Moyo Wabwino Tsopano Ndiponso Kwamuyaya
Moyo Wabwino Tsopano Ndiponso Kwamuyaya
N’CHIFUKWA chiyani moyo wabwino uli wovuta kuupeza? Ndipo n’chifukwa chiyani ukapezeka sukhalitsa? Kodi mwina zingakhale kuti moyo womwe timati ndi wabwino umangokhala woyerekezera chabe—kuyerekeza zinthu zomwe tikuganiza kuti tingapeze m’malo mwa zomwe tingapezedi? Kuganiza zimenezi kungakhale ngati kulota chabe.
Kuyerekeza zinthu kumachititsa munthu kusiya kuganiza za mavuto a m’moyo, n’kuyamba kuganiza za zinthu zokongola, malo abwino, kuiŵaliratu mavuto onse a m’dzikoli. Komabe, nthaŵi zambiri mavuto enieni amabwera m’maganizo a munthuyo ndipo iye amasiya kulotako n’kuyamba kuganizira zinthu zenizeni.
Tiyeni tione za kutauni komwe anthu amaganiza kuti ndiko kuli moyo wabwino. Mwachitsanzo, tauni yaikulu ingaoneke kuti ndiwo malo amene anthu angasangalale, kulandira ndalama zambiri, ndiponso kukhala m’nyumba zapamwamba. Inde, zimenezi zikuoneka ngati zingabweretsedi moyo wabwino womwe anthu akhala akuuyembekezera kwanthaŵi yaitali. Koma kodi zimenezi n’zoona?
Kodi Mungapezedi Moyo Wabwino M’tauni Kapena ndi Maloto Chabe?
M’mayiko amene akutukuka kumene, anthu angakopeke kupita m’tauni chifukwa cha anthu otsatsa malonda omwe angayambitse maganizo oti m’tauni ndi mwabwino. Makampani omwe amatsatsa malondawo cholinga chawo si chofuna kuti inuyo mupeze moyo wabwino koma kuti malonda awo agulidwe. Amaleka dala kunena za mavuto omwe aliko, n’kumangonena za moyo wabwino. Choncho, moyo wabwino amaugwirizanitsa ndi katundu yemwe akutsatsayo ndiponso tauniyo.
Taganizirani chitsanzo chotsatirachi. Akuluakulu a boma m’tauni ina ya ku West Africa anaika zikwangwani zooneka bwino zosonyeza kuti kusuta fodya n’kofanana ndi kuwononga ndalama zomwe munthu wazipeza movutikira. Kuika zikwangwanizo inali njira imodzi yochenjezera nzika za m’tauniyo kuopsa kosuta fodya. Makampani opanga ndudu ndi ogulitsa nduduzo nawonso anaika zikwangwani zawo zomwe anazipanga mwaukatswiri zosonyeza anthu osuta fodya akuoneka osangalala ndiponso kuti zinthu zikuwayendera bwino. Kuwonjezera pamenepo, kampani ina yopanga ndudu inapatsa antchito ake yunifolomu yapamwamba ndiponso zipewa za oseŵera mpira wa baseball kuti akagaŵe ndudu za fodya kwa achinyamata mumsewu, n’kumawauza kuti “amulawe fodyayo.” Ambiri mwa achinyamata amenewo anali atachokera kumidzi ndipo chifukwa chosadziŵa njira zokopa zotsatsira malonda, iwo anakopeka n’kuyamba kusuta fodyayo. Mapeto ake anakhala osuta fodya kwadzaoneni. Achinyamatawo anali atabwera m’tauni kudzafuna
moyo wabwino kuti azithandiza mabanja awo kapena kuti adzakhale olemera kwambiri. M’malo mwake, anali kuwononga ndalama zambiri zomwe akanazigwiritsa ntchito zina zopindulitsa.Mawu onena kuti m’tauni ndimo muli moyo wabwino sikuti amachokera kwa amalonda okha nthaŵi zonse ayi. Nthaŵi zina anthu amene anachoka kumudzi kupita m’tauni ndipo akuchita manyazi kubwerera amanenanso zimenezi. Pokana kuoneka ngati olephera, iwo amakokomeza chuma ndi zina zomwe amati azipeza kutauni. Komabe, kuonetsetsa zomwe akunenazo kumaonetsa kuti moyo wawo sunatukuke poyerekeza ndi kumudzi komwe ankakhala kale. Amavutika kupeza ndalama monga momwe ena ambiri okhala m’tauni amavutikira.
