Mmene Mwana Wamwamuna Anathandizira Bambo Ake
Mmene Mwana Wamwamuna Anathandizira Bambo Ake
JAMES, wa ku England, yemwe ali ndi zaka za m’ma 30, akudwala kwambiri matenda aubongo ndipo satha kulankhula bwinobwino. Ngakhale zili choncho, iye wakhala akupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova ndi mayi ake ndi mlongo wake kwa zaka zambiri ndithu. Komabe, bambo ake analibe chidwi ndi chipembedzo cha anthu atatuwo. Usiku wina James atabwerako kumsonkhano womwe unali ndi chitsanzo cha mmene tingaitanire anzathu ku Chikumbutso cha imfa ya Kristu, anathamangira kuchipinda chake. Mayi ake atadabwa ndi zimenezo anam’tsatira ndipo anakam’peza ali pakalapakala kusanthula magazini akale a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Anatengapo imodzi yomwe inali ndi mawu oitanira anthu ku Chikumbutso pa tsamba lake lomaliza ndipo anathamangira kwa bambo ake. Anayamba ndi kuloza chithunzi chomwe chinali pa tsambalo kenako n’kuloza bambo akewo, nati: “Inu!” Mayi ndi bambo ake anayang’anana modabwa. Kenako anadziŵa kuti James akuitanira bambo ake ku Chikumbutso. Bambo akewo anati mwina adzapita.
Usiku wa Chikumbutso, James anapita m’kabati yosungira zovala ya bambo ake ndipo anatenga buluku n’kupita nalo kwa bambo ake n’kuwauza ndi manja kuti avale. Bambowo anayankha kuti sapita kumsonkhanoko. Zitatero, James ndi mayi ake anapita okha ku Nyumba ya Ufumu.
Komabe patapita nthaŵi, James anayamba kukana kwambiri mayi ake akamafuna kuti iye akonzeke kupita kumisonkhano ya mpingo. Iye ankanena kuti akufuna kukhala pakhomo ndi bambo ake. Kenako, Lamlungu lina mmaŵa, James anakananso kwambiri pamene mayi ake ankafuna kuti iye akonzeke kupita kumsonkhano. Mayi ake anadabwa kwambiri pamene bambo ake anam’funsa kuti: “James, ngati ine nditapita kumsonkhano lero, kodi iwenso upita?” James anaonetsa nkhope yosangalala. Anakumbatira bambo akewo, nati: “Inde!” ndipo onse atatu ananyamuka kupita ku Nyumba ya Ufumu.
Kuchokera tsiku limenelo bambo a James anapitiriza kupita kumisonkhano ya Lamlungu. Pasanapite nthaŵi yaitali ananena kuti afunika kumapitanso kumisonkhano inayo kuti akhwime mwauzimu. (Ahebri 10:24, 25) Zimenezi anachitadi ndipo patangotha miyezi iŵiri anayamba kuphunzira Baibulo nthaŵi zonse. Anapita patsogolo mofulumira ndipo mwamsanga anasintha zina ndi zina pa moyo wawo. Posakhalitsa, anayamba kuchita nawo ntchito yolalikira Ufumu. Patatha chaka chimodzi chiyambireni kuphunzira Baibulo, anapatulira moyo wawo kwa Yehova ndipo anasonyeza kudzipatulira kwawoko mwa kumizidwa m’madzi. Panopa ndi mtumiki wotumikira ku mpingo wawo. Tsopano onse m’banjamo akutumikira Yehova mogwirizana.