneyi kuti itithandize kukhala ofanana kwambiri ndi Kristu amene anayeneretsedwa kwambiri kuposa wina aliyense kuti alalikire uthenga wabwino.
15. Kodi mawu a pa Yesaya 61:1-3 anagwira ntchito motani kwa Yesu komanso kuvumbula kuti alembi ndi Afarisi anali onyenga?
15 Kodi ziyeneretso za Yesu zinachokera kuti? “Mzimu wa Ambuye uli pa Ine,” iye anatero. (Luka 4:17-21) Inde, Yehova mwiniyo ndiye anasankha Yesu pogwiritsa ntchito mzimu woyera. Yesu sanafunikire ziyeneretso zina. Kodi atsogoleri achipembedzo a m’nthaŵi yake anaikidwa ndi mzimu woyera? Ayi. Sanalinso okonzeka kukwaniritsa mawu a pa Yesaya 61:1-3, amene Yesu anaŵerenga mokweza ndi kunena kuti mawuwo anali kunena za iye. Taŵerengani mavesi ameneŵa ndikuona nokha kuti alembi ndi Afarisi achinyengowo sanayenerere zimene mawuwo akunena. Analibe uthenga wabwino woti aulengeze kwa osauka. Ndipo akanalalikira bwanji za kumasulidwa kwa am’nsinga ndi kupenyanso kwa akhungu? M’lingaliro lauzimu, iwowo ndiwo anali akhungu ndi omangidwa m’miyambo ya anthu. Mosiyana ndi anthu amenewo, kodi si ndife oyenerera kuphunzitsa anthu?
16. Kodi anthu a Yehova lerolino angakhale ndi chidaliro chotani pa kuyeneretsedwa kwawo monga atumiki?
16 N’zoona kuti sitinaphunzire m’masukulu a maphunziro apamwamba a Matchalitchi Achikristu. Sitiikidwa kukhala aphunzitsi ndi maseminale a maphunziro azaumulungu. Kodi ndiye kuti tilibe ziyeneretso? Tili nazo! Yehova ndi amene amatiika kukhala Mboni zake. (Yesaya 43:10-12) Ngati tipempha mzimu wake ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi pemphero lathulo, tili ndi ziyeneretso zapamwamba zedi. Inde ndife opanda ungwiro, ndipo timalephera kufika pa chitsanzo chimene anapereka Mphunzitsi Wamkulu, Yesu. Komabe, kodi sitikuthokoza kuti Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake kutiyeneretsa ndi kutikonzekeretsa kukhala aphunzitsi a Mawu ake?
Gulu la Yehova Limatiyeneretsa
17-19. Kodi misonkhano isanu imene gulu la Yehova lapereka imatithandiza bwanji kuyenerera kukhala atumiki?
17 Tsopano tiyeni tikambirane njira yachitatu imene Yehova amagwiritsa ntchito potikonzekeretsa mokwanira kukhala aphunzitsi a mawu ake, yomwe ndi mpingo wake kapena gulu lake la padziko lapansi limene limatiphunzitsa kukhala atumiki. Motani? Tangoganizani za pulogalamu ya malangizo imene timakhala nayo. Nthaŵi zonse pamlungu, timakhala ndi misonkhano yachikristu isanu. (Ahebri 10:24, 25) Timasonkhana m’timagulu pa Phunziro la Buku la Mpingo kuti tiphunzire Baibulo mwakuya pogwiritsa ntchito buku limene gulu la Yehova limatipatsa. Mwa kumvetsera ndi kuyankhapo, timaphunzitsana ndi kulimbikitsana. Woyang’anira phunziro la buku amaperekanso malangizo ndi chisamaliro kwa aliyense payekha. Pa Msonkhano wa Onse ndi pa Phunziro la Nsanja ya Olonda, timadya chakudya china chauzimu chopatsa thanzi.