Anthu amene abwera kumene kudzafuna moyo wabwino amawachita chipongwe makamaka m’matauni akuluakulu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chachikulu n’chakuti amakhala asanapeze anzawo apamtima ndiponso amakhala ali kutali ndi abale awo. Choncho, amakhala alibe mlangizi amene angawathandize kupeŵa mbuna za moyo wa m’tauni wokondetsa chuma.
Josué sanakopeke kuyamba kusuta fodya. Komanso, anaona kuti zomwe moyo wa m’tauni umafuna sangazikwanitse. Kwa iye, anaona kuti chinthu chokhacho chomwe tauni ingamupatse ndicho maloto a zinthu zomwe sangazipeze. Anaona kuti kutauni sanali ndi moyo wabwino weniweni ndipo kuti sanali woyenera kukhala kumeneko. Anayamba kudziona kukhala wosayenera ndi wolephera ndipo m’kupita kwa nthaŵi anadzichepetsa n’kubwerera kumudzi.
Ankachita mantha kuti kumudziko akamuseka. Koma atafika, banja lake ndiponso anzake apamtima anamulandira ndi manja aŵiri. Chifukwa cha chikondi cha abale ake, kuona malo omwe anawazoloŵera, ndiponso chikondi cha anzake apamtima a mumpingo wachikristu, iye mwamsanga anayamba kuona kuti akukhala moyo wabwinopo kumudziko kusiyana ndi kutauni kumene zomwe ambiri amayembekeza zimangokhala maloto chabe. Anadabwa kwambiri kuona kuti chifukwa chogwira ntchito molimbika kumunda pamodzi ndi bambo ake, iye ndi banja lake ankapeza ndalama zambiri kuposa zomwe akanapeza kutauni.
Kodi Ndalama Ndizo Vuto Kwenikweni?
Kodi ndalama zingakubweretsereni moyo wabwino? Liz wa ku Canada anati: “Monga mtsikana, ndinkaganiza kuti ndalama zimathetsa nkhaŵa.” Anayamba chibwenzi ndi mwamuna wina wolemera. Pasanapite nthaŵi anakwatirana. Kodi anali ndi moyo wabwino? Liz anati: “Titakwatirana tinali ndi nyumba yabwino ndi magalimoto aŵiri. Chifukwa cha ndalama zomwe tinali nazo tinali ndi mwayi wogula pafupifupi chilichonse, kuyenda maulendo aatali ndiponso kupita kokasangalala. Simungakhulupirire kuti, ndinali kuvutikabe maganizo pankhani ya ndalama.” Iye anafotokoza chifukwa chake. Anati: “Tinali kusoŵa chinachake chofunika kwambiri. Zikuoneka kuti munthu ukakhala ndi ndalama zambiri, sukhala ndi moyo wabwino weniweni. Ndalama sizinathetse kudandaula kapena nkhaŵa.”
Ngati mukuona kuti mukulephera kukhala moyo wabwino chifukwa choti mulibe ndalama zokwanira, dzifunseni kuti, ‘Kodi vuto lenileni n’chiyani? Kodi kusoŵa ndalama ndiko vuto lenileni kapena ndikusoŵa nzeru zogwiritsa bwino ntchito ndalamazo?’ Pa za moyo wake wa m’mbuyo, Liz anati: “Tsopano ndazindikira kuti mavuto a m’banja la makolo anga pamene ndinali mwana ankabwera chifukwa chosadziŵa kugwiritsa bwino ntchito ndalama. Tinkagula zinthu pangongole ndipo tinkakhala ndi ngongole nthaŵi zonse. Zimenezi zinkatipatsa nkhaŵa.”
