Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Ngati Mkristu amva mawu koma osaona amene akulankhula, kodi ndiye kuti sichinanso koma ziwanda n’zimene zikum’vutitsa?
Ayi. Ngakhale kuti ziwanda zimachitadi zimenezo, anthu ambiri amene amva mawu koma osaona amene akulankhula kapena amene zawachitikira zinthu zina zosokoneza maganizo zomwe sangathe kuzifotokoza, atafufuza apeza kuti ali ndi matenda.
Ngakhale m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, anthu ankadziŵa bwino kuti nthaŵi zina ziwanda ndiponso matenda zinkayambitsa mavuto ofanana. Pa Mateyu 17:14-18, timaŵerengapo za mnyamata amene Yesu anamuchiritsa. Ngakhale kuti mnyamatayo anasonyeza zizindikiro za khunyu, ziwanda n’zimene zinayambitsa matenda akewo. Komabe, nthaŵi ina zimenezi zisanachitike, khamu la anthu odwala litapita kwa Yesu kuti likachiritsidwe, ena mwa iwo anali ‘ogwidwa ndi mizimu yoipa ndi akhunyu.’ (Mateyu 4:24) Mwachionekere, anthu ankadziŵa kuti ena amene anali ndi khunyu sanali oti agwidwa ndi ziwanda. Anali matenda enieni.
Akuti ena amene amadwala matenda ena oyambitsa misala, omwe nthaŵi zambiri munthu amatha kuchira akamwa mankhwala, amamva mawu koma osaona amene akulankhula kapena amaonetsa zizindikiro zina zimene zimasonyeza ngati agwidwa ndi mizimu. * Matenda enanso angayambitse kusokonezeka maganizo kumene kungachititse ena kuganiza molakwika kuti ziwanda n’zimene zayambitsa. Motero, ngakhale kuti munthu amene wamva mawu koma osaona amene akulankhula kapena zinthu zina zosokoneza maganizo zikamuchitikira safunika kunyalanyaza kuti n’ziwanda zimene zikumuvutitsa, ayenera kulimbikitsidwa kufufuza kuti aone ngati angakhale matenda amene akuchititsa zimenezo.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Onani nkhani yakuti “Taking the Mystery out of Mental Illness” mu Galamukani! yachingelezi ya September 8, 1986. Imeneyi ndi magazini inzake ya Nsanja ya Olonda.