Yehova Amadana ndi Chinyengo
Yehova Amadana ndi Chinyengo
‘Musanyengezane yense ndi mnzake.’—MALAKI 2:10.
1. Kodi Mulungu amafuna kuti tichite chiyani ngati tikufuna kudzalandira moyo wosatha?
KODI mukufuna moyo wosatha? Ngati mumakhulupirira kuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha monga mmene Baibulo limalonjezera, mwina mungayankhe kuti ‘Inde.’ Koma ngati mukufuna kuti Mulungu adzakupatseni moyo wosatha m’dziko lake latsopano, muyenera kuchita zimene iye amafuna. (Mlaliki 12:13; Yohane 17:3) Kodi n’kupanda chilungamo kufuna kuti anthu opanda ungwiro achite zimenezo? Ayi n’chilungamo, chifukwa Yehova akutilimbikitsa kuti: “Ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ayi; ndi kum’dziŵa Mulungu koposa nsembe zopsereza.” (Hoseya 6:6) Motero, ngakhale anthu opanda ungwiro angachite zimene Mulungu amafuna.
2. Kodi Aisrayeli ambiri anachitira bwanji Yehova monyenga?
2 Komabe, si anthu onse amene amafuna kuchita zimene Yehova amafuna. Hoseya akuvumbula kuti ngakhale Aisrayeli ambiri sanafune kuchita zimene Yehova ankafuna. Mtundu wonsewo unavomera kukhala m’pangano lakuti udzamvera malamulo a Mulungu. (Eksodo 24:1-8) Komabe posakhalitsa, iwo anali ‘kulakwira chipangano’ mwa kuswa malamulo ake. Motero, Yehova ananena kuti Aisrayeliwo ‘anamuchitira monyenga.’ (Hoseya 6:7) N’zimenenso achita anthu ambiri kuyambira nthaŵi imeneyo. Koma Yehova amadana ndi chinyengo, kaya kuchitira iyeyo kapena anthu amene amam’konda ndi kum’tumikira.
3. Kodi tikambirana zotani m’nkhani ino?
3 Si mneneri Hoseya yekha amene anafotokoza mmene Mulungu amaonera chinyengo. Ifenso tifunika kuona chinyengo monga mmene Mulungu amaonera ngati tikufunadi kudzakhala ndi moyo wachimwemwe. Tinayamba kukambirana uthenga waulosi wa Malaki m’nkhani yoyamba ija, kuyamba ndi chaputala choyamba cha bukuli. Tsopano tiyeni tione chaputala chachiŵiri cha bukuli ndi kuona mmene chikufotokozera bwino mmene Mulungu amaonera chinyengo. Ngakhale kuti Malaki anali kufotokoza zochitika pakati pa anthu a Mulungu zaka zambiri atabwerako ku Babulo, chaputala chachiŵirichi n’chofunika kwambiri kwa ife.
Ansembe Olakwa
4. Kodi Yehova anachenjeza chiyani ansembe?
4 Chaputala 2 chikuyamba ndi mawu a Yehova odzudzula ansembe achiyuda chifukwa chosiya njira zake zolungama. Ngati sakanamvera uphungu wake ndi kusintha njira zawo, iwo akanaona zoopsa. Taonani zimene mavesi aŵiri oyambirira akunena. Akuti: “Ansembe inu, lamulo ili ndi la kwa inu. Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu.” Ngati ansembewo akanaphunzitsa anthu malamulo a Mulungu ndi kuwatsatira, akanalandira madalitso. Koma akanalandira matemberero ngati akananyalanyaza zimene Mulungu ankafuna. Ngakhale madalitso amene ansembewo akanalengeza akanasintha kukhala matemberero.
5, 6. (a) Kodi n’chifukwa chiyani ansembe makamaka ndi amene anali ndi mlandu? (b) Kodi Yehova anasonyeza motani kuti anaipidwa ndi ansembe?