Komabe, Liz ndi mwamuna wake tsopano akukhala moyo wabwinopo ngakhale kuti ali ndi ndalama zochepa. Ataphunzira choonadi cha Mawu a Mulungu, iwo anasiya kumvera nkhani zokopa zokhudza chuma ndipo anayamba kumvera nzeru ya Mulungu, kuphatikizapo mawu awa: “Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.” (Miyambo 1:33) Iwo anafuna kuti moyo wawo ukhale waphindu kuposa zomwe akaunti yaikulu ya kubanki ingapereke. Liz ndi mwamuna wake omwe tsopano ndi amishonale m’dziko lakutali akuphunzitsa olemera ndi osauka kuti Yehova Mulungu posachedwapa adzabweretsa moyo wabwino weniweni padziko lonse lapansi. Ntchito imeneyi imapatsa chimwemwe ndi mphamvu zomwe zimabwera osati chifukwa chofuna chuma koma chifukwa cha cholinga chapamwamba ndiponso chamtengo wapatali kuposa zonse.
Kumbukirani mfundo yoona iyi: Kukhala wolemera kwa Mulungu n’kwamtengo wapatali kuposa kukhala ndi chuma chenicheni. Malemba Opatulika amatsindika kufunika kokhala ndi unansi wabwino ndi Yehova kusiyana ndi kupeza chuma. Unansi umenewu ungapitirize ngati nthaŵi zonse titamachita mwa chikhulupiriro zomwe Mulungu amafuna. Kristu Yesu anatilimbikitsa kukhala ndi “chuma cha kwa Mulungu” ndiponso kusunga “chuma chosatha m’Mwamba.”—Luka 12:21, 33.
Kodi Mukufuna Udindo Wapamwamba?
Ngati mukuganiza kuti kukhala paudindo wapamwamba ndiko kumabweretsa moyo wabwino, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndani amene ali paudindo
wapamwamba amene akukhala moyo wabwino weniweni? Kodi ndiyenera kukwera kufika pati kuti ndipeze moyo wabwino?’ Ntchito yapamwamba ingakunyengeni kuganiza kuti mukukhala moyo wabwino komano ingakukhumudwitseni kapenanso kutha kumene.Zochitika zenizeni zikusonyeza kuti kukhala ndi mbiri yabwino kwa Mulungu ndiko kumachititsa munthu kukhala ndi moyo wabwinopo kusiyana ndi kutchuka pamaso pa anthu. Yehova yekha ndiye angapatse anthu mphatso ya moyo wamuyaya. Zimenezi zimafuna kuti dzina lathu lilembedwe m’buku la moyo la Mulungu osati m’buku la anthu apamwamba ayi.—Eksodo 32:32; Chivumbulutso 3:5.
Mukaika pambali zinthu zomwe mumalakalaka mutakhala nazo, kodi mukuona kuti zinthu zikukuyenderani bwanji panopa? Ndipo kodi moona mtima mungayembekezere zotani m’tsogolo? Palibe munthu amene ali ndi chilichonse. Mkristu wina wanzeru anati, “Ndinazindikira kuti n’zosatheka kukhala ndi chilichonse pa moyo, munthu umafunika kusankha zina n’kusiya zina.” Lekezani pang’ono ndipo ŵerengani bokosi lakuti “Yosimbidwa ku Benin.”
Tsopano yankhani mafunso awa: Kodi cholinga changa chachikulu n’choti ndidzafike pati? Kodi njira yachidule yofikira pamenepo n’njotani? Kodi mwina ndatsata njira yoipa yozungulira ndipo kuti zomwe ndikufunazo n’zovuta kuzipeza poyerekeza ndi zina zomwe ndingazipeze mosavuta?
