Asanaphunzire ndi Ataphunzira Mawu a Mulungu Akugwira Ntchito
“Yandikirani kwa Mulungu, Ndipo Adzayandikira kwa Inu”
Asanaphunzire ndi Ataphunzira Mawu a Mulungu Akugwira Ntchito
MUKANAKUMANA ndi Tony nthaŵi imene anali ndi zaka 13 mpaka 16, mukanaona kuti anali mnyamata waukali ndiponso wamtopola amene ankakhala m’madera osaoneka bwino mumzinda wa Sydney ku Australia. Ena mwa anzake anali zigaŵenga. Nthaŵi zambiri anali kuba, kumenyana ndi zigaŵenga ndiponso kuwomberana mfuti m’miseŵu.
Tony anayamba kusuta ali ndi zaka zisanu ndi zinayi. Pamene amafika zaka 14 n’kuti ali wokonda kusuta chamba ndiponso wamakhalidwe oipa. Pamene anali ndi zaka 16, ankakonda kwambiri mankhwala osokoneza bongo a heroin, ndipo izi zinam’pangitsa kumagwiritsa ntchito cocaine, LSD—“inde china chilichonse chimene chikanandiledzeretsa,” monga mmene Tony akunenera. Ndiyeno anagwirizana ndi magulu aŵiri aupandu kuti azigulitsa mankhwala osokoneza bongo. Mosapita nthaŵi Tony anadziŵika monga mmodzi wa anthu odalirika kwambiri ogulitsa mankhwala osokoneza bongo m’mphepete mwa nyanja kum’maŵa kwa Australia.
Chizoloŵezi cha Tony chogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo a heroin ndi chamba chinali kumuwonongetsa ndalama zokwana madola kuyambira 160 mpaka 320 pa tsiku. Koma banja lake linali kukumana ndi mavuto aakulu kuposa pamenepo. Iye akuti: “Ine ndi mkazi wanga kangapo konse zigaŵenga zinatilozetsapo mfuti ndi mipeni kumaso pamene zinkafuna mankhwala osokoneza bongo ndi ndalama zimene tinali nazo m’nyumba mwathu.” Atatsekeredwa m’ndende katatu, Tony analimbikitsidwa kuona komwe moyo wake unali kupita.
Ngakhale ankapita ku tchalitchi, Tony ankaona kuti anali patali ndi Mulungu amene anthu amati amalanga anthu ochimwa mwa kuwawotcha m’helo kosatha. Komabe, Mboni za Yehova ziŵiri zitamufikira, Tony anadabwa kudziŵa kuti si mmene Mulungu alili. Ndipo Tony anasangalala kumva kuti angasinthedi moyo wake n’kulandira madalitso a Mulungu. Tony analimbikitsidwa ndi mawu a Yesu Kristu akuti: “Zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.” (Marko 10:27) Chinamukhudza mtima kwambiri Tony ndi mawu olimbikitsa akuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”—Yakobo 4:8.
Tsopano Tony anali ndi ntchito yovuta yosintha moyo wake kuti ugwirizane ndi miyezo ya m’Baibulo. Iye akuti: “Chinthu choyamba kusiya chinali kusuta, chimene sindikanatha m’mbuyomo, ngakhale kuti ndinayesa maulendo ambiri. Ndi mphamvu ya Yehova, ndinasiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo a heroin ndiponso chamba, zizoloŵezi zimene zinalamulira moyo wanga kwa zaka 15 za m’mbuyomo. Sindinkaganiza kuti zingatheke kusiya zizoloŵezi zimenezi.”
M’malo moopa Mulungu amene amazunza anthu kosatha ku helo, chiphunzitso chimene sichipezeka paliponse m’Baibulo, Tony ndi mkazi wake anakhala ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wamuyaya m’paradaiso padziko lapansi. (Salmo 37:10, 11; Miyambo 2:21) Tony akuti: “Panapita nthaŵi yaitali ndiponso panafunika khama kuti moyo wanga ugwirizane ndi miyezo ya Mulungu, koma ndapambana chifukwa cha thandizo la Yehova.”
Inde, munthu amene anali kukonda mankhwala osokoneza bongo ameneyu anakhala Mkristu. Popereka nthaŵi yawo ndi chuma chawo, iye ndi mkazi wake athera maola ambiri pantchito yophunzitsa Baibulo. Atanganidwanso kulera ana aŵiri oopa Mulungu. Kusintha kwakukulu kumeneku kunatheka mwa mphamvu yosalephera ya Mawu a Mulungu, Baibulo. Indedi, monga momwe mtumwi Paulo ananenera, “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita [“amphamvu,” NW].”—Ngakhale kuti pali zitsanzo zabwino zoterezi, ena amalankhula zopanda umboni kuti ntchito yophunzitsa Baibulo ya Mboni za Yehova imapasula mabanja ndiponso imawononga makhalidwe abwino a achinyamata. Nkhani ya Tony ikutsutsiratu mawu amenewo.
Monga Tony, ambiri aphunzira kuti zizoloŵezi zakupha zitha kugonjetsedwa. Motani? Mwa kukhulupirira Mulungu ndi kumudalira ndiponso kudalira Mawu ake, komanso mwa kuthandizidwa ndi mabwenzi achikristu amene amaganizira ndi kukonda anzawo. Tony mosangalala akuti: “Ndaona momwe mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo zatetezera ana anga. Ziphunzitso za Baibulo zapulumutsa ukwati wanga. Ndipo anthu amene ndikukhala nawo pafupi amagona tulo chifukwa chakuti sindiwawopsezanso.”
[Mawu Otsindika patsamba 9]
‘Mwa mphamvu ya Yehova ndinasiya chizoloŵezi chogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo chimene chinalamulira moyo wanga kwa zaka 15’
[Bokosi patsamba 9]
Mfundo za M’Baibulo Zikugwira Ntchito
Mfundo za m’Baibulo zosiyanasiyana zathandiza anthu ambiri okonda mankhwala osokoneza bongo kusiya chizoloŵezi chowononga chimenechi. Zina mwa mfundo zimenezi ndi izi:
“Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo n’kusamvera lamulo la Mulungu.
“Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova; kudziŵa Woyerayo ndiko luntha.” (Miyambo 9:10) Kuopa Yehova chifukwa chodziŵa zoona ponena za iye ndi njira zake kwathandiza anthu ambiri kumasuka ku mankhwala osokoneza bongo.
“Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Zizoloŵezi zowononga zingathetsedwe mwa kukhala ndi chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu ndi kumudalira kwambiri.