Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Onani Ena Monga Momwe Yehova Amawaonera

Onani Ena Monga Momwe Yehova Amawaonera

Onani Ena Monga Momwe Yehova Amawaonera

Yehova saona monga aona munthu.”​—1 SAMUELI 16:7.

1, 2. Kodi mmene Yehova anaonera Eliabu zinasiyana bwanji ndi mmene Samueli anamuonera, ndipo tikuphunzirapo chiyani pamenepa?

M’ZAKA za m’ma 1000 B.C.E., Yehova anatuma mneneri Samueli kuti akagwire ntchito yachinsinsi. Anauza mneneriyo kupita kunyumba ya munthu wina, dzina lake Jese kukadzoza mmodzi mwa ana ake aamuna kuti adzakhale mfumu ya Israyeli. Samueli ataona mwana woyamba wa Jese, dzina lake Eliabu, anakhulupirira kuti anapeza munthu amene Mulungu anasankha. Koma Yehova anati: “Usayang’ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza ine ndinam’kana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:6, 7) Samueli analephera kuona Eliabu monga momwe Yehova anali kumuonera. *

2 N’zosavuta kwambiri kuti anthu opanda ungwiro aone anzawo molakwika. Komanso, tinganyengeke ndi anthu a maonekedwe abwino koma ali oipa m’kati. Ndiponso, tingakhale okhwimitsa zinthu ndiponso osasintha maganizo a mmene timaonera anthu oona mtima amene chibadwa chawo sichitisangalatsa.

3, 4. (a) Akristu aŵiri akakangana, kodi onsewo ayenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani? (b) Kodi ndi mafunso ati amene tiyenera kudzifunsa tikakangana kwambiri ndi wokhulupirira mnzathu?

3 Pangabuke mavuto ngati timafulumira kuweruza ena​—ngakhale amene takhala tikuwadziŵa kwa zaka zambiri. Mwina munakangana kwambiri ndi Mkristu amene nthaŵi ina anali mnzanu wapamtima. Kodi mukufuna kukhala nayenso paubwenzi? N’chiyani chingakuthandizeni kuti zimenezi zitheke?

4 Bwanji osamuona mbale kapena mlongo wanu wachikristuyo mosamalitsa, mwachifatse ndiponso moyenera? Ndipo chitani izi mukulingalira mawu a Yesu akuti: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye.” (Yohane 6:44) Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi Yehova anam’kokeranji munthu uyu kwa Mwana Wake? Kodi ali ndi makhalidwe abwino ati? Kodi makhalidwe amenewo ndimawanyalanyaza kapena kuwaona monga osafunika? N’chiyani chinatipangitsa kukhala mabwenzi poyambapo? N’chifukwa chiyani ndinkafuna kuti akhale mnzanga?’ Poyamba, zingakuvuteni kuganizira za makhalidwe ake abwino, makamaka ngati mwakhala mukusunga chakukhosi kwanthaŵi yaitali. Komabe, kuchita zimenezi n’kofunika kuti aŵirinu mukonze ubwenzi wanu. Kuti tisonyeze mmene tingachitire zimenezi, tiyeni tione makhalidwe abwino a anthu aŵiri amene nthaŵi zina timangoona zolakwa zawo. Anthuwo ndiwo mneneri Yona ndi mtumwi Petro.

Kumuona Moyenera Yona

5. Kodi Yona anapatsidwa ntchito yanji, ndipo anachita chiyani?

5 Yona anatumikira monga mneneri mu ufumu wakumpoto wa Israyeli m’masiku a Mfumu Yerobiamu wachiŵiri, mwana wa Yoasi. (2 Mafumu 14:23-25) Tsiku lina, Yehova anamuuza Yona kuchoka ku Israyeli kupita ku Nineve, likulu la ufumu wamphamvu wa Asuri. Anamuuza kuti akatani? Kuti akachenjeze anthu kumeneko zoti mudzi wawo waukuluwo unali pafupi kuwonongedwa. (Yona 1:1, 2) M’malo mochita zimene Mulungu ananena, Yona anathawa. Anakwera chombo chopita ku Tarisi, kutali kwambiri ndi ku Nineve.​—Yona 1:3.

