Kukonda Anthu “Oyera Mtima” Masiku Ano
Kukonda Anthu “Oyera Mtima” Masiku Ano
“Kodi mukukumbukira nthaŵi imene tinkaoneka ngati tikunyansidwa ndi mawu akuti woyera mtima? Koma zimenezi sizinawakhudze anthu a ku America okwana 4.2 miliyoni amene anaonera maliro a Mayi Teresa pa September 13. Kuyambira pa September 5, tsiku limene anamwalira, anthu akhala akuvutitsa ku Vatican kuti am’vomereze mayiyu kukhala munthu woyera mtima. Anthu ochepa akukayikira ngati zimenezi zitheke.”—Sun-sentinel, United States, October 3, 1997.
ANTHU ambiri amaona kuti ntchito zothandiza anthu ovutika, zimene Mayi Teresa, mmishonale wachikatolika ankachita, n’zimene zimapangitsa munthu kukhala woyera mtima weniweni. M’zipembedzo zina mumapezekanso anthu oyera mtima. Koma palibe amene amavomerezedwa ndi anthu ambiri kuti ndi woyera mtima monga mmene amavomerezera woyera mtima woikidwa ndi Tchalitchi cha Roma Katolika.
Papa Yohane Paulo wachiŵiri, paudindo wake waupapa anaika anthu oposa 450 kukhala oyera mtima. Anthu ameneŵa anaposa chiŵerengero chonse cha anthu amene apapa a m’zaka za m’ma 1900 anawavomereza kukhala oyera mtima. * N’chifukwa chiyani anthu akukonda kwambiri anthu “oyera mtima,” amene ambiri a iwo si odziŵika kwenikweni kwa Akatolika ambiri?
Lawrence Cunningham katswiri wa zaumulungu pa yunivesite ya m’mzinda wa Notre Dame ku America anati: “Anthu amachita chidwi kumva kuti m’dzikoli muli anthu oyera mtima. Anthu oyera mtima amasonyeza kuti n’zotheka kukhala woyera mtima ngakhale masiku ano.” Komanso pali chikhulupiriro chakuti “oyera mtima” ali ndi mwayi wapadera wofika kwa Mulungu, zimene zimawapangitsa kukhala anthu oyenera kupempherera anthu amoyo. Akapeza zinthu kapena mafupa a munthu “woyera mtima” amazilambira pokhulupirira kuti zili ndi mphamvu ina yake.
Katekisimu wa Msonkhano wa ku Trent, amene anasindikizidwa m’zaka za m’ma 1500 wofuna kutsimikizira chikhulupiriro cha Akatolika anagamula kuti: “M’pake kunena kuti, kulemekeza anthu oyera mtima ‘amene anafa mwa Ambuye,’ kuwapempha kuti atipempherere, ndiponso kulambira zinthu zawo zopatulika ndi phulusa la mitembo yawo, sizichepetsa n’komwe ulemerero wa Mulungu koma zimauwonjezera. Chiyembekezo cha Mkristuyo chimalimbikitsidwa ndiponso zimamulimbikitsa kutsatira makhalidwe a anthu oyera mtimawo. (The Catechism of the Council of Trent, 1905) Akristu oona amafunadi kutsatira makhalidwe abwino pamoyo wawo, kum’fikira Mulungu moyenera, ndiponso kuti Mulungu awathandize. (Yakobo 4:7, 8) Choncho malinga ndi Mawu a Mulungu, kodi ndani akukwanira kukhala oyera mtima enieni? Ndipo kodi amagwira ntchito yanji?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Kuvomereza anthu kukhala oyera mtima kumapangitsa munthu watchalitchi cha Roma Katolika amene anamwalira kukhala woyenera kulemekezedwa ndi anthu onse.