Kodi Mumaphunzitsa Zogwira Mtima?
Kodi Mumaphunzitsa Zogwira Mtima?
MAKOLO, akulu, ndiponso olalikira uthenga wabwino ayenera kukhala aphunzitsi. Makolo amaphunzitsa ana awo, akulu amaphunzitsa anthu a mumpingo wachikristu, ndipo olalikira uthenga wabwino amaphunzitsa anthu atsopano amene ali ndi chidwi. (Deuteronomo 6:6, 7; Mateyu 28:19, 20; 1 Timoteo 4:13, 16) Kodi mungatani kuti kuphunzitsa kwanu kukhale kogwira mtima kwambiri? Njira imodzi ndiyo kutsatira zitsanzo ndi njira zimene ankagwiritsa ntchito aphunzitsi aluso amene awatchula m’Mawu a Mulungu. Mmodzi mwa aphunzitsi ameneŵa anali Ezara.
Kuphunzira pa Chitsanzo cha Ezara
Ezara anali wansembe amene anabadwa mumzere wa Aroni ndipo ankakhala ku Babulo zaka pafupifupi 2,500 zapitazo. M’chaka cha 468 B.C.E, iye anapita ku Yerusalemu kuti akapititse patsogolo kulambira koona pakati pa Ayuda amene ankakhala kumeneko. (Ezara 7:1, 6, 12, 13) Kuti achite zimenezo anafunika kuphunzitsa anthu Chilamulo cha Mulungu. Kodi Ezara anachita chiyani pofuna kuonetsetsa kuti kuphunzitsa kwake kunali kogwira mtima? Anatsatira njira zothandiza zingapo. Onani njirazi zimene zili pa Ezara 7:10.
‘Pakuti Ezara [1] adaikiratu [“anakonzekeretsa,” NW] mtima wake [2] kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi [3] kuchichita, ndi [4] kuphunzitsa m’Israyeli malemba ndi maweruzo.’ Tiyeni tikambirane mwachidule njirazi imodzi ndi imodzi ndi kuona zimene tingaphunzirepo.
“Ezara Anakonzekeretsa Mtima Wake”
Ezara anakonzekeretsa mtima wake mwapemphero kuti alandire Mawu a Mulungu, monga mmene mlimi amachitira pamene amayamba kugaula nthaka pogwiritsa ntchito pulawo asanafese mbewu. (Ezara 10:1) M’mawu ena, iye ‘analozetsa mtima wake’ ku zimene Yehova amaphunzitsa.—Miyambo 2:2.
Mofananamo, Baibulo limanena kuti Mfumu Yehosafati ‘inalunjikitsa mtima wake kufuna Mulungu.’ (2 Mbiri 19:3) Mosiyana ndi ameneŵa, mbadwo wa Aisrayeli umene ‘sunakonza mtima wawo’ unali ‘woukira ndi wopikisana.’ (Salmo 78:8) Yehova amaona “munthu wobisika wamtima.” (1 Petro 3:4) Inde, iye “adzaphunzitsa ofatsa njira yake.” (Salmo 25:9) Choncho, n’kofunika kwambiri kuti aphunzitsi lerolino atsanzire chitsanzo cha Ezara mwa kukonzekeretsa mtima wawo mwapemphero.
“Kuchifuna Chilamulo cha Yehova”
Ezara anafuna Mawu a Mulungu kuti akhale mphunzitsi wogwira mtima. Ngati mutapita kwa dokotala kuti akakuthandizeni, kodi simungamvetsere mwatcheru ndi kuonetsetsa kuti mwamvetsadi zonse zimene anali kunena kapena zimene wakuuzani kuchita? Mosakayika, mudzachita zimenezo chifukwa chakuti moyo wanu uli pangozi. Ndiyetu tifunikanso kumvetsera mwatcheru kwambiri zimene Yehova amanena kapena amatiuza kuchita kudzera m’Mawu ake, Baibulo, ndiponso kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Tifunika kuchita zimenezo chifukwa chakuti malangizo ake amakhudza moyo wathu weniweniwo. (Mateyu 4:4; 24:45-47) Dokotala atha kulakwitsa, komatu “malamulo a Yehova ali angwiro.” (Salmo 19:7) Sitingafunikirenso kufunafuna malangizo kwa wina kusiyapo iyeyo.
