Lambirani Mulungu “Mumzimu”
Lambirani Mulungu “Mumzimu”
“Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumuyerekeza ndi chithunzithunzi chotani?”—YESAYA 40:18.
MWINA mumatsimikiza ndi mtima wonse kuti kugwiritsa ntchito mafano polambira Mulungu n’kovomerezeka. Ndipo mwinanso mumaganiza kuti kutero kumakuthandizani kukhala bwenzi lenileni la Wakumva pemphero yemwe saoneka ndiponso yemwe munthu ungaganize kuti si weniweni komanso wosadziŵika bwino.
Koma kodi tili ndi ufulu wonse wosankha njira yathuyathu yolankhulirana ndi Mulungu? Kodi Mulungu sindiye woyenera kutilamulira njira yolankhulirana naye yovomerezeka komanso kutiletsa njira yosavomerezeka? Yesu anafotokoza maganizo a Mulungu pankhaniyi mwa kunena kuti: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” (Yohane 14:6) Mawuŵa pawokha akuletsa kugwiritsa ntchito mafano kapena zinthu zina zonse zopatulika.
Inde, pali mtundu umodzi wokha wa kulambira umene Yehova Mulungu amavomereza. Kodi mtundu umenewu ndi uti? Nthaŵi ina, Yesu ananena kuti: “Ikudza nthaŵi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omulambira Iye ayenera kumulambira mumzimu ndi m’choonadi.”—Yohane 4:23, 24.
Kodi fano lingaimire Mulungu yemwe ndi “mzimu.” Ayi. Ngakhale fano litakhala lokongola chotani silingafanane m’pang’ono pomwe ndi ulemerero wa Mulungu. Chotero, fano silingaimire Mulungu weniweni. (Aroma 1:22, 23) Kodi munthu angalambire Mulungu “m’choonadi” ngati amalankhula naye kudzera mwa mafano omwe anthu anapanga?
Chiphunzitso Chomveka Bwino cha m’Baibulo
Chilamulo cha Mulungu chinaletsa kulambira mafano. Lamulo lachiŵiri la Malamulo Khumi limati: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, Eksodo 20:4, 5) Malemba Achikristu ouziridwa amalamulanso kuti: “Thaŵani kupembedza mafano.”—1 Akorinto 10:14.
kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo.” (N’zoona kuti ambiri amanena kuti akamagwiritsa ntchito zithunzi polambira sikuti amapembedza mafano ayi. Mwachitsanzo, Akristu a tchalitchi cha Orthodox, nthaŵi zambiri akamaweramira zithunzi, kuzigwadira, ndiponso kupemphera, amakana kuti sakulambira zithunzizo. Wansembe watchalitchi cha Orthodox analemba kuti: “Timalemekeza kwambiri zithunzi chifukwa chakuti ndi zinthu zopatulika, komanso chifukwa chakuti timalemekeza kwambiri amene ali pazithunzi zimenezo.”
Komabe, funso n’lakuti: Kodi Mulungu amavomereza kugwiritsa ntchito mafano ngakhale cholinga chake chitakhala kupereka ulemu kwa Mulungu kudzera pa chithunzicho? Baibulo sililoleza m’pang’ono pomwe kuchita zimenezi. Aisrayeli ataimika fano la mwana wang’ombe lomwe cholinga chake ankati chinali kulemekeza Yehova, iye anawadzudzula kwambiri, ndipo ananena kuti iwo apanduka.—Eksodo 32:4-7.
Ngozi Yobisika
Kugwiritsa ntchito zinthu zina polambira n’koopsa. Anthu ochita zimenezi angayambe mosavuta kumalambira zinthuzo m’malo molambira Mulungu amene iwo amati zinthuzo zimamuimira. M’mawu ena, tingati zinthuzo ndizo zimakhala zofunika kwambiri polambira.
Zimenezi n’zimene zinachitika ndi zinthu zambiri Numeri 21:8, 9; 2 Mafumu 18:4.
zomwe zinaliko m’nthaŵi ya Aisrayeli. Mwachitsanzo, Mose anapanga njoka yamkuwa paulendo wochokera ku Igupto. Poyamba, chizindikiro cha njokayo pamtengo chinali njira yochiritsira. Anthu amene njoka zinkawaluma monga chilango ankayang’ana pa njoka yamkuwayo ndipo Mulungu anali kuwathandiza. Koma Aisrayeli atakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa, zikuoneka kuti anaika njoka yamkuwayo kukhala fano, ngati kuti njokayo payokha inali ndi mphamvu zochiritsa. Ankaifukizira zofukiza ndipo mpaka anaipatsa dzina lakuti Chimkuwa.—Aisrayeli anagwiritsaponso ntchito likasa la chipangano monga chithumwa chowathandiza polimbana ndi adani awo ndipo zotsatira zake zinali zoopsa. (1 Samueli 4:3, 4; 5:11) M’nthaŵinso ya Yeremiya, anthu okhala mu Yerusalemu anali kuika mtima kwambiri pa kachisi kusiyana ndi Mulungu amene anali kumulambira m’kachisiyo.—Yeremiya 7:12-15.