6. N’chifukwa chiyani Yehova anasankha kutuma Yona ku Nineve?

6 N’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukaganiza za Yona? Kodi mumaganiza kuti anali mneneri wosamvera? Mungakhaledi ndi maganizo ameneŵa ngati mupenda moyo wake mothamanga. Koma kodi Mulungu anamusankha Yona kukhala mneneri chifukwa chakuti anali wosamvera? Ndithudi ayi. Yona ayenera kuti anali ndi makhalidwe ena abwino. Onani mbiri yake ali mneneri.

7. Pamene Yona anali kutumikira Yehova ku Israyeli, kodi zinthu zinali bwanji kumeneko ndipo kudziŵa zimenezi kungakhudze bwanji mmene mumamuonera?

7 Yona anagwira ntchito mokhulupirika ku Israyeli, m’gawo la anthu osalabadira n’komwe. Mneneri Amosi, amene anakhala ndi moyo pafupifupi nthaŵi imodzi ndi Yona, anati Aisrayeli m’nthaŵi imeneyo anali okonda chuma ndi zosangalatsa. * Zinthu zoipa zinali kuchitika m’dzikolo, koma Aisrayeli anali kuzilekerera. (Amosi 3:13-15; 4:4; 6:4-6) Komabe, tsiku lililonse Yona anachita mokhulupirika ntchito yake yolalikira. Ngati ndinu wolengeza uthenga wabwino, mukudziŵa momwe zimavutira kulankhula ndi anthu amene siziwakhudza ndiponso amphwayi. Choncho, tikamaona zolakwa za Yona, tizikumbukiranso makhalidwe ake abwino kuti anali wokhulupirika ndi wopirira pamene anali kulalikira kwa Aisrayeli osakhulupirira.

8. Kodi ndi mavuto otani amene mneneri wachiisrayeli anali kukakumana nawo ku Nineve?

8 Kupita kukalalikira ku Nineve inali ntchito yovuta kwambiri kuposa pamenepo. Kuti akafike ku mudzi umenewu, Yona anafunika kuyenda ulendo wa pansi wa makilomita pafupifupi 800 womwe ndi ulendo wovuta kwambiri umene ukanam’tengera pafupifupi mwezi umodzi. Kumeneko, mneneriyu anafunika kulalikira kwa Asuri, amene anali odziŵika kuti anali ankhanza. Nthaŵi zonse nkhondo zawo zinali zankhanza moipa. Ndipo anafika podzitama ndi nkhanza zawozo. Sizodabwitsa kuti Nineve unkatchedwa kuti “mudzi wa mwazi!”​—Nahumu 3:1, 7.

9. Kodi Yona anasonyeza makhalidwe ati pamene namondwe wamkulu anaika pachiswe miyoyo ya oyendetsa chombo?

9 Posafuna kumvera lamulo la Yehova, Yona anakwera chombo chimene chinali kumupititsa kutali kwambiri ndi kumene anafunika kupita. Komabe, Yehova sanamusiye mneneri wake, kapena kupeza wina kuti aloŵe m’malo mwake. M’malo mwake, Yehova anamuthandiza Yona kuti azindikire kufunika kwa ntchito yake. Mulungu anautsa namondwe wamkulu panyanja. Chombo chimene Yona anakwera chinali kutengekatengeka ndi mafunde. Anthu osalakwa akanafa, chifukwa cha Yona. (Yona 1:4) Kodi Yona akanachita chiyani? Posafuna kuti oyendetsa chombowo afe chifukwa cha iye, Yona anawauza kuti: “Mundinyamule ndi kundiponya m’nyanja, momwemo nyanja idzachitira inu bata.” (Yona 1:10-12) Sanali kuyembekezera kuti Yehova amupulumutsa m’nyanjamo, oyendetsa chombowo akamuponyeramodi. (Yona 1:15) Komabe, Yona analolera kufa kuti oyendetsa chombowo apulumuke. Kodi apa sitikuona kuti anali wolimba mtima, wodzichepetsa, ndi wachikondi?

10. N’chiyani chinachitika Yehova atamutumanso Yona?

10 Mapeto ake, Yehova anapulumutsa Yona. Kodi zimene Yona anali atangochita kumenezi, zinapangitsa kuti asayenerere kutumikira monga woimira Mulungu mpaka kalekale? Ayi. Yehova, pomuchitira chifundo ndi kumukonda mneneriyu anamuuzanso kukalalikira Anineve. Yona atafika ku Nineve, anauza anthu kumeneko molimba mtima kuti Mulungu waona kuipitsitsa kwawo ndipo mudzi wawowo uwonongedwa pakatha masiku 40. (Yona 1:2; 3:4) Anineve analapa atamva uthenga wosapita m’mbali wa Yona, ndipo mudzi wawowo sunawonongedwe.

