Chifukwa Chake Sitingaime Patokha
Chifukwa Chake Sitingaime Patokha
“Aŵiri aposa mmodzi . . . akagwa, wina adzautsa mnzake.”—Inatero Mfumu Solomo
MFUMU SOLOMO ya Israyeli wakale inati: “Aŵiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphoto yabwino m’ntchito zawo. Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake; koma tsoka wakugwa wopanda wom’nyamutsa.” (Mlaliki 4:9, 10) Choncho, munthu wanzeru ameneyu amene anaonetsetsa khalidwe la anthu, anagogomezera mfundo yokhala ndi anthu ena ndiponso ubwino wosadzipatula. Komabe, ameneŵa sanali maganizo ake chabe. Zimene Solomo ananenazi zinali nzeru za Mulungu ndipo ndi amene anamuuzira kuti alembe zimenezi.
Si bwino kudzipatula. Anthu amafunika anthu ena. Tonsefe timafuna kupeza mphamvu ndi thandizo kwa anthu ena. Mwambi wa m’Baibulo umati: “Wopanduka [“Wodzipatula,” NW] afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.” (Miyambo 18:1) Choncho si zodabwitsa kuti akatswiri a sayansi ya kakhalidwe ka anthu amalimbikitsa anthu kukhala ndi anzawo ndiponso kuganizira anthu ena.
Ina mwa mfundo zimene Pulofesa Robert Putnam ananena kuti zingathandize anthu kuyambanso kukhalira limodzi ndiyo “kulimbikitsa kufunika kokhala ndi chikhulupiriro chauzimu.” Mboni za Yehova zikuchita bwino kwambiri pambali imeneyi chifukwa chakuti ndi zotetezeka m’mipingo yangati banja imene ili padziko lonse lapansi. Mogwirizana ndi mawu a mtumwi Petro, izo ‘zimakonda gulu lonse la abale’ amene ‘amaopa Mulungu’ ndiponso amam’patsa ulemu. (1 Petro 2:17, NW) Mboni zimapeŵanso kudzipatula ndi mavuto amene amabwera chifukwa chodzipatula, chifukwa chakuti zinthu zabwino zambiri zokhudza kulambira koona zimawapangitsa kuchita zinthu zothandiza anthu amene amakhala nawo pafupi kuphunzira choonadi cha m’Mawu a Mulungu, Baibulo.—2 Timoteo 2:15.
Chikondi Ndiponso Kukhala ndi Ena Zinasintha Moyo Wawo
Mboni za Yehova ndi gulu logwirizana limene aliyense m’gululi amagwira ntchito yofunika kwambiri. Mwachitsanzo, tamvani nkhani ya Miguel, Froylán, ndi Alma Ruth, anthu atatu a m’banja limodzi la ku Latin-America. Anabadwa ndi matenda a m’mafupa amene amachititsa munthu kukhala wamfupi kwambiri. Onseŵa amayenda pa njinga za opuwala. Kodi kusonkhana ndi Mboni kwathandiza bwanji moyo wawo?
Miguel anati: “Panali masiku ena amene ndinali kuvutika maganizo kwambiri, koma nditayamba kusonkhana ndi anthu a Yehova, moyo wanga unasintha. Kudzipatula n’koipa zedi.
Kusonkhana ndi okhulupirira anzanga pa misonkhano yachikristu, kukhala nawo mlungu uliwonse, kunandithandiza kwambiri kukhala wosangalala.”Alma Ruth anawonjezera kuti: “Nthaŵi zina ndinali kuvutika maganizo kwambiri; ndinkakhumudwa kwambiri. Koma nditaphunzira za Yehova, ndinaona kuti ndikhoza kukhala naye paubwenzi wapamtima. Chimenechi chinakhala chinthu chofunika kwambiri pamoyo wanga. Banja lathu latithandiza kwambiri, ndipo zimenezi zatipangitsa kukhala ogwirizana kwambiri.”
Bambo a Miguel anamuphunzitsa mwachikondi kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba. Ndiyeno Miguel anathandiza Froylán ndi Alma Ruth kudziŵanso kuŵerenga ndi kulemba. Izi zinali zofunika kwambiri pamoyo wawo wauzimu. Alma Ruth akuti: “Kudziŵa kuŵerenga kunatithandiza kwambiri chifukwa tinayamba kudya mwauzimu mwa kuŵerenga Baibulo ndi mabuku othandiza kuphunzira Baibulo.”
Panopo, Miguel akutumikira monga mkulu wachikristu. Froylán waŵerenga Baibulo lonse maulendo asanu ndi anayi. Alma Ruth wawonjezera zochita zake potumikira Yehova mwa kutumikira monga mpainiya, kapena kuti wolalikira Ufumu wanthaŵi zonse, kuyambira mu 1996. Iye anati: “Chifukwa cha thandizo la Yehova ndakwanitsa zimenezi, popeza ndili ndi alongo anga okondedwa amene amandithandiza kulalikira komanso kuphunzitsa pochititsa maphunziro a Baibulo 11 amene ndinayambitsa.”