Chizoloŵezi cholambira zinthu zina m’malo molambira Mulungu n’chofalabe masiku ano. Wofufuza wina Vitalij Ivanovich Petrenko anati: “Anthu . . . amalambira zithunzi ndipo ali pa ngozi ya kulambira mafano . . . Munthu ayenera kuvomereza kuti kulambira kotereku n’kwachikunja ndipo kunayamba chifukwa cha zikhulupiriro zotchuka.” Mofananamo, m’buku lake lakuti Understanding the Greek Orthodox Church, wansembe watchalitchi cha Greek Orthodox, Demetrios Constantelos, ananena kuti: “N’zotheka kwambiri Mkristu kumalambira chithunzi chinachake.”
Zomwe ena amanena kuti zithunzi ndi zinthu zothandizira chabe polambira sizoona ayi. Chifukwa chiyani tikutero? Eya, anthu olambira zithunziwo amati zithunzi zina za
Mariya kapena za “oyera mtima” omwe anafa kale n’zoyenera kuzilambira kwambiri ndiponso n’zothandiza zedi kuposa zithunzi zina za anthu omwewo. Mwachitsanzo, chithunzi china cha Mariya ku Tínos, Greece, chili ndi otsatira odzipereka akeake a tchalitchi cha Orthodox, ndipo otsatira ena okhulupirika a tchalitchi chomwechi alinso ndi chithunzi chawochawo cha Mariya yemweyo ku Soumela, kumpoto kwa Greece. Magulu aŵiri onseŵa amakhulupirira kuti chithunzi chawo ndicho chopambana, chimachita zozizwitsa zambiri kuposa chinacho, ngakhale kuti zonsezo n’zithunzi za munthu mmodzi yemwe anafa kale. Choncho, anthu ndiwo amapatsa mphamvu zithunzi kenako n’kumazilambira.Kupemphera kwa “Oyera Mtima” Kapena kwa Mariya
Bwanji nanga za kulambira anthu ngati Mariya kapena “oyera mtima”? Yesu poyankha Satana amene anali kumuyesa, anagwira mawu omwe ali pa Deuteronomo 6:13. Anati: “Ambuye Mulungu wako udzam’gwadira, ndipo iye yekha yekha udzam’lambira.” (Mateyu 4:10) Yesu kenako ananena kuti olambira oona adzalambira “Atate” osati wina aliyense ayi. (Yohane 4:23) Pozindikira zimenezi, mngelo anadzudzula mtumwi Yohane chifukwa chofuna kumulambira. Mngeloyo anati: ‘Usachite [zimenezi] . . . lambira Mulungu.’—Chivumbulutso 22:9.
Kodi n’koyenera kupemphera kwa Mariya, mayi wa Yesu, kapena kwa “oyera mtima” ena kuti atiimire kwa Mulungu? Yankho losapita m’mbali la m’Baibulo n’lakuti: “Pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu.”—1 Timoteo 2:5.
Tetezani Ubwenzi Wanu ndi Mulungu
Kugwiritsa ntchito mafano polambira sikungathandize anthu kuti Mulungu awakonde ndi kuwapulumutsa chifukwa chakuti n’kosemphana ndi chiphunzitso chomveka bwino cha m’Baibulo. Mosiyana ndi zimenezi, Yesu ananena kuti tingathe kupeza moyo wosatha pokhapokha titaphunzira za Mulungu woona yekha ndi kudziŵa bwinobwino makhalidwe ake omwe ndi oposa a wina aliyense, komanso zolinga zake ndi mmene amachitira zinthu ndi anthu. (Yohane 17:3) Mafano saona, samva kukhudza, ndiponso salankhula. Choncho, sangathandize munthu kudziŵa Mulungu ndi kumulambira m’njira yovomerezeka. (Salmo 115:4-8) Kuphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo, ndiko njira yokha yopezera maphunziro ofunika kwambiri ameneŵa onena za Mulungu woona yekha.
Kuwonjezera pa mfundo yoti mafano alibe phindu, kuwalambira kuli ndi ngozi zauzimu. Ngozi zotani? Ngozi yoyamba ndiponso yaikulu n’njakuti kulambira mafano kungawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Ponena za Aisrayeli omwe ‘anautsa mkwiyo wake ndi [mafano] onyansa,’ Mulungu ananeneratu kuti: “Ndidzawabisira nkhope yanga.” (Deuteronomo 32:16, 20) Iwo anafunikira ‘kutaya mafano’ awo auchimo kuti akhalenso ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu.—Yesaya 31:6, 7.