Mabuku a m’Baibulo a Mbiri (omwe poyambirira Ezara anawalemba ngati buku limodzi) akusonyeza kuti Ezara anali wophunzira wofufuza mosamala. Pofuna kulemba mabuku amenewo, iye anagwiritsa ntchito magwero osiyanasiyana. * Ayuda omwe anangobwera kumene kuchokera ku Babulo, anafunikira kudziŵa mwachidule mbiri ya mtundu wawo. Sanali kudziŵa zambiri zokhudza malamulo a chipembedzo chawo, utumiki wa pa kachisi, ndi ntchito za Alevi. Anafunikanso kudziŵa mizere yawo yobadwira. Ezara anasamala mwapadera nkhani zimenezo. Ayuda anafunika kukhalabe mtundu wokhala ndi dziko lawo, kachisi, ansembe, ndi kazembe mpaka pamene Mesiya adzafike. Zimene Ezara anasonkhanitsa zikanachititsa mtunduwo kukhalabe wogwirizana ndipo kulambira koona kukanapitirizabe.
Kodi kaphunziridwe kanu kakufanana ndi mmene Ezara ankachitira? Kuphunzira Baibulo mwakhama kudzakuthandizani kuliphunzitsa kwa ena mogwira mtima.
‘Funani Chilamulo cha Yehova’ Monga Banja
Sikuti munthu angafune chilamulo cha Yehova paphunziro laumwini lokha ayi. Phunziro la banja ndi mpata winanso wabwino kwambiri wochitira zimenezi.
Jan ndi mkazi wake Julia, omwe ndi a ku Netherlands, akhala akuŵerengera ana awo aamuna aŵiri mokweza kuyambira tsiku limene mwana aliyense anabadwa. Pakalipano, Ivo ali ndi zaka 15 ndipo Edo ali ndi zaka 14, koma makolowo amawaŵerengerabe anawo asanakagone. Amachitabe phunziro la banja kamodzi pa mlungu. Jan anafokoza kuti: “Cholinga chathu chachikulu si chakuti tikambirane zambiri pa phunzirolo, koma kuti anyamatawo amvetse zimene takambirana.” Iye anawonjezera kuti: “Anyamatawo amafufuza kwambiri mawu achilendo ndi anthu amene awatchula m’Baibulo. Amafufuza kuti adziŵe kumene anthuwo ankakhala, anali ayani, ntchito imene ankagwira, ndi zina zotero. Kuyambira pamene anaphunzira kuŵerenga, iwo agwiritsapo ntchito mabuku monga lakuti Insight on the Scriptures, mabuku otanthauzira mawu, ndi mainsaikulopediya. Zimenezi zimachititsa phunziro la banja kukhala losangalatsa kwambiri. Nthaŵi zonse anyamatawa amayembekezera mwachidwi phunziro labanja.” Phindu linanso lowonjezera pamenepa n’lakuti anyamatawa tsopano amaposa anzawo onse a m’kalasi mwawo pa luso la chinenero.
John ndi mkazi wake Tini, omwenso ndi a ku Netherlands, anali kuphunzira ndi mwana wawo wamwamuna, Esli (tsopano ali ndi zaka 24 ndipo akuchita upainiya mumpingo wina), ndiponso mwana wawo wamkazi, Linda (tsopano ali ndi zaka 20 ndipo anakwatiwa ndi mbale wachinyamata wabwino kwambiri). Komabe, m’malo mophunzira buku linalake pogwiritsa ntchito njira yozoloŵereka ya mafunso ndi mayankho, iwo anali kugwirizanitsa phunziro la banjalo ndi msinkhu ndi zofunika za anawo. Kodi ankagwiritsa ntchito njira yotani?
John akufotokoza kuti ana akewo ankasankha nkhani yosangalatsa ya “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” (mu Nsanja ya Olonda) ndi “Lingaliro la Baibulo” (mu Galamukani!) Ndiyeno anali kufotokozera banjalo zimene akonzekera, zimene nthaŵi zonse zinkachititsa kukambirana kwa banja kukhala kosangalatsa kwambiri. Mwa njira imeneyi, achinyamatawo ankapeza luso lofufuza zinthu ndi kufotokoza zimene apeza. Kodi inu ‘mumafuna chilamulo cha Yehova’ ndi ana anu? Zimenezi zidzapititsa patsogolo luso lanu lophunzitsa ndiponso zidzathandiza ana anu kukhala aphunzitsi ogwira mtima.