5 N’chifukwa chiyani ansembe makamaka ndi amene anali ndi mlandu? Vesi 7, likuyankha momveka bwino kuti: “Milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziŵitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.” Zaka zoposa 1000 m’mbuyomo, malamulo a Mulungu amene anapatsa Aisrayeli kudzera mwa Mose ananena kuti ansembe anali ndi ntchito ‘yophunzitsa ana a Israyeli malemba onse amene Yehova ananena nawo.’ (Levitiko 10:11) N’zomvetsa chisoni kuti patapita nthaŵi, amene analemba 2 Mbiri 15:3 anasimba kuti: “Masiku ambiri . . . Israyeli anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo.”
6 M’nthaŵi ya Malaki, m’zaka za m’ma 400 B.C.E., vuto losoŵa ansembe ophunzitsa linalipobe. Ansembe anali kulephera kuphunzitsa anthu Chilamulo cha Mulungu. Motero ansembe amenewo anayenerera kuwaimba mlandu. Onani mawu amphamvu amene Yehova akuwauza. Malaki 2:3 akuti: ‘Ndidzawaza chiphwidza pankhope panu, ndicho chiphwidza cha nsembe zanu.’ Kuwadzudzulatu kwambiri kumeneku! Chipwidza cha nyama zomwe ankazipereka nsembe ankayenera kukachitentha kunja kwa msasa. (Levitiko 16:27) Koma pamene Yehova anawauza kuti m’malo mokatentha adzawawaza nacho chipwidzacho pa nkhope zawo, zikusonyeza bwinobwino kuti anaipidwa nawo ndipo anakana nsembe zawo ndiponso amene anali kupereka nsembezo.
7. N’chifukwa chiyani Yehova anawakwiyira aphunzitsi a Chilamulo?
7 Zaka mazana ambiri nthaŵi ya Malaki isanafike, Yehova anapatsa Alevi ntchito yosamalira chihema ndipo kenako kusamalira kachisi ndi kuchita utumiki wopatulika. Iwo anali aphunzitsi a mtundu wa Israyeli. Kukwaniritsa ntchitoyo kukanachititsa Aleviwo ndiponso mtundu wonsewo kukhala ndi moyo ndiponso mtendere. (Numeri 3:5-8) Koma Alevi anasiya kuopa Mulungu monga momwe ankamuopera poyamba. Motero, Yehova anawauza kuti: “Koma inu mwapambuka m’njira; mwakhumudwitsa ambiri m’chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi. . . . Simunasunga njira zanga.” (Malaki 2:8, 9) Ansembe anasocheretsa Aisrayeli ambiri chifukwa cha kulephera kwawo kuphunzitsa choonadi ndiponso chitsanzo chawo choipa. Motero, Yehova anayeneradi kuwakwiyira.
Kutsatira Miyezo ya Yehova
8. Kodi anthu sangathe kutsatira miyezo ya Mulungu? Fotokozani.
8 Tisaganize kuti ansembe amenewo anayenera kuwamvera chisoni ndi kuwakhululukira popeza anali anthu opanda ungwiro ndipo sakanatha kutsatira miyezo ya Mulungu. Mfundo ndi yakuti anthu angathe kutsatira malamulo a Mulungu, chifukwa Yehova safuna kuti anthu achite zimene sangathe. Mwinanso ansembe ena anatha kutsatira miyezo ya Mulungu panthaŵiyo, ndipo sitikukayika konse za wina amene anachitadi zimenezo pambuyo pake, Yesu, “Mkulu wansembe” woposa onse. (Ahebri 3:1) Malemba ananenadi za iye molondola kuti: “Chilamulo cha zoona chinali m’kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeka m’milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi mowongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu.”—Malaki 2:6.
9. Kodi ndani amene afalitsa choonadi mokhulupirika m’nthaŵi yathu ino?
1 Petro 2:5) Atsogolera kufalitsa choonadi cha Baibulo kwa anthu ena. Pamene mwaphunzira choonadi cha m’Baibulo chimene amaphunzitsa, kodi simunaone nokha kuti chilamulo cha choonadi chilidi m’kamwa mwawo? Iwo athandiza ambiri kuchoka m’zipembedzo zonyenga motero kuti pakalipano pali anthu miyandamiyanda pa dziko lonse amene aphunzira choonadi cha m’Baibulo ndi kuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha. Ndiyeno anthu amene awaphunzitsaŵa ali ndi mwayi wapadera wophunzitsa chilamulo cha choonadi kwa anthu enanso miyandamiyanda.—Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9.
