Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuphunzitsa Ana Athu Kukonda Yehova

Kuphunzitsa Ana Athu Kukonda Yehova

Mbiri ya Moyo Wanga

Kuphunzitsa Ana Athu Kukonda Yehova

YOSIMBIDWA NDI WERNER MATZEN

Zaka makumi angapo zapitazo, mwana wanga wamwamuna wamkulu, Hans Werner, anandipatsa Baibulo. Kuchikuto analembako kuti: “Wokondedwa Bambo, Mawu a Yehova apitirizetu kutitsogolera tonse monga banja pa moyo wathu. Zikomo kwambiri, ndine mwana wanu.” Ndinayamikira komanso kusangalala kwambiri chifukwa cha mawu ameneŵa. Ndipo makolo angandivomereze kuti mawuwa ndi osangalatsadi. Panthaŵiyo sindinkadziŵa n’komwe mavuto omwe banja lathu lidzakumane nawo.

NDINABADWA m’chaka cha 1924, ku Halstenbek, makilomita 20 kuchokera ku doko la ku Germany la Hamburg. Mayi ndi agogo anga aamuna ndiwo anandilera. Popeza ndinaphunzira ntchito yokonza zida, anandiloŵetsa m’gulu la asilikali la Wehrmacht mu 1942. Zomwe ndinakumana nazo pankhondo yachiŵiri ya padziko lonse pamene ndinali kumenyana ndi asilikali a ku Russia zinali zoopsa, zosasimbika. Ndinadwala matenda a m’mimba mwa kamwazi koma n’talandira chithandizo chamankhwala ananditumizanso kunkhondo. Mu January 1945, ndinali ku Lodz, ku Poland, komwe ndinavulala koopsa, n’kundigoneka m’chipatala cha asilikali. Nkhondo inatha ndili komweko. Ndili kuchipatalako komanso kenako kundende ya ku Neuengamme ndinali kusinkhasinkha za moyo wanga. Ndinaima mutu kwambiri ndi mafunso awa: Kodi Mulungu alikodi? Ngati aliko, n’chifukwa chiyani amalola nkhanza zoterezi?

Atanditulutsa kundendeko mu September 1947, ndinakwatira Karla. Tinakulira m’tauni imodzi, koma Karla anali Mkatolika pamene ine sindinakulire m’chipembedzo. Wansembe amene anadalitsa ukwati wathu anatilangiza kuti tizikanena pamodzi Pemphero la Ambuye usiku uliwonse. Tinkachitadi zimenezo mosadziŵa zomwe tikupempherera.

Chitatha chaka chimodzi, mwana wathu Hans Werner anabadwa. Nthaŵi ina atabadwa mwanayu, ndinadziŵana ndi Mboni za Yehova chifukwa cha mnzanga wa kuntchito, Wilhelm Ahrens. Iye anandionetsa kuchokera m’Baibulo kuti tsiku lina nkhondo zidzatheratu. (Salmo 46:9) Mu 1950, ndinapatulira moyo wanga kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa. Patatha chaka chimodzi, ndinali ndi chimwemwe chodzaza tsaya pamene mkazi wanga wokondedwa nayenso anabatizidwa.

Kuphunzitsa Ana Kutsatira Njira za Yehova

Ndinaŵerenga m’Baibulo kuti Yehova ndiye anayambitsa ukwati. (Genesis 1:26-28; 2:22-24) Kuonerera pamene ana athu onse​—Hans Werner, Karl-Heinz, Michael, Gabriele, ndi Thomas ankabadwa, kunalimbitsa maganizo anga ofunitsitsa kukhala mwamuna komanso tate wabwino. Karla ndi ine tinkasangalala kwambiri mwana aliyense akabadwa.

Msonkhano wa Mboni za Yehova mu 1953 ku Nuremberg unali chochitika chosaiŵalika m’banja lathu. Lachisanu masana, yemwe anakamba nkhani yakuti, “Kulera Ana M’gulu Latsopano Lapadziko Lapansi” anatchula mfundo yomwe sitidzaiiŵala. Anati: “Chilakolako chofuna kutumikira Mulungu ndicho choloŵa chachikulu koposa chomwe tingapatse ana athu.” Mwa kudalira thandizo la Yehova, ine ndi Karla tinafuna kuchita zimenezo. Koma kodi zikanatheka bwanji?

