Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amatumikira Abale Awo Achikristu M’mayiko Ena

Amatumikira Abale Awo Achikristu M’mayiko Ena

Amatumikira Abale Awo Achikristu M’mayiko Ena

KODI munamvapo mawu akuti “atumiki a m’mayiko ena” ndi mawu akuti “antchito odzipereka a m’mayiko ena”? Mboni za Yehova zimene zimapanga magulu aŵiri ameneŵa zimathera nthaŵi yawo ndi luso lawo kuthandiza kumanga nyumba zimene zimagwiritsidwa ntchito posindikiza ndi kugawa uthenga wa Ufumu wa m’Baibulo. Abale ameneŵa amathandizanso kumanga Nyumba za Misonkhano ndi Nyumba za Ufumu, zimene zimakhala malo ophunzirirako Baibulo. Pakalipano, abale ameneŵa akuthandiza kumanga nyumba m’mayiko 34, makamaka m’madera amene alibe ndalama ndi zipangizo zokwanira. Kodi ndi mavuto apadera ati amene abale ameneŵa amakumana nawo pamene akutumikira abale awo achikristu m’mayiko ena, nanga ndi madalitso otani amene amapeza? Kodi amamva bwanji ndi ‘utumiki’ umene amachita? (Chivumbulutso 7:9, 15) Kuti tidziŵe, tiyeni timve kwa antchito ena odzipereka amene anatumikira ku Mexico.

Ogwira ntchito yodzipereka ochokera m’mayiko ena anafika koyamba ku Mexico mu May, 1992. Posakhalitsa, anatsogolera ntchito yowonjezera nthambiyo, yomwe imayang’anira ntchito ya Mboni za Yehova ku Mexico. Anawonjezera nyumba zatsopano zokwana 14, zomwe zina mwa izo zinali nyumba zogona antchito odzipereka amene amatumikira pa ofesi ya nthambiyo, nyumba yosindikizira mabuku, ndi nyumba ya maofesi.

Pofuna kuthandizira ntchito yomanga imeneyi, antchito odzipereka oposa 730 ochokera ku Canada, Great Britain, United States, ndi mayiko ena anatumikira mogwirizana ndi antchito odzipereka ambirimbiri ochokera m’madera onse a ku Mexico. Kuwonjezera pamenepo, Mboni zoposa 28,000 zimene zimasonkhana m’mipingo pafupifupi 1,600 imene ili pafupi ndi ofesi ya nthambiyi zinali kuthandiza nawo ntchito yomangayi pa Loŵeruka ndi Lamlungu. Onse anatumikira ndi mtima wofunitsitsa ndipo anagwiritsa ntchito luso lawo kwaulere. Anaona kuti ndi mwayi kutumikira Yehova m’njira imeneyi. Pa ntchito yonse yomangayo, iwo sanaiŵale mawu ouziridwa amene ali pa Salmo 127:1 akuti: “Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.”

Mavuto Amene Amakumana Nawo

Kodi ndi mavuto otani amene abale odzipereka a m’mayiko ena amakumana nawo akamatumikira m’dziko lachilendo? Tamvani zina mwa zimene amakumana nazo. Curtis ndi Sally, banja la ku United States, athandiza ntchito yomanga ku Germany, India, Mexico, Paraguay, Romania, Russia, Senegal, ndi Zambia. Curtis anati: “Vuto loyamba linali kumusiya mwana wathu wamkazi, amene anali mpainiya [mtumiki wa nthaŵi zonse], ndiponso kusiya mpingo wakwathu ku Minnesota. Ine ndi mkazi wanga takhala tikusonkhana mumpingo umenewu kwa zaka 24, ndipo tinauzoloŵera.”

Sally anati: “Kukhala m’malo achilendo n’kovuta kwambiri, makamaka kwa akazi kusiyana ndi amuna, koma ndinaphunzira kuti n’zotheka kusintha. Ndinaphunzira kupirira tizilombo, tomwe tinali tambiri zedi.” Anawonjezera kuti: “M’dziko lina, tinkagona antchito odzipereka okwana khumi m’nyumba imodzi yopanda kitchini ndiponso ya mabafa aŵiri okha basi. Kumeneko ndinaphunzira kukhala woleza mtima kwambiri.”

Kuphunzira chinenero chatsopano ndi vuto linanso limene limafuna khama ndi kudzichepetsa. Sharon, amene watumikira ndi mwamuna wake pa ntchito yomanga m’mayiko osiyanasiyana, anati: “Kusadziŵa chinenero cha m’dziko limene mukutumikira ndi vuto lalikulu. Poyambirira n’zovuta kwambiri kuti ugwirizane ndi abale ndi alongo ako auzimu pamene sungathe kulankhula momasuka. Zimenezo n’zokhumudwitsa kwambiri. Koma abale amene timakumana nawo mu ntchito yathu ya m’mayiko ena amatilezera mtima kwambiri ndipo amasamala kwambiri za moyo wathu. Pasanathe nthaŵi yaitali, timakhala tikuyesera kulankhulana.”