9 Mofanana ndi Yesu, abale ake odzozedwa amene akuyembekezera kudzapita kumwamba, atumikira monga ‘ansembe oyera mtima, kupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu.’ (Tifunika Kusamala
10. Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kusamala?
10 Komabe tifunika kusamala. Tingaphonye mfundo zazikulu za pa Malaki 2:1-9. Kodi tonsefe, aliyense payekha, tikusamala kuti chosalungama chisapezeke pamilomo yathu? Mwachitsanzo, kodi achibale athu amatikhulupirira kuti timanena zoona? Nanga abale ndi alongo athu auzimu mumpingo amatikhulupirira? N’kosavuta kukhala ndi chizoloŵezi chofuna kusocheretsa ena ndi mawu athu othyasika amene tanthauzo lake tikulidziŵa tokha pansi pa mtima. Kapenanso munthu angakokomeze kapena kubisa mfundo zina pankhani inayake ya bizinesi. Kodi Yehova sangaone zimenezo? Ndipo ngati timachitadi zimenezo, kodi iye angalandire nsembe zachitamando zochokera pamilomo yathu?
11. Kodi ndani makamaka amene afunika kukhala osamala?
11 Kwa amene ali ndi mwayi wophunzitsa Mawu a Mulungu m’mipingo lerolino, lemba la Malaki 2:7 liyenera kuwachenjeza. Ilo likunena kuti milomo yawo “iyenera kusunga chidziŵitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo” pakamwa pawo. Aphunzitsi ameneŵa ali ndi udindo waukulu kwambiri, chifukwa Yakobo 3:1 akusonyeza kuti iwo ‘adzalangika koopsa.’ Ngakhale kuti ayenera kuphunzitsa mwamphamvu ndiponso mwachangu, zomwe akuphunzitsazo ziyenera kuchokera m’Mawu olembedwa a Mulungu ndipo malangizo awo ayenera kudzera m’gulu la Yehova. Ngati achita zimenezo, adzakhala ‘odziŵa kuphunzitsa ena.’ N’chifukwa chake akuwalangiza kuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.”—2 Timoteo 2:2, 15.
12. Kodi aphunzitsi afunika kusamala kwambiri za chiyani?
12 Ngati sitisamala, tingaphatikizepo maganizo athuathu pa zimene tikuphunzitsa malinga ndi zimene ifeyo timakonda. Imeneyo ndi ngozi yaikulu makamaka kwa munthu wodalira kwambiri mfundo zake ngakhale zikutsutsana ndi zimene gulu la Yehova limaphunzitsa. Koma chaputala 2 cha Malaki chikusonyeza kuti tiyenera kuyembekeza kuti aphunzitsi a mumpingo adzatsatira chidziŵitso chochokera kwa Mulungu osati maganizo awoawo amene angakhumudwitse nkhosa. Yesu anati: “Yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m’khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja.”—Mateyu 18:6.
Kukwatira Kapena Kukwatiwa ndi Wosakhulupirira
13, 14. Kodi Malaki anafotokoza chinyengo chotani?
13 Malaki chaputala 2, kuyambira pa vesi 10 kumapita m’tsogolo, chikufotokoza mwatchutchutchu za chinyengo. Malaki anatsindika njira ziŵiri zofanana, zimene anazitcha “chinyengo” mobwerezabwereza. Choyamba, onani kuti Malaki anayamba malangizo ake mwa kufunsa kuti: “Kodi sitili naye Atate mmodzi ife tonse? Sanatilenga kodi Mulungu mmodzi? Tichita monyengezana yense ndi mnzake chifukwa ninji, ndi kuipsa chipangano cha makolo athu?” Ndiyeno vesi 11 likuwonjezera kuti chinyengo chawocho chinali kuipitsa ‘kupatulika kwa Yehova.’ Kodi ankachita chiyani chimene chinali cholakwika kwambiri? Vesili latchulapo imodzi mwa njira zolakwikazo kuti: “[A]nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.”