Yesu atapereka uphungu wokhudza kufunika kwa chuma poyerekeza ndi zinthu zauzimu, anati, diso lanu likhale la “kumodzi.” (Mateyu 6:22) Iye anatsindika kuti zinthu zofunika kwambiri pa moyo ndi zinthu zauzimu komanso zolinga zauzimu zomwe zimakhudza dzina la Mulungu ndi Ufumu wake. (Mateyu 6:9, 10) Inde, zinthu zina n’zosafunika kwenikweni.
Makamera ambiri ojambula zinthuzi masiku ano amangolunjika okha pa zinthu zilizonse popanda kuwachuna, kaya zinthuzo zili kutali kapena pafupi. Kodi mukufuna kukhala otero? Kodi mumaika mtima pa chilichonse chomwe mwaona, mukumaganiza kuti n’chabwino ndiponso n’chofunika kukhala nacho? Ngati mumaganiza choncho, ngakhale pang’ono chabe, ndiye kuti Ufumu womwe uli wofunika kwambiri kwa Akristu udzaoneka wopanda pake poyerekeza ndi zinthu zina zomwe zimafunanso kuti muzizikonda kwambiri. Yesu analangiza motsindika kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:33.
Moyo Wabwino Tsopano Ndiponso Kwamuyaya
Mwina tonse timalakalaka titakhala ndi moyo wabwino pamodzi ndi anthu amene timawakonda. Komabe, chifukwa choti ndife opanda ungwiro ndipo tikukhala m’dziko lopanda ungwiro, komanso timakhala ndi moyo nthaŵi yochepa, timalephera kupeza zinthu zomwe timazifuna. Zaka zambirimbiri zapitazo, wolemba Baibulo wina anafotokoza kuti: “Ndinabweranso kuona pansi pano kuti amene athamanga kwambiri sapambana liŵiro, ngakhale amphamvu sapambana nkhondo, ngakhalenso anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira sapeza chuma, ndipo ngakhale odziŵa zambiri sapeza chiyanjo, chifukwa nthaŵi ndi zochitika zadzidzidzi zimawagwera onse.”—Mlaliki 9:11, NW.
Nthaŵi zina timaika mtima kwambiri pa ntchito zathu za tsiku ndi tsiku moti mpaka timaiŵala Mlaliki 5:10, 12) Inde, kodi moyo wabwino mungaupeze kuti?
mbali yofunika kwambiri ya moyo wathu ndiponso zomwe zimafunika kuti tikhaledi ndi moyo wabwino weniweni. Taganizirani mawu akale anzeru awa: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe. Tulo ta munthu wogwira ntchito n’tabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikum’gonetsa tulo.” (Ngati mukuganizira zinthu zomwe simungazipeze monga ankachitira Josué, bwanji osasintha zolinga zanu? Anthu amene amakukondani adzakuthandizani monga momwe abale a Josué ndi anzake mumpingo wachikristu anam’thandizira. Mungakhale ndi moyo wabwinopo kumudzi pamodzi ndi amene amakukondani kusiyana ndi m’tauni momwe anthu angafune kungokudyerani masuku pamutu.
Ngati muli ndi chuma kale monga analili Liz ndi mwamuna wake, bwanji osasintha moyo wanu kuti muzithera nthaŵi yambiri ndiponso mphamvu zanu pa ntchito yothandiza anthu kaya olemera kapena osauka kuti aphunzire za Ufumu womwe udzabweretse moyo wabwino weniweni?
Ngati mukufuna udindo wapamwamba, mwina mufunika kuganizira moona mtima chomwe chikukuchititsani kufuna udindowo. N’zoona kuti zinthu zina zomwe timafuna zimawonjezera chimwemwe. Komabe, kodi mukuika mtima kwambiri pa Ufumu womwe ndiwo njira yokha yeniyeni yopezera moyo wabwino wamuyaya? Kumbukirani mawu a Yesu akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Ngati mutachita nawo ntchito zosiyanasiyana mumpingo wachikristu mudzapeza moyo wabwino wopindulitsa.