Kulalikira Kumafuna Kulimba Mtima

Ngakhale kuti antchito odzipereka amenewo amathandizira kwambiri kuti ntchito yomanga ipite patsogolo, amazindikira kuti koposa zonse, iwo ndi alaliki a uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Motero, iwo amachita nawo mokwanira ntchito yolalikira imene mipingo yomwe amasonkhana nawo imachita. Åke ndi Ing-Mari, banja limene lathandiza nawo ntchito yomanga ku Guadeloupe, Malawi, Mexico, ndi Nigeria, anavomereza kuti kugwiritsa ntchito chinenero china mu utumiki wa kumunda m’dziko lachilendo kumafuna kulimba mtima.

Ingi-Mari anati: “Poyamba sitinathe kulalikira nawo mokwanira, chifukwa nthaŵi zonse muutumiki tinali kuyenda ndi Mboni za komweko, ndipo poopa kuchita manyazi, nthaŵi zambiri tinali kuwasiyira iwowo kulankhula. Komano tsiku lina m’maŵa, tinaganiza zopita tokha mu utumiki wa kumunda. Tinanyamuka miyendo ikunjenjemera ndiponso mitima ikugunda. Tinakumana ndi mkazi wina wachitsikana amene anamvetsera ulaliki umene ndinakonzekera. Ndinaŵerenga lemba ndi kum’gaŵira buku. Mkaziyo anati: ‘Ndili ndi funso. Ndili ndi wachibale wanga amene amaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kodi ndingatani kuti nanenso ndiziphunzira?’ Ndinasoŵa chonena. Ndiyeno ndinalimba mtima ndi kumuuza kuti tiziphunzira Baibulo.”

Ingi-Mari anawonjezera kuti: “Tangoganizani chimwemwe changa ndi kuyamikira kwanga Yehova chifukwa chodalitsa kuyesetsa kwathu ndi kufunitsitsa kwathu kuuza ena choonadi.” Mkazi ameneyu anapita patsogolo ndipo anabatizidwa n’kukhala Mboni pa msonkhano wachigawo mu mzinda wa Mexico. Åke ndi Ing-Mari anafotokoza mwachidule za utumiki wawo kuti: “Ntchito yathu yomanga m’madera osiyanasiyana timaiona kukhala ya mtengo wapatali kwambiri, koma palibe chimene chingapose chimwemwe ndi chisangalalo chimene chimakhalapo chifukwa chothandiza munthu kuloŵa m’choonadi.”

Mtima Wodzipereka

Nzoona kuti antchito odzipereka amene amasiya achibale awo ndi anzawo, amadzimana kuti atumikire abale awo m’mayiko ena, koma amapeza chimwemwe chosaneneka. Kodi ndi chimwemwe chotani chimene amakhala nacho?

Howard, amene watumikira ndi mkazi wake, Pamela, ku Angola, Colombia, Ecuador, El Salvador, Guyana, Mexico, ndi Puerto Rico anati: “Ndi mwayi waukulu kukumana ndi abale ndi alongo a m’mayiko osiyanasiyana ndi kudzionera wekha mgwirizano wachikondi wa ubale wathu wa padziko lonse. Nthaŵi zambiri timaŵerenga za ubale umenewu, koma ukakhala pamodzi ndi abale ena a chikhalidwe chosiyana komanso okula mosiyana ndiponso kutumikira nawo limodzi, umatha kumvetsa kwambiri kuti ubale wathu ndi wamtengo wapatali zedi.”

Gary, amene wathandiza nawo ntchito yomanga ku Colombia, Costa Rica, Ecuador, Mexico, ndi Zambia, amaonanso kuti pulogalamu imeneyi yam’pindulitsa kwambiri. Iye anati: “Zimene ndaphunzira kwa zaka zimenezi mwa kucheza ndi abale okhwima mwauzimu amene akutumikira m’nthambi za m’mayiko amene ndakhala ndikutumizidwa zandithandiza kukhala wokonzeka mokwanira kuthana ndi mavuto amene ndimakumana nawo m’ntchito imene ndapatsidwa. N’zolimbikitsa chikhulupiro kwambiri chifukwa zimapatsa mpata woona mgwirizano umene uli m’gulu la Yehova padziko lonse. Mgwirizano umenewu suona kusiyana kwa chinenero, mtundu, ndi chikhalidwe.”

Pakadali pano, ntchito yomanga ku Mexico inatha, ndipo nyumba za panthambi zimene amawonjezerazo anazipatulira chaka chino. Chifukwa cha kukonda kwawo Mulungu, atumiki a m’mayiko ena ndiponso antchito odzipereka a m’mayiko ena athandiza kwambiri kupititsa patsogolo kulambira koona ku Mexico ndi mayiko ena. Mboni za Yehova padziko lonse zikuyamikira mtima wawo wodzipereka ndi wodzimana umene wawachititsa kukatumikira abale awo achikristu m’mayiko ena.

[Chithunzi patsamba 25]

Ecuador

[Chithunzi patsamba 25]

Colombia

[Chithunzi patsamba 25]

Angola

[Chithunzi patsamba 26]

Ntchito yomanga nyumba zatsopano pa nthambi ya ku Mexico ikuyambika

[Chithunzi patsamba 26]

Maluŵa a pa nthambi

[Chithunzi patsamba 26]

Pansipa: Ena mwa anthu a mu Dipatimenti Yomanga kumaso kwa mbali ina ya nyumba zatsopano

[Chithunzi patsamba 27]

Antchito odzipereka ogwira ntchito yomanga amasangalala kugwira nawo ntchito yolalikira ndi mipingo ya m’dzikolo