Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wanu Wonse

Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wanu Wonse

Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wanu Wonse

“Iwo akudziŵa dzina lanu adzakhulupirira Inu.”​—SALMO 9:10.

1, 2. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene anthu amazikhulupirira mwachabe kuti ziwateteza?

MASIKU ano, pamene zinthu zambiri zikuopseza moyo wathu, n’kwachibadwa kufunafuna munthu kapena chinthu chimene chingatiteteze. Ena amaganiza kuti kukhala ndi ndalama zambiri kudzathandiza kuti tsogolo lawo likhale labwino, koma zoona zake n’zakuti ndalama si malo othaŵirako odalirika. Baibulo limati: “Wokhulupirira chuma chake adzagwa.” (Miyambo 11:28) Ena amakhulupirira atsogoleri a anthu, koma ngakhale atsogoleri abwino kwambiri amalakwitsa. Ndipo pakapita nthaŵi, onse amamwalira. Baibulo linanena mwanzeru kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” (Salmo 146:3) Mawu ouziridwa amenewo akutichenjezanso kuti tisakhulupirire mphamvu zathu zokha popanda thandizo. Ifenso ndi ‘ana a anthu’ chabe.

2 Mneneri Yesaya anadzudzula atsogoleri a mtundu wa Israyeli a m’nthaŵi yake chifukwa chakuti anali kukhulupirira ‘pothawirapo pabodza.’ (Yesaya 28:15-17) Pofunafuna chitetezo, anapanga migwirizano ya ndale ndi mitundu imene anayandikana nayo. Kugwirizana koteroko kunali kosadalirika, kunali bodza. Masiku ano, mofanana ndi zimenezi, atsogoleri ambiri azipembedzo amapanga ubale ndi atsogoleri andale. Maubale amenewonso adzaonekera kuti ndi “mabodza.” (Chivumbulutso 17:16, 17) Sadzabweretsa chitetezo chokhalitsa.

Zitsanzo Zabwino za Yoswa ndi Kalebi

3, 4. Kodi zimene Yoswa ndi Kalebi anafotokoza zinasiyana bwanji ndi zimene anafotokoza azondi ena khumi?

3 Nangano kodi chitetezo tingachipeze kuti? Tingachipeze kumene Yoswa ndi Kalebi anachipeza m’nthaŵi ya Mose. Aisrayeli atangomasulidwa kumene ku Igupto, mtunduwo unali wokonzeka kuloŵa mu Kanani, Dziko Lolonjezedwa. Amuna khumi ndi aŵiri anatumidwa kuti akazonde dzikolo, ndipo patatha masiku 40, iwo anabwerera kuti adzafotokoze zimene anaona. Amuna aŵiri okha, Yoswa ndi Kalebi, anafotokoza kuti Aisrayeli zidzawayendera bwino m’Kanani. Enawo anavomereza kuti dzikolo linali labwino kwambiri koma anati: “Anthu okhala m’dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo nja malinga, yaikulu ndithu . . . Sitikhoza kuwakwerera anthuwo; popeza atiposa mphamvu.”​—Numeri 13:27, 28, 31.

4 Aisrayeli anamvera azondi khumiwo ndipo anaopa kwambiri mpaka kufika pong’ung’uza motsutsana ndi Mose. Pomaliza, Yoswa ndi Kalebi analankhula ndi mtima wonse kuti: “Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu. Yehova akakondwera nafe, adzatiloŵetsa m’dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Chokhachi musamapikisana naye Yehova; musamaopa anthu a m’dzikomo.” (Numeri 14:6-9) Komabe, Aisrayeli anakana kumvera ndipo chifukwa cha zimenezi, sanawalole kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa panthaŵi imeneyo.