Choyamba, tinakonza zopemphera pamodzi monga banja tsiku lililonse. Zimenezi zinachititsa ana athu kuzindikira kufunika kwa pemphero. Mwana aliyense anaphunzira akadali wamng’ono kuti timapemphera kaye tisanayambe kudya. Ngakhale akadali aang’ono, iwo ankagwetsa tinkhope tawo pansi ndi kupinda timanja tawo akangoona botolo lawo la mkaka. Nthaŵi ina, anatiitana ku ukwati wa wachibale wina wa mkazi wanga yemwe sanali wa Mboni. Utatha ukwatiwo, makolo a mkwatiyo anaitana alendo kupita kunyumba kukadya chakudya. Aliyense anafuna kungoyamba kudya. Koma mwana wathu, Karl-Heinz wa zaka zisanu, sanaone kuti zimenezo n’zoyenera. Anati: “Chonde pempherani kaye.” Alendo anamuyang’ana mwanayo, kenako n’kuyang’ana ife, n’kumalizira eninyumba. Pokana kuchita manyazi, ndinapempha kuti ndipemphere ndipo eninyumba anavomera.

Zimene zinachitikazi zinandikumbutsa mawu a Yesu akuti: “Mkamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza.” (Mateyu 21:16) Tikukhulupirira kuti mapemphero athu a nthaŵi zonse ochokera pansi pa mtima anathandiza ana athu kuona Yehova monga Atate wawo wachikondi wakumwamba.

Udindo Wathu kwa Yehova

Kuphunzitsa ana kukonda Mulungu kumafunanso kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu ake nthaŵi zonse. Pokumbukira zimenezi, tinkachita phunziro la banja mlungu uliwonse. Nthaŵi zambiri tinkachita Lolemba madzulo. Ana athu anali kufunikira thandizo losiyana popeza kuti mwana wamkulu kwambiri ndi wamng’ono kwambiri anasiyana zaka zisanu ndi zinayi. Choncho, sitinali kuphunzira ndi ana onse nkhani yofanana.

Mwachitsanzo, ana amene anali asanayambe kupita kusukulu tinali kuwaphunzitsa zinthu zosavuta. Mkazi wanga Karla anali kuwaphunzitsa lemba limodzi la m’Baibulo, kapena ankagwiritsa ntchito zithunzi za m’mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Ndimakumbukirabe ana athu aang’ono akukwera pa bedi lathu mmamaŵa kundidzutsa kuti andionetse zithunzi zomwe amazikonda kwambiri m’buku lakuti The New World. *

Karla anakonza njira yapamwamba yophunzitsira ana zifukwa zambiri zomwe tonsefe tili nazo zokondera Yehova. Zimenezi zingaoneke ngati zosavuta kuchita. Koma kwa Karla ndi ine, imeneyi inali ntchito yanthaŵi zonse yofuna mphamvu komanso kuganiza. Komabe, sitinasiye. Tinkafuna kuwaphunzitsa akadali aang’ono, anthu ena osadziŵa Yehova asanayambe kuwakopa. Pachifukwa chimenechi, tinkaonetsetsa kuti ana athu azipezeka pa phunziro la banja akangoyamba kukhala pansi.

Karla ndi ine monga makolo, tinazindikira kufunika kopereka chitsanzo chabwino kwa ana athu pankhani ya kulambira. Kaya tikudya, kulima, kapena tikupita kokayenda, tinkayesetsa kulimbitsa unansi wa mwana aliyense ndi Yehova. (Deuteronomo 6:6, 7) Tinkaonetsetsa kuti mwana aliyense ali ndi Baibulo lake akadali wamng’ono. Komanso tikalandira magazini, ndinkalemba dzina la aliyense wa m’banja lathu pa kope lake. Motero ana anaphunzira kudziŵa mabuku awo. Tinaganizanso zogaŵira mwana aliyense nkhani ya m’magazini a Galamukani! kuti aŵerenge. Lamlungu tikatha kudya chakudya chamasana, iwo anali kutiuza zomwe amva m’nkhanizo.

Kusamalira Zomwe Ana Akufuna

N’zoona kuti zinthu sizinali kuyenda bwino nthaŵi zonse. Pamene anawo anali kukula tinazindikira kuti kuwaphunzitsa chikondi kunafuna kuti tidziŵe zomwe zili m’mitima yawo. Kuti tidziŵe zimenezo, tinkamvetsera zomwe akunena. Nthaŵi zina ana athu anali ndi madandaulo. Motero, Karla ndi ine tinali kukambirana nawo. Tinapatula mphindi 30 zokambirana nkhani ngati zimenezi tikamaliza phunziro la banja. Aliyense anali ndi mwayi wolankhula zakukhosi momasuka.

Mwachitsanzo, Thomas ndi Gabriele, ana athu aang’ono kwambiri, ankaona kuti makolofe timakondera mkulu wawo. Nthaŵi ina, iwo analankhula mosapita m’mbali amvekere: “Bambo, tikuona kuti Mayi ndi inuyo nthaŵi zonse m’mamulekerera Hans Werner kuchita zomwe akufuna.” Ndinadabwa kwambiri. Komabe, titaiganizira mofatsa nkhaniyo, Karla ndi ine tinavomereza kuti anawo akunena zoona. Motero, tinayesetsa kusamalira ana onse mofanana.