11. N’chiyani chimasonyeza kuti Yona anaphunzira phunziro lofunika?

11 Komabe Yona anali nawobe maganizo olakwika. Koma, mwachitsanzo chogwira mtima, Yehova moleza mtima anathandiza Yona kuona kuti Iye amaona kuposa maonekedwe okha. Amapenda mtima. (Yona 4:5-11) Zoti Yona anaphunzira phunziro lofunika zikuonekera mwa nkhani yosabisa mawu imene iye mwini analemba. Kufunitsitsa kwake kulemba zolakwa zake ndi nkhani zochititsa manyazi zomwe, zimapereka umboni wina wakuti anali wodzichepetsa. Pamafunika kulimba mtima kuti munthu uvomereze cholakwa.

12. (a) Kodi tikudziŵa bwanji kuti Yesu amaona anthu monga momwe Yehova amawaonera? (b) Kodi tikulimbikitsidwa kuwaona bwanji anthu amene timawalalikira uthenga wabwino? (Onani bokosi patsamba 18.)

12 Patapita zaka zambiri, Yesu Kristu ananena mawu abwino okhudza zimene zinachitika pamoyo wa Yona. Anati: “Monga Yona anali m’mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.” (Mateyu 12:40) Yona akadzaukitsidwa, adzamva kuti Yesu anayerekezera nthaŵi imene Iye anakhala m’manda ndi nthaŵi imene mneneriyu anali m’mimba mwa chinsomba. Kodi sitikusangalala kutumikira Mulungu amene sataya atumiki ake akalakwa? Wamasalmo analemba kuti: “Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:13, 14) Inde, “fumbi” limeneli​—kuphatikizapo anthu opanda ungwiro masiku ano​—lingachite zambiri mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu.

Zimene Tikuphunzirapo Masiku Ano

13. Ndi makhalidwe a Petro ati amene angabwere m’maganizo, koma n’chifukwa chiyani Yesu anamusankha kukhala mtumwi?

13 Tsopano tiyeni tione mwachidule chitsanzo chachiŵiri, cha mtumwi Petro. Kodi atakufunsani kufotokoza za Petro, kodi mudzafulumira kunena makhalidwe ake monga kujijirika, kupupuluma ngakhalenso kudzikuza? Nthaŵi zina Petro anasonyezadi makhalidwe ameneŵa. Komabe, kodi Yesu akanasankha Petro kukhala mmodzi wa atumwi ake 12 ngati iye analidi munthu wojijirika, wopupuluma, kapena wodzikuza? (Luka 6:12-14) Ndithudi ayi. Mwachionekere Yesu sanaganizire zolakwa zimenezi ndipo anaona makhalidwe abwino a Petro.

14. (a) N’chiyani chingakhale chifukwa chake Petro akuoneka kuti anali wolankhulalankhula? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira kuti Petro anali wokonda kufunsa mafunso?

14 Nthaŵi zina Petro anali kulankhula m’malo mwa atumwi enawo. Ena angaone zimenezi monga umboni wakuti anali wodzikuza. Koma kodi ndi mmenedi zinalili? Ena amati Petro anali wamkulu kuposa atumwi ena onse mwina wamkulunso kuposa Yesu amene. Ngati zimenezi n’zoona, zingathandize kudziŵa chifukwa chake Petro nthaŵi zambiri anali woyamba kulankhula. (Mateyu 16:22) Komabe, pali mfundo ina yofunika kuilingalira. Petro anali munthu wokonda zauzimu. Chifukwa choti anali wofunitsitsa kudziŵa zinthu ankakonda kufunsa mafunso. Ifenso timapindula nawo mafunso akewo. Yesu ananena mawu ofunika kwambiri poyankha mafunso a Petro, ndipo zimenezi zasungidwa m’Baibulo. Mwachitsanzo, Yesu anali kuyankha funso la Petro pomwe ananena za “mdindo wokhulupirika.” (Luka 12:41-44) Ndipo talingalirani funso la Petro ili: “Ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?” Izi zinapangitsa Yesu kunena lonjezo lolimbikitsa ili: “Onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amayi, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzaloŵa moyo wosatha.”​—Mateyu 15:15; 18:21, 22; 19:27-29.