5. N’chifukwa chiyani Yoswa ndi Kalebi anapereka lipoti labwino?

5 N’chifukwa chiyani Yoswa ndi Kalebi anapereka lipoti labwino pamene azondi khumi aja anapereka lipoti loipa? Azondi onse khumi ndi aŵiriwo anaona mizinda yamphamvu ndi mitundu yokhazikika imodzimodzi. Ndipo khumiwo anali kunena zoona pamene anati Israyeli sanali ndi mphamvu kwambiri moti n’kugonjetsa dzikolo. Yoswa ndi Kalebi anadziŵanso zimenezo. Koma khumiwo anaona zinthu mwaumunthu, pamene Yoswa ndi Kalebi anakhulupirira Yehova. Iwo anali ataona mphamvu zake ku Igupto, pa Nyanja Yofiira, ndiponso m’mbali mwa phiri la Sinai. Ndipotu, patapita zaka zambiri, mbiri yokha ya zimene zinachitikazo inakhudza mtima kwambiri Rahabi wa ku Yeriko moti anafika poika moyo wake pachiswe chifukwa cha anthu a Yehova. (Yoswa 2:1-24; 6:22-25) Yoswa ndi Kalebi, omwe anadzionera okha zimene Yehova anachita, anali ndi chikhulupiriro chonse kuti Mulungu adzapitiriza kumenyera nkhondo anthu ake. Patapita zaka 40, kukhulupirira kwawo kunatsimikiziridwa kuti kunali koyenera pamene mbadwo watsopano wa Aisrayeli, motsogoleredwa ndi Yoswa, unaloŵa mu Kanani ndi kulanda dzikolo.

Chifukwa Chake Tiyenera Kukhulupirira Yehova ndi Mtima Wonse

6. N’chifukwa chiyani Akristu masiku ano amayesedwa, ndipo ayenera kukhulupirira ndani?

6 ‘M’nthaŵi zoŵaŵitsa’ zino, ife, mofanana ndi Aisrayeli, timakumana ndi adani amphamvu kuposa ife. (2 Timoteo 3:1) Timayesedwa pankhani ya makhalidwe, moyo wathu wauzimu, ndipo nthaŵi zina ngakhale mwakuthupi. Mwa ife tokha sitingathe kuthana ndi mayesero oterowo, popeza amene amayambitsa ndi Satana Mdyerekezi yemwe ndi wamphamvu kuposa anthu. (Aefeso 6:12; 1 Yohane 5:19) Nangano tingapeze kuti thandizo? Popemphera kwa Yehova, munthu wina wokhulupirika wakale anati: “Iwo akudziŵa dzina lanu adzakhulupirira Inu.” (Salmo 9:10) Ngati timadziŵadi Yehova ndipo timadziŵa zimene dzina lake limaimira, tidzam’khulupirira kwambiri monga mmene anachitira Yoswa ndi Kalebi.​—Yohane 17:3.

7, 8. (a) Kodi chilengedwe chimatipatsa bwanji zifukwa zokhulupirira Yehova? (b) Kodi Baibulo likupereka zifukwa zotani zokhulupirira Yehova?

7 N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Yehova? Chifukwa chimodzi chimene Yoswa ndi Kalebi anachitira zimenezo n’chakuti anaona umboni wa mphamvu zake. Ifenso timaona umboni wa mphamvu zake. Mwachitsanzo, taganizirani ntchito za Yehova za m’chilengedwe, monga thambo limene lili ndi magulu akuluakulu a nyenyezi miyandamiyanda. Mphamvu zazikulu za m’chilengedwe zimene Yehova amazilamulira zimasonyeza kuti iye alidi Wamphamvuyonse. Pamene tisinkhasinkha zodabwitsa za m’chilengedwe, tiyenera kugwirizana ndi Yobu amene ananena za Yehova kuti: “Adzam’bwezetsa ndani? Adzanena naye ndani, Mulikuchita chiyani?” (Yobu 9:12) Inde, ngati Yehova ali ku mbali yathu sitifunika kuopa aliyense m’chilengedwe chonse.​—Aroma 8:31.

