Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anapindula Chifukwa cha Khama

Anapindula Chifukwa cha Khama

Anapindula Chifukwa cha Khama

Anthu ambiri oona mtima amafuna kuti amene amawakonda aphunzire zolinga za Mulungu kuti nawonso akhale ndi moyo wosangalatsa. Munthu akapatulira moyo wake kwa Mulungu, anthu ena, achichepere ndi achikulire omwe, amakhala kuti anam’thandiza kusankha chinthu chabwino chimenechi mwa makhalidwe awo abwino. Ndi mmene zinalili ndi mtsikana wina wa ku Mexico, dzina lake Jearim amene anapereka kakalata ka mawu ali m’munsiŵa kwa abale ena patsiku la msonkhano wapadera wa Mboni za Yehova:

“Ndikufuna ndikuuzeni mmene ndasangalalira. Ndiloleni ndikuuzeni chifukwa chake. Zaka 18 zapitazo, ine ndisanabadwe, makolo anga anaphunzira choonadi. Mayi anga analimbikira kwambiri, ndipo kenako ine ndi mchimwene wanga tinalimbikiranso. Tonse tinkapempha Yehova kuti nawonso bambo adzakhale pa njira ya kumoyo. Papita zaka 18, ndipo lero ndi tsiku lapadera kwambiri kwa ife. Bambo anga akubatizidwa lero. Ndikuthokoza Yehova kuti sanabweretse chimaliziro tsiku limene takhala tikulidikirali lisanafike. Zikomo kwambiri, Yehova!”

Mosakayikira kwa zaka zambiri, banja la mtsikana ameneyu lakhala likuganizira mfundo za makhalidwe abwino zimene zili pa malangizo ouziridwa a pa 1 Petro 3:1, 2, amene amati: “Akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu.” Ndipo mosakayikira Jearim wachichepereyo anagwiritsira ntchito mawu a pa Deuteronomo 5:16 amene amati: “Lemekeza atate wako ndi amako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira.” Ndithudi, kugwiritsa ntchito mfundo za makhalidwe abwino zimenezi ndiponso kudikira Yehova moleza mtima kunapindulitsa Jearim ndi a m’banja lake.