15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Petro analidi wokhulupirika?

15 Petro analinso ndi khalidwe lina labwino​—anali wokhulupirika. Ophunzira ambiri atasiya kutsatira Yesu chifukwa chakuti sanamvetse chiphunzitso chake china, Petro ndi amene analankhula m’malo mwa atumwi 12, kuti: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.” (Yohane 6:66-68) Mawu ameneŵa ayenera kuti anasangalatsa kwambiri mtima wa Yesu! Patapita nthaŵi, gulu la anthu litabwera kudzagwira Mbuyeyo, atumwi ake ambiri anathawa. Komabe, Petro anatsatira gululo pang’onopang’ono mpaka kukaloŵa mu bwalo la mkulu wa ansembe mwenimwenimo. Ndi kulimba mtima kokhakokha kumene kunamupangitsa kupita kumeneko, osati mantha. Yesu akufunsidwa, Petro anakhala pa gulu la Ayuda amene anali kuwotha moto. M’modzi mwa akapolo a mkulu wa ansembe anamuzindikira ndipo anati iyenso anali ndi Yesu. Inde, Petro anakana Ambuye wake, koma tisaiŵale kuti Petro anadziika pangozi imeneyi chifukwa chakuti anali wokhulupirika ndiponso anali kudera nkhaŵa za Yesu. Atumwi enawo sanayerekeze n’komwe kudziika pangozi imeneyi.​—Yohane 18:15-27.

16. N’chifukwa chiti kwenikweni chimene tapendera makhalidwe abwino a Yona ndi Petro?

16 Makhalidwe abwino a Petro anaposa kwambiri zolakwa zake. Chimodzimodzinso Yona. Monga momwe tawaonera moyenera Yona ndi Petro kuposa momwe tinkachitira, tiyeneranso kuphunzira kuwaona moyenera abale ndi alongo athu auzimu amasiku ano. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kukhala nawo bwino. N’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika kwambiri?

Zimene Tikuphunzirapo Masiku Ano

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani Akristu angasemphane maganizo? (b) Ndi uphungu wa m’Baibulo uti umene ungatithandize kuthetsa mikangano ndi okhulupirira anzathu?

17 Masiku ano amuna, akazi, ndi ana opeza mosiyana komanso ophunzira mosiyanasiyana ndi a mitundu yosiyanasiyana akutumikira Yehova mogwirizana. (Chivumbulutso 7:9, 10) Mu mpingo wachikristu tili ndi anthu osiyana mitima kwambiri. Popeza nthaŵi zambiri timatumikira Mulungu tili limodzi, nthaŵi zina pamakhala kusemphana maganizo.​—Aroma 12:10; Afilipi 2:3.

18 Ngakhale kuti timaona zolakwa za abale athu, tisamaike mtima pa zimenezo. Tiziyesetsa kutsatira Yehova, amene wamasalmo anaimba za iye kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) M’malo moika mtima pa makhalidwe amene amatisiyanitsa, ‘tizilondola zinthu za mtendere, ndi zinthu zolimbikitsana wina ndi mnzake.’ (Aroma 14:19) Tiziyesetsa kuona anthu monga momwe Yehova amawaonera, kusaganizira zolakwa zawo ndi kuika mtima pa makhalidwe awo abwino. Tikachita zimenezi, zidzatithandiza “kulolerana wina ndi mnzake.”​—Akolose 3:13.