Amene akukhulupirira Yehova ndi Ufumu wake amasangalala ndi moyo wabwino tsopano ndipo amayembekezera kudzakhala ndi moyo wabwino kotheratu m’tsogolo. Wamasalmo ananena kuti: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthaŵi zonse: Popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.”—Salmo 16:8, 9.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]
Yosimbidwa ku Benin
Nkhani ino aisimba kambirimbiri m’njira zosiyanasiyana. Posachedwapa, nyakwaŵa ina ku Benin, West Africa, inasimbira ana nkhaniyi motere.
Msodzi wina akubwerera kunyumba m’bwato lake, anakumana ndi katswiri wina wazamalonda wochokera kunja amene ankagwira ntchito m’dziko losaukalo. Katswiriyo anamufunsa msodziyo chifukwa chomwe wabwerera kunyumba mwamsanga. Iye anayankha kuti, akanatha kukhalabe komweko koma wagwira nsomba zokwanira kusamalira banja lake.
Katswiriyo anafunsa kuti: “Ndiyeno pa moyo wanu m’machita chiyani?”
Msodziyo anayankha kuti: “Ndimapita kokasodza, kenako ndimaseŵera ndi ana anga. Kukatentha, tonse timagona, ndipo madzulo tonse timadya chakudya chamadzulo pamodzi. Kenako, timacheza ndi anzathu, kusangalala ndi nyimbo ndi zina zotero.”
Katswiriyo anati: “Tamverani, ine ndili ndi digiri ya ku yunivesite ndipo ndinaphunzira kwambiri mbali imeneyi. Ndikufuna kukuthandizani. Musamabwere msanga mukapita kokasodza. Mukatero mudzapeza ndalama zambiri ndipo mudzagula boti lalikulu kuposa kabwato aka. Mukakhala ndi boti lalikulu mudzapeza ndalama zochuluka ndipo mudzagula maboti akuluakulu a injini ophera nsomba.”
Msodziyo anafunsa kuti: “Ndikadzatero ndidzatani?”
Mkuluyo anayankha kuti: “Ndiyeno m’malo mogulitsa nsomba kwa anthu wamba, mutha kumadzagulitsa ku kampani, ngakhale kuyambitsa kampani yanu kumene. Mukhoza kudzachoka m’mudzi n’kupita mumzinda wa Cotonou, kapena Paris, kapena New York, n’kumachita bizinesi yanu muli kumeneko. Mwinanso mungadzaganize zoika kampani yanuyo pa msika wogulitsa makampani, n’kukhala wolemera kwambiri.”
Msodziyo anafunsa kuti: “Kodi zimenezi zingatenge nthaŵi yaitali bwanji?”
Mkuluyo anati: “Mwina zaka 15 kulekeza 20.”
Msodziyo anapitiriza kuti: “Kenako ndidzatani?”
Mkuluyo anati: “Pamenepo mpamene moyo umasangalatsa kwambiri. Mutha kudzasiya kugwira ntchito, kusiya moyo wotanganidwa nthaŵi zonse wa m’tauni, n’kupita kumudzi.”
Msodziyo anafunsa kuti: “Zikadzatero ndidzatani?”
Mkuluyo anati: “Muzidzapita kokasodza nthaŵi pang’ono, kusewera ndi ana anu, kugona kukatentha, kudya chakudza chamadzulo pamodzi ndi banja, komanso kucheza ndi anzanu ndi kusangalala ndi nyimbo.”
[Zithunzi patsamba 7]
Kodi kukwezedwa paudindo kumabweretsa moyo wabwino?
[Zithunzi patsamba 8]
Akristu anzanu amafunitsitsa mutakhala ndi moyo wabwino