8 Taganiziraninso Mawu a Yehova, Baibulo. Gwero losatha la nzeru za Mulungu limeneli n’lamphamvu potithandiza kugonjetsa makhalidwe oipa ndi kugwirizanitsa miyoyo yathu ndi zimene Yehova amafuna. (Ahebri 4:12) Kudzera m’Baibulo timadziŵa dzina la Yehova ndi kudziŵa tanthauzo la dzina lakelo. (Eksodo 3:14) Timadziŵa kuti Yehova akhoza kukhala chimene iye akufuna, kaya Tate, Woweruza wolungama, kapena Womenya nkhondo wopambana, kuti akwaniritse zolinga zake. Ndipo timaona mmene zimene iye wanena zimachitikira nthaŵi zonse monga momwe wanenera. Pamene tikuphunzira Mawu a Mulungu, timalimbikitsika kunena monga mmene ananenera wamasalmo kuti: “Ndikhulupirira mawu anu.”​—Salmo 119:42; Yesaya 40:8.

9. Kodi dipo ndi kuuka kwa Yesu zimalimbitsa bwanji kukhulupirira kwathu Yehova?

9 Dipo ndi chifukwa china chokhulupirira Yehova. (Mateyu 20:28) N’zosangalatsatu kwambiri kuti Mulungu anatumiza Mwana wake kudzafa monga dipo lathu! Ndipo dipolo ndi lamphamvudi kwambiri. Limakwirira machimo a anthu onse amene alapa ndi kupita kwa Yehova ndi mtima woona. (Yohane 3:16; Ahebri 6:10; 1 Yohane 4:16, 19) Kuti dipolo liperekedwe panafunika kuti Yesu auke kwa akufa. Chozizwitsa chimenecho chimene anthu ambirimbiri anachitira umboni podzionera okha, ndi chifukwa china chokhulupirira Yehova. Ndi umboni wakuti zimene tikuyembekezera m’tsogolo zidzakwaniritsidwa.​—Machitidwe 17:31; Aroma 5:5; 1 Akorinto 15:3-8.

10. Kodi munthu aliyense payenkha ali ndi zifukwa ziti zokhulupirira Yehova?

10 Zimenezi ndi zina chabe mwa zifukwa zimene tingakhulupirire ndipo tiyenera kukhulupirira ndi mtima wonse Yehova. Pali zambiri ndipo zina mwa izo n’zokhudza munthu payekha. Mwachitsanzo, nthaŵi zina timakumana ndi mavuto m’moyo wathu. Pamene tifunafuna thandizo la Yehova posamalira mavutowo, timaona mmene thandizolo limagwirira bwino ntchito. (Yakobo 1:5-8) Tikamadalira kwambiri Yehova m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku ndi kuona zinthu zabwino zimene zimachitika chifukwa cha zimenezi, tidzamukhulupirira kwambiri.

Davide Anakhulupirira Yehova

11. Kodi Davide anakhulupirira Yehova ngakhale kuti panali mavuto otani?

11 Davide wa ku Israyeli wakale ndi m’modzi mwa anthu amene anakhulupirira Yehova. Davide anaopsezedwa ndi Mfumu Sauli, imene inkafuna kumupha, ndiponso gulu lankhondo lamphamvu la Afilisti, limene linkafuna kulanda Israyeli. Komabe, iye anapulumuka ndiponso anapambana. Chifukwa chiyani? Mwiniwakeyo Davide anafotokoza kuti: “Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?” (Salmo 27:1) Ifenso tidzapambana ngati mofanana ndi iye tikhulupirira Yehova.

12, 13. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti tiyenera kukhulupirira Yehova ngakhale pamene adani agwiritsa ntchito lilime lawo ngati zida zolimbana nafe?