19. Tchulani zinthu zothandiza zimene Mkristu angachite pothetsa mikangano ikuluikulu.

19 Bwanji ngati pali mikangano imene sitingaithetse mu mtima mwathu? (Salmo 4:4) Kodi uli pakati pa inu ndi wokhulupirira mnzanu? Bwanji osayesa kuthetsa nkhaniyo? (Genesis 32:13-15) Choyamba, lankhulani ndi Yehova m’pemphero, m’pempheni kuti akutsogolereni. Ndiyeno, mukuganizira makhalidwe abwino a munthuyo, mulankhuleni “mu nzeru yofatsa.” (Yakobo 3:13) Muuzeni kuti mukufuna kukhazikitsa mtendere. Kumbukirani uphungu wouziridwa wakuti: ‘Khalani wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.’ (Yakobo 1:19) Langizo lokhala “wodekha pakupsa mtima” limatanthauzanso kuti munthu winayo akhoza kuchita kapena kunena chinthu chokupsetsani mtima. Zimenezi zikachitika, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukhalabe wodziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) M’siyeni mbale wanuyo anene zakukhosi kwake ndipo mvetserani mosamalitsa. Musamudule mawu, ngakhale mutapanda kugwirizana ndi zina zimene akunena. Maganizo ake angakhale olakwika, komabe amenewo ndi maganizo ake basi. Yesani kuona nkhaniyo mmene iye akuionera. Zimenezi zingaphatikizepo kuti inuyo mudzione monga momwe mbale wanuyo akukuonerani.​—Miyambo 18:17.

20. Pothetsa mikangano, kodi ndi zinthu zina ziti zimene zingathandize kuti muyanjanenso

20 Ikafika nthaŵi yanu yoti mulankhule, lankhulani mwachisomo. (Akolose 4:6) Muuzeni mbale wanuyo makhalidwe amene mumakonda mwa iye. Pepesani chifukwa cha chilichonse chimene munachita kuti pakhale mkanganowo. Ngati zinthu zosonyeza kudzichepetsa zimene mwachita zathandiza kuti muyanjanenso, thokozani Yehova. Ngati sizinatero, pitirizani kupempha Yehova kuti akutsogolereni pamene mukuyesa njira zina zoti mukhazikitsire mtendere.​—Aroma 12:18.

21. Kodi nkhani ino yakuthandizani bwanji kuona anthu ena monga momwe Yehova amawaonera?

21 Yehova amakonda atumiki ake onse. Amasangalala kutigwiritsa ntchito tonse mu utumiki wake ngakhale tili opanda ungwiro. Pamene tikuphunzira zambiri za mmene iye amaonera ena, tidzawakonda kwambiri abale ndi alongo athu. Ngati kukonda mbale wathu wachikristu kunazilala, tingakusonkhezerenso. Si mmene tidzapindulire ngati tiyesetsa kuona anthu ena moyenera​—inde, kuwaona monga momwe Yehova amawaonera.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Patapita nthaŵi zinaonekeratu kuti Eliabu yemwe anali wokongolayo, analibe makhalidwe a mfumu yoyenera ya Israyeli. Pamene chimphona chachifilisiti, Goliati, chinaderera Aisrayeli kunkhondo, Eliabu ndi amuna ena achiisrayeli anachita mantha.​—1 Samueli 17:11, 28-30.

^ ndime 7 Chifukwa chopambana nkhondo zikuluzikulu ndi kutenganso dera limene linali m’manja mwa adani ndiponso zopereka zimene ankatolera chifukwa cha kupambanako, Yerobiamu wachiŵiri ayenera kuti anathandiza kwambiri ufumu wa kumpoto kukhala wachuma.​—2 Samueli 8:6; 2 Mafumu 14:23-28; 2 Mbiri 8:3, 4; Amosi 6:2.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Yehova amaona bwanji zolakwa za atumiki ake okhulupirika?

• Kodi ena mwa makhalidwe abwino a Yona ndi Petro anali ati?

• Kodi mwatsimikiza mtima kuwaona bwanji abale anu achikristu?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 18]

Lingalirani Momwe Mulungu Amaonera Anthu Ena

Pamene mukusinkhasinkha za nkhani ya m’Baibulo ya Yona, kodi mukuona kuti ndi kofunika kuwaona moyenera anthu amene nthaŵi zonse mumawalalikira uthenga wabwino? Angaoneke kuti siziwakhudza kapena ndi amphwayi, monga analili Aisrayeli, kapena angakane uthenga wa Mulungu. Komabe, kodi Yehova Mulungu amawaona bwanji? Ngakhale anthu ena amene ndi otchuka m’dzikoli tsiku lina angayambe kufuna Yehova, monga mfumu ya ku Nineve inalapa chifukwa cha kulalikira kwa Yona.​—Yona 3:6, 7.

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi mumaona anthu ena monga momwe Yehova amawaonera?

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Yesu anapeza chinthu china chabwino choti anene pankhani ya Yona