“Kuchichita”
Ezara ankachita zimene ankaphunzira. Mwachitsanzo, pamene anali ku Babulo, ayenera kuti ankakhala moyo wabwino kwambiri. Komabe, atazindikira kuti akanatha kuthandiza anthu ake omwe anali kunja kwa Babulo, iye anasiya moyo wabwino wa ku Babulo n’kupita ku mzinda wa Yerusalemu womwe unali kutali ndiponso komwe kunali zosoŵa zambiri, mavuto, ndiponso moyo sunali wotetezeka kwenikweni. Mwachionekere, Ezara sanangodziŵa kokha za m’Baibulo koma anali wokonzeka kuchita zimene anaphunzirazo.—1 Timoteo 3:13.
Kenako, pamene anali kukhala mu Yerusalemu, Ezara anasonyeza kuti ankachita zimene anaphunzira ndi kuphunzitsa. Zimenezi zinaoneka pamene iye anamva kuti amuna achiisrayeli anakwatira akazi achilendo. Baibulo limatiuza kuti iye ‘anang’amba chovala chake, ndi malaya ake, ndi kumwetula tsitsi la pamutu pake ndi ndevu zake, ndi kukhala pansi m’kudabwa mpaka madzulo.’ Iye mpaka ‘anagwa nkhope ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yake’ kwa Yehova.—Ezara 9:1-6.
Kuphunzira kwake Chilamulo cha Mulungu kunakhudza kwambiri mtima wake. Ezara anadziŵa bwino kuti anthuwo adzakumana ndi mavuto aakulu chifukwa cha kusamvera kwawo. Ayuda amene anabwerera kudziko lawo anali ochepa kwambiri. Ngati akanakwatirana ndi anthu akunja, akanatha kusakanikirana ndi mitundu yachikunjayo, ndipo kulambira koona kukanatheratu padziko lapansi mosavuta.
N’zosangalatsa kuti chitsanzo cha Ezara cha mantha enieni ndi changu zinachititsa Aisrayeli kuwongolera njira zawo. Anachotsa akazi awo achilendowo. Miyezi itatu isanathe, zonse zinali zili bwino. Kukhulupirika kwa Ezara pa Chilamulo cha Mulungu kunathandiza kwambiri kuti kuphunzitsa kwake kukhale kogwira mtima.
N’chimodzimodzinso lerolino. Tate wina wachikristu anati: “Ana sachita zimene umanena, amachita zimene umachita!” Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito mumpingo wachikristu. Akulu amene amapereka chitsanzo chabwino, mpingo ungamvere zimene akuphunzitsa.
“Kuphunzitsa m’Israyeli Malemba ndi Maweruzo”
Palinso chifukwa china chimene chinachititsa kuphunzitsa kwa Ezara kukhala kogwira mtima. Sanaphunzitse za m’mutu mwake, m’malo mwake anaphunzitsa “malemba ndi maweruzo.” Ankaphunzitsa malamulo a Yehova. Umenewu unali udindo wake monga wansembe. (Malaki 2:7) Ankaphunzitsanso maweruzo kapena kuti chilungamo, ndipo anapereka chitsanzo pa zimene anali kuphunzitsa mwa kutsatira malamulo mosakondera ndiponso mopanda tsankho, ankachita malinga ndi mmene zinayenera kukhalira. Amene ali ndi ulamuliro akamachita chilungamo, anthu adzakhala okhazikika ndipo zotsatira zake zingakhale zokhalitsa. (Miyambo 29:4) Mofananamo, akulu achikristu, makolo, ndi olalikira Ufumu amene akudziŵa bwino Mawu a Mulungu adzalimbitsa moyo wauzimu wa mpingo, mabanja awo, ndiponso anthu achidwi ngati aphunzitsa malamulo a Yehova ndi chilungamo chake.
Kodi simukuvomereza kuti kuphunzitsa kwanu kungakhale kogwira mtima ngati mutsanzira kwambiri chitsanzo cha Ezara wokhulupirika? Choncho, ‘konzekeretsani mtima wanu, funani chilamulo cha Yehova, chichiteni, ndiponso phunzitsani malamulo ndi maweruzo a Yehova.’—Ezara 7:10.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 M’buku la Insight on the Scriptures Voliyumu 1, lomwe Mboni za Yehova zimafalitsa, pa masamba 444-5 mungapeze ndandanda ya magwero okwana 20.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 22]
KODI N’CHIYANI CHINACHITITSA KUPHUNZITSA KWA EZARA KUKHALA KOGWIRA MTIMA?
1. Anakonzekeretsa mtima wake
2. Anafuna Chilamulo cha Yehova
3. Anapereka chitsanzo chabwino mwa kuchita zimene anaphunzira
4. Anaphunzira mwakhama kuti aphunzitse zimene Malemba amanena