12 Nthaŵi ina Davide anapemphera kuti: “Imvani Yehova, mawu anga, m’kudandaula kwanga; sungani moyo wanga angandiopse mdani. Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa; pa phokoso la ochita zopanda pake: amene anola lilime lawo ngati lupanga, napiringidza mivi yawo, ndiyo mawu akuwaŵitsa; kuponyera wangwiro mobisika.” (Salmo 64:1-4) Sitikudziŵa kwenikweni chimene chinachititsa Davide kulemba mawu ameneŵa. Koma tikudziŵa kuti masiku ano, adani mofananamo ‘amanola lilime lawo,’ kugwiritsa ntchito mawu ngati chida chankhondo. ‘Amaponyera’ Akristu osalakwa mawu amene alankhula kapena kulemba monga “mivi” yotiipitsira mbiri. Kodi chidzachitika n’chiyani ngati tikhulupirira Yehova mosagwedera?

13 Davide anapitiriza kuti: “Mulungu adzawaponyera muvi; adzalaswa modzidzimutsa. Adzawakhumudwitsa, lilime lawo lidzawatsutsa . . . Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye.” (Salmo 64:7-10) Inde, ngakhale kuti adani amanola lilime lawo kulimbana nafe, pamapeto pake ‘lilime lawolo limawatsutsa.’ N’kupita kwa nthaŵi, Yehova amasintha zinthu kuti ziyende bwino, kuti amene amamukhulupirira akondwere mwa iye.

Kukhulupirira kwa Hezekiya Kunali Koyenera

14. (a) Kodi Hezekiya anakhulupirira Yehova ngakhale kuti panali zinthu zoopsa ziti? (b) Kodi Hezekiya anasonyeza bwanji kuti sanakhulupirire mabodza a Asuri?

14 Mfumu Hezekiya anali munthu wina amene kukhulupirira kwake Yehova kunatsimikiziridwa kuti kunali koyenera. Panthaŵi imene Hezekiya anali kulamulira, gulu la asilikali lamphamvu la Asuri linaopseza Yerusalemu. Asilikaliwo anali atagonjetsa mitundu ina yambiri. Anali atagonjetsanso ngakhale mizinda ya Yuda mpaka anangotsala Yerusalemu yekha, ndipo Sanakeribu anadzitama kuti adzagonjetsanso mzindawo. Iye anafotokoza kudzera mwa kazembe kuti kukhulupirira Aigupto kuti awathandize kunali kopanda nzeru, zomwe zinali zoona ndithu. Koma iye kenako anati: “Asakunyenge Mulungu wako, amene iwe um’khulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sadzaperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.” (Yesaya 37:10) Koma Hezekiya anadziŵa kuti Yehova sanganame. Choncho, iye anapemphera kuti: “Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m’manja [mwa Asuri], kuti maufumu onse a dziko adziŵe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.” (Yesaya 37:20) Yehova anamvera pemphero la Hezekiya. Usiku umodzi wokha mngelo anapha asilikali a Asuri okwana 185,000. Yerusalemu anapulumuka, ndipo Sanakeribu anachoka m’dziko la Yuda. Onse amene anamva zimene zinachitikazi anadziŵa kuti Yehova ndi wamkulu.

15. Kodi n’chiyani chokha chimene chingatikonzekeretse kuthana ndi mavuto ena alionse amene tingakumane nawo m’dziko losakhazikika lino?

15 Masiku ano, mofanana ndi Hezekiya, ifenso tili pankhondo. Nkhondo ya ife ndi yauzimu. Komabe, monga omenya nkhondo yauzimu, tiyenera kukhala ndi luso limene lingatithandize kukhalabe ndi moyo mwauzimu. Tiyenera kuoneratu oukira ndi kudzikonzekeretsa kuti tiziteteze. (Aefeso 6:11, 12, 17) M’dziko losakhazikika lino, zinthu zingasinthe mwadzidzidzi. Nkhondo yapachiweniweni ingabuke mosayembekezeka. Mayiko amene akhala akulolera zipembedzo zosiyanasiyana kwa nthaŵi yaitali angayambe kusalolera. Tidzakhala okonzekera chilichonse chimene chingachitike kokha ngati tidzikonzekeretsa mwa kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse monga anachitira Hezekiya.