14 Kunena kwina, Aisrayeli ena, amene anali anthu amtundu wodzipatulira kwa Yehova, anali atakwatira anthu amene sankamulambira iye. Kudziŵa nkhani yake yonse kukutithandiza kuona chifukwa chake kuchita zimenezi kunali kulakwa kwakukulu. vesi 10 likuti iwo anali ndi Atate mmodzi. Sanali kutanthauza Yakobo (wotchedwanso Israyeli), kapena Abrahamu, kapenanso Adamu. Malaki 1:6 akusonyeza kuti Yehova ndiye anali “Atate mmodzi.” Mtundu wa Israyeli unali paubale ndi Yehova. Analoŵa m’pangano lomwe Yehova anapangana ndi makolo awo. Limodzi mwa malamulo a m’pangano limenelo linali lakuti: “Musakwatitsane nawo; musam’patse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.”—Deuteronomo 7:3.
15. (a) Kodi anthu ena angaganize motani pamene akufuna kukwatira kapena kukwatiwa ndi wosakhulupirira? (b) Kodi Yehova anafotokoza chiyani pankhani ya ukwati?
15 Anthu ena lero angaganize kuti: ‘Munthu amene ndikufuna kukwatirana nayeyu ndi wabwino kwambiri. Nthaŵi ina yake adzayamba kutsatira kulambira koona.’ Kuganiza koteroko kukungotsimikizira chenjezo louziridwa lakuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika?” (Yeremiya 17:9) Pa Malaki 2:12 anafotokoza m’mene Mulungu amaonera kukwatira kapena kukwatiwa ndi wosakhulupirira. Anati: “Yehova adzalikha munthu wakuchita ichi.” Motero, Akristu akulangizidwa kukwatira kapena kukwatiwa “mwa ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Pakati pa Akristu, wokhulupirira akakwatira kapena kukwatiwa ndi wosakhulupirira, ‘salikhidwa.’ Komabe, ngati wosakhulupirirayo sasintha, n’chiyani chidzamuchitikire pamene Mulungu posachedwapa adzabweretse mapeto a dongosolo lino?—Salmo 37:37, 38.
Kuchitira Nkhanza Mwamuna Kapena Mkazi Wako
16, 17. Kodi ndi chinyengo chotani chimene ena anachita?
16 Malaki kenako akutchula cholakwa chachiŵiri: kuchitira nkhanza mwamuna kapena mkazi wako, makamaka mwa kusudzula popanda chifukwa chenicheni. vesi 14 ya chaputala 2 ikuti: “Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unam’chitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.” Mwa kuchitira chinyengo akazi awo, amuna achiyuda anachititsa guwa lansembe la Yehova kudzaza “misozi.” (Malaki 2:13). Amuna amenewo anali kuleka akazi awo pazifukwa zosamveka, kusiya akazi a ubwana wawo mosayenera, mwina kuti akwatire akazi achitsikana kapena achikunja. Ndipo ansembe achinyengo analola zimenezo. Koma, Malaki 2:16 akuti: “Ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israyeli.” Patapita nthaŵi, Yesu anasonyeza kuti ukwati ungathe chifukwa cha chigololo chokha basi ndipo wosalakwayo angakhale ndi ufulu wokwatira kapena kukwatiwanso.—Mateyu 19:9.
17 Taganizirani mawu a Malakiwo ndi kuona mmene akutikhudzira mtima ndi kutilimbikitsa kusonyeza chifundo. Akuti “mnzako, mkazi wa pangano lako.” Mwamuna aliyense wokhudzidwa ndi zimenezi anakwatira wolambira mnzake, mkazi wachiisrayeli, amene anam’sankha kukhala bwenzi lake lapamtima woti akhale naye kwa moyo wake wonse. Ngakhale kuti mwina anakwatirana ali achinyamata, kupita kwa nthaŵi ndi kukalamba sizinathetse pangano lawo loti adzakhalira limodzi monga banja kwa moyo wawo wonse.