Nthaŵi zina, ndinkalanga ana mwankhanza kwambiri. Zikatero, makolofe tinali kuwapepesa anawo. Kenako, tinalinso kupepesa kwa Yehova m’pemphero. Zinali zofunika kuti ana azidziŵa kuti bambo awo anali kupepesa kwa Yehova ndiponso kwa iwowo. Motero, makolofe ndi ana tinali ogwirizana ndiponso okondana kwambiri. Nthaŵi zambiri iwo anali kunena kuti: “Inu ndinu anzathu apamtima.” Zimenezi zinkatisangalatsa kwambiri.

Kugwirira ntchito pamodzi kumachititsa banja kukhala logwirizana. Choncho, aliyense anali ndi ntchito yake yanthaŵi zonse. Hans Werner anali kukagula zakudya ndi zinthu zina ku masitolo kamodzi pa mlungu. Tinkam’patsa ndalama ndiponso mndandanda wa zinthu zofunika kukagula. Mlungu wina sitinam’patse chilichonse ndipo anafunsa mayi ake. Mayiwo anamuyankha kuti pakali pano tikadalibe ndalama. Anawo anayamba kunong’onezana, kenako aliyense anakatenga bokosi lake la ndalama n’kuzikhuthulira patebulo. Onse pamodzi anati: “Mayi, titha kupita kukagula zinthu tsopano.” Inde ana athu anaphunzira kuthandiza zinthu zikathina, ndipo zimenezi zinachititsa banja lathu kukhala logwirizana kwambiri.

Ana athu aamuna atakula ndithu, anayamba kufuna atsikana. Mwachitsanzo, Thomas ankafuna mtsikana wina wa Mboni mnzake wa zaka 16. Ndinamuuza kuti ngati watsimikizadi za mtsikanayo ayenera kukhala wokonzeka kumukwatira ndiponso kumusamalira pamodzi ndi ana. Thomas anazindikira kuti sanali wokonzeka kukwatira popeza anali ndi zaka 18 zokha.

Kupita Patsogolo Monga Banja

Ana athu, mmodzi ndi mmodzi ankaloŵa Sukulu ya Utumiki Wateokalase akadali aang’ono. Tinkawamvetsera kwambiri akamakamba nkhani zomwe awapatsa ndipo anali kutilimbikitsa kwambiri chifukwa tinkaona chikondi chochokera pansi pa mtima chomwe ali nacho kwa Mulungu. Oyang’anira dera ndiponso oyang’anira chigawo nthaŵi zina ankakhala nafe ndipo ankatisimbira zomwe akumana nazo pa moyo wawo kapena kutiŵerengera m’Baibulo. Amuna ameneŵa pamodzi ndi akazi awo anathandiza kwambiri kukulitsa chikondi chofuna utumiki wa nthaŵi zonse kwa aliyense wa m’banja lathu.

Tinkayembekezera misonkhano mwachidwi. Misonkhano inali njira yaikulu yophunzitsira ana athu kukhala ndi chilakolako chotumikira Mulungu. Kwa iwo, misonkhano inali nthaŵi yapadera yomwe ankavala mabaji awo asananyamuke kupita ku malo a msonkhano. Tinali osangalala kwambiri pamene Hans Werner anabatizidwa ali ndi zaka khumi. Anthu ambiri ankaona kuti anali akadali wamng’ono wosayenera kudzipatulira kwa Yehova, koma atakwanitsa zaka 50, iye anandiuza kuti akuthokoza kwambiri kuti watumikira Yehova kwa zaka 40.

Ana athu tinkawauza kuti ubale wa munthu aliyense payekha ndi Yehova ndi wofunika kwambiri, koma sitinali kuwaumiriza kuti adzipatulire. Komabe, tinali osangalala ana ena atapitanso patsogolo mpaka kubatizidwa panthaŵi yomwe iwowo anali okonzeka kutero.

Kuphunzira Kutula Nkhaŵa Zathu kwa Yehova

Tinalitu osangalala kwambiri mu 1971 pamene Hans Werner anamaliza maphunziro m’kalasi ya 51 ya Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo ndi kumutumiza ku Spain kukakhala mmishonale. Ana athu ena, mmodzi ndi mmodzi, nawonso anachitapo utumiki wa nthaŵi zonse. Zimenezi zinasangalatsa makolofe kwambiri. Nthaŵi imeneyi m’pamene Hans Werner anandipatsa Baibulo lomwe ndatchula koyambirira kwa nkhani ino. Banja lonse linaoneka ngati linali ndi chimwemwe chokwanira tsopano.

