Asanaphunzire ndi Ataphunzira Kale Loipa, Tsogolo Labwino
“Yandikirani kwa Mulungu, Ndipo Adzayandikira kwa Inu”
Asanaphunzire ndi Ataphunzira Kale Loipa, Tsogolo Labwino
“MAWU a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, . . . nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) Ananena zimenezi ndi mtumwi Paulo pofotokoza za mphamvu yaikulu imene uthenga wa Mulungu uli nayo. Zoti mawu a Mulungu amatha kum’fikadi munthu pamtima zinaoneka makamaka m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Amene anasanduka Akristu nthaŵi imeneyo anavala umunthu watsopano, ngakhale kuti makhalidwe oipa anali ofala.—Aroma 1:28, 29; Akolose 3:8-10.
Mphamvu ya mawu a Mulungu yotha kusintha munthu, malinga ndi mmene Baibulo limanenera, ikuonekanso masiku ano. Mwachitsanzo, taganizirani za bambo wina wamtali, wamphamvu zake, Richard. Chifukwa anali wosachedwa kupsa mtima, Richard amati munthu akangom’puta pang’ono, amamenyana naye. Anali ndi mavuto ambiri pa moyo wake chifukwa cha chiwawa. Richard mpaka analowa bungwe la anthu ochita maseŵera a nkhonya. Anachita khama pa maseŵera amenewa, ndipo anasanduka katswiri woposa onse wa maseŵera a nkhonya ku Westphalia, ku Germany. Richard anali kumwanso mowa kwambiri, ndipo nthaŵi zambiri ankachita ndewu ndiponso mapokoso. Nthaŵi ina patachitika ndewu yoteroyo, munthu mmodzi anaphedwa, ndipo Richard anatsala pang’onong’ono kuti apite ku ndende.
Nanga bwanji banja lake? Richard akunena kuti: “Ine ndi Heike tisanaphunzire Baibulo, aliyense ankangochita zimene akufuna payekha. Heike ankakhala nthaŵi yaitali ali ndi atsikana anzake, pamene ine ndinkasangalala ndi maseŵera anga apamtima amene anali nkhonya, kuyenda pamafunde nditakwera pakathabwa, komanso kudumphira m’madzi.”
Pamene Richard ndi Heike anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, Richard anagwa ulesi ataona zinthu zambiri zimene amafunikira kusintha m’moyo wake kuti agwirizane ndi malamulo apamwamba kwambiri amene ali m’Mawu a Mulungu, chifukwa zimaoneka zovuta kwambiri. Koma pamene anayamba kum’dziŵa bwino Yehova Mulungu, Richard anayamba kulakalaka kum’sangalatsa. Richard anazindikira kuti Mulungu amadana ndi anthu amene amakonda chiwawa, komanso anthu amene amaona zachiwawa ngati zosangalatsa. Richard anaphunzira kuti: “Moyo wa [Yehova] umuda . . . iye wakukonda chiwawa.”—Salmo 11:5.
Ndiponso, chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha m’paradaiso pa dziko lapansi chinasangalatsa kwambiri Richard ndi Heike. Anafuna kuti adzakhale m’paradaiso ameneyo limodzi! (Yesaya 65:21-23) Atamva pempho loti, “yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu,” Richard anakhudzidwa mtima kwambiri. (Yakobo 4:8) Anaona phindu lomvera malangizo ouziridwa akuti: “Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse. Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka.”—Miyambo 3:31, 32.
Ngakhale kuti Richard ankafunitsitsa kuti asinthe, anazindikira kuti sangathe kutero payekha. Anazindikira kufunika kopempha Mulungu kuti am’thandize m’pemphero. Choncho, anachita zogwirizana ndi zimene Yesu ananena kwa atumwi ake kuti: “Chezerani ndi kupemphera, kuti mungaloŵe m’kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.”—Mateyu 26:41.
Ataphunzira mmene Mulungu amaonera chiwawa komanso kupsa mtima pafupifupi, Richard sanakayikirenso koma anazindikira kuti maseŵera a nkhonya ndi
osayenera. Atathandizidwa ndi Yehova komanso kulimbikitsidwa ndi anthu amene ankaphunzira naye Baibulo, Richard anasiya chiwawa. Anasiya maseŵera a nkhonya komanso ndewu ndi mapokoso, ndipo anaganiza zochitapo kanthu kuti moyo wake wabanja ukhale wabwino. “Kuphunzira choonadi cha m’Baibulo kwandithandiza kuti ndiziyamba ndaganiza kaye ndisanachite kanthu kalikonse,” akutero Richard, amene tsopano ali woyang’anira wofatsa mu mpingo wina wa Mboni za Yehova. Iye akupitiriza kunena kuti: “Tsopano ndikamachita zinthu ndi mkazi wanga ndi ana anga, ndimatsatira mfundo zakuti tizikondana ndi kulemekezana. Chifukwa cha zimenezi, banja lathu tsopano n’logwirizana kwambiri.”Anthu ena osamvetsa zinthu bwino nthaŵi zina amanena kuti Mboni za Yehova zimawononga mabanja a anthu. Koma zitsanzo za anthu ngati Richard zimasonyeza kuti zimenezo si zoona. Zoona zake n’zakuti, choonadi cha Baibulo chingathandize mabanja kukhala olimba, komanso anthu amene anali ndi kale loipa kukhala ndi tsogolo labwino.—Yeremiya 29:11.
[Mawu Otsindika patsamba 9]
“Chiyembekezo cha dziko lapansi la paradaiso chinandilimbikitsa kuti ndisinthe”
[Bokosi patsamba 9]
Mfundo za Baibulo Zimathandiza
Baibulo likhoza kusintha kwambiri miyoyo ya anthu. Pano pali mfundo zina za m’Malemba zimene zathandiza anthu achiwawa kuti asinthe:
“Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi.” (Miyambo 16:32) Kukanika kubweza mkwiyo ndi chizindikiro cha kufooka, osati mphamvu.
“Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo.” (Miyambo 19:11) Kuzindikira ndi kulingalira bwino kumathandiza munthu kuti adziŵe zifukwa zenizeni zimene zachititsa kusamvana ndipo kungabweze mkwiyo.
‘Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga kuti ungaphunzire mayendedwe ake.’ (Miyambo 22:24, 25) Akristu mwanzeru amapeŵa kuyanjana ndi anthu amene sachedwa kukwiya.