Chotero, uphungu wa m’Malemba ndi woyenerera kwambiri. Umati: “Tiana, dzisungireni nokha kupeŵa mafano.”—1 Yohane 5:21.
[Bokosi patsamba 6]
Anawathandiza Kulambira “Mumzimu”
Olivera anali wokonda mapemphero kwambiri ku Tchalitchi chake cha Orthodox ku Albania. Dzikolo litatseka zipembedzo mu 1967, Olivera anapitiriza kuchita mapemphero a tchalitchi chakecho mobisa. Anagula mafano a golide ndi siliva, zofukiza, ndi makandulo pogwiritsa ntchito ndalama zochepa zomwe analandira atapuma pantchito. Iye ankabisa mafanowo mkati mwa bedi lake ndipo nthaŵi zambiri ankagona pampando womwe unali pafupi ndi bedilo poopa kuti ena angawaone mafanowo kapena kuwaba. Atakumana ndi Mboni za Yehova kumayambiriro kwa m’ma 1990, Olivera anazindikira choonadi chenicheni cha m’Baibulo muuthenga wawo. Anaona zomwe Baibulo limanena kuti amene afuna kulambira Mulungu moona ayenera kumulambira “mumzimu.” Anadziŵanso mmene Mulungu amamvera pankhani ya kugwiritsa ntchito mafano. (Yohane 4:24) Mboni yomwe inkaphunzira naye Baibulo inaona kuti m’nyumba ya Olivera mafano akucheperachepera nthaŵi iliyonse yomwe Mboniyo yapita kunyumbako. Mapeto ake, mafano onse anatha. Olivera atabatizidwa, anati: “Lero ndili ndi mzimu woyera wa Yehova, m’malo mwa mafano achabechabe. Ndikuthokoza kwambiri kuti mzimu wake umangobwera pa ine popanda kugwiritsa ntchito mafano.”
Athena, wa pa chilumba cha Lesbos ku Greece, nayenso anali wokonda mapemphero kwambiri ku Tchalitchi chake cha Orthodox. Iye anali wa kwaya ndipo ankatsatira kwambiri miyambo yachipembedzo kuphatikizapo kugwiritsa ntchito mafano. Mboni za Yehova zinamuthandiza Athena kuzindikira kuti si zonse zomwe anamuphunzitsa zomwe zili zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Mwa zina, Mbonizo zinamuuza kuti Baibulo limaletsa kugwiritsa ntchito mafano ndiponso mitanda polambira. Athena anaumirirabe ndipo anati akafufuza yekha za chiyambi cha mafano achipembedzowo. Atafufuza mozama kwambiri m’mabuku osiyanasiyana, anapezadi kuti amene anayambitsa mafanowo sanali Akristu ayi. Chifukwa chofunitsitsa kulambira Mulungu “mumzimu,” iye anataya mafano ake onse ngakhale kuti anawagula ndi ndalama zambiri. Komabe, Athena anali wokonzeka kutaya chilichonse n’cholinga chofuna kulambira Mulungu m’njira yoyera mwauzimu ndiponso yovomerezeka.—Machitidwe 19:19.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]
Kodi Mafano Azithunzi ndi Luso Chabe la Zojambulajambula?
M’zaka zaposachedwapa, anthu asonkhanitsa mafano azithunzi a tchalitchi cha Orthodox padziko lonse. Anthuŵa amaona kuti mafanoŵa si zinthu zopatulika zachipembedzo koma kuti ndi luso chabe la zojambulajambula zosonyeza chikhalidwe cha anthu a mu ufumu wa Byzantine. Sizachilendo kupeza mafano ambiri azithunzi ngati ameneŵa atawaika monga zokongoletsa m’nyumba kapena mu ofesi ya munthu wokana Mulungu.
Komabe, Akristu oona saiwala cholinga choyambirira cha mafano azithunziŵa. Cholinga chake chinali kuwalambira. Ngakhale kuti Akristu satsutsana ndi ufulu wa anthu ena ngati akufuna kukhala ndi mafanoŵa, Akristuwo sasunga mafano, ngakhale kuwaona ngati zinthu wamba. Iwo amatero mogwirizana ndi mfundo yomwe ili pa Deuteronomo 7:26 yomwe imati: “Musamaloŵa nacho chonyansachi [fano] m’nyumba mwanu, kuti mungawonongeke konse pamodzi nacho; muziipidwa nacho konse, ndi kunyansidwa nacho konse.”
[Chithunzi patsamba 7]
Mulungu sanavomereze kugwiritsa ntchito mafano polambira
[Chithunzi patsamba 8]
Kudziŵa zomwe Baibulo limanena kumatithandiza kulambira Mulungu mumzimu