Kodi Kukhulupirira Yehova Kumatanthauza Chiyani?

16, 17. Kodi timasonyeza bwanji kuti timakhulupirira Yehova?

16 Kukhulupirira Yehova si kungovomereza chabe kuti munthu umatero. Kumakhudza mtima wathu ndipo timasonyeza zimenezo mwa zochita zathu. Ngati tikhulupirira Yehova, tidzakhulupirira kwambiri Mawu ake, Baibulo. Tidzaliŵerenga tsiku ndi tsiku, kusinkhasinkha zimene tikuŵerengazo, ndi kulilola kuti litsogolere moyo wathu. (Salmo 119:105) Kukhulupirira Yehova kumafunanso kukhulupirira mphamvu ya mzimu woyera. Mothandizidwa ndi mzimu woyera, tingakhale ndi chipatso chimene chimasangalatsa Yehova ndipo tingagonjetse makhalidwe oipa amene anakhazikika mwa ife. (1 Akorinto 6:11; Agalatiya 5:22-24) Motero, mothandizidwa ndi mzimu woyera, ambiri asiya kusuta fodya kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ena asiya khalidwe la chiwerewere. Inde, ngati tikhulupirira Yehova, timachita zinthu m’mphamvu yake, osati yathu.​—Aefeso 3:14-18.

17 Kuwonjezera pamenepo, kukhulupirira Yehova kumatanthauza kukhulupirira anthu amene iye amawakhulupirira. Mwachitsanzo, Yehova wakonza zoti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” azisamalira zinthu za Ufumu za padziko lapansi. (Mateyu 24:45-47) Sitifunika kuchita zinthu patokha, ndipo sitifunika kunyalanyaza kuikidwa kwake, popeza timakhulupirira makonzedwe a Yehova. Kuwonjezera pamenepo, akulu amatumikira mumpingo wachikristu ndipo, malinga ndi mtumwi Paulo, iwo amaikidwa ndi mzimu woyera. (Machitidwe 20:28) Mwa kugwirizana ndi akulu mumpingo, timasonyezanso kuti timakhulupirira Yehova.​—Ahebri 13:17.

Tsatirani Chitsanzo cha Paulo

18. Kodi Akristu masiku ano amatsatira bwanji chitsanzo cha Paulo, koma kodi sakhulupirira chiyani?

18 Mtumwi Paulo anakumana ndi mayesero ambiri muutumiki wake, monga mmene ife timachitira. Mbiri yachikristu m’nthaŵi yake inaipitsidwa kwa olamulira, ndipo iye nthaŵi zina anayesetsa kukonza maganizo olakwikawo kapena kukhazikitsa mwalamulo ntchito yolalikira. (Machitidwe 28:19-22; Afilipi 1:7) Akristu masiku ano amatsatira chitsanzo chake. Mpata ukapezeka, timathandiza ena kudziŵa za ntchito yathu pogwiritsa ntchito njira iliyonse imene ingapezeke. Ndipo timayesetsa kuteteza ndi kukhazikitsa mwalamulo uthenga wabwino. Komabe, sitikhulupirira ndi mtima wonse zinthu zimenezi, chifukwa sitiona kuti kuyenda bwino kapena kukanika kwa zinthu kumadalira kuwina kwathu milandu ku khoti kapena kufalitsidwa kwa nkhani zotikomera. M’malo mwake, timakhulupirira Yehova. Timakumbukira zimene iye anawalimbikitsa Aisrayeli akale kuti: “M’kukhala chete ndi m’kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu.”​—Yesaya 30:15.