18. Kodi uphungu wa Malaki pankhani ya chinyengo ukugwira ntchito motani lerolino?
18 Uphungu umenewo ukugwiranso ntchito chimodzimodzi lerolino. N’zomvetsa chisoni kuti ena amanyalanyaza malangizo a Mulungu onena za kukwatira kokha mwa Ambuye. N’zomvetsanso chisoni kuti ena sapitiriza kuyesetsa kuti ukwati wawo ukhalebe wolimba. M’malo mwake, amayesa kupeza chifukwa china ndi kuchita zimene Mulungu amadana nazo mwa kusudzula mosagwirizana ndi zifukwa za m’Malemba n’cholinga choti akwatire wina. Mwa kuchita zimenezo, iwo ‘amalemetsa Yehova.’ M’nthaŵi ya Malaki, amene ananyalanyaza malangizo a Mulungu anafika polingalira kuti maganizo a Yehova anali olakwika. Ndipotu ananena kuti: “Ali kuti Mulungu wa chiweruzo?” Kuganiza kopotokatu kumeneko! Tiyeni tisagwere mu msampha umenewo.—Malaki 2:17.
19. Kodi amuna okwatira ndi akazi okwatiwa angalandire bwanji mzimu wa Mulungu?
19 N’zolimbikitsa kuti Malaki akusonyeza kuti Vesi 15) N’zosangalatsa kuti gulu la Yehova lerolino ladzala ndi amuna oterowo amene ‘amachitira ulemu akazi awo.’ (1 Petro 3:7) Amuna ameneŵa sazunza akazi awo kapena kuwatukwana, saumirira kuti azichita machitidwe ena a kugonana osayenera, ndiponso sapeputsa akazi awo mwa kuyamba zibwenzi ndi akazi ena kapena kuonera zolaula. N’zosangalatsanso kuti gulu la Yehova ladzala ndi akazi achikristu okhulupirika amene amamvera Mulungu ndi kutsatira malamulo ake. Amuna ndi akazi ameneŵa amadziŵa zimene Mulungu amadana nazo, ndipo amaganiza ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi zimenezo. Pitirizanibe kukhala ngati amuna ndi akazi ameneŵa, ‘kumvera Mulungu’ ndi kudalitsidwa ndi mzimu wake woyera.—Machitidwe 5:29.
amuna ena sanachitire chinyengo akazi awo. ‘Mzimu woyera wa Mulungu unawatsalira’ amuna ameneŵa. (20. Kodi n’chiyani chidzachitikira anthu onse posachedwapa?
20 Posachedwapa, Yehova aweruza dziko lonse lapansili. Munthu aliyense adzadziŵerengera mlandu kwa iye pa zimene anali kukhulupirira ndi kuchita. “Munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.” (Aroma 14:12) Tsopano funso lochititsa chidwi n’lakuti: Kodi ndani adzapulumuka tsiku la Yehova? Nkhani yachitatu komanso yomaliza m’nkhani zotsatizana zino ifotokoza mfundo imeneyi.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi Yehova anadzudzula ansembe a Israyeli pa chifukwa chachikulu chiti?
• N’chifukwa chiyani miyezo ya Mulungu siili yoti anthu sangakwanitse kuitsatira?
• N’chifukwa chiyani tifunika kusamala pophunzitsa lerolino?
• Kodi ndi zinthu ziŵiri ziti zimene Yehova anadana nazo?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 15]
M’nthaŵi ya Malaki ansembe anawadzudzula chifukwa chosatsatira malangizo a Yehova
[Chithunzi patsamba 16]
Tiyenera kusamala kuphunzitsa malangizo a Yehova osati maganizo athu
[Zithunzi patsamba 18]
Yehova anadzudzula Aisrayeli amene anasudzula akazi awo pazifukwa zosamveka ndi kukwatira akazi ena achikunja
[Chithunzi patsamba 18]
Akristu lerolino amalemekeza pangano lawo la ukwati