Kukumbukira Mboni za Yehova Zimene Zinaphedwa
Kukumbukira Mboni za Yehova Zimene Zinaphedwa
PA March 7, 2002, chikwangwani cha chikumbutso anachionetsa m’tauni ya Körmend kumadzulo kwa Hungary. Chinali chokumbukira Mboni za Yehova zitatu zomwe zinaphedwa ndi Anazi mu 1945.
Chikwangwanichi anachiika pa khoma lomwe lili pa likulu la dipatimenti yozimitsa moto yomwe ili mu msewu wa Hunyadi, kumene anaphera anthu ameneŵa anthu ena akuona. Chikwangwanichi anachipatulira pokumbukira ‘Akristu amene anaphedwa chifukwa chokana kuchita zinthu zotsutsana ndi chikhulupiriro chawo mu March 1945. Antal Hőnisch (1911-1945), Bertalan Szabó (1921-1945), János Zsondor (1923-1945), 2002, Mboni za Yehova.’
Kuphedwa kumeneku kunachitika kutangotsala miyezi iŵiri kuti nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse ithe. Kodi n’chifukwa chiyani Akristu ameneŵa anaphedwa? Nyuzipepala ya ku Hungary yakuti Vas Népe inafotokoza kuti: “Hitler atayamba kulamulira Germany, Ayuda komanso Mboni za Yehova zinali m’gulu la ozunzidwa, kuikidwa m’ndende zachibalo ndiponso kuphedwa ngati sasiya chikhulupiriro chawo cha chipembedzo. . . . Mu 1945, anthu omwe ankakhala kumadzulo kwa Hungary anaopsezedwa kwambiri. . . . Njira ina yoopsezera inali yochotsa Mboni za Yehova m’dzikolo ndi kukazipha.”
Pulogalamu yoonetsa chikwangwani inagawidwa m’mbali ziŵiri. Mbali yoyamba inachitikira ku bwalo lotchedwa Batthyány Castle. Kumeneku omwe analankhula anali pulofesa Szabolcs Szita, yemwe ndi mkulu wa likulu losungira mabuku onena za anthu amene anapululidwa ku Budapest, László Donáth wa m’komiti ya ku nyumba ya malamulo yoona za ufulu wa anthu komanso nkhani za magulu ang’onoang’ono achipembedzo, ndiponso Kálmán Komjáthy, yemwe anaona ndi maso kuphedwa kwa anthuwo ndipo tsopano ndi katswiri wa mbiri ya tauniyo. Pa mbali yachiŵiri ya pulogalamuyo, anthu oposa 500 anayenda m’tauniyo, mkulu woyang’anira tauniyo József Honfi akuonetsa chikwangwani.
M’kalata yake yotsanzikira, Ján Žondor (János Zsondor) anauza abale ndi alongo ake achikristu kuti asalire. Iye analemba kuti: “Ndikukumbukirabe mawu a Yohane opezeka pa Chivumbulutso 2:10 akuti: ‘Khala wokhulupirika kufikira imfa.’ . . . Auzeni omwe ali ku nyumba kuti asalire chifukwa ndikufera choonadi osati chifukwa chakuti ndachita cholakwa.”
[Chithunzi patsamba 32]
Bertalan Szabó
[Chithunzi patsamba 32]
Antal Hőnisch
[Chithunzi patsamba 32]
Ján Žondor