Nayenso Emelia amene anachita ngozi imene inachititsa kuti aziyenda pa njinga ya opuwala chifukwa chovulala miyendo ndi msana, wapereka chitsanzo chabwino. Mboni za Yehova ku mzinda wa Mexico zinaphunzira naye Baibulo, ndipo anabatizidwa mu 1996. Emelia akuti: “Ndisanaphunzire choonadi, ndinkafuna kudzipha; sindinkafuna kukhala ndi moyo. Ndinkadziona kuti ndinali wopanda ntchito, ndinkalira usana ndi usiku. Koma nditayamba kusonkhana ndi anthu a Yehova, ndinaona kuti abale amandikonda. Chidwi chimene amasonyeza kwa ine chandilimbikitsa kwambiri. Mmodzi mwa akulu mu mpingomo ali ngati mchimwene wanga kapena bambo anga. Iye ndi atumiki ena otumikira amanditenga popita ku misonkhano ndiponso pokalalikira ndili pa njinga yanga ya opuwala.”
José, amene anabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova mu 1992, amakhala yekha. Ali ndi zaka 70, ndipo anapuma pantchito mu 1990. José ankavutika maganizo, koma Mboni ina itam’lalikira, nthaŵi yomweyo anayamba kupezeka pamisonkhano yachikristu. Anasangalala ndi Afilipi 1:1; 1 Petro 5:2) Okhulupirira anzake ngati ameneŵa ndi ‘chomutonthoza mtima.’ (Akolose 4:11) Amapita naye kwa dokotala, amapita kukacheza kunyumba kwake, ndiponso anamuthandiza maulendo anayi amene anam’chita opaleshoni. Iye anati: “Amasonyeza kuti amandidera nkhaŵa, lilidi banja langa. Ndimasangalala kwambiri kukhala nawo.”
zimene anamva ndiponso zimene anaona kumeneko. Mwachitsanzo, anaona ubwenzi wa abale ndipo anaona kuti anali kumudera nkhaŵa monga munthu payekha. Tsopano akulu ndi atumiki otumikira a mu mpingo wake ndi amene akumusamalira. (Muli Chimwemwe Chenicheni M’kupatsa
Pamene Mfumu Solomo inati “aŵiri aposa mmodzi,” inali itangonena kumene kupanda phindu kothera mphamvu zonse za munthu pofuna kulemera. (Mlaliki 4:7-9) Zimenezi n’zimene anthu ambiri masiku ano amafunafuna ndi mtima wonse, ngakhale kuti zimenezo zingawachititse kusacheza ndi a m’banja mwawo kapena anthu ena.
Mtima wa umbombo ndi wodzikonda umenewu wapangitsa anthu ambiri kudzipatula. Izi sizinawabweretsere chimwemwe pamoyo wawo, chifukwa anthu amene ali ndi mtima umenewu nthaŵi zambiri amakhala okhumudwa ndiponso othedwa nzeru. Koma, nkhani za anthu amene tangowafotokoza kumenewa zikusonyeza ubwino wosonkhana ndi anthu amene amatumikira Yehova ndipo amatero chifukwa chomukonda ndiponso chokonda anthu anzawo. Kupezeka pa misonkhano yachikristu nthaŵi zonse, kuthandizidwa ndi Akristu anzawo ndi kuwadera nkhaŵa, ndiponso kuchita utumiki mwachangu zinali zinthu zofunika kwambiri zimene zinawathandiza anthu ameneŵa kuthana ndi kuvutika maganizo chifukwa chodzipatula.—Miyambo 17:17; Ahebri 10:24, 25.
Popeza timadalirana, n’zachidziŵikire kuti kuchitira zinthu anthu ena kumabweretsa chimwemwe. Albert Einstein, amene ntchito yake inathandiza anthu ena, anati: “Kufunika kwa munthu . . . kuzioneka ndi zimene amapatsa anthu ena osati zimene amalandira.” Izi n’zogwirizana ndi mawu a Ambuye wathu Yesu Kristu akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Choncho, ngakhale kuti ndi bwino kuti anthu azitikonda, n’zothandizanso kwambiri pamoyo wa munthu kusonyeza kukonda anthu ena.
Woyang’anira woyendayenda amene kwa zaka zambiri wayendera mipingo, kuilimbikitsa mwauzimu ndi kuthandiza Akristu osauka kumanga malo osonkhanira, ananena maganizo ake motere: “Chimwemwe chimene ndapeza chifukwa chotumikira abale anga ndi kuwaona akusangalala moyamikira zimandilimbikitsa kufunafuna njira zimene ndingathandizire ena. Zimene ndaona n’zakuti kuganizira anthu ena ndicho chinsinsi cha chimwemwe. Ndipo ndikudziŵa kuti monga akulu, tiyenera kukhala ‘monga pobisalira mphepo, . . . monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.’”—Yesaya 32:2.