Kenako tinaona kuti tifunika kukhala pafupi kwambiri ndi Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti tinaona ana athu ena akuluakulu akukumana ndi mavuto amene anayesa chikhulupiriro chawo kwambiri. Mwachitsanzo, mwana wathu wamkazi wokondedwa Gabriele anakumana ndi vuto lalikulu. Mu 1976, iye anakwatirana ndi Lothar. Mwamunayo anadwala kwambiri atangokwatirana kumene. Gabriele anadwazika matendawo mpaka mwamunayo anamwalira atafooka kwambiri. Kuona munthu wa m’banja lathu akuyamba kudwala mpaka kumwalira kunatikumbutsa kuti tifunika thandizo lachikondi la Yehova.​—Yesaya 33:2.

Mwayi Wotumikira M’gulu la Yehova

Atandiika kukhala mtumiki wa mpingo (tsopano amati woyang’anira wotsogolera) mu 1955, ndinaona kuti sindine woyenerera udindo umenewo. Panali ntchito yambiri yofunika kuchitika, moti kuti ntchito za mpingo ziziyenda bwino nthaŵi zina ndinkadzuka folo koloko mmamaŵa. Mkazi wanga ndi ana anga anali kundithandiza kwambiri poonetsetsa kuti sakundisokoneza usiku ngati pali zina zoti ndichite.

Komabe, tinkakhala ndi nthaŵi yosangalala pamodzi monga banja mmene tingathere. Nthaŵi zina bwana wanga anali kundipatsa galimoto lake kuti ndipite ndi banja langa kokasangalala. Ana athu ankasangalala kwambiri tikapita kunkhalango kukaphunzira Nsanja ya Olonda. Tinalinso kupita limodzi kukaseŵera kumapiri. Nthaŵi zina tinali kuyimba motsatira limba langa uku tikuyenda m’nkhalango.

Mu 1978 anandiika kukhala woyang’anira dera wogwirizira (mtumiki woyendayenda). N’taona kuti utumikiwo ndachepa nawo, ndinapemphera kuti: “Yehova, ndikuona kuti utumikiwu sindingaukwanitse. Koma ngati mukufuna kuti ndiyesere, ndidzayesetsa mmene ndingathere.” Kenako patatha zaka ziŵiri, ndili ndi zaka 54, ndinapatsa bizinesi yanga mwana wanga wamwamuna wamng’ono Thomas kuti ndiye aziyendetsa.

Ana athu onse tsopano anali atakula ndipo zimenezi zinapatsa Karla ndi ine mwayi wochita zambiri mu utumiki wa Yehova. Chaka chomwecho anandiika kukhala woyang’anira dera ndipo anandipatsa dera lina la Hamburg ndiponso dera lonse la Schleswig-Holstein. Chifukwa choti tinalerapo ana kwa nthaŵi yaitali, tinali kumvetsa mwapadera mavuto amene makolo ndi ana akukumana nawo. Abale ambiri anali kutitchula kuti makolo awo a dera.

Patatha zaka khumi Karla akuyenda nane m’ntchito yadera, anamuchita opaleshoni. Chaka chomwecho, inenso madokotala anandipeza ndi kansa ya mu ubongo. Choncho, ndinasiya utumiki woyang’anira dera, n’kukandichita opaleshoni yaubongo. Zitatha zaka zitatu ndinayambanso kutumikira monga woyang’anira dera wogwirizira. Karla ndi ine tsopano tili ndi zaka za m’ma 70 ndipo sindikutumikiranso monga woyang’anira woyendayenda. Yehova watithandiza kuona kuti palibe chifukwa chokakamira maudindo amene sindingawakwanitse.

Tikayang’ana mmbuyo, Karla ndi ine timathokoza Yehova kwambiri chifukwa chotithandiza kuphunzitsa ana athu kukonda choonadi. (Miyambo 22:6) Zaka zonsezi, Yehova watitsogolera, kutiphunzitsa, ndiponso kutithandiza kukwaniritsa udindo wathu. Ngakhale ndife okalamba ndi ofooka tsopano, chikondi chathu kwa Yehova chidakali chanthete ndiponso champhamvu monga kale.​—Aroma 12:10, 11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, koma tsopano silikupezeka.

[Chithunzi patsamba 26]

Banja lathu likuyenda m’mphepete mwa m’tsinje wa Elbe, ku Hamburg, mu 1965

[Chithunzi patsamba 28]

A m’banja lathu ena pa msonkhano wa mayiko ku Berlin mu 1998

[Chithunzi patsamba 29]

Ndi mkazi wanga Karla