19. Atakumana ndi chizunzo, kodi kukhulupirira Yehova kwa abale athu kwatsimikiziridwa bwanji kuti kunali koyenera?

19 Nthaŵi zina m’mbiri yathu yamakono, ntchito yathu yaletsedwa kapena kuponderezedwa kum’mawa ndi kumadzulo kwa Ulaya, m’mayiko ena a ku Asia ndi ku Africa kuno, ndiponso m’mayiko a ku South America ndi ku North America. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kukhulupirira kwathu Yehova kunali kopanda pake? Ayi. Ngakhale kuti Yehova nthaŵi zina walola chizunzo chankhanza kwambiri pa zifukwa zimene anaona kuti n’zoyenera, iye walimbitsa mwachikondi anthu amene avutika ndi chizunzocho. M’kati mwa chizunzocho, Akristu ambiri akhala ndi mbiri yabwino kwambiri ya kukhulupirira ndi kudalira Mulungu.

20. Ngakhale kuti tingapindule ndi ufulu woperekedwa mwalamulo, kodi sitidzagonjera m’mbali ziti?

20 Komabe, m’mayiko ambiri ndife ovomerezeka mwalamulo, ndipo nthaŵi zina manyuzipepala, mawailesi ndi ma TV amafalitsa nkhani zabwino zokhudza ife. Timayamikira zimenezi ndipo timazindikira kuti zimenezinso zimakwaniritsa zolinga za Yehova. Ndi madalitso ake, timagwiritsa ntchito ufulu wowonjezerekawo kutumikira Yehova pamaso pa anthu onse ndiponso mokwanira, osati kuugwiritsa ntchito kutukula miyoyo yathu. Komabe sitidzagonjera pa mfundo ya kusaloŵerera kwathu m’zinthu zadziko, kubwerera m’mbuyo m’ntchito yathu yolalikira, kapena kufooka mwa njira ina iliyonse pa kutumikira kwathu Yehova n’cholinga choti anthu aulamuliro azitilemekeza. Ife timalamulidwa ndi Ufumu Waumesiya ndipo tili nganganga kumbali ya Ufumu wa Yehova. Chiyembekezo chathu sichili m’dongosolo la zinthu lino, m’malo mwake tikuyembekezera dziko latsopano limene Ufumu Waumesiya wakumwamba udzakhala boma lokhalo limene lidzalamulira padziko lapansili. Mabomba, ngakhalenso zida za nyukiliya sizidzagwedeza boma limenelo kapena kuligwetsera pansi kuchokera kumwamba. Ilo n’losagonjetseka ndipo lidzakwaniritsa zolinga za Yehova.​—Danieli 2:44; Ahebri 12:28; Chivumbulutso 6:2.

21. Kodi ndife otsimikiza mtima kuchita chiyani?

21 Paulo anati: “Ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Ndiyetu tiyeni tonsefe titumikire Yehova mokhulupirika mpaka mapeto. Tili ndi zifukwa zonse zokhulupirira Yehova ndi mtima wonse tsopano lino ndiponso mpaka kalekale.​—Salmo 37:3; 125:1.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• N’chifukwa chiyani Yoswa ndi Kalebi anabweretsa lipoti labwino?

• Kodi zifukwa zina zimene tiyenera kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse n’ziti?

• Kodi kukhulupirira Yehova kumatanthauza chiyani?

• Kodi tatsimikiza mtima kuchita chiyani pa kukhulupirira Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

N’chifukwa chiyani Yoswa ndi Kalebi anapereka lipoti labwino?

[Zithunzi patsamba 16]

Chilengedwe chimatipatsa chifukwa champhamvu chokhulupirira Yehova

[Mawu a Chithunzi]

Zithunzi zonse zitatu: Mwa chilolezo cha Anglo-Australian Observatory, zojambulidwa ndi David Malin

[Chithunzi patsamba 18]

Kukhulupirira Yehova kumatanthauza kukhulupirira anthu amene iye amawakhulupirira