N’kokoma Kukhalira Pamodzi Mogwirizana
Ndithudi tingapeze phindu lochuluka ndiponso chimwemwe chenicheni pothandiza ena ndiponso pokhala ndi anthu otumikira Yehova. Wamasalmo anati: “Onani, n’kokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!” Salmo 133:1) Kugwirizana m’banja n’kofunika kwambiri pothandizana, monga taonera pankhani ya Miguel, Froylán, ndi Alma Ruth. Ndipo ndi dalitso zedi kukhala ogwirizana pa kulambira koona. Mtumwi Petro atalangiza amuna ndi akazi achikristu omwe ali pabanja, analemba kuti: “Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa.”—1 Petro 3:8.
(Ubwenzi weniweni umapindulitsa kwambiri pa maganizo a munthu ndiponso pa moyo wake wauzimu. Mtumwi Paulo polankhula ndi okhulupirira anzake, anawalimbikitsa kuti: “Limbikitsani amantha mtima [“ovutika maganizo,” NW] chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse. . . . Nthaŵi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.”—1 Atesalonika 5:14, 15.
Choncho, funani njira zabwino zochitira ena zinthu zabwino. ‘Chitirani onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro,’ chifukwa zimenezi zidzathandiza kwambiri moyo wanu kukhala watanthauzo ndipo zidzakuthandizani kukhala wosangalala. (Agalatiya 6:9, 10) Yakobo amene anali wophunzira wa Yesu, analemba kuti: “Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikam’soŵa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nawo, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosoŵa za pathupi; kupindula kwake n’chiyani?” (Yakobo 2:15, 16) Yankho la funsoli n’lodziŵikiratu. Tifunika ‘kusapenyerera za ife tokha, koma tonse tipenyererenso za anzathu.’—Afilipi 2:4.
Kuwonjezera pa kuthandiza ena mwa kuwapatsa zinthu ngati akufunikira thandizo lapadera kapena pakagwa masoka, Mboni za Yehova n’zotanganidwa kwambiri kuthandiza anzawo mwa njira yofunika kwambiri, kuwalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Kulengeza uthenga wa chiyembekezo ndi wolimbikitsa umenewu kumene Mboni zoposa 6,000,000 zikuchita, kumatsimikizira kuti zimaganizira anthu ndiponso zimawakonda. Koma kuwathandiza ndi Malemba Opatulika kumathandizanso kukwaniritsa chinthu china chofunika kwa anthu. Kodi ndi chiyani?
Kukwaniritsa Chinthu Chofunika Kwambiri
Kuti tipeze chimwemwe chenicheni, tifunika kukhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu. Anthu ena anena kuti: “Mfundo yakuti, munthu kulikonse ndiponso nthaŵi zonse, kuyambira pachiyambi mpaka pakalipano, amaona kuti ayenera kudalira chinachake chimene amachiona kuti n’chapamwamba ndiponso champhamvu kwambiri kuposa iye, zimasonyeza kuti munthu anabadwa ndi chikhumbo chofuna kupembedza ndipo asayansi ayenera kuvomereza zimenezi. . . . Tiyenera kuchita mantha, kudabwa ndiponso kupereka ulemu poona kuti anthu kulikonse amafunafuna ndiponso kukhulupirira chinthu chapamwamba kwambiri.”—Linatero buku lakuti Man Does Not Stand Alone, lolembedwa ndi A. Cressy Morrison.
Yesu Kristu anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) Anthu siziwayendera bwino ngati adzipatula kwa anzawo kwa nthaŵi yaitali. Komabe, kudzipatula kwa Mlengi wathu, n’koipa kuposa pamenepa. (Chivumbulutso 4:11) “Kum’dziŵadi Mulungu” ndiponso kutsatira zimenezi kuyenera kukhala chinthu chofunika pamoyo wathu. (Miyambo 2:1-5) Indedi, tiyenera kutsimikiza mtima kukwaniritsa kusoŵa kwathu kwauzimu, popeza sitingaime patokha ndiponso popanda Mulungu. Moyo wosangalatsa ndiponso wopindulitsa kwambiri umadalira ubwenzi wabwino ndi Yehova, “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”—Salmo 83:18.
[Chithunzi patsamba 5]
Miguel: “Panali masiku ena amene ndinali kuvutika maganizo kwambiri, koma nditayamba kusonkhana ndi anthu a Yehova, moyo wanga unasintha”
[Chithunzi patsamba 5]
Alma Ruth: “Nditaphunzira za Yehova, ndinaona kuti ndikhoza kukhala naye paubwenzi wapamtima”
[Chithunzi patsamba 6]
Emelia: “Ndisanaphunzire choonadi, . . . ndinkadziona kuti ndine wopanda ntchito”
[Chithunzi patsamba 7]
Kusonkhana ndi olambira oona kumathandiza kukwaniritsa kusoŵa kwathu mwauzimu