Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandizidwa Poonabe Magazi Kukhala Opatulika

Kuthandizidwa Poonabe Magazi Kukhala Opatulika

Olengeza Ufumu Akusimba

Kuthandizidwa Poonabe Magazi Kukhala Opatulika

ATUMIKI a Yehova padziko lonse asonyeza kukhulupirika kwa Mulungu pankhani yoona magazi kukhala opatulika. (Machitidwe 15:28, 29) Gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru lathandiza abale onse achikristu. (Mateyu 24:45-47) Tiyeni tione zimene zinachitika chifukwa cha thandizo limeneli ku Philippines.

Nthambi ya ku Philippines inati: “Mu 1990 tinadziŵitsidwa kuti nthumwi zochokera ku Beteli ya ku Brooklyn zidzachititsa maphunziro apadera kuno ku Philippines. Abale anaitanidwa kuchokera ku nthambi zina za mu Asia monga ya ku Korea, Taiwan, ndi Hong Kong. Cholinga chinali choti athandize kukhazikitsa Madipatimenti Opereka Chidziwitso cha Zachipatala m’nthambi zawo ndiponso kukonza zoti pakhale Makomiti Olankhulana ndi Chipatala. Ku Philippines, makomiti ameneŵa poyambirira anakhazikitsidwa m’mizinda yaikulu inayi.” Makomitiwo anali oti ayesetse kupeza madokotala amene angavomere kutithandiza pa chikhulupiriro chathu chachikristu pankhani ya magazi. Analinso oti azithandiza abale pakabuka mavuto okhudza magazi.

Remegio anamusankha kukhala m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala ya ku Baguio. Pamene nthaŵi inali kupita, madokotala anayamba kuzindikira ntchito ya makomiti ameneŵa. Remegio akukumbukira nthaŵi ina imene madokotala angapo amene anakumana ndi Komiti Yolankhulana ndi Chipatala anafuna kudziŵa mmene angathandizire odwala a Mboni amene akana kulandira magazi. Remegio anati: “Madokotala anayamba kufunsa mafunso, koma ndinapanikizika chifukwa mafunso ake anali ovuta kwambiri.” Iye anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize pothana ndi vuto limeneli. Remegio anapitiriza kuti: “Wina ankati akamaliza kufunsa, madokotala ena ankakweza manja n’kufotokoza mmene iwo anachitira ndi vuto ngati limenelo.” Remegio anasangalala chifukwa cha thandizo limenelo, makamaka popeza nthaŵi ya mafunso ndi mayankhoyo inapitirira mpaka kutha maola aŵiri.

Tsopano kuli makomiti 21 m’dziko lonselo, ndipo abale okwana 77 akutumikira m’makomiti ameneŵa. Danilo, wa Mboni yemwe ndi dokotala, anati: “Madokotala akuzindikira kuti odwala awo omwe ndi Mboni amathandizidwa ndi gulu limene limawasamalira mwachikondi.” Dokotala wina poyamba ananyinyirika kuti amuchite opaleshoni mbale wina popanda kumuika magazi. Komabe, mbaleyo analimba kwambiri pa chikhulupiriro chake. Opaleshoniyo inachitika ndipo inayenda bwino kwabasi. Dipatimenti Yopereka Chidziwitso cha Zachipatala inati: “Dokotalayo anadabwa kwambiri pamene mbaleyo anapeza bwino. Iye anati: ‘Poona zimene zachitikazi, wina aliyense wa m’gulu lanu akadzafunika kumuchita opaleshoni yonga imeneyi popanda kumuika magazi, ndidzakonda kuichita.’”