18 Sukulu yathu ya Utumiki Wateokalase inalinganizidwa kutipatsa malangizo a mmene 1 Petro 3:15) Kodi munayamba mwapatsidwapo nkhani yoti mukakambe imene munkaona kuti munaizoloŵera kwambiri, ndiyeno n’kupeza kuti mukuphunzirapo kanthu kena katsopano? Zimenezi zimachitika kaŵirikaŵiri. Palibe chimene chimatithandiza kudziŵa bwino kwambiri nkhani inayake kuposa kuiphunzitsa kwa anthu ena. Ngakhale pamene sanatipatse nkhani yoti tikambe, tingaphunzirebe kukhala aphunzitsi abwino. Timaona maluso abwino mwa wophunzira aliyense, ndipo timaganizira za mmene tingatsanzirire maluso amenewo.
tingaphunzitsire. Mwa kukonzekera nkhani za ophunzira, timaphunzira mmene tingagwiritsire ntchito Mawu a Mulungu pophunzitsa pa nkhani zosiyanasiyana. (19 Nawonso Msonkhano wa Utumiki unalinganizidwa kutikonzekeretsa kukhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Mlungu ndi mlungu timasangalala ndi nkhani, kukambirana, ndi zitsanzo zosangalatsa zokonzedwa kuthandiza utumiki wathu. Kodi tidzagwiritsa ntchito ulaliki wotani? Kodi tingathetse bwanji zovuta zapadera za m’gawo lathu? Kodi ndi njira zotani za kulalikira zimene tingagwiritse ntchito zomwe tifunika kuziyesa mowonjezeka? Kodi n’chiyani chidzatithandiza kukhala aphunzitsi ogwira mtima pa maulendo obwereza ndi pochititsa maphunziro a Baibulo? (1 Akorinto 9:19-22) Mafunso oterowo amayankhidwa ndi kufotokozedwa mwatsatanetsatane pa Msonkhano wa Utumiki. Nkhani zambiri za msonkhanowo zimachokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu, chida china chimene tapatsidwa potikonzekeretsa ntchito yathu yofunika kwambiri.
20. Kodi tingapindule bwanji mokwanira pa misonkhano yampingo ndi yadera?
20 Mwa kukonzekera ndi kupezeka pa misonkhano ndiyeno n’kugwiritsa ntchito zimene taphunzirazo pa ntchito yathu monga aphunzitsi, timalandira maphunziro ochuluka. Koma palinso zina. Timakhalanso ndi misonkhano ikuluikulu—yadera ndi yachigawo—imene amaikonza kuti itikonzekeretse kukhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Ndipotu timayembekezera kumvetsera mwatcheru ndi kugwiritsa ntchito malangizowo.—Luka 8:18.
21. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti maphunziro athu athandiza, ndipo ndani amene wachititsa kuti zonsezi zitheke?
21 Kodi maphunziro amene Yehova wapereka athandiza? Tiyeni tingoona zimene zakhala zikuchitika. Chaka chilichonse, anthu zikwi mazanamazana amathandizidwa kuphunzira ziphunzitso zikuluzikulu za Baibulo ndi kuchita zimene Mulungu amafuna kwa iwo. Tikuchulukana, koma palibe aliyense wa ife amene anganyadire kuti ndiye akuchititsa zimenezi. Tiyenera kuona zinthu moyenerera monga anachitira Yesu. Iye anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amukoka iye.” Mofanana ndi atumwi akale, kwakukulukulu ife ndife anthu wamba ndiponso osaphunzira. (Yohane 6:44; Machitidwe 4:13) Kuchita bwino kwathu kumadalira Yehova, amene amakokera anthu oona mtima ku choonadi. Paulo ananena bwino kuti: “Ndinawoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa.”—1 Akorinto. 3:6.
22. N’chifukwa chiyani sitifunika kugwa mphwayi mopambanitsa pochita nawo utumiki wachikristu mokwanira?
22 Inde, Yehova Mulungu akutithandiza zedi pa ntchito yathu yophunzitsa Mawu ake. Nthaŵi zina tingamve ngati sitikuyenerera kukhala aphunzitsi. Koma kumbukirani kuti Yehova ndiye amakokera anthu kwa iyemwini ndi kwa Mwana wake. Yehova ndiye amatiyeneretsa kutumikira anthu atsopano pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake woyera, ndi gulu lake la padziko lapansi. Tiyeni tilabadire zomwe Yehova amatiphunzitsa mwa kugwiritsa ntchito zinthu zabwino zimene akutipatsa tsopano lino potikonzekeretsa mokwanira kukhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Baibulo limatikonzekeretsa bwanji kuchita ntchito yolalikira?
• Kodi mzimu woyera umathandiza bwanji potiyeneretsa kukhala atumiki?
• Kodi gulu la padziko lapansi la Yehova lakuthandizani m’njira zotani kuti muyenerere kukhala mlaliki wa uthenga wabwino?
• N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chidaliro pochita utumiki?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 25]
Yesu anasonyeza chikondi kwa anthu monga mphunzitsi wa Mawu a Mulungu